Vulani Umunthu Wakale Ndipo Musauvalenso

Vulani Umunthu Wakale Ndipo Musauvalenso

Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.”​—AKOL. 3:9.

NYIMBO: 83, 129

1, 2. Kodi anthu anena zotani pofotokoza za Mboni za Yehova?

 ANTHU ambiri amanena kuti anthu a Yehova ali ndi makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, munthu wina amene analemba nkhani yokhudza abale ndi alongo athu a ku Germany anati: “A chipani cha Nazi ankadana kwambiri ndi Mboni za Yehova. . . . Pofika mu 1939, a Mboni za Yehova okwana 6,000 anali ataikidwa m’ndende.” Ngakhale kuti ankazunzidwa koopsa, wolemba nkhaniyo ananena kuti a Mboniwo anasonyeza kuti “ndi odalirika komanso odekha” ndipo sanasiye “kukhala okhulupirika komanso ogwirizana.”

2 Nakonso ku South Africa, anthu anaona umboni wakuti anthu a Yehova ali ndi makhalidwe abwino. M’mbuyomo, a Mboni osiyana khungu sankaloledwa kuti azisonkhana limodzi. Koma Lamlungu pa 18 December 2011, zinali zosangalatsa kuona abale ndi alongo oposa 78,000 a mitundu yosiyanasiyana a ku South Africa komweko komanso akumayiko ena atasonkhana musitediyamu yaikulu kwambiri ku Johannesburg kuti aphunzitsidwe ndi Yehova. Pofotokoza za anthu amene anasonkhanawo, mmodzi wa akuluakulu a pasitediyamuyo anati: “Sindinaonepo gulu la anthu amakhalidwe abwino ngati limeneli musitediyamuyi. Onse avala bwino kwambiri ndipo ayeretsa bwino malowa. Koma chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti alipo a mitundu yosiyanasiyana.”

3. N’chiyani chimatithandiza kuti tizigwirizana kwambiri ndi abale athu?

3 Mawu ngati amenewa amasonyezeratu kuti mgwirizano wathu padziko lonse ndi wapadera kwambiri. (1 Pet. 5:9) Koma kodi n’chiyani chimatithandiza kukhala osiyana ndi magulu ena? Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera zimatithandiza kuti tiziyesetsa ‘kuvula umunthu wakale n’kuvala umunthu watsopano.’​—Akol. 3:9, 10.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi, ndipo n’chifukwa chiyani?

4 Munthu akhoza kuvula umunthu wakale koma n’kumavutika kuti asauvalenso. Munkhaniyi tikambirana mmene tingavulire umunthu wakale ndiponso chifukwa chake tiyenera kuuvula mwamsanga. Tionanso kuti n’zotheka kuchita zimenezi ngakhale pamene zoipazo zatilowerera kwambiri. Tikambirananso zimene anthu omwe akhala m’choonadi kwa zaka zambiri angachite kuti asavalenso umunthu wakale. N’chifukwa chiyani tiyenera kukumbutsana mfundo zimenezi? N’zomvetsa chisoni kuti atumiki a Yehova ena ayamba kusintha khalidwe n’kumachita zimene ankachita kale. Choncho m’pofunika kutsatira malangizo akuti: “Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.”​—1 Akor. 10:12.

‘CHITITSANI ZIWALO ZANU KUKHALA ZAKUFA PA NKHANI YA DAMA’

5. (a) Perekani fanizo losonyeza chifukwa chake tiyenera kuvula umunthu wakale mwamsanga. (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Mogwirizana ndi Akolose 3:5-9, kodi ndi makhalidwe ati akale amene tiyenera kusiya?

5 Kodi mungatani ngati zovala zanu zada kwambiri mwina mpaka kufika ponunkha? Mukhoza kuvula zovalazo mwamsanga. Tingachitenso bwino kumvera mwamsanga lamulo loti tisiye makhalidwe akale omwe Mulungu sasangalala nawo. Tiyenera kumvera malangizo osapita m’mbali amene Paulo anauza Akhristu akale akuti: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu.” Tiyeni panopa tikambirane za zinthu ziwiri zimene Paulo ananena kuti tiyenera kusiya zomwe ndi dama ndiponso zinthu zodetsa.​—Werengani Akolose 3:5-9.

6, 7. (a) Kodi mawu a Paulo amasonyeza bwanji kuti munthu ayenera kuchita zinthu mwamphamvu kuti avule umunthu wakale? (b) Kodi Sakura anali ndi khalidwe lotani, nanga zinatheka bwanji kuti asinthe?

6 Dama. Mawu a m’Baibulo amene anawamasulira kuti “dama” amanena za kugonana pakati pa anthu amene sanakwatirane motsatira malamulo komanso pakati pa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Paulo anauza Akhristu anzake kuti ‘achititse ziwalo za thupi lawo kukhala zakufa ku dama’ kapena kuti asiyiretu kulakalaka chilichonse chokhudza dama. Mawu amene Paulo anagwiritsa ntchitowa akusonyeza kuti munthu ayenera kuchita zinthu mwamphamvu kuti asiye kulakalaka zoipa. Koma chomwe tiyenera kudziwa n’chakuti n’zotheka kuchita zimenezi.

7 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira mlongo wina wa ku Japan dzina lake Sakura. a Ali mwana, ankavutika kupeza anzake enieni ndipo ankakhala wokhumudwa. Atakwanitsa zaka 15, anayamba kugonana ndi anthu osiyanasiyana n’cholinga choti azimva ngati ali ndi anzake apamtima. Iye ananena modandaula kuti: “Izi zinachititsa kuti ndichotse mimba katatu.” Anafotokozanso kuti: “Poyamba, ndikagonana ndi anthu ndinkamva ngati ndine wofunika komanso ndimakondedwa. Koma kenako ndinayamba kudziona ngati wachabechabe.” Sakura anapitiriza khalidweli mpaka pamene anakwanitsa zaka 23. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye ankakonda kwambiri zimene ankaphunzira ndipo Yehova anamuthandiza kuti asiye kuchita dama komanso kudziimba mlandu. Panopa Sakura akuchita upainiya ndipo sakusowanso anthu ocheza nawo. Iye ananena kuti: “Ndine wosangalala kwambiri chifukwa tsiku lililonse ndimaona umboni woti Yehova amandikonda.”

ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUSIYA ZINTHU ZODETSA

8. Kodi ndi makhalidwe ena ati amene angachititse kuti Mulungu aone kuti ndife odetsedwa?

8 Zinthu zodetsa. Mawu a m’Baibulo amene anawamasulira kuti “zinthu zodetsa” amatanthauza zambiri osati zokhudza kugonana basi. Akhoza kutanthauza zinthu monga kusuta kapena nthabwala zotukwana. (2 Akor. 7:1; Aef. 5:3, 4) Angatanthauzenso zinthu zimene munthu angachite ali kwayekha monga kuwerenga mabuku onena zachiwerewere kapena kuonera zolaula ndipo zimenezi zingamuchititse kuti ayambe khalidwe lodetsa la kuseweretsa maliseche.​—Akol. 3:5. b

9. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamakonda kuonera zolaula?

9 Anthu amene amakonda kuonera zolaula amakhala ndi “chilakolako cha kugonana” champhamvu moti sangathe kudziletsa ndipo izi zingachititse kuti akhale achiwerewere. Ochita kafukufuku anapeza kuti anthu amene amakonda kuonera zolaula zimawavuta kusiya ngati mmene zimakhalira ndi zidakwa kapena anthu omwe amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. M’pake kuti anthu amene amaonera zolaula nthawi zambiri amadziimba mlandu, sagwira bwino ntchito, amakhala ndi mavuto a m’banja komanso nthawi zina amadzipha. Munthu wina atakwanitsa kukhala chaka chathunthu osaonera zolaula ananena kuti: “Panopa ndasiya kudziona ngati wachabechabe.”

10. N’chiyani chinathandiza Ribeiro kuti asiye kuonera zolaula?

10 Pali anthu ambiri amene amavutika kuti asiyiretu kuonera zolaula. Koma zimene zinachitikira munthu wina wa ku Brazil dzina lake Ribeiro zimasonyeza kuti n’zotheka kusiyiratu. Ribeiro anachoka kwawo ali wachinyamata ndipo kenako anayamba kugwira ntchito pakampani ina ya mapepala. Kumeneko anayamba kuona zithunzi zolaula. Iye ananena kuti: “Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kukonda kwambiri zithunzizi. Zinafika poipa kwambiri moti chibwenzi changa chikakhala m’nyumba, ndinkalakalaka kuti chituluke kuti ndiyambe kuonera mafilimu olaula.” Tsiku lina ali kuntchito anaona buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lili pa mulu wa mabuku ena. Iye analitenga n’kuyamba kuliwerenga. Zimene anamva m’bukulo zinamulimbikitsa kuti ayambe kuphunzira ndi Mboni za Yehova koma zinamutengera nthawi yaitali kuti asiye kuonera zolaula. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asiyiretu? Iye anati: “Kupemphera, kuphunzira Baibulo komanso kuganizira kwambiri zimene ndaphunzira zinandithandiza kuyamikira kwambiri makhalidwe a Mulungu. Kenako ndinayamba kukonda kwambiri Yehova kuposa kuonera zolaula.” Mphamvu ya Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera zinathandiza Ribeiro kuti avule umunthu wake wakale moti anabatizidwa ndipo panopa ndi mkulu.

11. Kodi n’chiyani chingathandize munthu kuti asiyiretu kuonera zolaula?

11 N’zochititsa chidwi kuti chimene chinathandiza Ribeiro si kungophunzira Baibulo basi. Iye ankaganiziranso kwambiri zimene wawerenga n’cholinga choti uthenga wa m’Baibulowo umufike pamtima. Kupemphera ndiponso kusinkhasinkha zinamuthandiza kuti ayambe kukonda kwambiri Mulungu n’kusiya kukonda zolaula. Munthu akayamba kukonda kwambiri Yehova n’kumadana ndi zoipa amatha kusiya bwinobwino khalidwe loonera zolaula.​—Werengani Salimo 97:10.

TIYENERA KUSIYA KUPSA MTIMA, MAWU ACHIPONGWE KOMANSO KUNAMA

12. N’chiyani chinathandiza Stephen kuti asiye kulankhula mawu achipongwe?

12 Anthu amene amakonda kupsa mtima nthawi zambiri amalankhulanso mawu achipongwe. N’zosachita kufunsa kuti khalidwe limeneli likhoza kuyambitsa mavuto m’banja. M’bale wina wa ku Australia dzina lake Stephen ananena kuti: “M’mbuyomu ndinkakonda kutukwana ndipo sindinkachedwa kupsa mtima. Ine ndi mkazi wanga tinapatukana katatu ndipo tinkafuna kuthetsa banja lathu.” Koma kenako iwo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Kodi n’chiyani chinachitika Stephen atayamba kutsatira malangizo a m’Baibulo? Iye anati: “Banja lathu linayamba kuyenda bwino. Yehova wandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere mumtima komanso ndikhale wodekha. Koma kale ndinkangokhalira kukwiya ndipo ndinali ngati bomba limene likhoza kuphulika nthawi iliyonse.” Panopa Stephen ndi mtumiki wothandiza ndipo mkazi wake wakhala akuchita upainiya wokhazikika kwa zaka zambiri. Akulu amumpingo umene Stephen amasonkhana ananena kuti: “Stephen ndi m’bale wofatsa, wakhama komanso wodzichepetsa.” Sanamuonepo atakwiya. Kodi Stephen amaona kuti anatha kusintha payekha? Iye anati: “Sindikanalandira madalitso amene ndili nawo panopa ndikanapanda kulola kuti Yehova andithandize kusinthiratu makhalidwe anga.”

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kupsa mtima n’koopsa, nanga Baibulo limapereka chenjezo lotani?

13 M’pake kuti Baibulo limatichenjeza kuti tizipewa kupsa mtima, mawu achipongwe komanso kulalata. (Aef. 4:31) N’zomvetsa chisoni kuti anthu amene sapewa makhalidwewa amafika pochitanso chiwawa. Anthu ambiri a m’dzikoli amaona kuti kupsa mtima si nkhani yaikulu koma khalidweli limanyoza Mlengi wathu. Akhristu ambiri anayenera kusiya makhalidwe oipa kuti avale umunthu watsopano.​—Werengani Salimo 37:8-11.

14. Kodi n’zotheka kuti munthu wolusa asinthe n’kukhala wofatsa?

14 Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi mkulu wina wamumpingo wina ku Austria dzina lake Hans. Wogwirizanitsa ntchito ya akulu mumpingowo ananena kuti Hans ndi “m’bale wofatsa kwambiri.” Koma poyamba Hans sanali wofatsa. Ali wachinyamata, anayamba kumwa kwambiri mowa ndipo anali wolusa. Tsiku lina ataledzera, anakwiya kwambiri moti anapha chibwenzi chake. Iye anaweruzidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka 20. Moyo wakundendewo sunamuthandize kuti asinthe. Koma kenako mayi ake anakonza zoti mkulu wina akamuone kundendeko ndipo Hans anayamba kuphunzira Baibulo. Iye anati: “Zinandivuta kwambiri kuti ndivule umunthu wanga wakale. Koma malemba amene anandithandiza kwambiri ndi Yesaya 55:7 ndiponso 1 Akorinto 6:11. Loyambali limati: ‘Munthu woipa asiye njira yake,’ pomwe lachiwirili limafotokoza za Akhristu amene anasiya makhalidwe oipa kuti: ‘Ndipo ena mwa inu munali otero.’ Kwa zaka zambiri, Yehova anandithandiza ndi mzimu wake woyera kuti ndivale umunthu watsopano.” Atakhala m’ndende kwa zaka 17 ndi hafu, Hans anamasulidwa ndipo pa nthawiyo n’kuti atabatizidwa. Iye ananena kuti: “Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chondichitira chifundo chachikulu komanso kundikhululukira.”

15. Kodi anthu ambiri amakonda kutani, nanga Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?

15 Khalidwe lina limene anthu ayenera kusiya ndi kunama. Anthu ambiri amakonda kunama n’cholinga choti asalipire msonkho wochuluka kapena kuti asaimbidwe mlandu. Koma Yehova ndi “Mulungu wachoonadi.” (Sal. 31:5) Choncho amafuna kuti munthu “aliyense” amene amamulambira ‘azilankhula zoona’ ndipo ‘asamanamize’ anzake. (Aef. 4:25; Akol. 3:9) Choncho tiyenera kunena zoona zokhazokha ngakhale pamene tikuona kuti zingakhale zochititsa manyazi kapena zovuta.​—Miy. 6:16-19.

ZIMENE ZINAWATHANDIZA KUVULA UMUNTHU WAKALE

16. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tivule umunthu wakale?

16 Anthufe patokha sitingakwanitse kuvula umunthu wakale. Anthu amene tawatchula munkhaniyi monga Sakura, Ribeiro, Stephen ndi Hans anavutika kwambiri kuti asiye makhalidwe awo oipa. Koma anakwanitsa chifukwa cholola kuti Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera ziwathandize kusintha maganizo ndi mitima yawo. (Luka 11:13; Aheb. 4:12) Kuti nafenso tivule umunthu wakale, tiyenera kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kusinkhasinkha komanso kupempha Mulungu nthawi zonse kuti atipatse nzeru ndi mphamvu zotithandiza kutsatira malangizo a m’Baibulo. (Yos. 1:8; Sal. 119:97; 1 Ates. 5:17) Kukonzekera misonkhano komanso kupezekapo zimathandizanso kuti tizitsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera. (Aheb. 10:24, 25) Tiyenera kugwiritsanso ntchito njira zosiyanasiyana zimene gulu la Yehova limaperekera chakudya chauzimu masiku ano.​—Luka 12:42.

N’chiyani chingatithandize kuti tivule umunthu wakale? (Onani ndime 16)

17. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

17 Munkhaniyi takambirana makhalidwe oipa amene Akhristu ayenera kusiyiratu. Koma zofunika kuti tisangalatse Mulungu si zokhazi. Tiyeneranso kuvala umunthu watsopano. Munkhani yotsatira tidzakambirana mbali zosiyanasiyana za umunthu watsopano umene tiyenera kuuvala.

a Mayina ena asinthidwa munkhaniyi.

b Onani mutu 25 m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba.