Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Masomphenya a Zekariya Akukukhudzani Bwanji?

Kodi Masomphenya a Zekariya Akukukhudzani Bwanji?

“Bwererani kwa ine, . . . ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.”​ZEK. 1:3.

NYIMBO: 120, 117

1-3. (a) Kodi anthu a Mulungu ankakumana ndi zotani pa nthawi imene Zekariya anayamba ntchito yake? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anauza anthu ake kuti ‘abwerere kwa iye’?

ZEKARIYA anaona masomphenya a zinthu zodabwitsa kwambiri. Anaona mpukutu ukuuluka, mkazi atavundikiridwa m’chinthu chinachake komanso akazi awiri akuuluka ndi mapiko ooneka ngati a dokowe. (Zek. 5:1, 7-9) N’chifukwa chiyani Yehova anaonetsa mneneriyu masomphenya amenewa? Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawiyo ku Isiraeli? Nanga kodi masomphenyawa akutikhudza bwanji masiku ano?

2 M’chaka cha 537 B.C.E. anthu a Yehova anasangalala kwambiri chifukwa anamasulidwa ku ukapolo ku Babulo komwe anakhalako zaka 70. Iwo anasangalala kubwerera ku Yerusalemu kuti akamangenso kachisi n’kumalambira Yehova. Maziko a kachisiyu atamangidwa mu 536 B.C.E., anthu “anali kufuula kwambiri, ndipo phokoso lawo linali kumveka kutali kwambiri.” (Ezara 3:10-13) Koma pasanapite nthawi yaitali, anthu anayamba kulimbana nawo kuti asapitirize kumanga kachisiyo. Chifukwa chokhumudwa, Aisiraeliwo anagwa ulesi pa ntchito yomangayo n’kuyamba kumanga nyumba zawo komanso kulima minda yawo. Pofika zaka 16, ntchito yomanga kachisi wa Yehova inali itaimiratu. Anthu a Mulungu anafunika kukumbutsidwa kuti abwerere kwa Yehova m’malo moika patsogolo zochita zawo. Yehova ankafuna kuti anthuwo abwerere kwa iye n’kuyambiranso kumulambira ndi mtima wonse komanso mopanda mantha.

3 Choncho mu 520 B.C.E., Yehova anatuma mneneri Zekariya kuti akumbutse Aisiraeliwo chifukwa chimene anawamasulira ku ukapolo wa ku Babulo. Ndipotu n’kutheka kuti dzina loti Zekariya, lomwe limatanthauza kuti “Yehova Wakumbukira,” linawakumbutsa za mfundo ina yofunika. Mfundo yake ndi yakuti ngakhale kuti Aisiraeli anaiwala zimene Yehova anawachitira, Mulungu ankawakumbukirabe. (Werengani Zekariya 1:3, 4.) Iye anawatsimikizira kuti adzawathandiza kuti ayambirenso kumulambira moyenera, koma anawachenjeza kuti sadzalekerera anthu amene samulambira ndi mtima wonse. Tiyeni tione mmene Yehova analimbikitsira anthuwo kuti ayambirenso kumulambira pogwiritsa ntchito masomphenya a nambala 6 ndi 7 amene Zekariya anaona. Tikambirananso zimene tikuphunzira pa masomphenya amenewa.

CHILANGO CHA MULUNGU KWA ANTHU AKUBA

4. Kodi Zekariya anaona chiyani m’masomphenya ake a nambala 6, nanga n’chifukwa chiyani mpukutu umene anaona unalembedwa mbali zonse? (Onani chithunzi 1.)

4 Chaputala 5 cha buku la Zekariya chimayamba ndi masomphenya odabwitsa. (Werengani Zekariya 5:1, 2.) Zekariya anaona mpukutu ukuuluka m’mwamba ndipo unali wa mamita 9 m’litali komanso mamita 4 ndi hafu m’lifupi. Anthu akanatha kuuwerenga mosavuta chifukwa unali wofunyulula kale. Mbali zonse za mpukutuwu zinali ndi uthenga wachiweruzo. (Zek. 5:3) Nthawi zambiri mpukutu unkalembedwa mbali imodzi yokha. Koma popeza mpukutuwu unalembedwa mbali zonse, ndiye kuti unali ndi uthenga wamphamvu komanso wofunika kwambiri.

Akhristu ayenera kupewa kuba kwa mtundu uliwonse (Onani ndime 5-7)

5, 6. Kodi Yehova amaona bwanji kuba kwa mtundu uliwonse?

5 Werengani Zekariya 5:3, 4Timadziwa kuti munthu aliyense adzayankha kwa Yehova, koma anthu amene amadziwika ndi dzina lake ali ndi udindo waukulu kwambiri pa nkhaniyi. Anthu amene amakonda Mulungu amadziwa kuti kuba kwa mtundu uliwonse ‘kumanyozetsa dzina la Mulungu wawo.’ (Miy. 30:8, 9) Kaya munthu waba pa zifukwa ziti, amasonyeza kuti chofunika kwambiri pa moyo wake ndi zinthu zimene wabazo osati kusangalatsa Mulungu. Amasonyeza kuti salemekeza malamulo a Yehova komanso dzina lake.

6 Lemba la Zekariya 5:3, 4 lanena kuti ‘temberero lidzalowa m’nyumba ya munthu wakuba n’kukakhala m’nyumba mwake n’kuwonongeratu nyumbayo.’ Izi zikusonyeza kuti chiweruzo cha Yehova sichithawika ngakhale munthu atadzikiyira m’nyumba. Chikhoza kufika paliponse pamene munthu wabisala n’kuchititsa kuti zoipa zimene wachita ziululike. Ngakhale munthu wakuba atayesetsa kuti zisadziwike kwa olamulira, mabwana ake, akulu kapena makolo ake, sangabisire Yehova chifukwa iye amatitsimikizira kuti adzaonetsetsa kuti wakuba aliyense wadziwika. (Aheb. 4:13) Zimakhala zosangalatsa kwambiri kukhala ndi anthu amene amayesetsa “kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheb. 13:18.

7. Kodi tingapewe bwanji temberero limene lili mumpukutu wouluka uja?

7 Yehova amanyansidwa ndi kuba kwa mtundu uliwonse. Ifeyo timaona kuti ndi mwayi waukulu kutsatira mfundo zake komanso kukhala ndi makhalidwe amene sanganyozetse dzina lake. Tikamachita zimenezi timapewa chiweruzo chimene Yehova adzapereke kwa anthu amene amaphwanya malamulo ake mwadala.

TIZIKWANIRITSA MALONJEZO ATHU “TSIKU NDI TSIKU”

8-10. (a) Kodi lumbiro n’chiyani? (b) Kodi Zedekiya sanakwaniritse lumbiro liti?

8 Uthenga wina umene unali mumpukutu uja unali wochenjeza anthu ‘olumbira mwachinyengo m’dzina la Mulungu.’ (Zek. 5:4) Lumbiro ndi mawu amene munthu amanena kapena kulemba potsimikizira kuti zinazake ndi zoona, kapena polonjeza kuti adzachita kapena sadzachita zinthu zinazake.

9 Kulumbira m’dzina la Yehova ndi nkhani yaikulu kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira Zedekiya, yemwe anali mfumu yomaliza kulamulira ku Yerusalemu. Iye analumbira m’dzina la Yehova kuti adzapitirizabe kugonjera mfumu ya ku Babulo. Koma sanakwaniritse lumbiro lake. Zimenezi zinachititsa kuti Yehova anene mawu akuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, [Zedekiya,] amene ananyoza lumbiro ndi kuphwanya pangano limene anachita ndi mfumu imene inamulonga ufumu, adzafera m’dziko la mfumu yomweyo, dziko la Babulo.”​—Ezek. 17:16.

10 Popeza Zedekiya analumbira m’dzina la Mulungu, Yehova ankayembekezera kuti iye akwaniritse zimene analonjezazo. (2 Mbiri 36:13) Koma m’malomwake, Zedekiya anachita mgwirizano wosathandiza ndi Aiguputo pofuna kuti achoke m’manja mwa mfumu ya Babulo.​—Ezek. 17:11-15, 17, 18.

11, 12. (a) Kodi lumbiro lofunika kwambiri pa malumbiro onse amene tinapanga ndi liti? (b) Kodi lumbiro limene tinapanga podzipereka kwa Yehova liyenera kukhudza bwanji zochita zathu za tsiku ndi tsiku?

11 Yehova amamvanso malonjezo amene ifeyo timapanga. Iye amaona kuti malonjezo athuwo ndi ofunika kwambiri, ndipo kuti timusangalatse tiyenera kukwaniritsa zimene talonjezazo. (Sal. 76:11) Pa malonjezo onse amene timapanga, lonjezo lofunika kwambiri ndi limene tinapanga podzipereka kwa Yehova. Munthu akadzipereka kwa Yehova amalumbira kuti azimutumikira zivute zitani.

12 Ndiye kodi tingakwaniritse bwanji lumbiro limeneli? Zimene timachita tikakumana ndi mayesero, kaya aakulu kapena aang’ono, ziyenera kusonyeza kuti timafunitsitsa kukwaniritsa lonjezo loti tizitamanda Yehova “tsiku ndi tsiku.” (Sal. 61:8) Mwachitsanzo, kodi tingatani ngati munthu wina kuntchito kapena kusukulu akutikopa? Kodi tidzakana zimene akufunazo n’cholinga choti tisonyeze kuti ‘timasangalala ndi njira’ za Yehova? (Miy. 23:26) Ngati anthu ena m’banja lathu si Mboni, kodi timapempha Yehova kuti atithandize kukhalabe ndi khalidwe labwino ngakhale pamene anthu enawo sakuchita zimenezo? Kodi tsiku lililonse timapemphera kwa Yehova n’kumamuthokoza chifukwa choti amatikonda komanso kutilamulira bwino? Kodi timayesetsa kuwerenga Baibulo tsiku lililonse? Pajatu tinalonjeza kuti tizichita zinthu ngati zimenezi. Tikamamvera Yehova ndiponso kumulambira ndi mtima wonse timasonyeza kuti timamukonda komanso tinadziperekadi kwa iye. Tiyenera kuona kuti kulambira Mulungu n’kofunika kwambiri pa moyo wathu, osati kumangomulambira mwamwambo chabe. Tikamakwaniritsa zimene tinalonjeza, ifeyo ndi amene timapindula chifukwa Yehova watilonjeza zinthu zabwino ngati tingapitirize kukhala okhulupirika.​—Deut. 10:12, 13.

13. Kodi taphunzira chiyani pa masomphenya a nambala 6 a Zekariya?

13 Masomphenya a nambala 6 amene Zekariya anaona atithandiza kudziwa kuti anthu amene amakonda Yehova ayenera kupewa kuba kwa mtundu uliwonse komanso kulumbira zabodza. Taonanso kuti Yehova sanawasiyiretu Aisiraeli ngakhale kuti ankalakwitsa zinthu zina. Iye ankamvetsa mavuto amene ankakumana nawo pamene anazunguliridwa ndi adani. Yehova amapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yosunga malonjezo ndipo adzatithandiza kukwaniritsa zimene talonjeza. Njira imodzi imene amatithandizira ndi kutipatsa chiyembekezo choti adzachotsa zinthu zoipa padziko lonse. Masomphenya otsatira amene Zekariya anaona amatsimikizira mfundo imeneyi.

KUIPA ANAKUIKA PAMALO AKE OYENERA

14, 15. (a) Kodi Zekariya anaona chiyani m’masomphenya ake a nambala 7? (Onani chithunzi 2.) (b) Kodi mkaziyo akuimira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani anatsekeredwa m’chiwiyacho?

14 Pambuyo poona mpukutu umene unkauluka, mngelo anauza Zekariya kuti ‘akweze maso ake.’ Kodi iye anaona chiyani m’masomphenya a nambala 7? Iye anaona “chiwiya choyezera chokwana muyezo wa efa” chikubwera. (Werengani Zekariya 5:5-8.) Chiwiyacho chinali ndi “chivundikiro chamtovu.” Atavundukula chiwiyacho, Zekariya anaona kuti mkati mwake munali “mkazi atakhala pansi.” Mngeloyo ananena kuti mkazi amene ali m’chiwiyacho “dzina lake ndi Kuipa.” Zekariya ayenera kuti anachita mantha ataona kuti mkaziyo akuyesetsa kuti atuluke m’chiwiyacho. Zitatero, mngeloyo anakankhira mkaziyo m’chiwiyacho mwamsanga n’kuchivundikiranso ndi chivundikiro cholemera chija. Kodi masomphenya amenewa akutanthauza chiyani?

15 Masomphenya amenewa akusonyeza kuti Yehova sadzalekerera kuipa kwa mtundu uliwonse pakati pa anthu ake. Iye adzaonetsetsa kuti kuipako kwasamaliridwa n’kuchotsedwa mwamsanga. (1 Akor. 5:13) Zimene mngelo uja anachita povundikira chiwiya chija mwamsanga zikutsimikizira mfundo imeneyi.

Yehova anaonetsetsa kuti kulambira koyera kusaipitsidwe (Onani ndime 16-18)

16. (a) Kodi kenako Zekariya anaona chiyani? (Onani chithunzi 3.) (b) Kodi akazi awiri okhala ndi mapiko anapita nacho kuti chiwiya chija?

16 Kenako, Zekariya anaona akazi awiri okhala ndi mapiko amphamvu ooneka ngati a dokowe. (Werengani Zekariya 5:9-11.) Akazi amenewa ndi osiyana kwambiri ndi mkazi amene anatsekeredwa m’chiwiya uja. Iwo ananyamula chiwiya chija mmene munali “Kuipa” n’kuuluka nacho. Kodi anapita nacho kuti? Anapita nacho “kudziko la Sinara” kapena kuti ku Babulo. Koma n’chifukwa chiyani anapita nacho kumeneko?

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani dziko la Sinara linali ‘malo oyenera’ kukhala “Kuipa”? (b) Kodi kuipa tiyenera kukuona bwanji?

17 Mu nthawi ya Zekariya, Aisiraeli sakanavutika kumvetsa chifukwa chake kuipa anapita nako kudziko la Sinara. Zekariya ndi Ayuda anzake ankadziwa kuti Babulo unali mzinda woipa kwambiri pa nthawiyo. Popeza anakulira mumzindawu womwe anthu ake anali a makhalidwe oipa komanso olambira mafano, tsiku lililonse ankayenera kuyesetsa kuti asatengere makhalidwe oipawo. Masomphenya amenewa ayenera kuti anawakhazika mtima pansi chifukwa anawatsimikizira kuti Yehova sadzalekerera anthu ofuna kuipitsa kulambira koyera.

18 Komabe masomphenyawa anakumbutsanso Ayuda kuti ayenera kuyesetsa kuti kulambira kwawo kuzikhala koyera nthawi zonse. Anthu a Yehova sayenera kulola kuti zinthu zoipa zilowe m’gulu lawo n’kukhazikika. Yehova watilola kuti tikhale m’gulu lake loyera limene limatisamalira mwachikondi choncho tili ndi udindo woonetsetsa kuti gululi lipitirizebe kukhala loyera. Kodi ifeyo timayesetsa kuchita zimenezi? M’paradaiso wathu wauzimu simuyenera kupezeka kuipa kwa mtundu uliwonse.

ANTHU OYERA AMALEMEKEZA YEHOVA

19. Kodi tikuphunzira chiyani pa masomphenya a Zekariya?

19 Masomphenya a nambala 6 ndi 7 amene Zekariya anaona ndi chenjezo lamphamvu kwa anthu amene amakonda kuchita zachinyengo. Masomphenyawa akutikumbutsanso kuti Yehova sadzalekerera anthu ochita zoipa. Anthu amene amalambira Yehova ndi mtima wonse, ayenera kudana kwambiri ndi zoipa. Masomphenya amenewa amatitsimikiziranso kuti tikamayesetsa kusangalatsa Yehova, iye adzatiteteza ndiponso kutidalitsa, osati kutitemberera. Zonse zimene timachita poyesetsa kukhalabe oyera m’dziko loipali sizidzapita pachabe. Dziwani kuti Yehova adzatithandiza kuti tikwanitse kupewa zoipa. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti kulambira koyera kudzapitirira kuyenda bwino m’dziko loipali? Nanga n’chiyani chikutitsimikizira kuti Yehova adzateteza gulu lake pamene chisautso chachikulu chikuyandikira? Tidzakambirana mafunso amenewa munkhani yotsatira.