Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Magaleta na Cisoti Cacifumu Zimakutetezani

Magaleta na Cisoti Cacifumu Zimakutetezani

“Ici cidzacitika ngati mudzamvela mwacangu mau a Yehova [Mulungu] wanu.”—ZEK. 6:15, Buku Lopatulika.

NYIMBO: 61, 22

1, 2. Kodi zinthu zinali bwanji pakati pa Ayuda ku Yerusalemu pambuyo pakuti Zekariya waona masomphenya a namba 7?

ZEKARIYA ayenela kuti anayamba kuganizila zambili pambuyo poona masomphenya a namba 7. Yehova anali atatsimikizila kuti adzapeleka ciweluzo kwa anthu acinyengo cifukwa ca zocita zawo zoipa. Izi ziyenela kuti zinamulimbikitsa. Komabe, zinthu sizinasinthe kweni-kweni. Anthu anali kucitabe cinyengo ndi zinthu zina zoipa, ndipo nchito yomanga kacisi wa Yehova ku Yerusalemu inali kutali kuti isile. Kodi n’cifukwa ciani Ayuda analeka mwamsanga conco kugwila nchito imene Mulungu anawapatsa? Kodi iwo anabwelele ku dziko lawo kuti akacite zofuna zawo cabe?

2 Zekariya anali kudziŵa kuti Ayuda amene anacoka ku Babulo kupita ku Yerusalemu anali na cikhulupililo colimba. Amenewo ni anthu amene ‘Mulungu woona analimbikitsa mitima yawo’ kuti asiye nyumba zawo na mabizinesi awo. (Ezara 1:2, 3, 5) Iwo anacoka m’dziko limene anajaila kukhalamo n’kupita kukakhala m’dziko limene ambili a iwo anali asanalionepo. Akanakhala kuti anali kuona nchito yomanga kacisi wa Yehova monga yosafunika, sembe sanayende mtunda wautali wa makilomita pafupi-fupi 1,600, kupitila m’dziko loopsa.

3, 4. Kodi Ayuda amene anabwelela ku Yerusalemu anakumana ndi mavuto anji?

3 Kodi ulendo umenewo unali bwanji? Pamene Ayuda anali kuyenda, nthawi zambili ayenela kuti anali kuganizila za Yerusalemu, malo awo atsopano okhala. Iwo anali atamvelapo kuti Yerusalemu unali mzinda wokongola kwambili poyamba. Okalamba amene anali pakati pawo anali ataonapo ulemelelo wa kacisi wa Yehova woyambilila. (Ezara 3:12) Mukanakhalapo pa ulendowo, kodi mukanamvela bwanji kuona Yerusalemu, malo anu atsopano okhala? Kodi sembe munamvela cisoni poona nyumba zogumuka-gumuka komanso zomela maudzu? Kapena sembe munayamba kuyelekezela mipanda yolimba ya Babulo ndi mpanda wogumuka-gumuka wa Yerusalemu, wokhala na mipata ikulu-ikulu m’malo amene munali zipata ndi nsanja za alonda? Koma izi sizinawafooketse Ayuda. Iwo anaona mmene Yehova anawatetezela pa ulendo wautali wobwelela ku dziko lawo. Conco, atangofika m’dzikolo, anamanga guwa la nsembe pamalo pamene panali kacisi woyambilila, ndipo anayamba kupeleka nsembe kwa Yehova tsiku lililonse. (Ezara 3:1, 2) Iwo anali okondwa ngako, ndipo zinali kuoneka monga kuti palibe cimene cikanawafooketsa.

4 Kuwonjezela pa nchito yomanga kacisi, Aisiraeli anafunikanso kumanga mizinda yawo. Anafunika kukonzanso nyumba zowonongeka, kubyala mbewu m’minda, na kusakila zakudya. (Ezara 2:70) Anali na nchito yaikulu ngako. Koma mwadzidzidzi panabuka citsutso coopsa. Poyamba Aisiraeli anacita zinthu molimba mtima, koma patapita zaka 15, anafooka. (Ezara 4:1-4) Mu 522 B.C.E., nchito yomanga ku Yerusalemu inaimilatu cifukwa mfumu ya Perisiya inapeleka lamulo loletsa nchitoyo. Panthawiyo, zinaoneka ngati kuti mzindawo sudzamangiwanso.—Ezara 4:21-24.

5. Kodi Yehova anacita ciani ataona kuti anthu ake aleka kugwila nchito yake?

5 Yehova anadziŵa kuti anthu ake afunikila cilimbikitso. Conco, Mulungu anaonetsa Zekariya masomphenya otsilizila pofuna kutsimikizila Ayuda kuti amawakonda ndiponso kuti adzawateteza akayambanso kugwila nchito yake. Anafunanso kuwayamikila pa zonse zimene anacita. Ponena za nchito yomanganso kacisi, Yehova analonjeza kuti: “Ici cidzacitika ngati mudzamvela mwacangu mau a Yehova [Mulungu] wanu.”—Zek. 6:15, Buku Lopatulika.

MAGULU ANKHONDO A ANGELO OKWELA PA MAGALETA

6. (a) Kodi masomphenya a namba 8 a Zekariya anayamba bwanji? (Onani pikica kuciyambi.) (b) N’cifukwa ciani mahosi a m’masomphenyawo anali a mitundu yosiyana-siyana?

6 Masomphenya a namba 8 komanso otsilizila a Zekariya ni olimbitsa cikhulupililo ngako. (Ŵelengani Zekariya 6:1-3.) Yelekezelani kuti mukuona magaleta anayi, okonzekeletsedwa bwino kaamba ka nkhondo, akuthamanga “kucokela pakati pa mapili aŵili . . . amkuwa.” Mahosi amene akudonsa magaletawo ni a mitundu yosiyana-siyana. Kusiyana mitundu kwa mahosi kunali kothandiza pofuna kusiyanitsa okwela pa mahosiwo. Zekariya anafunsa kuti, “Kodi magaleta amenewa akuimila ciani?” (Zek. 6:4) Ifenso tifunika kudziŵa zimenezi, cifukwa masomphenyawa amatikhudza.

Yehova akali kuseŵenzetsa angelo poteteza na kulimbikitsa anthu ake

7, 8. (a) Kodi mapili aŵili amkuwa aimila ciani? (b) N’cifukwa ciani ni amkuwa?

7 M’Baibo, mapili nthawi zina amaimila maufumu, kapena maboma. Mapili a m’masomphenya a Zekariya ni olingana na mapili aŵili ochulidwa mu ulosi wa Danieli. Phili loyamba liimila ulamulilo wa Yehova wosatha komanso wa cilengedwe conse. Phili linalo liimila Ufumu wa Mesiya wolamulidwa na Yesu. (Dan. 2:35, 45) Kucokela pamene Yesu anayamba kulamulila mu 1914, mapili onse aŵiliwa akhalapo, ndipo athandiza kwambili pa kukwanilitsa cifunilo ca Mulungu pano padziko lapansi.

8 N’cifukwa ciani mapiliwo ni amkuwa? Molingana ndi golide, mkuwa kapena kuti kopa, ni mwala wonyezimila wamtengo wapatali. Yehova analamula anthu ake kuti aseŵenzetse mkuwa pomanga cihema. Pambuyo pake, anawalamulanso kuseŵenzetsa mkuwa pomanga kacisi ku Yerusalemu. (Eks. 27:1-3; 1 Maf. 7:13-16) Conco, m’pomveka kuti mapili aŵili ophiphilitsa amenewa ni amkuwa. Zimenezi zitikumbutsa kuti ulamulilo wa Yehova wa cilengedwe conse komanso Ufumu wa Mesiya ni maulamulilo abwino kwambili, amene adzabweletsa mtendele na madalitso kwa anthu onse.

9. Kodi okwela pa magaleta n’ndani? Nanga anapatsiwa nchito yanji?

9 Nanga bwanji za magaleta? Kodi akuimila ciani pamodzi na okwelapo ake? Okwela pa magaletawo ni angelo; mwacionekele ndi magulu osiyana-siyana a angelo. (Ŵelengani Zekariya 6:5-8.) Iwo anali kubwela kucokela “pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi,” ndipo anatumiwa kukacita nchito yapadela. Kodi anapatsiwa nchito yanji? Magaleta na okwelapo ake anatumiwa kumadela osiyana-siyana a dziko lapansi. Anawatuma kuti akateteze anthu a Yehova kwa Babulo, “dziko la kumpoto.” Izi zinaonetsa kuti Yehova sadzalola kuti anthu ake akagwidwenso ukapolo na Babulo. Zimenezi ziyenela kuti zinawalimbikitsa ngako Ayuda amene anali kumanga kacisi m’nthawi ya Zekariya. Iwo sanafunikenso kudela nkhawa zakuti adani awo adzawalepheletsa kutsiliza nchitoyo.

10. Kodi anthu a Mulungu masiku ano angalimbikitsidwe bwanji na masomphenya a Zekariya a magaleta ndi okwelapo ake?

10 Monga zinalili m’nthawi ya Zekariya, Yehova wa makamu akali kuseŵenzetsa angelo poteteza na kulimbikitsa anthu ake. (Mal. 3:6; Aheb. 1:7, 14) Isiraeli wauzimu anamasulidwa mu ukapolo wophiphilitsa kwa Babulo Wamkulu mu 1919. Kuyambila nthawiyo, kulambila koona kwapitabe patsogolo olo kuti anthu a Mulungu akhala akutsutsiwa mosalekeza. (Chiv. 18:4) Popeza kuti angelo amatiteteza, sitifunika kuda nkhawa kuti gulu la Yehova lidzagwidwanso ukapolo wauzimu. (Sal. 34:7) M’malomwake, tifunika kukhala otsimikiza kuti atumiki a Mulungu padziko lonse adzapitiliza kupita patsogolo mwauzimu. Pamene tiganizila mozama za masomphenya a Zekariya, timadziŵa kuti ndise otetezeka mu mthunzi wa mapili aŵili ophiphilitsa.

11. Ngakhale kuti anthu a Mulungu adzaukilidwa mtsogolo, n’cifukwa ciani sitifunika kucita mantha?

11 Posacedwapa, magulu andale m’dziko la Satanali adzagwilizana kuti awononge anthu a Mulungu. (Ezek. 38:2, 10-12; Dan. 11:40, 44, 45; Chiv. 19:19) Ulosi wa Ezekieli umakamba kuti magulu amenewo adzabwela ngati mitambo yophimba dziko. Adzabwela na ukali kudzatiukila atakwela pa mahosi. (Ezek. 38:15, 16) * Kodi tiyenela kucita mantha? Iyai. Cifukwa ku mbali yathu kuli magulu ankhondo okwela pa mahosi. Panthawi yovuta imeneyo ya cisautso cacikulu, angelo a Yehova wa makamu adzateteza anthu a Mulungu ndi kuwononga amene amatsutsa ulamulilo wake. (2 Ates. 1:7, 8) Ndithudi, limenelo lidzakhala tsiku lapadela kwambili. Koma kodi n’ndani adzatsogolela gulu lankhondo lakumwamba la Yehova?

YEHOVA AVEKA WANSEMBE CISOTI CACIFUMU

12, 13. (a) Kodi Zekariya anauziwa kuti acite ciani? (b) N’cifukwa ciani tikamba kuti munthu wochedwa kuti Mphukila anacitila cithunzi Yesu Khristu?

12 Pambuyo poona masomphenya 8, Zekariya anacita zinthu zokhala na tanthauzo la ulosi, zimene zinalimbikitsa anthu a Mulungu amene anali kumanga kacisi wake. (Ŵelengani Zekariya 6:9-12.) Zekariya anauziwa kuti akatenge siliva na golide kwa Heledai, Tobiya, ndi Yedaya, amuna atatu amene anali atafika kumene kucokela ku Babulo. Anamuuzanso kuti zinthuzo apangile “cisoti cacifumu caulemelelo.” (Zek. 6:11) Kodi Zekariya anauziwa kuti cisotico akaveke Bwanamkubwa Zerubabele, amene anali wa fuko la Yuda ndi mbadwa ya Davide? Iyai. Anthu ayenela kuti anadabwa kwambili kuona iye akutenga cisotico n’kuveka Mkulu wa Ansembe, Yoswa.

13 Kodi Mkulu wa Ansembe, Yoswa, anakhala mfumu atavekedwa cisoti cacifumu? Iyai. Yoswa sanabadwile mumzela wa mfumu Davide. Conco sanali woyenelela kukhala mfumu. Koma kuvekedwa kwake cisoti cacifumu inali mbali ya ulosi. Iye anali kucitila cithunzi mfumu yosatha komanso wansembe wamtsogolo. Mkulu wa ansembe amene anaikidwa kukhala mfumu akuchedwa Mphukila. Malemba amaonetselatu kuti Mphukilayo ni Yesu Khristu.—Yes. 11:1; Mat. 2:23. *

14. Monga Mfumu na Mkulu wa Ansembe, kodi Yesu amagwila nchito yanji?

14 Pokhala Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe, Yesu ndiye mtsogoleli wa gulu lankhondo lakumwamba la Yehova. Kaamba ka ici, iye amagwila nchito mwakhama n’colinga cakuti anthu a Mulungu monga gulu akhale otetezeka olo kuti akukhala m’dziko loipa. (Yer. 23:5, 6) Posacedwa, Khristu adzatsogolela makamu akumwamba pogonjetsa mitundu ya anthu kuti akweze Ucifumu wa Mulungu ndi kuteteza anthu a Yehova. (Chiv. 17:12-14; 19:11, 14, 15) Koma Mphukila asanapeleke ciweluzo, ali na nchito yaikulu yofunika kugwila.

IYE ADZAMANGA KACISI

15, 16. (a) Ni nchito iti ya kubwezeletsa na kuyenga imene yakhala ikucitika m’nthawi yathu? Nanga akugwila nchitoyi n’ndani? (b) Kodi zinthu zidzakhala bwanji pambuyo pa Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000?

15 Kuwonjezela pa udindo wokhala Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe, Yesu anapatsiwanso nchito ‘yomanga kachisi wa Yehova.’ (Ŵelengani Zekariya 6:13.) Nchito yomanga ya Yesu inaphatikizapo kumasula olambila oona ku ukapolo wa Babulo Wamkulu na kukhazikitsanso mpingo wacikhristu mu 1919. Iye anaikanso “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azitsogolela pa nchito imene ikucitika m’mabwalo a padziko lapansi a kacisi wamkulu wauzimu. (Mat. 24:45) Yesu wakhalanso akugwila nchito mwakhama yoyenga anthu a Mulungu na kuwathandiza kuti kulambila kwawo kukhale koyela.—Mal. 3:1-3.

16 Panthawi ya Ulamulilo wa Zaka 1,000, Yesu pamodzi na mafumu komanso ansembe anzake okwana 144,000 adzathandiza anthu okhulupilika kukhala angwilo. Izi zikadzacitika, pa dziko lapansi padzakhala olambila oona a Mulungu okha-okha. Panthawiyo, kulambila koona kudzabwezeletsedwa kothelatu.

TENGANKONI MBALI M’NCHITO YOMANGA

17. Kodi Yehova anawatsimikizila za ciani Ayuda? Nanga zimene anawauzazo zinawakhudza bwanji?

17 Kodi uthenga wa Zekariya unawakhudza bwanji Ayuda a m’nthawi yake? Yehova anawatsimikizila kuti adzawapatsa mtendele ndi kuwateteza kuti agwile bwino nchito yawo yomanga. Izi zinawapatsa ciyembekezo. Nanga zikanatheka bwanji kuti Ayuda ocepa akwanitse kugwila nchito yaikuluyo? Mau otsatila amene Zekariya anakamba, anathandiza kuti Ayudawo asakhalenso amantha kapena okayikila. Kuwonjezela pa thandizo la amuna okhulupilika monga Heledai, Tobiya, na Yedaya, Mulungu anakamba kuti anthu enanso ambili “adzabwela kudzamanga nawo kacisi wa Yehova.” (Ŵelengani Zekariya 6:15.) Ayuda atalimbikitsidwa na Mulungu, mosazengeleza anayambanso kugwila nchito yomanga ngakhale kuti inali ikali yoletsedwa. Pasanapite nthawi, Yehova anathetsa ciletso cimene cinali copinga cacikulu ngati phili, ndipo nchito yomanga kacisi inatha mu 515 B.C.E. (Ezara 6:22; Zek. 4:6, 7) Komabe, mau a Yehova amenewa alinso na tanthauzo lalikulu lokhudza zimene zikucitika masiku athu ano.

Yehova sadzaiŵala ngakhale pang’ono cikondi cimene timamuonetsa! (Onani palagilafu 18, 19)

18. Kodi lemba la Zekariya 6:15 likukwanilitsidwa bwanji masiku ano?

18 Masiku ano, anthu mamiliyoni ambili amalambila Yehova. Iwo na mtima wonse amaseŵenzetsa ‘zinthu zawo zamtengo wapatali,’ monga nthawi yawo, mphamvu, na cuma cawo, pocilikiza nchito yomanga kacisi wamkulu wauzimu wa Yehova. (Miy. 3:9) Tingatsimikize bwanji kuti Yehova amayamikila zimene timacita pomutukila mokhulupilika? Kumbukilani kuti Heledai, Tobiya, ndi Yedaya anapeleka golide na siliva amene Zekariya anapangila cisoti cacifumu. M’kupita kwa nthawi, cisotico cinathandiza anthu ‘kukumbukila’ zimene iwo anacita pocilikiza kulambila koona. (Zek. 6:14) Mofananamo, Yehova sadzaiŵala ngakhale pang’ono zonse zimene timacita pom’tumikila, ndi cikondi cimene timamuonetsa!—Aheb. 6:10.

19. Kodi masomphenya a Zekariya ayenela kutikhudza bwanji masiku ano?

19 Zonse zimene zakhala zikucitika pa kulambila koona masiku otsiliza ano, ni umboni wamphamvu wakuti Yehova akutidalitsa ndi kuti Khristu akutitsogolela. Ndithudi, tili m’gulu lodalilika, lotetezeka, ndiponso limene silidzatha. Colinga ca Yehova cokhudza kulambila koona “cidzacitika.” Conco, muziyamikila malo anu m’gulu la Yehova, ndipo ‘muzimvela mau a Yehova Mulungu wanu.’ Mukacita conco, ndiye kuti Mfumu yathu amenenso ni Mkulu wa Ansembe, kuphatikizapo okwela pa mahosi akumwamba, adzapitiliza kukutetezani. Muzicita zilizonse zimene mungakwanitse pocilikiza kulambila koona. Mukacita zimenezi, mungakhale wotsimikiza kuti Yehova wa makamu adzakutetezani panthawi yonse yotsala m’dongosolo lino la zinthu, komanso mpaka muyaya!

^ par. 11 Kuti mudziŵe zambili, onani “Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi” mu Nsanja ya Mlonda ya May 15, 2015, mape. 29-30.

^ par. 13 Liu lakuti “Mnazareti” pa Mateyu 2:23 linacokela ku liu la Ciheberi limene limatanthauza kuti “Mphukila.”