Timatetezedwa ndi Magaleta Komanso Chisoti Chachifumu

Timatetezedwa ndi Magaleta Komanso Chisoti Chachifumu

“Anthu inu mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu, mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.”​—ZEK. 6:15.

NYIMBO: 17, 136

1, 2. Kodi Zekariya ataona masomphenya ake a nambala 7, zinthu zinali bwanji kwa Ayuda ku Yerusalemu?

ZEKARIYA ataona masomphenya ake a nambala 7, anali ndi zambiri zoti aganizire. Yehova analonjeza kuti adzalanga anthu amene amachita zinthu mwachinyengo. Lonjezoli liyenera kuti linalimbikitsa Zekariya. Koma pa nthawiyo anthu ankachitabe zachinyengo ndiponso zinthu zina zoipa. Komanso ntchito yomanga kachisi wa Yehova ku Yerusalemu inali isanapite patali. Kodi n’chiyani chinachititsa Ayuda kuti asiye kugwira ntchito imene Mulungu anawapatsayi? Kodi iwo anabwerera kwawo n’cholinga choti azikangochita zofuna zawo?

2 Zekariya ankadziwa kuti Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu anali anthu okhulupirika. Paja anali anthu amene ‘Mulungu woona analimbikitsa mitima yawo’ kuti asiye nyumba zawo komanso mabizinezi awo. (Ezara 1:2, 3, 5) Ayudawo anachoka m’dziko limene analizolowera n’kusamukira kudziko lomwe ambiri mwa iwo anali asanalionepo. Ngati analolera kuyenda ulendo wovuta wa makilomita 1,600 wodutsa m’mapiri ndi m’zipululu, ndiye kuti ankaona kuti kumanganso kachisi wa Yehova ndi kofunika kwambiri.

3, 4. Kodi Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu anakumana ndi mavuto otani?

3 Pa ulendowo Ayuda ayenera kuti ankaganizira kwambiri za mmene zinthu zidzakhalire ku Yerusalemu. Iwo anali atamva kale kwa achikulire kuti mzindawu unali wokongola kwambiri komanso kuti kachisi anali waulemerero. (Ezara 3:12) Kodi mukanakhala nawo pa ulendowu mukanamva bwanji mutaona Yerusalemu koyamba? Muyenera kuti mukanamva chisoni poona mmene mzindawu wawonongekera n’kungokhala tchire lokhalokha. Mwina mukanaona kuti mpanda wake ndi wosiyana kwambiri ndi mpanda wolimba wa ku Babulo chifukwa unali utagumukagumuka. Ngakhale zinali choncho, anthuwo sanataye mtima. Iwo anali ataona kale Yehova akuwathandiza pa ulendo wawo wautali wobwerera ku Yerusalemu. Atangofika, anakonza guwa lansembe pamalo pamene panali kachisi ndipo anayamba kupereka nsembe kwa Yehova tsiku lililonse. (Ezara 3:1, 2) Iwo anasangalala kwambiri ndipo zinkaoneka kuti palibe chimene chingawalepheretse kumaliza ntchito yawo.

4 Kuwonjezera pa kumanga kachisi, Aisiraeliwo ankayenera kumanganso mizinda yawo. Analinso ndi nyumba zoti amange, minda yoti alime komanso ankayenera kupeza chakudya. (Ezara 2:70) Ntchito imene anali nayo inkaoneka kuti ndi yaikulu. Komanso pasanapite nthawi yaitali anthu ena anayamba kuwatsutsa kwambiri. Ngakhale kuti poyamba ankagwira ntchitoyo molimba mtima, iwo anataya mtima chifukwa kutsutsidwako kunapitirira kwa zaka 15. (Ezara 4:1-4) Zinthu zinafika poipa kwambiri mu 522 B.C.E. pamene mfumu ya Aperisiya inaletsa ntchito yonse yomanga ku Yerusalemu. Pa nthawiyo zinkaoneka kuti mzindawu sudzamangidwanso.​—Ezara 4:21-24.

5. Kodi Yehova anatani ataona kuti anthu ake asiya kugwira ntchito?

5 Yehova ankadziwa zimene zingathandize anthu ake. Iye anaonetsa Zekariya masomphenya omaliza n’cholinga choti atsimikizire Ayuda kuti amawakonda ndipo amayamikira zonse zimene anachita pogwira ntchito yake. Anawatsimikiziranso kuti awateteza akayambiranso kugwira ntchitoyo. Yehova analonjeza Ayudawo kuti adzakwanitsa kumanganso kachisi ngati ‘adzamvera mawu ake.’​—Zek. 6:15.

MAGALETA ANKHONDO A ANGELO

6. (a) Kodi Zekariya anaona chiyani m’masomphenya ake a nambala 8? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) N’chifukwa chiyani mahatchi okoka magaletawo anali amitundu yosiyana?

6 Masomphenya a nambala 8 amene Zekariya anaona ndi olimbikitsa kwambiri. (Werengani Zekariya 6:1-3.) Tayerekezerani kuti mukuona ‘magaleta 4 akubwera kuchokera pakati pa mapiri awiri amkuwa’ ndipo akuoneka kuti akonzekera nkhondo. Mahatchi amene akukoka magaletawo ndi amitundu yosiyanasiyana n’cholinga choti okwera pamagaletawo azizindikiridwa mosavuta. Kenako mukumva Zekariya akufunsa kuti: “Kodi magaleta amenewa akuimira chiyani?” (Zek. 6:4) Kudziwa yankho la funsoli n’kofunika kwambiri chifukwa masomphenyawa akutikhudza.

Yehova amagwiritsabe ntchito angelo ake kuti aziteteza komanso kulimbikitsa anthu ake

7, 8. (a) Kodi mapiri awiri amene Zekariya anaona akuimira chiyani? (b) N’chifukwa chiyani mapiriwo ndi amkuwa?

7 M’Baibulo, nthawi zina mapiri amaimira maufumu kapena kuti maboma. Mapiri awiri amene Zekariya anaona m’masomphenya ake ndi ofanana ndi mapiri awiri otchulidwa mu ulosi wa Danieli. Phiri limodzi likuimira ulamuliro wa Yehova wa chilengedwe chonse womwe wakhalapo kuyambira kalekale ndipo sudzatha. Phiri linalo likuimira Ufumu wa Mesiya womwe wolamulira wake ndi Yesu. (Dan. 2:35, 45) Phiri lachiwirili lakhalapo kuyambira pamene Yesu anapatsidwa ufumu mu 1914 ndipo kuchokera nthawi imeneyo mapiri onsewa akhala akuthandiza kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Mulungu padziko lapansi.

8 N’chifukwa chiyani mapiriwa ndi amkuwa? Mofanana ndi golide, mkuwa ndi wamtengo wapatali, moti Yehova analamula kuti anthu ake agwiritse ntchito mkuwa popanga chihema komanso pomanga kachisi ku Yerusalemu. (Eks. 27:1-3; 1 Maf. 7:13-16) Choncho popeza kuti mapiri awiriwa ndi amkuwa, zikusonyeza kuti ulamuliro wa Yehova komanso Ufumu wa Mesiya ndi wabwino kwambiri. Maulamuliro awiriwa adzathandiza anthu kuti adalitsidwe komanso akhale otetezeka.

9. Kodi okwera pamagaletawo akuimira ndani, nanga ntchito yawo inali yotani?

9 Tsopano tiyeni tikambirane za magaleta aja. Kodi magaletawo ndiponso amene anakwerapo akuimira chiyani? Okwera pamagaletawo akuimira angelo ndipo zikuoneka kuti wokwera aliyense sakuimira mngelo mmodzi koma gulu la angelo. (Werengani Zekariya 6:5-8.) Angelowo akuchokera pamaso pa “Ambuye wa dziko lonse lapansi” ndipo apatsidwa ntchito yapadera. Kodi ntchito yawo ndi yotani? Iwo atumidwa kuti aziyang’anira zigawo zosiyanasiyana za dziko lapansi. Udindo wawo waukulu ndi kuteteza anthu a Yehova kuti asasokonezedwe ndi anthu a “kudziko la kumpoto” lomwe ndi Babulo. Izi zikusonyeza kuti Yehova adzaonetsetsa kuti anthu ake asakhalenso akapolo. Mfundo imeneyi iyenera kuti inalimbikitsa kwambiri anthu amene ankamanga kachisi m’masiku a Zekariya. Iwo sankafunika kuda nkhawa kuti adani awo awasokoneza.

10. Kodi masomphenya a Zekariya a magaleta ndi okwerapo ake angatilimbikitse bwanji masiku ano?

10 Mofanana ndi nthawi ya Zekariya, Yehova amagwiritsabe ntchito angelo ake kuti ateteze anthu ake komanso awalimbikitse. (Mal. 3:6; Aheb. 1:7, 14) Kuchokera nthawi imene Isiraeli wauzimu anamasulidwa mu Babulo Wamkulu mu 1919, kulambira koona kwakhala kukuyenda bwino ngakhale kuti pali anthu ambiri otsutsa. (Chiv. 18:4) Mfundo yoti angelo amatiteteza imasonyeza kuti n’zosatheka kuti tidzakhalenso mu ukapolo wauzimu. (Sal. 34:7) Tisamakayikirenso kuti zinthu zidzapitiriza kutiyendera bwino mwauzimu padziko lonse. Masomphenya amene Zekariya anaona akusonyeza kuti ndife otetezeka pakati pa mapiri awiriwo.

11. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa mgwirizano umene udzatiukire?

11 Posachedwapa, andale a m’dziko la Satanali adzachita mgwirizano womwe cholinga chake chidzakhala kuwononga anthu a Mulungu. (Ezek. 38:2, 10-12; Dan. 11:40, 44, 45; Chiv. 19:19) Ezekieli analosera kuti otiukirawo adzakwiya kwambiri ndipo adzakwera mahatchi n’kufika ngati mitambo yophimba dziko. (Ezek. 38:15, 16) * Kodi tiyenera kuopa zimenezi? Ayi. Paja pali gulu la nkhondo limene likutiteteza. Pa nthawi ya chisautso chachikuluyi, gulu la angelo a Yehova lidzafika kuti lititeteze ndipo lidzapha anthu onse otsutsana ndi ulamuliro wa Yehova. (2 Ates. 1:7, 8) Tsiku limenelo lidzakhala losaiwalika. Koma kodi ndani amene azidzatsogolera gulu la angelowo?

YEHOVA ANAVEKA MFUMU NDI WANSEMBE WAKE CHISOTI CHACHIFUMU

12, 13. (a) Kodi Zekariya anauzidwa kuti achite chiyani? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Mphukira ndi Yesu Khristu?

12 Zekariya anaona masomphenya 8. Ataona masomphenyawo anachita zinthu zina zolimbikitsa anthu amene ankamanganso kachisi wa Mulungu. (Werengani Zekariya 6:9-12.) Iye anauzidwa kuti atenge siliva ndi golide kwa Heledai, Tobiya ndi Yedaya, omwe anali atangobwera kumene kuchokera ku Babulo, n’kupangira “chisoti chachifumu chaulemerero.” (Zek. 6:11) Koma Zekariya sanauzidwe kuti aveke chisoticho Bwanamkubwa Zerubabele wa mu fuko la Yuda yemwe anali mumzere wa banja la Davide. Ndipo anthu ayenera kuti anadabwa pamene anaveka chisoticho Yoswa yemwe anali mkulu wa ansembe.

13 Kodi zimenezi zinatanthauza kuti Yoswa anali mfumu? Ayi. Iye sanali mumzere wachifumu wa Davide choncho sanali woyenera kukhala mfumu. Koma zimene Zekariya anachitazo zinasonyeza kuti kudzabwera wina amene adzakhale mfumu mpaka kalekale komanso wansembe. Dzina la amene adzakhale mfumu komanso wansembeyo ndi Mphukira. Malemba amasonyeza kuti Yesu Khristu ndi amene ali Mphukira.​—Yes. 11:1; Mat. 2:23. *

14. Kodi Yesu adzachita chiyani pokwaniritsa udindo wake monga Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe?

14 Yesu, yemwe ndi Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe, ndi amene akutsogolera gulu lankhondo la angelo. Iye amagwira ntchito mwakhama n’cholinga choti gulu la anthu a Mulungu likhale lotetezeka m’dziko loipali. (Yer. 23:5, 6) Posachedwapa, Khristu adzatsogolera pa ntchito yogonjetsa anthu oipa n’cholinga choti ateteze anthu a Mulungu komanso asonyeze kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. (Chiv. 17:12-14; 19:11, 14, 15) Koma Khristu, kapena kuti Mphukira, ali ndi zinthu zina zambiri zoti achite asanagonjetse adaniwo.

ADZAMANGA KACHISI

15, 16. (a) Kodi anthu a Mulungu athandizidwa bwanji kuti ayambenso kulambira Mulungu moyenera komanso akhale oyera, nanga ndi ndani amene wawathandiza? (b) Kodi zinthu zidzakhala bwanji padzikoli pofika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu?

15 Kuwonjezera pa udindo wake monga Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe, Yesu wapatsidwa ntchito ‘yomanga kachisi wa Yehova.’ (Werengani Zekariya 6:13.) Pa ntchito yake yomangayi, Yesu wamasula anthu a Mulungu mu ukapolo wa Babulo Wamkulu ndipo anakhazikitsanso mpingo wachikhristu mu 1919. M’chaka chimenechi anasankhanso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitsogolera pa ntchito imene ikugwiridwa pabwalo la padziko lapansi la kachisi wamkulu wauzimu. (Mat. 24:45) Yesu wakhala akugwiranso ntchito yoyeretsa anthu a Mulungu powathandiza kuti azilambira Mulungu m’njira yoyenera.​—Mal. 3:1-3.

16 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu ndi anthu 144,000, amenenso ndi mafumu ndi ansembe, adzathandiza anthu okhulupirika kuti akhale angwiro. Zimenezi zikadzachitika, padzikoli padzatsala anthu olambira Yehova okhaokha ndipo kulambira koyera kudzakhala kutabwezeretsedwa padziko lonse.

TIZIGWIRA NAWO NTCHITO YOMANGA

17. Kodi Yehova anatsimikizira Ayuda za chiyani, nanga mawu ake anawakhudza bwanji?

17 Kodi Ayuda anamva bwanji atamva uthenga wa Zekariya? Yehova anawatsimikizira kuti awathandiza komanso kuwateteza pa ntchito yomanga kachisi. Mfundo imeneyi iyenera kuti inalimbikitsa kwambiri anthu amene anataya mtima. Koma kodi zikanatheka bwanji kuti anthu ochepa agwire bwinobwino ntchitoyi? Mawu ena amene Zekariya ananena anawalimbikitsa kwambiri pa nkhaniyi. Kuwonjezera pa anthu okhulupirika monga Heledai, Tobiya ndi Yedaya, Mulungu ananena kuti padzakhala anthu ena ambiri omwe “adzabwera kudzamanga nawo kachisi wa Yehova.” (Werengani Zekariya 6:15.) Yehova atawatsimikizira zimenezi, Ayuda anayambanso mwamsanga kumanga kachisi ngakhale kuti ntchitoyo inali italetsedwa. Kuletsa ntchito yomanga kachisi kunali vuto lalikulu kwambiri koma Yehova analithetsa ndipo Ayudawo anamaliza ntchitoyi mu 515 B.C.E. (Ezara 6:22; Zek. 4:6, 7) Koma mawu a Yehova a pa Zekariya 6:15 akufotokozanso zinthu zazikulu kwambiri zomwe zikuchitika masiku ano.

Yehova sadzaiwala zimene timachita posonyeza kuti timamukonda (Onani ndime 18 ndi 19)

18. Kodi lemba la Zekariya 6:15 likukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

18 Masiku ano, anthu mamiliyoni ambiri ayamba kulambira Yehova ndipo iwo amapereka ndi mtima wonse ‘zinthu zawo zamtengo wapatali’ monga nthawi, mphamvu komanso chuma kuti azithandiza pakachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. (Miy. 3:9) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amayamikira zimene timachita? Kumbukirani kuti Heledai, Tobiya ndi Yedaya anabweretsa zinthu zawo kuti Zekariya apangire chisoti chija. Chisoticho chinathandiza “kuti anthu azidzakumbukira” zimene iwo anachita pothandiza pa kulambira koona. (Zek. 6:14) N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Zimene timachita posonyeza kuti timakonda Yehova sizidzaiwalika. (Aheb. 6:10) Yehova adzazikumbukira komanso kuziyamikira mpaka kalekale.

19. Kodi masomphenya a Zekariya angatithandize bwanji masiku ano?

19 M’masiku otsiriza ano, anthu a Yehova achita zinthu zazikulu kwambiri zomwe zikusonyeza kuti Yehova akuwadalitsa komanso Khristu akuwatsogolera. Gulu lathu ndi lotetezeka kwambiri komanso lidzakhalapo mpaka kalekale. Cholinga cha Yehova chokhudza kulambira koona sichidzalephereka. Tiziyamikira kwambiri kuti tili m’gulu la Yehova ndipo tisasiye ‘kumvera mawu a Yehova Mulungu wathu.’ Tikatero, Mfumu yathu yomwenso ndi Mkulu wa Ansembe limodzi ndi angelo amene akwera pamagaleta adzapitiriza kutiteteza. Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe pothandiza kuti kulambira koona kuziyenda bwino. Tikamachita zimenezi, Yehova wa makamu adzatiteteza nthawi imene yatsala m’dziko loipali ndipo sadzatisiya mpaka kalekale.

^ ndime 11 Kuti mumve zambiri onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2015, tsamba 29-30.

^ ndime 13 Mawu oti “Mnazareti” amachokera ku mawu achiheberi akuti “mphukira.”