Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Ndidziŵa Kuti Adzauka”

“Ndidziŵa Kuti Adzauka”

“Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.”—YOH. 11:11.

NYIMBO: 142, 129

1. Kodi Marita anali kukhulupilila ciani ponena za mlongosi wake? (Onani pikica pamwambapa.)

MARITA, amene anali wophunzila wa Yesu komanso bwenzi lake anali na cisoni. Mlongosi wake, Lazaro, anali atamwalila. Kodi n’ciani cikanamutonthoza? Yesu anamutsimikizila kuti: “Mlongo wako adzauka.” Mau amenewa sanathetseletu cisoni ca Marita. Koma iye anakhulupilila zimene Yesu anakamba. Anati: “Ndikudziŵa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.” (Yoh. 11:20-24) Iye anali kukhulupilila kuti m’tsogolo, mlongosi wake adzauka. Ndiyeno, Yesu anacita cozizwitsa. Anaukitsa Lazaro tsiku lomwelo.

2. N’cifukwa ciani mufuna kukhala na cikhulupililo monga ca Marita?

2 Sitiyembekezela kuti Yesu kapena Atate wake angaticitile cozizwitsa ngati cimeneci masiku ano. Koma kodi inu muli na cikhulupililo monga cimene Marita anali naco cakuti m’tsogolo okondedwa anu amene anamwalila adzauka? Mwina munafeledwa mnzanu wa m’cikwati, amayi, atate, kapena ambuye anu. Mwinanso muli na cisoni cifukwa munataikilidwa mwana. Mwacionekele, mumamuyewa wokondedwa wanuyo. Mumayewa kukamba naye, kumukumbatila, kapena kuseka naye. Cokondweletsa n’cakuti monga Marita, muli na cifukwa cabwino cokambila kuti, ‘Nidziŵa kuti wokondedwa wanga adzauka pa kuuka kwa akufa.’ Komabe, kukambilana umboni wakuti ciyembekezo cimeneci n’codalilika kungalimbikitse kwambili cikhulupililo cathu.

3, 4. Pamene Yesu anali kukamba na Marita, kodi anali ataukitsapo kale ndani? Nanga zimenezi ziyenela kuti zinalimbitsa bwanji cikhulupililo ca Marita?

3 Marita anali kukhala kufupi na Yerusalemu osati ku Galileya. Conco, n’zokayikitsa kuti iye anaona pamene Yesu anaukitsa mwana wa mkazi wa masiye, amene anali kukhala kufupi na mzinda wa Naini, ku Galileya. Komabe, n’kutheka kuti Marita anamvela zimene Yesu anacita. N’kuthekanso kuti iye anamvela zakuti Yesu anaukitsa mwana wa Yairo. Anthu amene anali kunyumba kwa mtsikanayo “anali kudziŵa kuti wamwalila.” Ngakhale zinali conco, Yesu anagwila dzanja la wakufayo, na kukamba kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!” Ndipo nthawi yomweyo mtsikanayo anauka. (Luka 7:11-17; 8:41, 42, 49-55) Marita na m’bululu wake Mariya anali kudziŵa kuti Yesu anali kukwanitsa kucilitsa odwala. Conco, iwo anaona kuti Yesu akanakhalapo, sembe mlongosi wawo Lazaro sanamwalile. Koma popeza kuti Lazaro, bwenzi lapamtima la Yesu, anali atamwalila kale, kodi iwo anali na ciyembekezo canji? Onani kuti Marita anakamba kuti Lazaro adzakhalanso na moyo mtsogolo, “m’tsiku lomaliza.” N’cifukwa ciani iye sanakayikile kuti zimenezi zidzacitikadi? Nanga n’cifukwa ciani imwe muyenela kukhulupilila kuti mtsogolo akufa adzauka, kuphatikizapo okondedwa anu?

4 Tili na zifukwa zomveka zokhulupilila kuti akufa adzauka. Pamene tikambilana zina mwa zifukwazo, mungapeze mfundo zina za m’Baibo zimene nthawi zambili simuzigwilizanitsa na ciyembekezo canu cakuti okondedwa anu adzauka.

ZOCITIKA ZIMENE ZIMATIPATSA CIYEMBEKEZO

5. N’ciani cinacititsa Marita kukhulupilila kuti mlongosi wake Lazaro adzauka?

5 Onani kuti Marita sanakambe kuti: ‘Nili na ciyembekezo cakuti mlongosi wanga adzauka.’ Koma anakamba kuti, “Ndikudziŵa kuti adzauka.” Marita anali wotsimikizila za ciukililo cifukwa ayenela kuti anamvapo za anthu amene anaukitsidwa Yesu asanayambe ulaliki wake. Iye anali kuphunzila zimenezi ku nyumba pamene anali wacicepele komanso ku sunagoge. Pali nkhani zitatu za m’Malemba ouzilidwa zimene mwina anali kuzikumbukila.

6. Ni cozizwitsa capadela citi cimene Eliya anacita? Nanga cozizwitsaci cigwilizana bwanji na nkhani ya Marita?

6 Munthu woyamba kuukitsidwa, anaukitsidwa na mneneli Eliya pamene Mulungu anam’patsa mphamvu yocita zozizwitsa. Panthawi ina, mkazi wamasiye ndiponso wosauka wa ku Zarefati, tauni ya m’mbali mwa nyanja m’cigawo ca Foinike, anaceleza mneneli Eliya. Mwa ici, Mulungu mozizwitsa anacititsa kuti ufa na mafuta ake ophikila zisathe, n’colinga cakuti iye na mwana wake asafe na njala. (1 Maf. 17:8-16) Patapita nthawi, mwana wake anadwala mpaka kufa. Koma Eliya anamuthandiza mayiyo. Anagwila mtembo wa mwanayo na kupemphela kwa Mulungu kuti: “Mulungu wanga, conde cititsani kuti moyo wa mwanayu ubwelele mwa iye.” Zimenezi zinacitikadi. Mulungu anamvela pemphelo la Eliya, ndipo mwanayo anakhalanso na moyo. Ameneyu anali munthu woyamba wochulidwa m’Baibo amene anaukitsidwapo. (Ŵelengani 1 Mafumu 17:17-24.) Mwacionekele, Marita anamvelapo za cocitika capadela cimeneci.

7, 8. (a) Fotokozani zimene Elisa anacita pofuna kuthetsa cisoni cimene mzimayi wina anali naco. (b) Kodi cozizwitsa cimene Elisa anacita citsimikizila ciani ponena za Yehova?

7 Munthu waciŵili wochulidwa m’Malemba amene anaukitsidwa, anamuukitsa ni mneneli Elisa, amene analoŵa m’malo mwa Eliya. Mzimayi wina wodziŵika wa ku Sunemu waciisiraeli , anaceleza Elisa mwacikondi kwambili. Iye analibe mwana, koma kupitila mwa mneneli Elisa, Mulungu anadalitsa mzimayiyo na mwamuna wake wokalamba mwa kuwapatsa mwana. Koma patapita zaka, mwanayo anamwalila. Ganizilani cabe cisoni cimene mzimayiyo anakhala naco! Mwamuna wake atamulola, iye anayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 30 kupita ku Phili la Karimeli, kumene kunali Elisa. Mneneliyo anatuma mtumiki wake Gehazi kuti atsogole kupita ku Sunemu. Gehazi analephela kuukitsa mwanayo. Ndiyeno, Elisa anafika pamodzi na amake a mwanayo.—2 Maf. 4:8-31.

8 Atafika ku Sunemu, Elisa analoŵa m’nyumba imene munali mtembowo, ndipo anakhala pa mbali pa mtembowo n’kuyamba kupemphela. Atacita izi, mwanayo anauka ndipo anam’peleka kwa amayi ake. Iwo anakondwela ngako! (Ŵelengani 2 Mafumu 4:32-37) Mzimayiyo ayenela kuti anakumbukila pemphelo la Hana, mkazi amene poyamba anali wosabeleka. Pamene Hana anali kupeleka Samueli ku cihema kuti azitumikila Mulungu, anapemphela kuti: “Yehova . . . ndi Wotsitsila Kumanda, ndiponso Woukitsa.” (1 Sam. 2:6) Mogwilizana ndi mau amenewa, Mulungu anaukitsa mnyamata wa ku Sunemu, kutsimikizila kuti alidi na mphamvu zoukitsa akufa.

9. Fotokozani mmene Mulungu anaseŵenzetsela Elisa pa ciukililo cacitatu cochulidwa m’Baibo.

9 Koma sikuti cimeneci cinali cozizwitsa cothela cimene Mulungu anacita kupitila mwa Elisa. Iye atatumikila monga mneneli kwa zaka 50, “anadwala matenda amene pamapeto pake anafa nawo.” M’kupita kwa nthawi, thupi la Elisa linawonongeka n’kukhala mafupa okha-okha. Panthawi imeneyo, m’dziko la Isiraeli munabwela gulu la acifwamba. Tsiku lina, pamene Aisiraeli ena anali kupita kukaika munthu wina m’manda, anaona gulu la acifwambalo. Cifukwa ca mantha, iwo anangoponya mtembowo m’manda a Elisa n’kuthaŵa. Baibo imakamba kuti: “Mtembowo utangokhudza mafupa a Elisa, munthuyo anakhalanso wamoyo ndipo anaimilila.” (2 Maf. 13:14, 20, 21) Ganizilani cabe mmene nkhani za ciukililo zimenezi zinam’khudzila Marita. Ndithudi, Mulungu ali na mphamvu yogonjetsa imfa. Kodi kuganizila zimenezi kumakukhudzani bwanji? Kodi sikukucititsani kukhulupilila kuti Mulungu ali na mphamvu zopanda malile?

ANTHU AMENE ANAUKITSIDWA M’NTHAWI YA ATUMWI

10. Kodi Petulo anam’thandiza bwanji mlongo wacikhristu amene panthawiyo anali atamwalila?

10 M’Malemba Acigiriki Acikhristu, timaŵelengamo za anthu ena amene Mulungu anawaukitsa kupitila mwa atumiki ake. Mwacitsanzo, Yesu anaukitsa mwana wa mkazi wamasiye kunja kwa mzinda wa Naini, na mwana wa Yairo ku nyumba kwawo. Komanso, mtumwi Petulo anaukitsa mzimayi wacikhristu Dorika (Tabita). Petulo analoŵa m’cipinda cimene munaikidwa mtembo wa mzimayiyo poyembekezela kukauika m’manda. Iye atakhala pa mbali pa mtembowo, anapemphela. Kenako, anati: “Tabita, dzuka!” Mzimayiyo anauka nthawi yomweyo, ndipo Petulo “anamupeleka kwa” Akhristu anzake “ali wamoyo.” Cocitika cimeneci cinali cokhutilitsa kwambili cakuti “ambili anakhala okhulupilila mwa Ambuye.” Iwo anayamba kucitila umboni za Ambuye, ndi kutsimikizila kuti Yehova ali na mphamvu zoukitsa akufa.—Mac. 9:36-42.

11. Kodi Luka anakamba kuti n’ciani cinacitika kwa Utiko? Nanga izi zinawakhudza bwanji anthu ena?

11 Anthu enanso anali na mwayi woona kuukitsidwa kwa munthu wina. Tsiku lina, mtumwi Paulo anali pa msonkhano m’cipinda capamwamba ku Torowa, kumene manje ni kumpoto ca kum’madzulo kwa dziko la Turkey. Pamsonkhanowo, Paulo anakamba nkhani mpaka pakati pa usiku. Mnyamata wina dzina lake Utiko anali kumvetsela atakhala pawindo. Koma anagona ndipo anagwa kucoka pa nyumba yacitatu yosanja mpaka pansi. Mwina Luka, amene anali dokota, ndi amene anayambila kufika pamene Utiko anagwela. Iye atamuona, anakamba kuti Utiko sanavulale cabe kapena kukomoka, koma wafa. Paulo atatsika, anakumbatila mtembowo. Kenako, anakamba mau osangalatsa akuti: “Ali moyo tsopano.” Anthu amene anaona zimenezi ayenela kuti analimbikitsiwa ngako. Iwo anadziŵa kuti mnyamatayo anali atafadi, ndipo anaukitsidwa. Zimenezi “zinawatonthoza kwambili.”—Mac. 20:7-12.

CIYEMBEKEZO COTSIMIKIZILIKA

12, 13. Popeza tadziŵa ena mwa anthu amene anaukitsidwa, kodi lomba tidzakambilana mafunso ati?

12 Nkhani zimene takambilanazi ziyenela kukuthandizani kukhala na cikhulupililo monga ca Marita. Muyenela kukhulupilila kuti Mulungu, amene anatipatsa moyo, ali na mphamvu zoukitsa akufa. N’zocititsa cidwi kuti nthawi iliyonse pamene Yehova anaukitsa munthu wakufa, panaliko mtumiki wokhulupilika wa Mulungu, monga Eliya, Yesu, ndi Petulo. Koma bwanji za anthu ena amene anafa pa nthawi ina m’mbili ya anthu? Kodi anthu okhulupilika amene anali na moyo m’nthawi imene Mulungu sanali kuukitsa akufa, anali naco cikhulupililo cakuti Mulungu adzaukitsa akufa m’tsogolo? Kodi iwo anali na cikhulupililo monga ca Marita, amene anakamba kuti: “Ndikudziŵa kuti [mlongosi wanga] adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza”? N’cifukwa ciani Marita anali kukhulupilila zimenezi? Nanga n’cifukwa ciani na ise tingakhale na cikhulupililo ngati cimeneci?

13 Pali malemba ena m’Baibo amene aonetsa kuti atumiki okhulupilika a Yehova akale, anali kukhulupilila kuti m’tsogolo akufa adzauka. Onani zitsanzo izi:

14. Kodi nkhani ya Abulahamu itiphunzitsa ciani zokhudza ciukililo?

14 Ganizilani zimene Mulungu anauza Abulahamu kuti acite kwa Isaki, mwana wake wolandila coloŵa amene anamuyembekezela kwa nthawi yaitali. Yehova anati: “Tenga Isaki mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiliyo, ndipo . . . ukamupeleke nsembe yopseleza.” (Gen. 22:2) Lamulo limeneli liyenela kuti linamukhudza ngako Abulahamu. Kumbukilani kuti Yehova analonjeza kuti kudzela mwa mbeu ya Abulahamu, mitundu yonse ya anthu idzadalitsidwa. (Gen. 13:14-16; 18:18; Aroma 4:17, 18) Komanso, Yehova anakamba kuti mbeuyo ‘idzacokela mwa Isaki.’ (Gen. 21:12) Koma kodi izi zikanatheka bwanji Abulahamu akanapha mwana wake mwa kumupeleka nsembe? Paulo anauzilidwa kulemba kuti Abulahamu anali kukhulupilila kuti Mulungu ali na mphamvu zoukitsa Isaki kwa akufa. (Ŵelengani Aheberi 11:17-19.) Baibo siikamba kuti Abulahamu anali kukhulupilila kuti akamvela lamulo la Mulungu, Isaki adzaukitsidwa pakapita maola ocepa, tsiku limodzi, kapena wiki imodzi. Abulahamu sanali kudziŵa nthawi imene mwana wake adzaukitsidwa n’kukhalanso na moyo. Koma anali na cikhululupililo cakuti Yehova adzamuukitsa Isaki.

15. Kodi Yobu anali na ciyembekezo canji?

15 Nayenso Yobu wa m’nthawi zakale, anali na ciyembekezo cakuti akufa adzauka mtsogolo. Iye anali kudziŵa kuti mtengo ukadulidwa, umaphukanso n’kukhala ngati watsopano. Koma kwa munthu sizikhala conco. (Yobu 14:7-12; 19:25-27) Munthu akafa, sangauke yekha kumanda n’kukhalanso na moyo. (2 Sam. 12:23; Sal. 89:48) Koma izi sizitanthauza kuti Mulungu angalephele kuukitsa munthu wakufa. Ndipo Yobu anali kukhulupilila kuti nthawi ina m’tsogolo, Yehova adzam’kumbukila. (Ŵelengani Yobu 14:13-15.) Yobu sanali kudziŵa kuti n’liti pamene Mulungu adzacita zimenezo. Komabe, anali na cikhulupililo cakuti Yehova, amene analenga anthu, sangalephele kumukumbukila na kumuukitsa.

16. Kodi mngelo anamulimbikitsa bwanji Danieli?

16 Munthu winanso wokhulupilika amene amachulidwa m’Malemba Aciheberi ni Danieli. Iye anatumikila Mulungu mokhulupilika kwa zaka zambili, ndipo Yehova anali kum’cilikiza. Panthawi ina, mngelo analimbikitsa Danieli, “munthu wokondedwa kwambili,” kuti akhale na “mtendele” ndi kuti akhale “wolimba mtima.”—Dan. 9:22, 23; 10:11, 18, 19.

17, 18. Kodi Mulungu anamulonjeza ciani Danieli cokhudza tsogolo lake?

17 Panthawiyo, Danieli anali atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 100, ndipo masiku a moyo wake anali ku mapeto. N’kutheka kuti iye anali kuganizila za tsogolo lake. Kodi iye anali na ciyembekezo cakuti adzaukitsidwa? Inde! Kumapeto kwa buku la Danieli, timaŵelenga mau olimbikitsa amene Mulungu anamuuza, akuti: “Iwe pita ku mapeto ndipo udzapuma.” (Dan. 12:13) Danieli wokalambayo anadziŵa kuti akufa akupumula; ali ku manda, kumene kulibe ‘kuganiza zocita, kudziŵa zinthu, kapena nzelu.’ Iye anali kudziŵa kuti posacedwa, nayenso adzapita kumeneko. (Mlal. 9:10) Koma sikuti amenewo ndiwo anali mapeto a zonse kwa iye. Mulungu anamulonjeza tsogolo labwino.

18 Mngeloyo anapitiliza kuuza mneneli Danieli kuti: “Udzauka kuti ulandile gawo lako pa mapeto a masikuwo.” Danieli sanauzidwe tsiku limene adzaukitsidwa, kapena kutalika kwa nthawi imene idzapitapo kuti aukitsidwe. Cimene anali kudziŵa n’cakuti adzamwalila na kupumula. Koma pamene mngelo anauza Danieli kuti ‘adzauka kuti alandile gawo lake,’ anaonetselatu kuti Danieli adzaukitsidwa pa ciukililo cam’tsogolo cimene cinali kudzacitika zaka zambili pambuyo pa imfa yake. Mngeloyo anakamba kuti izi zidzacitika “pa mapeto a masikuwo.” Pokamba za lonjezo la Mulungu kwa Danieli, Baibo yochedwa Jerusalem Bible imati: “Udzauka kuti ulandile gawo lako kumapeto kwa nthawiyo.”

Monga Marita, na imwe mungakhale na cidalilo cakuti akufa adzauka (Onani palagilafu 19, 20)

19, 20. (a) Kodi zimene takambilana zigwilizana bwanji na mau amene Marita anakamba kwa Yesu? (b) Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

19 Mwacionekele, Marita anali na zifukwa zomveka zomupangitsa kukhulupilila kuti mlongosi wake wokhulupilika, Lazaro, “adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.” Lonjezo limene Danieli anapatsiwa, komanso yankho loonetsa cikhulupililo limene Marita anapeleka pamene anali kukamba na Yesu, ziyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu cakuti akufa adzauka.

20 Zocitika za m’Baibo zimene takambilana zatithandiza kuona kuti ciukililo n’cotheka. Ndithudi, akufa adzakhalanso na moyo. Taonanso kuti atumiki akale a Mulungu anali na ciyembekezo cakuti pa nthawi ina m’tsogolo, akufa adzaukitsidwa. Koma kodi pali umboni uliwonse woonetsa kuti lonjezo lakuti akufa adzauka lingakwanilitsidwe ngakhale patapita zaka zambili? Ngati umboni ulipo, zingatipatse cifukwa cina cokhalila na ciyembekezo monga ca Marita, cakuti akufa adzauka. Komabe, tingafunse kuti, kodi zimenezi zidzacitika liti? Tidzakambilana mafunso amenewa m’nkhani yotsatila.