Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Makolo—Thandizani Ana Anu Kupeza ‘Nzelu Zowathandiza Kuti Akapulumuke’

Makolo—Thandizani Ana Anu Kupeza ‘Nzelu Zowathandiza Kuti Akapulumuke’

“Kuyambila pamene unali wakhanda, wadziŵa malemba oyela amene angathe kukupatsa nzelu zokuthandiza kuti udzapulumuke.”—2 TIM. 3:15.

NYIMBO: 141, 134

1, 2. N’cifukwa ciani makolo ena amakhala na nkhawa pamene mwana wawo afuna kudzipeleka na kubatizika?

CAKA ciliconse, maphunzilo a Baibo masauzande ambili amadzipeleka kwa Yehova na kubatizika. Ambili mwa iwo ni acicepele amene makolo awo ni Mboni. Acicepele amenewa anasankha umoyo wabwino kwambili. (Sal. 1:1-3) Ngati ndinu kholo lacikhristu, mosakayikila muyembekezela mwacidwi nthawi pamene mwana wanu adzabatizika.—Yelekezelani na 3 Yohane 4.

2 Ngakhale n’conco, mwina mungakhale na nkhawa. N’kutheka kuti mwaonapo acicepele ena amene anabatizika, koma pambuyo pake anayamba kukayikila ngati kutsatila mfundo za Mulungu n’cinthudi canzelu. Ena afika mpaka posiya coonadi. Conco, mukhoza kudela nkhawa kuti mwina mwana wanu angayambe bwino-bwino kutumikila Mulungu, koma m’kupita kwa nthawi angasinthe n’kuleka kukonda coonadi. Ngati zingakhale conco, iye angakhale monga Akhristu a mu mpingo wa Aefeso wa m’nthawi ya atumwi. Ponena za Akhristu amenewo, Yesu anati: “Wasiya cikondi cimene unali naco poyamba.” (Chiv. 2:4) Kodi inu mungam’thandize bwanji mwana wanu kupewa vuto limeneli kuti ‘akule ndi kukhala oyenela cipulumutso’? (1 Pet. 2:2) Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambilane citsanzo ca Timoteyo.

“WADZIŴA MALEMBA OYELA”

3. (a) Kodi Timoteyo anaphunzila bwanji cikhristu? Nanga anacita bwanji na zimene anaphunzilazo? (b) Kodi Paulo analangiza Timoteyo pa mbali zitatu ziti zokhudza kuphunzila?

3 Timoteyo ayenela kuti anaphunzila Cikhristu m’caka ca 47 C.E., pa ulendo woyamba wa mtumwi Paulo wokacezela Akhristu a ku Lusitara. Ngakhale kuti pa nthawiyo Timoteyo anali wacicepele, iye anali kuseŵenzetsa zimene anaphunzila. Patapita zaka ziŵili, anayamba kuyenda na Paulo. Zaka 16 pambuyo pake, Paulo analembela Timoteyo kalata na kumuuza kuti: “Pitiliza kutsatila zimene unaphunzila ndi zimene unakhulupilila pambuyo pokhutila nazo, cifukwa ukudziŵa anthu amene anakuphunzitsa. Kuyambila pamene unali wakhanda, wadziŵa malemba oyela [Malemba Aciheberi] amene angathe kukupatsa nzelu zokuthandiza kuti udzapulumuke kudzela m’cikhulupililo cokhudza Khristu Yesu.” (2 Tim. 3:14, 15) Pamenepa, Paulo anachula zinthu zitatu, (1) kudziŵa malemba oyela, (2) kukhulupilila pambuyo pokhutila na zimene anaphunzila, ndi (3) kupeza nzelu zomuthandiza kuti akapulumuke kudzela m’cikhulupililo cokhudza Khristu Yesu.

4. Ni zida ziti zimene muona kuti n’zothandiza pophunzitsa ana anu? (Onani pikica kuciyambi.)

4 Monga kholo lacikhristu, mumafuna kuti mwana wanu adziŵe malemba oyela, amene masiku ano amaphatikizapo Malemba Aciheberi na Malemba Acigiriki Acikhristu. Malinga ni luso lawo, ngakhale ana aang’ono kwambili angathe kumvetsa zinthu zosavuta monga zokhudza anthu na zocitika za m’Baibo. Gulu la Yehova lapeleka zida zambili zimene makolo angaseŵenzetse pophunzitsa ana awo. Kodi mukumbukilako zida zina zimene zilipo m’citundu canu? Kumbukilani kuti kudziŵa Malemba ndiwo maziko a ubwenzi wolimba na Yehova.

“UNAKHULUPILILA PAMBUYO POKHUTILA NAZO”

5. (a) Kodi ‘kukhulupilila pambuyo pokhutila nazo’ kumatanthauzanji? (b) Tidziŵa bwanji kuti Timoteyo anakhutila na uthenga wabwino wokamba za Yesu?

5 Kudziŵa malemba oyela n’kofunika. Komabe, kuphunzitsa ana coonadi kumafuna zambili kuposa kuwauza cabe za anthu na zocitika za m’Baibo. Kumbukilani kuti Timoteyo ‘anakhulupilila pambuyo pokhutila’ na zimene anaphunzila. M’citundu coyambilila, mau akuti ‘kukhulupilila pambuyo pokhutila,’ amatanthauza “kukhala wosakayikila kuti zinazake n’zoona.” Timoteyo anadziŵa Malemba Aciheberi kuyambila ali wakhanda. Koma m’kupita kwa nthawi, iye anakhulupilila kuti Yesu anali Mesiya cifukwa ca umboni wokhutilitsa umene anapeza. Cikhulupililo ca Timoteyo cinalimba, cakuti anabatizika na kukhala wophunzila wa Yesu. Kenako, anayamba kugwila nchito ya umishonale na Paulo.

6. Kodi mungam’thandize bwanji mwana wanu kuti akhutile na zimene amaphunzila m’Mau a Mulungu na kuzikhulupilila?

6 Kodi mungawathandize bwanji ana anu kukhutila na zimene amaphunzila na kuzikhulupilila ngati mmene Timoteyo anacitila? Coyamba, muzikhala oleza mtima. Pamatenga nthawi kuti munthu akhulupilile zimene amaphunzila. Komanso, ngati inu mumakhulupilila zinazake, sizitanthauza kuti nawonso ana anu adzazikhulupilila. Mwana aliyense amafunika kuseŵenzetsa ‘luntha lake la kuganiza’ kuti akhulupilile coonadi ca m’Baibo. (Ŵelengani Aroma 12:1.) Koma imwe monga kholo, muli na udindo waukulu wom’thandiza mwanayo, maka-maka ngati amakonda kufunsa mafunso. Tiyeni tikambilane citsanzo ca kholo lina.

7, 8. (a) Kodi kholo lina lacikhristu limaonetsa bwanji kuleza mtima pophunzitsa mwana wake? (b) N’cifukwa ciani na imwe muona kuti mufunika kukhala woleza mtima na mwana wanu?

7 Thomas, m’bale amene ali na mwana wa zaka 11 anati: “Nthawi zina, mwana wanga amafunsa mafunso monga akuti, ‘Kodi n’kutheka kuti Yehova anaseŵenzetsa cisanduliko polenga zamoyo padziko?’ kapena, ‘N’cifukwa ciani siticitako zinthu zina zimene anthu ena amacita, monga kuvota, kuti tikonze zinthu padzikoli?’ Nthawi zina, nimacita kudzigwila kuti nisangomuyankha na mfundo imodzi yacindunji. Nimadziŵa kuti munthu sakhuta na nthongo imodzi. Mwana amafunika kumufotokozela zinthu pang’ono ndi pang’ono kuti akakhutile.”

8 Monga mmene Thomas anaonela, kuphunzitsa mwana kumafuna kuleza mtima. Ndipo kuleza mtima n’kofunika kwa Akhristu onse. (Akol. 3:12) Thomas anazindikila kuti mwana angafunike kukamba naye nkhani zina mobweleza-bweleza kuti afike pokhutila. Conco, iye amafotokoza Malemba momveka bwino kwa mwanayo kuti am’thandize kukhulupilila zimene akuphunzila. Thomas anati: “Maka-maka pa nkhani zofunika kwambili, ine na mkazi wanga timafuna kudziŵa ngati mwana wathu akumvetsetsa na kukhulupilila zimene tikumuphunzitsa. Conco, akamafunsa mafunso, timaona kuti zili bwino. Kukamba zoona, timakhalako na nkhawa ngati iye avomeleza zilizonse popanda kufunsa mafunso.”

9. Kodi mungakhomeleze bwanji Mau a Mulungu mwa ana anu?

9 Ngati makolo apitiliza kuphunzitsa ana awo moleza mtima, pang’ono ndi pang’ono anawo adzadziŵa “m’lifupi ndi m’litali ndi kukwela ndi kuzama,” kwa coonadi. (Aef. 3:18) Muyenela kuwaphunzitsa zinthu zogwilizana na msinkhu wawo ndiponso luso lawo lomvetsa zinthu. M’kupita kwa nthawi, adzayamba kukhulupilila zimene akuphunzila, ndipo adzakhala okonzeka kuteteza cikhulupililo cawo pamaso pa ena, kuphatikizapo anzawo a ku sukulu. (1 Pet. 3:15) Mwacitsanzo, kodi ana anu angakwanitse kuseŵenzetsa Baibo pofotokoza zimene zimacitika munthu akamwalila? Kodi zimene Baibo imakamba pankhaniyi amazikhulupilila? * Kukhomeleza Mau a Mulungu mwa ana anu kumafuna kukhala woleza mtima, koma kuli na mapindu ambili.—Deut. 6:6, 7.

10. N’ciani cina cofunika pophunzitsa ana anu?

10 Citsanzo canu n’cofunikanso kwambili pothandiza ana anu kukhulupilila zimene amaphunzila. Stephanie, amene ni kholo la ana atatu, anati: “Kucokela pamene ana anga anali aang’ono, nakhala nikudzifunsa kuti, ‘Kodi nimawauza ana anga cifukwa cake ine nimakhulupilila kuti Yehova aliko, amatikonda komanso kuti mfundo zake n’zabwino? Kodi ana anga amaona kuti ine nimam’kondadi Yehova?’ Siningayembekezele ana anga kukhulupilila zinthu zimene ine sinizikhulupilila.

“NZELU ZOKUTHANDIZA KUTI UDZAPULUMUKE”

11, 12. Kodi nzelu n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani sitingakambe kuti kuculuka kwa zaka ni umboni wakuti munthu ali na nzelu?

11 Monga taonela, Timoteyo, coyamba anali kudziŵa Malemba, ndipo caciŵili anakhulupilila zimene anaphunzila. Koma kodi Paulo anatanthauza ciani pamene anakamba kuti malemba oyela adzathandiza Timoteyo kupeza ‘nzelu zomuthandiza kuti akapulumuke’?

12 Buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, limakamba kuti m’Baibo, nzelu zimatanthauza “luso loseŵenzetsa bwino zimene timadziŵa pofuna kuthetsa mavuto, kupewa ngozi, kukwanilitsa zolinga zinazake, kapena kulangiza ena mmene angacitile zimenezi. Munthu wanzelu ni uja amene sacita zinthu mwaucitsilu.” Baibo imakamba kuti “ucitsilu umakhazikika mumtima mwa mwana.” (Miy. 22:15) Conco, popeza kuti munthu wanzelu sacita zinthu mwaucitsilu, ndiye kuti nzelu n’cizindikilo cakuti munthu ni wacikulile kuuzimu. Cimene cimaonetsa kuti munthu ni wacikulile kuuzimu si kuculuka kwa zaka zake ayi, koma kuopa kwake Yehova na kukhala wokonzeka kumvela malamulo ake.—Ŵelengani Salimo 111:10.

13. Kodi wacicepele angaonetse bwanji kuti ali na nzelu zomuthandiza kuti akapulumuke?

13 Acicepele amene ni acikulile kuuzimu ‘satengekatengeka ngati kuti akukankhidwa ndi mafunde, ndiponso satengeka kupita uku ndi uku’ ndi zilakolako zawo kapena zocita za anzawo. (Aef. 4:14) M’malomwake, amayesetsa kuphunzitsa “mphamvu zawo za kuzindikila” kuti azikwanitsa “kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.” (Aheb. 5:14) Iwo amaonetsa kuti akukula kuuzimu mwa kupanga zosankha mwanzelu, olo pamene makolo awo kapena anthu ena aakulu sakuwaona. (Afil. 2:12) Kucita zinthu mwanjila imeneyi kumaonetsa kuti ali na nzelu zimene n’zofunika kuti akapulumuke. (Ŵelengani Miyambo 24:14.) Kodi mungawathandize bwanji ana anu kukhala na nzelu zaconco? Coyamba, muyenela kuwauza momveka bwino mfundo za m’Baibo zimene imwe mumatsatila. Ndipo mwa zokamba na zocita zanu, muzionetsa kuti mumatsatiladi mfundo za m’Mau a Mulungu pa umoyo wanu.—Aroma 2:21-23.

N’cifukwa ciani makolo afunika kupitiliza kuphunzitsa ndi kuthandiza ana awo? (Onani palagilafu 14-18)

14, 15. (a) Kodi wacicepele amene afuna kubatizika ayenela kuganizila mfundo ziti? (b) Kodi mungam’thandize bwanji mwana wanu kuganizila madalitso amene angapeze cifukwa comvela malamulo a Mulungu?

14 Komabe, kuuza ana anu kuti ici n’cabwino ici n’coipa, pakokha si kokwanila. Mungacitenso bwino kuwathandiza kuganizila pa mafunso monga awa: ‘N’cifukwa ciani Baibo imaletsa zinthu zina zimene zimaoneka zokopa? N’cifukwa ciani nimakhulupilila kuti kutsatila mfundo za m’Baibo n’kopindulitsa pa umoyo wanga?’—Yes. 48:17, 18.

15 Ngati mwana wanu afuna kubatizika, muyenela kumuthandiza kuganizila mosamala za udindo umene munthu amakhala nawo ngati wakhala Mkhristu. Kodi adziŵa mapindu amene angapeze, komanso mavuto amene angakumane nawo cifukwa cokhala Mkhristu? Kodi adziŵa kuti mapindu amakhala oculuka kwambili kuposa mavuto? (Maliko 10:29, 30) Izi n’zimene adzayang’anizana nazo pambuyo pobatizika. Conco, n’kofunika kwambili kuti wacicepele aganizile mafunso amenewa asanapange cosankha cacikulu cobatizika. Makolo, muyenela kuthandiza ana anu kuganizila mosamala za madalitso amene angapeze cifukwa cokhala omvela, komanso mavuto amene angakumane nawo cifukwa ca kusamvela. Mukatelo, cimakhala cosavuta kwa iwo kukhulupilila kuti ngati atsatila mfundo za m’Baibo nthawi zonse, zinthu zidzawayendela bwino.—Deut. 30:19, 20.

NGATI CIKHULUPILILO CA WACICEPELE WOBATIZIKA CAYAMBA KUFOOKA

16. Kodi makolo afunika kuzindikila mfundo iti ngati mwana wawo wobatizika wayamba kufooka m’cikhulupililo?

16 Nanga bwanji ngati pambuyo pobatizika, mwana wanu wayamba kukayikila mfundo zimene timaphunzila? Mwacitsanzo, wacicepele wobatizika wosinkhukilako angayambe kukopeka na zinthu za m’dzikoli, kapena angayambe kukayikila ngati kutsatila mfundo za m’Baibo n’cinthudi coyenela. (Sal. 73:1-3, 12, 13) Monga kholo, mufunika kuzindikila kuti zimene mungacite na mwana wanu amene amakayikila zikhulupililo zake, zingacititse kuti cikhulupililo cake cilimbe kapena cifookeletu. Conco, kaya mwana wanu ni wamng’ono kapena wosinkhukilako, musakangane naye pokambilana nkhani imeneyi. Colinga canu ciyenela kukhala kum’thandiza mwacikondi ndi mokoma mtima.

17, 18. Kodi makolo angathandize bwanji wacicepele amene wayamba kukayikila zimene amakhulupilila?

17 Wacicepele amene wabatizika, amakhala kuti anadzipeleka kwa Yehova. Kudzipeleka ni lonjezo lakuti tidzayamba kukonda Mulungu na kuika cifunilo cake patsogolo kuposa cina ciliconse. (Ŵelengani Maliko 12:30.) Yehova salitenga mopepuka lonjezo limeneli, ndipo aliyense amene wapanga lonjezoli sayenela kuliona mopepuka. (Mlal. 5:4, 5) Conco, panthawi yoyenela, muyenela kukumbutsa mwana wanu mokoma mtima mfundo zimenezi. Koma musanacite izi, seŵenzetsani mwaluso zofalitsa zokhala na malangizo othandizila acicepele, zimene gulu la Yehova lapeleka kwa makolo. Mwa kucita izi, mudzayala maziko abwino othandizila mwana wanu kudziŵa kuti kudzipeleka na kukhala Mkhristu ni nkhani yaikulu, ndiponso kumabweletsa madalitso oculuka.

18 Mwacitsanzo, mungapeze malangizo othandiza pa kamutu kakuti “Mafunso Amene Makolo Amadzifunsa,” kamene kali m’cigawo ca zakumapeto m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa—Buku Loyamba. M’nkhaniyo, muli malangizo akuti: “Musafulumile kuganiza kuti mwana wanu sakugwilizana ndi zimene mumakhulupilila. Nthawi zambili pamakhala cinacake cimene cikumucititsa kuti asamakondenso zinthu zauzimu.” Mwina cingakhale cifukwa cotunthiwa na anzake. Kapena cingakhale cifukwa cosungulumwa, kapenanso cifukwa codziona kuti sacita bwino mwauzimu poyelekeza na acicepele anzake acikhristu. Nkhaniyo inapitiliza kuti: “Dziŵani kuti zimene mwana wanu akucitazo sizikusonyeza kuti akudana ndi zimene mumakhulupilila. Vuto limene lilipo ndi lakuti akukumana ndi zinthu zimene zikumucititsa kuona kuti kutsatila zimene mumakhulupilila n’kovuta.” Ndiyeno, inafotokoza zimene kholo lacikhristu lingacite pothandiza mwana wawo amene wayamba kukayikila zimene amakhulupilila.

19. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukhala na ‘nzelu zowathandiza kuti akapulumuke’?

19 Monga kholo, muli na udindo waukulu ndiponso mwayi wolela ana anu “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Ndipo monga mmene taonela, izi zimaphatikizapo zambili kuposa kuwaphunzitsa cabe zimene Baibo imakamba. Zimaphatikizaponso kuwathandiza kukhulupilila zimene amaphunzila. Ana amafunika kukhala na cikhulupililo colimba, cimene cingawalimbikitse kudzipeleka kwa Yehova mwa kufuna kwawo na kum’tumikila na mtima wonse. Conco, tili na cikhulupililo cakuti mwa Mau a Yehova, mzimu wake, na khama lanu, mudzakwanitsa kuthandiza ana anu kukhala na ‘nzelu zowathandiza kuti akapulumuke.’

^ par. 9 Mfundo zothandiza pophunzila buku lakuti “Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni” ni cida camphamvu cimene cingathandize acicepele na acikulile. Mfundo zimenezi zingawathandize kumvetsetsa coonadi ca m’Baibo na kudziŵa mmene angaphunzitsileko ena. Mfundo zimenezi zilipo m’zitundu zosiyana-siyana pa webusaiti yathu. Pitani pa peji ya Chichewa ya jw.org, na kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA >ZOKUTHANDIZANI POPHUNZIRA BAIBULO.