Makolo, Thandizani Ana Anu Kupeza Nzeru Kuti Adzapulumuke

Makolo, Thandizani Ana Anu Kupeza Nzeru Kuti Adzapulumuke

Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke.”​—2 TIM. 3:15.

NYIMBO: 141, 134

1, 2. N’chifukwa chiyani makolo ena amada nkhawa akaona kuti ana awo akufuna kubatizidwa?

ANTHU ambiri amene amaphunzira Baibulo amadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. Ambiri mwa anthuwa amakhala ana obadwira m’banja la Mboni ndipo amakhala kuti asankha moyo wabwino kwambiri. (Sal. 1:1-3) Ngati ndinu makolo, muyenera kuti mumalakalaka kuona mwana wanu akubatizidwa.​—Yerekezerani ndi 3 Yohane 4.

2 Koma mwina mumada nkhawa mukaganizira zimene achinyamata ena amachita. Ena amabatizidwa koma pakapita nthawi amayamba kukayikira ngati ndi nzeru kutsatira mfundo za m’Baibulo. Ana ena amafika posiya kutumikira Yehova. Ndiye mwina mumaganiza kuti mwana wanu akhoza kuyamba bwinobwino kutumikira Yehova koma kenako n’kusiya. Mumaona kuti angafanane ndi Akhristu a ku Efeso amene Yesu anawauza kuti: ‘Mwasiya chikondi chimene munali nacho poyamba.’ (Chiv. 2:4) Kodi inuyo mungatani kuti mwana wanu asachite zimenezi koma apeze ‘nzeru zomuthandiza kuti adzapulumuke’? (1 Pet. 2:2) Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane chitsanzo cha Timoteyo.

“WADZIWA MALEMBA OYERA”

3. (a) Kodi Timoteyo anayamba kudziwa za Chikhristu pa nthawi iti, nanga anatani ndi zimene ankaphunzira? (b) Kodi Paulo anatchula zinthu zitatu ziti zokhudza kuphunzira?

3 Zikuoneka kuti Timoteyo anayamba kudziwa za Chikhristu mu 47 C.E., pa nthawi yoyamba imene Paulo anafika ku Lusitara. Ngakhale kuti pa nthawiyo Timoteyo anali wachinyamata, ayenera kuti ankayesetsa kutsatira zimene ankaphunzira. Tikutero chifukwa chakuti patangopita zaka ziwiri, iye anayamba kuyenda ndi Paulo. Patapitanso zaka 16, Paulo analembera Timoteyo kalata ndipo anati: “Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo, chifukwa ukudziwa anthu amene anakuphunzitsa. Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.” (2 Tim. 3:14, 15) N’zochititsa chidwi kuti Paulo anatchula (1) kudziwa malemba oyera, (2) kukhulupirira pambuyo pokhutira ndi zimene waphunzira komanso (3) kupeza nzeru zothandiza kuti apulumuke chifukwa chokhulupirira Khristu Yesu.

4. Kodi inuyo mwaona kuti ndi zinthu ziti zimene zimakuthandizani pophunzitsa ana aang’ono? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 Ngati ndinu makolo, muyenera kuti mumafuna kuti mwana wanu adziwe malemba oyera, omwe masiku ano ndi Malemba Achiheberi komanso Achigiriki. Ngakhale ana aang’ono akhoza kuphunzira za anthu ena komanso nkhani zina za m’Baibulo. Ndipo gulu la Yehova lapereka zinthu zambiri zimene zingathandize makolo pophunzitsa ana awo. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimapezeka m’chilankhulo chanu? Musaiwale kuti kudziwa Malemba n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

“UNAKHULUPIRIRA PAMBUYO POKHUTIRA NAZO”

5. (a) Kodi mawu oti “unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo” amatanthauza chiyani? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Timoteyo anayamba kukhulupirira kwambiri uthenga wabwino wonena za Yesu?

5 N’zoona kuti kudziwa malemba oyera n’kofunika kwambiri. Koma kuti mwana ayambe kukonda Yehova pamafunika zambiri osati kungodziwa nkhani kapena anthu otchulidwa m’Baibulo. Paja tanena kale kuti Timoteyo ‘anakhulupirira zinthu pambuyo pokhutira nazo.’ M’Chigiriki, mawu amenewa amatanthauza kuti “anatsimikiziridwa” kapena kuti “anapeza umboni wakuti ndi zoona.” Timoteyo ankadziwa Malemba Achiheberi kuyambira ali wakhanda. Koma kenako iye anapeza umboni womutsimikizira kuti Yesu ndi Mesiya. M’mawu ena tingati iye anatsimikizira kuti zimene ankadziwa n’zolondola. Zimene anatsimikizirazo zinamuthandiza kukhulupirira kwambiri uthenga wabwino moti anabatizidwa n’kuyamba kuchita umishonale limodzi ndi Paulo.

6. Kodi inuyo mungathandize bwanji mwana wanu kuti azikhulupirira zimene waphunzira m’Mawu a Mulungu?

6 Kodi inuyo mungathandize bwanji ana anu kuti akhale ndi chikhulupiriro ngati cha Timoteyo? Choyamba muyenera kukhala oleza mtima. Chikhulupiriro choterechi sichingayambe lero ndi lero ndipo ana anu sangayambe kukhulupirira zinthu chifukwa choti inuyo mumazikhulupirira. Mwana aliyense amafunika kugwiritsa ntchito luso lake la kuganiza kuti ayambe kukhulupirira mfundo za m’Baibulo? (Werengani Aroma 12:1.) Ndiyeno inuyo monga makolo muli ndi udindo wothandiza ana anu pa nkhaniyi, makamaka ngati akukufunsani zinazake. Tiyeni tikambirane chitsanzo chimodzi.

7, 8. (a) Kodi m’bale wina amasonyeza bwanji kuleza mtima pophunzitsa mwana wake? (b) Kodi inuyo mumafunika kuleza mtima pa nthawi iti?

7 M’bale wina dzina lake Thomas, yemwe ali ndi mwana wazaka 11, ananena kuti: “Mwana wanga akhoza kundifunsa funso monga lakuti, ‘Kodi n’zotheka kuti Yehova analenga zinthu padzikoli pochititsa kuti zamoyo zisinthe kuchokera ku zinthu zina?’ kapena lakuti, ‘N’chifukwa chiyani sitichita nawo zinthu zina zothandiza m’dzikoli monga kuvota?’ Nthawi zina ndimafunika kudziletsa kuti ndisamangomuuza zimene ayenera kukhulupirira. Ndimadziwa kuti munthu sangakhulupirire zinthu chifukwa chongouzidwa mfundo zambiri nthawi imodzi koma amayamba kukhulupirira ataona umboni wosiyanasiyana.”

8 Thomas amadziwanso kuti pamafunika kuleza mtima pophunzitsa mwana. Ndipotu kuleza mtima n’kofunika kwa Akhristu onse. (Akol. 3:12) Thomas amadziwa kuti pamafunika kukambirana ndi mwana wakeyo maulendo ambiri kuti afike pokhulupirira zinthu. Amafunika kukambirana naye pogwiritsa ntchito Malemba kuti atsimikizire kuti zimene akuphunzira n’zoona. Thomas ananenanso kuti: “Ine ndi mkazi wanga timayesetsa kutsimikizira ngati mwana wathu akumvetsa komanso kukhulupirira zimene akuphunzira, makamaka ngati zili mfundo zofunika kwambiri. Ndimasangalala akamatifunsa mafunso. Ndipo ndikaona kuti wangovomereza mfundo inayake popanda kufunsa mafunso, zimandidetsa nkhawa.”

9. Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti amvetse Mawu a Mulungu n’kumawakhulupirira?

9 Ana akamaphunzitsidwa ndi makolo awo moleza mtima, pang’ono ndi pang’ono amayamba kudziwa bwino ‘m’lifupi ndi m’litali komanso kukwera ndi kuzama’ kwa zimene amakhulupirira. (Aef. 3:18) Tiyenera kuwaphunzitsa zinthu mogwirizana ndi msinkhu wawo komanso luso lawo. Akafika pokhutira ndi zimene akuphunzira, akhoza kuzifotokoza momveka bwino kwa anzawo kusukulu komanso kwa anthu ena. (1 Pet. 3:15) Mwachitsanzo, kodi mwana wanu akhoza kugwiritsa ntchito Malemba pofotokoza zimene zimachitika munthu akamwalira? Nanga kodi amaona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi n’zomveka? * Kunena zoona, kuphunzitsa mwana kuti afike pomvetsa bwino Mawu a Mulungu n’kumawakhulupirira kumafuna khama, koma n’kothandiza kwambiri.​—Deut. 6:6, 7.

10. Kodi chinthu china chofunika pophunzitsa ana anu n’chiyani?

10 Koma pa nkhani yothandiza ana kuti azikhulupirira Mawu a Mulunguyi, chinthu china chofunika ndi chitsanzo chanu. Mlongo wina dzina lake Stephanie, yemwe ali ndi ana atatu anati: “Kuyambira ana anga ali aang’ono ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ndimafotokozera ana anga chifukwa chake ineyo sindikayikira zoti Yehova aliko, amatikonda komanso kuti njira zake zonse ndi zolungama. Kodi ana anga amaona kuti ineyo ndimakonda kwambiri Yehova?’ Sindingayembekezere kuti ana anga azikhulupirira Mawu a Mulungu ngati ineyo sindiwakhulupirira kwambiri.”

“NZERU ZOKUTHANDIZA KUTI UDZAPULUMUKE”

11, 12. Kodi nzeru n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti sizidalira msinkhu wa munthu wokha?

11 Taona kale kuti Timoteyo (1) ankadziwa Malemba ndipo (2) ankakhulupirira zimene anaphunzira. Koma kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti malemba oyera angathandize Timoteyo ‘kupeza nzeru zomuthandiza kuti adzapulumuke’?

12 Buku lakuti Insight on the Scriptures, voliyumu 2, limanena kuti m’Baibulo, mawu oti nzeru amatanthauza “kugwiritsa ntchito bwino zimene ukudziwa pofuna kuthana ndi mavuto, kupewa zinthu zoopsa, kukwaniritsa zolinga kapena kulangiza anthu ena. Nzeru ndi zosiyana kwambiri ndi uchitsiru.” Baibulo limanena kuti: “Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.” (Miy. 22:15) Choncho tinganene kuti munthu akamachita zinthu mwanzeru umakhala umboni wakuti ndi wamkulu. Ndipo kukula mwauzimu sikudalira msinkhu wa munthu koma zimene amachita pomvera Yehova ndi mtima wonse komanso kumuopa.​—Werengani Salimo 111:10.

13. Kodi achinyamata angasonyeze bwanji kuti ali ndi nzeru zowathandiza kuti adzapulumuke?

13 Achinyamata amene akula mwauzimu salola kuti zimene amalakalaka kapena zimene anzawo amachita ziwasokoneze. Tingati sakhala ‘otengekatengeka ngati kuti akukankhidwa ndi mafunde, ndiponso otengeka kupita uku ndi uku.’ (Aef. 4:14) M’malomwake ‘amaphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kuti azisiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheb. 5:14) Iwo amasonyeza kuti akukula mwauzimu akamasankha zochita mwanzeru, ngakhale pamene kulibe makolo awo kapena anthu ena. (Afil. 2:12) Nzeru zoterezi n’zimene zingathandize munthu kuti adzapulumuke. (Werengani Miyambo 24:14.) Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti apeze nzeru zoterezi? Choyamba, muyenera kufotokozera ana anu momveka bwino mfundo za m’Baibulo zimene mumatsatira. Zolankhula komanso zochita zanu zizisonyeza kuti mumatsatiradi mfundo za m’Mawu a Mulungu.​—Aroma 2:21-23.

N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuchitabe khama pophunzitsa ana awo? (Onani ndime 14-18)

14, 15. (a) Kodi wachinyamata amene akufuna kubatizidwa ayenera kuganizira zinthu ziti? (b) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti aziganizira madalitso amene angapeze chifukwa chomvera malamulo a Mulungu?

14 Koma kungouza ana anu kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika si kokwanira. Ndi bwino kuwathandiza kuganizira mafunso monga akuti: ‘N’chifukwa chiyani Baibulo limatsutsa zinthu zimene thupi lathu limalakalaka? N’chiyani chikunditsimikizira kuti kutsatira mfundo za m’Malemba kungandithandize kuti zinthu zizindiyendera bwino?’​—Yes. 48:17, 18.

15 Mwana amene akufuna kubatizidwa ayenera kuthandizidwa kuti aganizire bwino zinthu zina. Ayenera kuganizira udindo umene munthu amakhala nawo akabatizidwa. Ayeneranso kuona zinthu zabwino zimene angapeze komanso mavuto amene angakumane nawo. Ndiyeno ayenera kuyerekezera zinthu ziwirizi n’cholinga choti aone kuti ubwinowo ndi waukulu kwambiri kuposa mavuto amene angakumane nawo. (Maliko 10:29, 30) Kuganizira mfundo zimenezi munthu asanabatizidwe n’kofunika chifukwa chakuti n’zimene zingamuthandize akadzabatizidwa. Mwana akathandizidwa kuzindikira madalitso amene angapeze akamamvera Mulungu komanso mavuto amene angapeze ngati samumvera, akhoza kukhutira ndi zimene amakhulupirira. Iye sangakayikire kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza nthawi zonse.​Deut. 30:19, 20.

NGATI WACHINYAMATA WOBATIZIDWA AKUKAYIKIRA ZIMENE AMAKHULUPIRIRA

16. Kodi makolo ayenera kuchita chiyani ngati mwana wawo wobatizidwa wayamba kukayikira zimene amakhulupirira?

16 Kodi mungatani ngati mwana wanu wobatizidwa wayamba kukayikira zimene amakhulupirira? Mwachitsanzo, wachinyamata wobatizidwa akhoza kuyamba kukopeka ndi zinthu za m’dzikoli kapena kukayikira zoti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza. (Sal. 73:1-3, 12, 13) Zimenezi zikachitika, yankho limene makolo angapereke lingachititse kuti mwanayo ayambe kukhulupirira kwambiri mfundo za m’Malemba kapena asiye kuzikhulupirira. Koma kaya mwanayo ndi wamng’ono kapena wamkulu, simuyenera kukangana naye pa nkhani imeneyi. Cholinga chanu chizikhala kumuthandiza mwachikondi kuti asinthe maganizo akewo.

17, 18. Kodi makolo angathandize bwanji mwana amene wayamba kukayikira zimene amakhulupirira?

17 N’zoona kuti mwana amene wabatizidwa amakhala atadzipereka kwa Yehova. Ndipo podziperekapo amalonjeza kuti azikonda Mulungu komanso kuika patsogolo zofuna zake. (Werengani Maliko 12:30.) Yehova amaona kuti lonjezo limeneli ndi lofunika kwambiri ndipo ndi mmene aliyense ayenera kulionera. (Mlal. 5:4, 5) Choncho makolo ayenera kupeza nthawi yabwino komanso njira yabwino yomukumbutsira mwana wawo mfundo imeneyi. Koma asanachite zimenezi, ayenera kufufuza kaye zinthu zothandiza pophunzitsa ana zimene gulu la Yehova lapereka. Akatero adzatha kuthandiza mwanayo kuti amvetse zoti munthu akadzipereka kwa Mulungu n’kukhala Mkhristu amakhala ndi udindo waukulu koma amapezanso madalitso ambiri.

18 Mwachitsanzo, malangizo abwino mungawapeze m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba. Malangizowa akupezeka pa Zakumapeto pa kamutu kakuti “Mafunso Amene Makolo Amadzifunsa.” Bukuli limati: “Musafulumire kuganiza kuti mwana wanu sakugwirizana ndi zimene mumakhulupirira. Nthawi zambiri pamakhala chinachake chimene chikumuchititsa kuti asamakondenso zinthu zauzimu.” Nthawi zina angakhale anzake amene akumusokoneza, apo ayi mwina akusowa ocheza nawo kapena akuona kuti anzake amumpingo zikuwayendera bwino kuposa iyeyo. Bukulo limapitiriza kuti: “Dziwani kuti zimene mwana wanu akuchitazo sizikusonyeza kuti akudana ndi zimene mumakhulupirira. Vuto limene lilipo ndi lakuti akukumana ndi zinthu zimene zikumuchititsa kuona kuti kutsatira zimene mumakhulupirira n’kovuta.” Ndiyeno m’bukuli muli mfundo zimene makolo angagwiritse ntchito pothandiza mwana wawo amene wayamba kukayikirayo.

19. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kupeza ‘nzeru zowathandiza kuti adzapulumuke’?

19 Makolo ali ndi mwayi komanso udindo waukulu wolera ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Munkhaniyi taona kuti izi zingatheke ngati makolowo amaphunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo komanso kuwathandiza kuti azizikhulupirira kwambiri. Chikhulupiriro chawo chiyenera kukhala champhamvu moti chingawalimbikitse kudzipereka kwa Yehova n’kumamutumikira ndi mtima wonse. Tikukhulupirira kuti Mawu a Yehova, mzimu wake komanso khama lanu zidzathandiza kuti ana anu apeze ‘nzeru zowathandiza kuti adzapulumuke.’

^ ndime 9 Pawebusaiti yathu pali nkhani zakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?” Nkhani zimenezi zikhoza kuthandiza ana ndi akulu omwe kuti azitha kumvetsa komanso kufotokoza mfundo za m’Baibulo. Mungazipeze pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ZOKUTHANDIZANI POPHUNZIRA BAIBULO.