Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Inuyo Mukuganiza Bwanji?

Kodi Inuyo Mukuganiza Bwanji?

Kodi Baibulo lingakuthandizeni kuti Mulungu akhale mnzanu?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA . . .

kuti sangakhale mabwenzi a Mulungu chifukwa amaona kuti ndi ochimwa. Ena amaganiza kuti Mulungu satidera nkhawa. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu “amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Tikamamvera Mulungu, tingathe kukhala mabwenzi ake.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Mulungu amafuna kuti tikhale anzake.​—Yakobo 4:8.

  • Popeza Yehova ndi Mnzathu, amakhala wokonzeka kutithandiza komanso kutikhululukira.​—Salimo 86:5.

  • Mabwenzi a Mulungu amakonda zimene iye amakonda ndiponso amadana ndi zimene iye amadana nazo.​—Aroma 12:9.