Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muganiza Bwanji?

Muganiza Bwanji?

Kodi Baibo ingakuthandizeni kukhala bwenzi la Mulungu?

ANTHU ENA AMAKHULUPILILA KUTI . . .

sangakhale mabwenzi a Mulungu cifukwa amadziona kuti ni odetsedwa komanso ocimwa. Ena amakamba kuti Mulungu satidela nkhawa. Imwe muganiza bwanji?

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

Mulungu “amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Ngati timvela Mulungu, tingakhale mabwenzi ake.

MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

  • Mulungu afuna kuti tikhale mabwenzi ake. —Yakobo 4:8.

  • Monga Bwenzi lathu, Mulungu ni wokonzeka kutikhululukila na kutithandiza.—Salimo 86:5.

  • Mabwenzi a Mulungu amakonda zimene iye amakonda na kudana na zimene amadana nazo. —Aroma 12:9.