Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Okhulupirira Nyenyezi Komanso Olosera Angatithandizedi Kudziwa Zam’tsogolo?

Kodi Okhulupirira Nyenyezi Komanso Olosera Angatithandizedi Kudziwa Zam’tsogolo?

OKHULUPIRIRA NYENYEZI

Kukhulupirira nyenyezi ndi mtundu wina wa kuombeza. Okhulupirira nyenyezi amaona kuti zinthu zakuthambo monga nyenyezi, mwezi komanso mapulaneti zimakhudza zochita za anthu padziko lapansi pano. Amanena kuti kayendedwe ka zinthu zakuthambo pa nthawi imene munthuyo anabadwa kangawathandize kudziwa za tsogolo la munthuyo komanso khalidwe lake.

Kukhulupirira nyenyezi n’kofala m’madera ambiri masiku ano ngakhale kuti kunayamba kale kwambiri ku Babulo.Malinga ndi kafukufuku wina yemwe anachitika mu 2012 ku United States, munthu m’modzi pa atatu aliwonse amene anafunsidwa ananena kuti kukhulupirira nyenyezi “kukhoza kukhala sayansi,” pomwe munthu mmodzi pa 10 aliwonse ananena kuti kukhulupirira nyenyezi ndi “sayansi yeniyeni.” Koma kodi zimenezi n’zoona? Ayi. Tiyeni tione zifukwa zake.

  • Mapulaneti komanso nyenyezi sizimakhala ndi mphamvu iliyonse yomwe ingakhudze zochita za anthu ngati mmene okhulupirira nyenyezi amanenera.

  • Nthawi zambiri zimene wolosera mmodzi anganene zimakhala zoti zikhoza kuchitikira wina aliyense.

  • Mmene anthu okhulupirira nyenyezi amawerengera madeti awo amatengera chikhulupiriro chakuti mapulaneti amayenda mozungulira dziko lapansi. Koma zoona zake n’zakuti mapulaneti amazungulira dzuwa.

  • Zimene okhulupirira nyenyezi osiyanasiyana amalosera zokhudza munthu mmodzimodziyo zimakhala zosiyana.

  • Okhulupirira nyenyezi amaika anthu m’magulu 12 a zizindikiro zakuthambo mogwirizana ndi tsiku limene munthu anabadwa. Koma n’kupita kwa nthawi kayendedwe ka dziko kamasintha, choncho tsiku lomwe munthu anabadwa siligwirizananso ndi gulu la nyenyezi zomwe zikuoneka pa nthawiyo.

Okhulupirira nyenyeziwa amanena kuti zizindikiro zakuthambo zingawathandize kudziwa khalidwe la munthu. Koma kunena zoona, anthu omwe anabadwa patsiku limodzi sakhala ndi khalidwe lofanana. Choncho tsiku limene munthu anabadwa silingachititse kuti akhale ndi khalidwe linalake. M’malo moona anthu mmene alilidi, okhulupirira nyenyezi amangoweruza kuti munthu ali ndi khalidwe linalake chifukwa cha tsiku limene anabadwa. Kodi kuchita zimenezi si tsankho?

OLOSERA ZAM’TSOGOLO

Kuyambira kale, anthu akhala akupita kwa olosera kuti akawathandize kudziwa za tsogolo lawo. Oloserawo amanena kuti angathe kudziwa zimenezi poona zochita za nyama komanso anthu. Ena amalosera potengera mmene mizera ya m’manja ilili, potanthauzira kulira kwa mbalame kapenanso kumasulira maloto. M’madera ena anthu amakonda kugwiritsa ntchito makadi, galasi lamatsenga, miyala komanso zinthu zina kuti adziwe tsogolo la munthu. Kodi anthu olosera zam’tsogolo angatithandizedi kudziwa tsogolo lathu? Ayi, sangatithandize. Tiyeni tione zifukwa zake.

Zinthu zimene amalosera sizifanana. Olosera zam’tsogolowa amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana ndipo zimapezeka kuti zimene apeza zikutsutsana. Ngakhale akakhala kuti akugwiritsa ntchito njira imodzi, amapezabe zinthu zosiyana. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti munthu wapempha olosera zam’tsogolo omwe amagwiritsa ntchito makadi kuti amuuze zokhudza tsogolo lake pogwiritsa ntchito makadi ofanana. Munthuyu angayembekezere kumva zofanana kuchokera kwa olosera onsewo. Komatu zimenezi si zomwe zimachitika.

Anthu amakayikira njira komanso zolinga zomwe anthu olosera zam’tsogolo amakhala nazo. Anthu ena amanena kuti makadi olosera kapena magalasi amatsenga ndi zipangizo chabe. Oloserawa amaona zimene munthu akuchita komanso mmene akuyankhulira osati zipangizo zawozi. Mwachitsanzo, munthu yemwe ndi katswiri pa nkhani yoloserayi, amafunsa mafunso n’kumamvetsera mosamala komanso kuona zimene munthu akuchita zomwe zingamuthandize kudziwa zambiri. Munthu akamva woloserayo akumuuza zinthu zomwe anazitchula yekha mosazindikira, amaona kuti woloserayo ndi katswiri. Anthu amayamba kuwakhulupirira ndipo olosera ena adyapo ndalama zankhaninkhani atanamiza anthu mwa njira imeneyi.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kukhulupirira nyenyezi komanso kulosera zam’tsogolo kumachititsa anthu kukhulupirira kuti tsogolo la wina aliyense linalembedweratu. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Baibulo limanena kuti munthu aliyense amasankha yekha zimene akufuna kukhulupirira kapena kuchita ndipo zosankha zakezo n’zimene zimakhudza tsogolo lake.​—Yoswa 24:15.

Anthu amene amalambira Mulungu ali ndi chifukwa chinanso chopewera kukhulupirira nyenyezi komanso kulosera zam’tsogolo. Chifukwa chake ndi chakuti Mulungu amadana ndi anthu amene amachita zimenezi. M’Baibulo mumapezeka mawu awa: “Pakati panu pasapezeke munthu . . . wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa. Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.” *​—Deuteronomo 18:10-12.

^ ndime 17 Yehova ndi dzina la Mulungu “Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”​—Salimo 83:18.