Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kukhulupilila Nyenyezi Komanso Kulosela Zakutsogolo—Kodi N’kodalilika?

Kukhulupilila Nyenyezi Komanso Kulosela Zakutsogolo—Kodi N’kodalilika?

KUKHULUPILILA NYENYEZI

Kukhulupilila zinthu zakuthambo monga nyenyezi, dzuŵa, mwezi, na mapulaneti, ni m’tundu winanso wa kuombeza. Anthu amakhulupilila kuti zinthu zimenezi zimatsogolela umoyo wa anthu padziko lapansi. Okhulupilila zakuthambo amakamba kuti zinthuzi zikaima pa malo ena ake panthawi imene munthu wabadwa, ndiye kuti munthuyo adzakhala ndi khalidwe lakuti-lakuti kapena tsogolo lake lidzakhala lakuti-lakuti. Ngakhale kuti kukhulupilila zakuthambo kunayamba kale-kale ku Babulo wakale, mpaka pano kukali kofala. Malinga na kafuku-fuku amene anacitika mu 2012 ku United States, mmodzi pa anthu atatu amene anafunsiwa mafunso, anati kukhulupilila zakuthambo “kumagwilizanako na sayansi,” ndipo 10 pelesenti anati “kumagwilizana kwambili na sayansi.” Kodi zimenezi n’zoona? Iyayi. Zifukwa zake ni izi.

  • Mapulaneti na nyenyezi zilibe mphamvu yotsogolela umoyo wa anthu, monga mmene okhulupilila zakuthambo amakambila.

  • Nthawi zambili olosela amakamba zinthu zakuti zingacitike kwa aliyense.

  • Zimene okhulupilila zakuthambo amalosela masiku ano, zimazikidwa pa cikhulupililo cakale cakuti mapulaneti amazungulila dziko. Koma zoona n’zakuti mapulaneti amazungulila dzuŵa.

  • Zimene okhulupilila zakuthambo osiyana-siyana amalosela zokhudza munthu mmodzi zimasiyana.

  • Okhulupilila zakuthambo amaika anthu m’magulu 12 poseŵenzetsa zizindikilo za zinthu zakuthambo. Ndiyeno amagwilizanitsa madeti a kubadwa kwa anthu na zizindikilo zimenezo. Koma cifukwa cakuti dziko limasintha malo ake m’cilengedwe pakapita zaka mahandiledi ambili, madeti amene anawagwilizanitsa na zizindikilo zakumwamba sagwilizananso na nthawi pamene dzuŵa likudutsa m’magulu a nyenyezi.

Anthu ena amakamba kuti zizindikilo za zinthu zakuthambo zimaonetsa mmene khalidwe la munthu lidzakhalila. Koma zoona n’zakuti anthu amene anabadwa tsiku limodzi-modzi sakhala na makhalidwe ofanana. Deti la kubadwa la munthu silionetsa ciliconse cokhudza khalidwe limene adzakhala nalo. M’malo moona anthu kuti ndiye mmene alili, okhulupilila zakuthambo amaweluza anthu mwa kuona makhalidwe na zocita zawo. Kodi kumeneku si kuweluzilatu anthu?

KULOSELA ZAKUTSOGOLO

Kuyambila kale-kale, anthu akhala akufunsila kwa olosela zakutsogolo. Pofuna kudziŵa zakutsogolo, olosela ena anali kuseŵenzetsa matumbo a zinyama ndi a anthu komanso kuona mmene tambala adobela zakudya. Ena anali kuseŵenzetsa tumizela twa pa tsamba la tiyi, kapena pa njele ya khofi. Masiku ano, olosela zakutsogolo amaseŵenzetsa makhadi a njuga za matsenga, mipila ya gilasi, tunthu tocitila mayele, na zina za conco pofuna “kudziŵa” tsogolo la munthu. Kodi kufunsila kwa olosela ndiye njila yodalilika yodziŵila zakutsogolo? Iyayi. Tiyeni tikambilane zifukwa zake.

Ganizilani za kusadalilika kwake. Njila zimene olosela amaseŵenzetsa pofuna kudziŵa zakutsogolo zimasiyana-siyana, koma zimene amapeza kambili sizigwilizana. Olo kuti aseŵenzetse njila yofanana, zimene amapeza zimasiyana. Mwacitsanzo, ngati munthu angafunse funso limodzi-modzi lokhudza zam’tsogolo kwa anthu aŵili “oseŵenzetsa” makhadi a njuga za matsenga, mwacionekele mayankho awo afunika kufanana. Koma kambili amakhala osiyana.

Anthu ayamba kukaikila njila zimene olosela amaseŵenzetsa na zolinga zawo. Ena amakamba kuti zinthu zimene olosela amaseŵenzetsa ni zinthu wamba. Olosela zakutsogolo amaona mmene anthu ofunsilawo acitila zinthu na mmene ayankhila powafunsa mafunso. Mwacitsanzo, munthu amene ni katswili wolosela zam’tsogolo, amafunsa mafunso osiyana-siyana na kuyang’anitsitsa pamene munthuyo akamba na zizindikilo zinazake zimene aonetsa. Iye amatengelapo mwayi pa zimene wofunsilayo wamuululila mosadziwa, ndiyeno woloselayo amadziŵa zeni-zeni zokhudza munthuyo na mmene zinthu zilili mu umoyo wake. Olosela ena akadziŵa kuti anthu ayamba kuwakhulupilila, mwacinyengo amatenga ndalama zambili-mbili kwa makasitoma awo.

ZIMENE BAIBO IMATIUZA

Zimene okhulupilila zakuthambo na olosela zakutsogolo amakamba, zimaonetsa kuti tsogolo lathu linakonzedwelatu. Kodi izi n’zoona? Baibo imatiuza kuti tili na ufulu wosankha zimene tingakhulupilile kapena kucita, ndipo zimene timasankha zimakhudza tsogolo lathu.—Yoswa 24:15.

Anthu amene amalambila Mulungu ali na cifukwa cina cokanila kukhulupilila zakuthambo na kuwombeza. Mulungu amadana na kuombeza kwa mtundu ulionse. M’Baibo timapeza mau aya: “Pakati panu pasapezeke munthu . . . wolosela, wocita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsila kwa wolankhula ndi mizimu, wolosela zam’tsogolo kapena aliyense wofunsila kwa akufa. Pakuti aliyense wocita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.” aDeuteronomo 18:10-12.

a Dzina la “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi”—Salimo 83:18, Buku Lopatulika.