Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Umboni Woonetsa Kuti Maulosi a M’baibo Ni Azoona

Umboni Woonetsa Kuti Maulosi a M’baibo Ni Azoona

CAPAKATI PA MZINDA WA ROMA KU ITALY, PALI CIPILALA CIMENE CIMACITITSA CIDWI ALENDO OCOKELA KOSIYANA-SIYANA OKAONA MALO. CIPILALA CIMENECI CIMALEMEKEZA TITO AMENE ANALI MMODZI WA MAFUMU OCHUKA A ULAMULILO WACIROMA.

Cipilala ca Tito cili na zosema ziŵili zikulu-zikulu zoonetsa cocitika codziŵika bwino cokhudza mbili yakale. Koma cimene ambili sadziŵa ni mgwilizano umene ulipo pakati pa cipilala na Baibo. Cipilala ca Tito cimacitila umboni woonetsa kuti maulosi a m’Baibo ni azoonadi.

MZINDA WOTEMBELEDWA

Kumayambililo kwa zaka za m’nthawi ya atumwi, Ufumu wa Roma unali kulamulila kuyambila ku Britain kufika ku Gaul, (imene tsopano ni dziko la France) mpaka kukafikanso ku Egypt. Ufumu umenewu unali wokondwa kukhala na mtendele woculuka komanso cuma. Koma cigawo cimodzi ca kutali ca Yudeya cinali kukhumudwitsa boma la Roma, cifukwa kunali kubuka mavuto kaŵili-kaŵili.

Buku lochedwa Encyclopedia of Ancient Rome limakamba kuti: “Mu ufumu wa Aroma munali madela ena ocepa amene anali pa cidani cacikulu na Aroma. Limodzi mwa madelawo linali Yudeya. Ayuda anali kudana ndi atsamunda aciroma, amene analibe nazo nchito za miyambo yawo. Koma naonso Aroma anakwimitsila zinthu Ayuda cifukwa ca nthota zawo.” Ayuda ambili anali kuyembekezela kuti Mesiya adzacotsa ulamulilo wa Aroma na kubwezeletsa ufulu kwa Aisiraeli. Koma mu 33 C.E, Yesu Khristu anakamba motsimikiza kuti Yerusalemu adzaonongedwa.

Yesu anakamba kuti: “Masiku adzakufikila pamene adani ako adzamanga mpanda wazisonga kukuzungulila. Adaniwo adzakutsekeleza ndi kukusautsa kucokela kumbali zonse. Iwo adzakuwononga limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwala unzake mwa iwe.”Luka 19:43, 44.

Mwacionekele, mau a Yesu amenewa anadabwitsa kwambili ophunzila ake. Patapita masiku aŵili, ophunzila ake akuyang’ana kacisi mu Yerusalemu, mmodzi wa iwo anafuula kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekela!” Amati miyala ina ya kacisi inali kufika mamita 11 muutali mwake, mamita 5 muufupi, na mamita atatu kukwela m’mwamba! Koma Yesu anawauza kuti: “Kunena za zinthu izi mukuzionazi, masiku adzafika pamene sipadzakhala mwala wosiyidwa pano pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”Maliko 13:1; Luka 21:6.

Yesu anapitiliza kuwauza kuti: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulila Yerusalemu, mudzadziwe kuti ciwonongeko cake cayandikila. Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawila kumapili, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madela akumidzi asadzalowe mumzindawo.” (Luka 21:20, 21) Kodi zimene Yesu anakamba zinacitikadi?

KUONONGEDWA KWA MZINDA

Ayuda anali kuvutikabe pansi pa ulamulilo wa Aroma, ngakhale patapita zaka 33 kucokela pamene Yesu anapeleka cenjezo. Koma mu 66 C.E, pamene bwanamkubwa waciroma ku Yudeya, dzina lake Gessius Florus analanda ndalama zocokela m’thumba la kacisi wopatulika, Ayuda okwiya anafika polema nazo. Posapita nthawi, asilikali aciyuda analoŵa mu Yerusalemu, na kupha kagulu ka asilikali aciroma. Kenako iwo analengeza ufulu wawo kwa Aroma.

Patapita pafupi-fupi miyezi itatu, asilikali aciroma opitilila 30,000 otsogoleledwa na Cestius Gallus, anayenda ku Yerusalemu kuti akakhaulitse Ayuda opandukawo. Mwamsanga Aroma analoŵa mu mzinda na kuyamba kuononga mpanda wakunja wa kacisi. Ndiyeno pazifukwa zosadziŵika bwino, iwo anabwelela. Ayuda oukila anasangalala, ndipo anathamangila asilikali amenewo. Popeza kuti asilikali aciroma komanso Aciyuda anali atacoka mu mzinda, Akhristu amene anamvela cenjezo la Yesu anatuluka mu Yerusalemu na kuthaŵila ku mapili kupitilila Mtsinje wa Yorodano.—Mateyu 24:15, 16.

Caka cotsatila asilikali aciroma anapitanso kukagonjetsa mzinda wa Yudeya motsogoleledwa na Kazembe wa nkhondo dzina lake Vespasian na mwana wake Tito. Koma pamene mfumu Nero anamwalila mu 68 C.E., Vespasian anabwelela ku Roma kukakhala mfumu. Pulogilamu yogonjetsa Yudeya, anaisiila mwana mwake Tito, pamodzi na gulu la asilikali pafupi-fupi 60,000.

Mu 70 C.E. m’mwezi wa June, Tito analamula asilikali ake kudula mitengo m’dela la Yudeya imene anaiseŵenzetsa kumangila mpanda wa mitengo yosongoka wa makilomita 7 kuzungulila Yerusalemu. Kudzafika mu September, Aroma analanda mzinda na kacisi wake, ndipo anaushoka na kuupasula, osasiya mwala pa mwala unzake monga mmene Yesu analoselela. (Luka 19:43, 44) Malipoti akuonetsa kuti anthu “pakati pa 250,000 na 500,000 anafa mu mzinda wa Yerusalemu komanso mu Yudeya monse.”

CIPAMBANO CAUFUMU WA ROMA

Mu 71 C.E., Tito anabwelela ku Italy, ndipo analandilidwa na nzika za Roma mwa cisangalalo cacikulu. Mu mzinda wonse, anthu anacita cikondwelelo cacikulu cacipambano cimene cinali cikalibe kucitikapo mu mzinda waukulu umenewo.

Khamu la anthu linadabwa kuona cuma cambili cimene cinali kudutsa m’miseu ya mu mzinda wa Roma. Iwo anali kuyang’ana mwacidwi maboti akulu-akulu amene analandiwa, zikwangwani zoonetsa zithunzi za nkhondo na zinthu zina zimene anatenga mu kacisi ku Yerusalemu.

Tito anakhala mfumu mu 79 C.E., kuloŵa m’malo atate wake, Vespasian. Koma patapita zaka ziŵili, mosayembekezela Tito anamwalila. Domitian mng’ono wake ndiye anakhala mfumu. Mwamsanga anamanga cipilala cacipambano polemekeza Tito.

CIPILALA CIMENECO MASIKU ANO

Cipilala ca Tito

Masiku ano, caka ciliconse Cipilala ca Tito cimacititsa cidwi anthu masauzande ambili amene amapita kukaona malo ku Rome. Ena amaona cipilala cimeneci monga cinthu copangiwa mwaluso cabe. Koma ena amaona kuti cimalemekeza ulamulilo wa mphamvu wa Roma. Ndipo enanso amaona kuti ni cikumbutso ca kugwa kwa Yerusalemu na kacisi wake.

Koma anthu oŵelenga Baibo mwakhama, amaona Cipilala ca Tito kuti cili na tanthauzo lalikulu kwambili. Cimacitila umboni kuti maulosi a m’Baibo ni odalilika, komanso azoona, ndiponso ni ouzilidwa na Mulungu.—2 Petulo 1:19-21.