Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Posacedwa Mulungu Adzacotsapo Mavuto Onse

Posacedwa Mulungu Adzacotsapo Mavuto Onse

“Inu Yehova, kodi ndidzalilila thandizo koma inu osandimva kufikila liti? Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku ciwawa koma inu osandimva kufikila liti?” (Habakuku 1:2, 3) Aya ni mau a Habakuku, munthu wabwino amene anali wokondwa kukhala pa ubwenzi wabwino na Mulungu. Kodi mafunso ake anaonetsa kuti analibe cikhulupililo? Kutali-tali! Mulungu anatsimikizila Habakuku kuti adzathetsa mavuto panthawi yake yoikika.—Habakuku 2:2, 3.

Ngati imwe kapena munthu wina amene mumam’konda kwambili avutika, cimakhala capafupi kuganiza kuti Mulungu akucedwa kucitapo kanthu, cakuti podzafika pano akanaloŵelelapo kale. Koma, Baibo imatiuza kuti: “Yehova sakucedwa kukwanilitsa lonjezo lake, ngati mmene anthu ena amaonela kuti akucedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”—2 Petulo 3:9.

KODI N’LITI PAMENE MULUNGU ADZACITAPO KANTHU?

Adzacitapo kanthu posacedwa! Yesu anafotokoza kuti, m’badwo wina wake udzaona zocitika zapadela zimene zidzakhala cizindikilo ca masiku otsiliza “a nthawi ino.” (Mateyu 24:3-42) Kukwanilitsika kwa ulosi umene Yesu anakamba m’masiku athu ano, kuonetsa kuti Mulungu ali pafupi kwambili kugwapo pa mavuto a anthu. *

Koma kodi Mulungu adzacotsapo bwanji mavuto onse? Pamene Yesu anali padziko, anaonetsa mphamvu za Mulungu mwa kucepetsa mavuto a anthu. Onani zitsanzo zotsatilazi.

Masoka a Zacilengedwe: Pamene Yesu na atumwi ake anali kuyenda pa Nyanja ya Galileya, cimphepo camphamvu cinafuna kumiza boti yawo. Koma Yesu anaonetsa kuti iye na Atate wake ali na mphamvu zolamulila cilengedwe. (Akolose 1:15, 16) Yesu anangokamba kuti: “Leka! Khala bata!” Cotulukapo cake? “Mphepoyo inaleka. Kenako panacita bata lalikulu.”—Maliko 4:35-39.

Matenda: Yesu anali kudziŵika kuti ali na mphamvu zocilitsa ogontha, olemala, akhunyu, akhate, komanso nthenda ina iliyonse. “Onse amene sanali kumva bwino m’thupi anawacilitsa.”—Mateyu 4:23, 24; 8:16; 11:2-5.

Njala: Yesu anaseŵenzetsa mphamvu zimene anapatsidwa na Atate wake kuculukitsa cakudya cocepa. Malemba amaonetsa kuti, pamene Yesu anali padziko lapansi anadyetsa anthu masauzande kaŵili konse.—Mateyu 14:14-21; 15:32-38.

Imfa: Kuukitsa akufa katatu konse kolembedwa m’Baibo kumene Yesu anacita, kumaonetsa kuti Yehova ali na mphamvu zocotsapo imfa. Mmodzi wa amene iye anaukitsa, anakhala m’manda kwa masiku 4.—Maliko 5:35-42; Luka 7:11-16; Yohane 11:3-44.

^ Kuti mudziŵe zambili zokhudza masiku otsiliza, onani phunzilo 32 m’buku yakuti, Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! yopangiwa na Mboni za Yehova ndipo mungaicite daunilodi mahala pa webusaiti ya www.pr418.com.