Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikhala Okhulupirika Komanso Omvera Ngati Nowa, Danieli ndi Yobu

Tizikhala Okhulupirika Komanso Omvera Ngati Nowa, Danieli ndi Yobu

“Nowa, Danieli ndi Yobu . . . akanapulumutsa miyoyo yawo chifukwa chokhala olungama.”​—EZEK. 14:14.

NYIMBO: 89, 119

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani chitsanzo cha Nowa, Danieli ndi Yobu chingatilimbikitse? (b) Kodi Ezekieli anali kuti pamene ankalemba mawu a mulemba la Ezekieli 14:14, ndipo anawalemba liti?

KODI mukukumana ndi mavuto azachuma, matenda kapena mukuzunzidwa? Nanga kodi nthawi zina zimakuvutani kutumikira Yehova mosangalala? Ngati zili choncho, mungalimbikitsidwe ndi chitsanzo cha Nowa, Danieli ndi Yobu. Nawonso sanali angwiro ndipo ankakumana ndi mavuto ngati amene ife timakumana nawo. Mavuto awo ena anali oopsa moti miyoyo yawo inali pa ngozi. Koma sanasiye kukhala okhulupirika komanso omvera ndipo Mulungu amaona kuti anapereka chitsanzo chabwino.​—Werengani Ezekieli 14:12-14.

2 Ezekieli analemba mawu amene ali mulemba lotsogolerali ali ku Babeloniya mu 612 B.C.E. * (Ezek. 1:1; 8:1) Pa nthawiyi n’kuti mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuwonongedwa, ndipo unawonongedwadi mu 607 B.C.E. Panali anthu ochepa kwambiri amene anali atalembedwa chizindikiro kuti adzapulumuka chifukwa choti anali ndi makhalidwe abwino ngati a Nowa, Danieli ndi Yobu. (Ezek. 9:1-5) Ena mwa anthuwo anali Yeremiya, Baruki, Ebedi-meleki ndiponso Arekabu.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Masiku anonso, anthu amene Yehova amawaona kuti ali ndi makhalidwe abwino ngati a Nowa, Danieli ndi Yobu ndi amene adzalembedwe chizindikiro choti adzapulumuka dziko loipali likamadzawonongedwa. (Chiv. 7:9, 14) Tiyeni tsopano tikambirane chifukwa chake Yehova amaona kuti anthu atatuwa ndi chitsanzo chabwino. Tikamakambirana za munthu aliyense tidzaona (1) mavuto amene anakumana nawo komanso (2) mmene tingamutsanzirire pokhala okhulupirika ndiponso omvera.

NOWA ANALI WOKHULUPIRIKA NDIPONSO WOMVERA KWA ZAKA 900

4, 5. Kodi Nowa anakumana ndi mavuto ati, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti analidi wopirira?

4 Mavuto amene Nowa anakumana nawo. Mu nthawi ya Inoki, yemwe anali agogo a bambo a Nowa, anthu anali atalowerera kwambiri. Iwo anafika ponena ‘zinthu zonyoza kwambiri’ Yehova. (Yuda 14, 15) Zachiwawa zinkawonjezerekawonjezereka moti munthawi ya Nowa dziko lapansi “linadzaza ndi chiwawa.” Angelo oipa anabwera padziko n’kumakhala ngati anthu, anakwatira ndipo anabereka ana ankhanza kwambiri. (Gen. 6:2-4, 11, 12) Koma Nowa anali wosiyana kwambiri ndi anthu ena. Baibulo limanena kuti: “Nowa anayanjidwa ndi Yehova. . . . Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.”​—Gen. 6:8, 9.

5 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu amenewa? Choyamba, sikuti Nowa anangoyenda ndi Mulungu m’dziko loipalo kwa zaka 70 kapena 80 zokha, zomwe anthu amakhala ndi moyo masiku ano. Iye anakhala m’dziko loipalo kwa zaka pafupifupi 600. (Gen. 7:11) Komanso mosiyana ndi ifeyo, Nowa analibe mpingo wa abale ndi alongo amene akanamulimbikitsa. Zikuonekanso kuti ngakhale azibale ake sankamulimbikitsa. *

6. Kodi Nowa anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima?

6 Nowa sankangofuna kukhala munthu wabwino basi. Koma iye anakhalanso “mlaliki wa chilungamo” n’kumasonyeza anthu molimba mtima kuti ankakhulupirira Yehova. (2 Pet. 2:5) Mtumwi Paulo analemba kuti “mwa chikhulupiriro chimenecho, Nowa anatsutsa dziko.” (Aheb. 11:7) Choncho Nowa ayenera kuti ankanyozedwa, kutsutsidwa komanso kuopsezedwa. Koma iye ‘sankaopa anthu.’ (Miy. 29:25) M’malomwake anali wolimba mtima chifukwa cha mphamvu zimene Yehova amapereka kwa atumiki ake okhulupirika.

7. N’chifukwa chiyani kupanga chingalawa kunali kovuta?

7 Nowa atayenda ndi Mulungu kwa zaka zoposa 500, Yehova anamuuza kuti apange chingalawa kuti anthu apulumukiremo limodzi ndi nyama. (Gen. 5:32; 6:14) Ntchitoyi iyenera kuti inkaoneka yovuta kwambiri. Zili choncho chifukwa ntchito yopanga chingalawa inali yaikulu kwambiri. Komanso Nowa ayenera kuti ankadziwa kuti adzanyozedwa ndiponso kutsutsidwa kwambiri chifukwa cha ntchitoyi. Komabe iye anamvera ndipo “anachitadi momwemo.”​—Gen. 6:22.

8. Kodi Nowa anasonyeza bwanji kuti ankadalira Yehova?

8 Nowa anayeneranso kupezera mkazi wake ndi ana ake zofunika pa moyo. Chigumula chisanachitike, anthu ankayenera kulimbikira kwambiri kulima kuti apeze chakudya ndipo ndi mmene zinalilinso ndi Nowa. (Gen. 5:28, 29) Ngakhale zinali choncho, iye ankaika zinthu zokhudza Mulungu pamalo oyamba osati zofuna zake. N’kutheka kuti kupanga chingalawa kunatenga zaka 40 kapena 50. Koma ngakhale pa nthawiyi, Nowa sanasiye kuika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba. Ndipotu iye anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zina 350 Chigumula chitachitika. (Gen. 9:28) Nowa analidi chitsanzo chabwino pa nkhani yokhulupirika komanso kumvera.

9, 10. (a) Kodi tingatani kuti tikhale okhulupirika ndiponso omvera ngati Nowa? (b) Ngati mumamvera Mulungu, kodi simuyenera kukayikira za chiyani?

9 Zimene tingachite kuti tikhale okhulupirika ndiponso omvera ngati Nowa. Tiyenera kutsatira mfundo zachilungamo za Mulungu, kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba komanso kupewa kukhala mbali ya dziko la Satanali. (Mat. 6:33; Yoh. 15:19) N’zoona kuti zimene timachita pa moyo wathu sizisangalatsa anthu a m’dzikoli. Ndipo kutsatira malamulo a Mulungu pa nkhani zokhudza ukwati ndiponso kugonana kwachititsa kuti anthu a m’mayiko ena afalitse nkhani zoipa zokhudza ifeyo. (Werengani Malaki 3:17, 18.) Koma mofanana ndi Nowa, timaopa Yehova osati anthu. Timadziwa kuti ndi iye yekha amene amapereka moyo wosatha.​—Luka 12:4, 5.

10 Koma kodi inuyo mudzapitiriza ‘kuyenda ndi Mulungu’ ngakhale pamene anthu akukunyozani kapena kukutsutsani? Nanga mutakumana ndi mavuto azachuma, kodi mudzapitiriza kudalira Yehova? Ngati ndinu okhulupirika ndiponso omvera ngati Nowa, simuyenera kukayikira kuti Yehova adzakusamalirani.​—Afil. 4:6, 7.

DANIELI ANALI WOKHULUPIRIKA NDIPONSO WOMVERA MUMZINDA WOIPA

11. Kodi Danieli ndi anzake atatu anakumana ndi mavuto akuluakulu ati ku Babulo? (Onani chithunzi choyambirira.)

11 Mavuto amene Danieli anakumana nawo. Danieli anali ku ukapolo mumzinda wa Babulo, womwe anthu ake ankalambira mafano komanso kuchita zamatsenga. Ndipo Ababulo ankanyoza Ayuda komanso Mulungu wawo Yehova. (Sal. 137:1, 3) Zimenezi ziyenera kuti zinkapweteka kwambiri Danieli komanso Ayuda ena okhulupirika. Komanso anthu a ku Babulo ankaona chilichonse chimene Danieli limodzi ndi anzake, Hananiya, Misayeli ndi Azariya ankachita chifukwa ankaphunzitsidwa kuti akhale atumiki a mfumu. Iwo ankauzidwa zimene ayenera kudya ndipo zimenezi zinali zovuta chifukwa Danieli sankafuna ‘kudzidetsa ndi zakudya zabwino za mfumu.’​—Dan. 1:5-8, 14-17.

12. (a) Kodi Danieli anali ndi makhalidwe abwino ati? (b) Kodi Yehova ankaona kuti Danieli anali munthu wotani?

12 Chinthu china chimene chikanasokoneza Danieli chinali maluso ake omwe anachititsa kuti alandire udindo wapadera. (Dan. 1:19, 20) Koma m’malo mokhala wonyada komanso womva zake zokha, Danieli anakhalabe wodzichepetsa ndipo nthawi zonse ankalemekeza Yehova. (Dan. 2:30) Ndipotu Danieli anali adakali wachinyamata pamene Yehova anachititsa kuti atchulidwe limodzi ndi Nowa komanso Yobu monga chitsanzo cha munthu wolungama. Kodi Yehova analakwitsa pokhulupirira Danieli chonchi? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti Danieli anakhalabe wokhulupirika komanso womvera mpaka mapeto a moyo wake. N’kutheka kuti iye anali ndi zaka za m’ma 90 pamene mngelo wa Mulungu anamuuza kuti: “Iwe Danieli, munthu wokondedwa kwambiri.”​—Dan. 10:11.

13. Kodi mwina n’chifukwa chiyani Yehova anathandiza Danieli kuti akhale ndi udindo waukulu?

13 Yehova anathandiza kuti Danieli apatsidwe udindo waukulu mu ufumu wa Babulo ndiponso wa Amedi ndi Aperisiya. (Dan. 1:21; 6:1, 2) Mwina Yehova anachita zimenezi n’cholinga choti Danieli azithandiza anthu ake ngati mmene zinalili ndi Yosefe ku Iguputo komanso Moredekai ndi Esitere ku Perisiya. * (Dan. 2:48) Ezekieli ndiponso Ayuda ena ku ukapolo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kuona Yehova akutsogolera zinthu chonchi.

Yehova amaona kuti anthu amene amakhalabe okhulupirika ndi amtengo wapatali (Onani ndime 14 ndi 15)

14, 15. (a) Kodi tikufanana bwanji ndi Danieli? (b) Kodi makolo amasiku ano angaphunzire chiyani kwa makolo a Danieli?

14 Zimene tingachite kuti tikhale okhulupirika ndiponso omvera ngati Danieli. Masiku ano tikukhala m’dziko limene laipitsidwa kwambiri ndi Babulo Wamkulu, yemwe akuimira zipembedzo zonse zonyenga ndipo amatchedwa “malo okhala ziwanda.” (Chiv. 18:2) Choncho nafenso timakhala osiyana kwambiri ndi anthu ena ndipo nthawi zina timanyozedwa. (Maliko 13:13) Mofanana ndi Danieli, tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu wathu. Tikamadalira Yehova modzichepetsa ndiponso kumumvera, nafenso timakhala amtengo wapatali kwa iye.​—Hag. 2:7.

15 Makolo angaphunzire zambiri pa chitsanzo cha makolo a Danieli. N’chifukwa chiyani tikutero? Ngakhale kuti ku Yuda zinthu zinali zoipa kwambiri pamene Danieli anali wamng’ono, iye anaphunzira kukonda Mulungu. Zimenezi sizinangochitika pa zokha ayi. Koma makolo ake ayenera kuti ankamuphunzitsa bwino. (Miy. 22:6) Ngakhale dzina la Danieli lomwe limatanthauza kuti “Mulungu Ndi Woweruza Wanga” limasonyeza kuti makolo ake ankakonda Mulungu. Choncho ngati ndinu makolo, musataye mtima koma pitirizani kuphunzitsa ana anu moleza mtima. (Aef. 6:4) Muyeneranso kumapemphera nawo komanso kuwapempherera. Mukamayesetsa kuwafika pamtima ndi mfundo za m’Baibulo Yehova adzakudalitsani.​—Sal. 37:5.

YOBU ANALI WOKHULUPIRIKA NDIPONSO WOMVERA ATALEMERA KOMANSO ATASAUKA

16, 17. Kodi Yobu anakhala wokhulupirika kwa Yehova pa nthawi zosiyana ziti?

16 Mavuto amene Yobu anakumana nawo. Zinthu zambiri zinasintha pa moyo wa Yobu. Iye asanakumane ndi mayesero ake, anali “munthu wolemekezeka kwambiri pa anthu onse a Kum’mawa.” (Yobu 1:3) Yobu anali wolemera, wotchuka komanso anthu ambiri ankamulemekeza. (Yobu 29:7-16) Ngakhale zinali choncho, sankadziona kuti ndi wapamwamba kwambiri kapena kuona kuti sakufunikira thandizo la Mulungu. Ndipotu Yehova anatchula Yobu kuti “mtumiki wanga” ndipo anati: “Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.”​—Yobu 1:8.

17 Koma pa nthawi yochepa kwambiri, zinthu pa moyo wa Yobu zinasinthiratu. Zinthu zake zonse zinawonongeka ndipo anakhumudwa kwambiri moti ankangolakalaka atafa. Tikudziwa kuti Satana ndi amene anayambitsa zonsezi pamene ananama kuti Yobu ankalambira Mulungu chifukwa chongofuna kupeza phindu basi. (Werengani Yobu 1:9, 10.) Yehova sanangonyalanyaza zimene Satana ananena. Koma anapereka mwayi kwa Yobu kuti asonyeze zoti ankamutumikira chifukwa chomukonda ndi mtima wonse osati chifukwa chofuna kupeza phindu.

18. (a) N’chiyani chimakuchititsani chidwi pa nkhani ya kukhulupirika kwa Yobu? (b) Kodi tikuphunzira chiyani za Yehova tikaganizira mmene anachitira zinthu ndi Yobu?

18 Satana anabweretsera Yobu mavuto osiyanasiyana moti Yobu ankaganiza kuti mavutowo akuchokera kwa Yehova. (Yobu 1:13-21) Kenako anthu atatu omwe ankangonamizira kuti ndi anzake anabwera kudzamuona ndipo analankhula mawu opweteka kwambiri. Ananena zinthu zosonyeza kuti Mulungu akumulanga chifukwa cha zimene analakwitsa. (Yobu 2:11; 22:1, 5-10) Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika. N’zoona kuti nthawi zina analankhula mosaganiza koma Yehova anamvetsa mmene ankamvera mumtima mwake. (Yobu 6:1-3) Mulungu anazindikira kuti Yobu anakhumudwa kwambiri koma anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti Satana anamuzunza koopsa komanso kumunamizira. Mayeserowo atatha, Yehova anamubwezera zinthu zake kuwirikiza kawiri pa zimene anali nazo poyamba ndipo anakhalanso moyo zaka zina 140. (Yak. 5:11) Pa zaka zimenezinso, Yobu anapitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Pamene Ezekieli ankalemba mawu amulemba lotsogolera lija, panali patapita zaka zambirimbiri chimwalirire Yobu.

19, 20. (a) Kodi tingatsanzire bwanji Yobu pa nkhani yokhulupirika ndi kumvera? (b) Kodi tingatsanzire bwanji chifundo cha Yehova?

19 Zimene tingachite kuti tikhale okhulupirika ndiponso omvera ngati Yobu. Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tiyenera kuika patsogolo zofuna za Yehova ndipo tizimukhulupirira komanso kumumvera ndi mtima wonse. Ndipotu ifeyo tili ndi zifukwa zambiri zochitira zimenezi kuposa Yobu. Mwachitsanzo, timadziwa zambiri zokhudza Satana komanso ziwembu zake. (2 Akor. 2:11) Ndipo Baibulo, makamaka buku la Yobu, limatithandizanso kumvetsa chifukwa chake Yehova amalola kuti tizivutika. Ulosi wa Danieli umatithandizanso kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma limene wolamulira wake ndi Khristu Yesu. (Dan. 7:13, 14) Komanso tikudziwa kuti Ufumu umenewu udzathetsa mavuto athu onse posachedwapa.

20 Nkhani ya Yobu imatiphunzitsanso kuti tiyenera kuchitira chifundo Akhristu anzathu amene akuvutika. Mofanana ndi Yobu, ena angalankhule zinthu mosaganiza. (Mlal. 7:7) Koma m’malo mowaimba mlandu, tiyenera kuwamvetsa komanso kuwachitira chifundo. Tikamachita zimenezi ndiye kuti tikutsanzira Yehova yemwe ndi Atate wathu wachifundo.​—Sal. 103:8.

YEHOVA “ADZAKULIMBITSANI”

21. Kodi zimene zinachitika pa moyo wa Nowa, Danieli ndi Yobu zimatsimikizira bwanji mawu a pa 1 Petulo 5:10?

21 Nowa, Danieli ndi Yobu anakhala ndi moyo pa nthawi yosiyana ndipo anakumana ndi zinthu zosiyana koma onse anapirira mavuto awo. Zimene zinachitika pa moyo wawo zimatsimikizira mawu a mtumwi Petulo akuti: “Koma mukavutika kwa kanthawi, Mulungu, yemwe amapereka kukoma mtima konse kwakukulu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.”​—1 Pet. 5:10.

22. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

22 Mawu amene Petulo analembawa amatitsimikizira kuti Yehova azithandiza atumiki ake kukhala olimba komanso amphamvu. Mfundo imeneyi ikugwiranso ntchito kwa anthu a Mulungu masiku ano. Tonsefe timafuna kuti Yehova atilimbitse ndiponso kutipatsa mphamvu n’cholinga choti tizimulambirabe mokhulupirika. Choncho tiyeni tizitsanzira Nowa, Danieli komanso Yobu pa nkhani yokhulupirika komanso kumvera. Munkhani yotsatira tidzaona kuti kudziwa bwino Yehova n’kumene kunawathandiza kuti akhalebe okhulupirika. Ndipo iwo ‘ankamvetsa chilichonse’ chimene Yehova ankafuna kuti achite. (Miy. 28:5) Nafenso tikhoza kuchita zomwezo.

^ ndime 2 Ezekieli anatengedwa ku ukapolo mu 617 B.C.E. Ndipo analemba Ezekieli chaputala 8 mpaka 19 “m’chaka cha 6” cha ukapolowo, chomwe ndi 612 B.C.E.

^ ndime 5 Bambo a Nowa dzina lawo a Lameki anamwalira zaka pafupifupi 5 Chigumula chisanachitike. Ngati mayi a Nowa kapena azibale ake ena anali ndi moyo pamene Chigumula chinkachitika, ndiye kuti sanapulumuke.

^ ndime 13 N’kutheka kuti Yehova ndi amene anathandizanso kuti anzake a Danieli atatu aja apatsidwenso udindo waukulu.​—Dan. 2:49.