Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumam’dziŵa Yehova Monga Mmene Nowa, Danieli, na Yobu Anam’dziŵila?

Kodi Mumam’dziŵa Yehova Monga Mmene Nowa, Danieli, na Yobu Anam’dziŵila?

“Anthu okonda kucita zoipa sangamvetse cilungamo, koma amene akufunafuna Yehova amamvetsa ciliconse.”—MIY. 28:5.

NYIMBO: 126, 150

1-3. (a) N’ciani cingatithandize kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu m’masiku otsiliza ano? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

PAMENE masiku otsiliza akufika kumapeto, anthu oipa akupitiliza ‘kuphuka ngati msipu.’ (Sal. 92:7) Conco, n’zosadabwitsa kuti masiku ano, anthu ambili satsatila mfundo za makhalidwe abwino. Popeza dziko limene tikukhalamoli n’loipa, kodi tingacite ciani kuti tikhale “tiana pa zoipa” koma “aakulu msinkhu” pa “luntha la kuzindikila?”—1 Akor. 14:20.

2 Yankho la funsoli lili m’lemba la mfundo yaikulu ya nkhani ino. Mbali yothela ya lembali imati: “Amene akufunafuna Yehova amamvetsa ciliconse,” kutanthauza ciliconse cofunikila kuti munthu athe kukondweletsa Mulungu. (Miy. 28:5) Lemba la Miyambo 2:7, 9 limakambanso mfundo yolingana na imeneyi. Limati: “Anthu owongoka mtima, iye [Yehova] amawasungila nzelu zopindulitsa.” Pa cifukwa ici, oongoka mtima amatha ‘kumvetsetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njila yonse ya zinthu zabwino.’

3 Nowa, Danieli, na Yobu anapeza nzelu zaconco. (Ezek. 14:14) N’cimodzi-modzinso na atumiki a Mulungu masiku ano. Nanga bwanji imwe pamwekha? Kodi ‘mumamvetsetsa ciliconse’ cofunikila kuti mukwanitse kukondweletsa Yehova? Cinsinsi cake cagona pa kum’dziŵa molondola Mulungu. Tili na zimenezi m’maganizo, tiyeni tikambilane (1) mmene Nowa, Danieli, na Yobu anadziŵila Mulungu, (2) mmene kudziŵa Mulungu kunawathandizila, ndi (3) zimene ise tingacite kuti tikhale na cikhulupililo monga cawo.

NOWA ANAYENDA NA MULUNGU M’DZIKO LOIPA

4. Kodi Nowa anam’dziŵa bwanji Yehova? Nanga kum’dziŵa molondola kunamuthandiza bwanji?

4 Mmene Nowa anadziŵila Yehova. Kuyambila kale-kale, anthu acikhulupililo akhala akuphunzila za Mulungu m’njila zitatu zikulu-zikulu. Yoyamba, mwa kuona cilengedwe cake. Yaciŵili, kuphunzitsidwa na anthu ena oopa Mulungu, ndipo yacitatu, mwa kudzionela okha ubwino wotsatila mfundo zake zolungama. (Yes. 48:18) Mwa kuyang’ana zacilengedwe, Nowa anaona umboni wosatsutsika wakuti Mulungu alipo. Anathanso kudziŵa makhalidwe ake osaoneka na maso, monga “mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake.” (Aroma 1:20) Mwa ici, Nowa anakhala na cikhulupililo colimba mwa Mulungu.

5. Kodi Nowa anadziŵa bwanji colinga ca Mulungu kwa anthu?

5 Munthu amakhala na cikhulupililo “cifukwa ca zimene wamva.” (Aroma 10:17) Kodi Nowa anamva kwa ndani za Yehova? Mwacionekele, anaphunzila zambili kwa makolo ake na azimbuye ake. Mwacitsanzo, ayenela kuti anaphunzitsidwa na atate wake, a Lameki, amene anali munthu wacikhulupililo. Iwo anakhalako na moyo Adamu asanamwalile. (Onani pikica kuciyambi.) Nowa ayenela kuti anaphunzilanso kwa ambuye ake, a Metusela, ndi kwa a Yaredi, ambuye awo a ambuye ake. A Yaredi anakhalabe na moyo kwa zaka 366 kucokela pamene Nowa anabadwa. * (Luka 3:36, 37) Mwina kucokela kwa anthu amenewa kapena akazi awo, Nowa anaphunzila za ciyambi ca umoyo wa anthu, colinga ca Mulungu codzaza dziko lapansi ndi anthu olungama, ndi za kupanduka kwa mu Edeni. Pa nthawiyo, iye anali kudzionela yekha mavuto obwela cifukwa ca kupanduka kumeneko. (Gen. 1:28; 3:16-19, 24) Mulimonse mmene zinalili, mfundo ni yakuti zimene Nowa anaphunzila zinamugwila mtima na kum’sonkhezela kuyamba kutumikila Mulungu.—Gen. 6:9.

6, 7. Kodi ciyembekezo cinalimbitsa bwanji cikhulupililo ca Nowa?

6 Cikhulupililo cimalimba ngati munthu ali na ciyembekezo. Conco, ganizilani mmene Nowa anamvelela atadziŵa kuti dzina lake lili na tanthauzo lopatsa ciyembekezo. Cioneka kuti dzina lakuti Nowa limatanthauza “Mpumulo” kapena “Citonthozo.” (Gen. 5:29) Mouzilidwa, Lameki anati: “Uyu ndi amene adzatibweletsele mpumulo ku nchito yathu yopweteketsa manja, cifukwa colima nthaka imene Yehova anaitembelela.” Nowa anali na ciyembekezo mwa Mulungu. Mofanana ndi Abele na Inoki, iye anali kukhulupilila kuti “mbewu” yochulidwa mu Edeni idzaphwanya mutu wa njoka.—Gen. 3:15.

7 N’kutheka kuti Nowa sanamvetsetse zambili zokhudza ulosi wa pa Genesis 3:15. Koma mwacionekele anazindikila kuti ulosiwu umapeleka ciyembekezo cakuti anthu adzapulumutsidwa m’tsogolo. Kuwonjezala apo, iye anaona kuti ulosi wa mu Edeni umenewu unali wogwilizana ndi uthenga wa Inoki, amene anakambilatu kuti anthu oipa adzaonongedwa na Mulungu. (Yuda 14, 15) Mosakayikila, ulosi wa Inoki unathandiza Nowa kukhala na ciyembekezo komanso cikhulupililo colimba. Ulosi umenewu udzakwanilitsika kothelatu pa Aramagedo.

8. Kodi kudziŵa coonadi ponena za Mulungu kunam’teteza bwanji Nowa?

8 Kodi kudziŵa Mulungu molondola kunam’thandiza bwanji Nowa? Kukhala na cidziŵitso colongosoka kunathandiza Nowa kukhala na cikhulupililo komanso nzelu yocokela kwa Mulungu. Izi zinam’teteza, maka-maka mwauzimu. Mwacitsanzo, popeza Nowa anali ‘kuyenda ndi Mulungu woona,’ anapewa kugwilizana ndi anthu osaopa Mulungu. Iye sanakopeke na ziwanda zimene zinavala matupi a anthu. Ziwanda zimenezo ziyenela kuti zinali kucita zinthu zodabwitsa pofuna kukopa anthu opanda cikhulupililo ndi otengeka-tengeka. N’kutheka kuti ena anafika pomazilambila. (Gen. 6:1-4, 9) Cinanso, Nowa anali kudziŵa kuti Mulungu anauza anthu kuti abalane na kudzaza dziko lapansi. (Gen. 1:27, 28) Conco, iye ayenela kuti anadziŵa kuti kugonana pakati pa anthu na ziwanda n’kulakwa komanso n’kosagwilizana ndi cilengedwe. Mwacidziŵikile, iye anatsimikiza mfundoyi ataona kuti akazi amene ziwanda zinadzitengela ayamba kubeleka viphona. M’kupita kwa nthawi, Mulungu anauza Nowa kuti adzabweletsa cigumula pa dziko lapansi. Nowa anakhulupilila zimenezi, ndipo anamanga cingalawa. Mwakutelo, anapulumutsa banja lake.—Aheb. 11:7.

9, 10. Tingatengele bwanji cikhulupililo ca Nowa?

9 Tingatengele bwanji cikhulupililo ca Nowa? Cofunika ni kuŵelenga Mau a Mulungu mwakhama, kusinkha-sinkha zimene taŵelenga, na kulola zimene taphunzilazo kusintha umoyo wathu na kutitsogolela. (1 Pet. 1:13-15) Tikatelo, tidzakhala na cikhulupililo na nzelu yocokela kwa Mulungu. Izi zidzatiteteza kuti tisagonje ku misampha ya Satana ndi kuti tisatengele mzimu wa dziko. (2 Akor. 2:11) Mzimu wa dziko umasonkhezela anthu kukonda ciwawa na ciwelewele. Umacititsanso kuti azingofuna kukhutilitsa zilakolako zawo za thupi. (1 Yoh. 2:15, 16) Komanso, umacititsa anthu ofooka mwauzimu kunyalanyaza zizindikilo zoonetsa kuti tsiku lalikulu la Mulungu lili pafupi. Kumbukilani kuti pamene Yesu anayelekezela masiku athu ano na masiku a Nowa, sanagogomeze za khalidwe la ciwawa kapena la ciwelewele, koma za kuopsa konyalanyaza zinthu zauzimu.—Ŵelengani Mateyu 24:36-39.

10 Dzifunseni kuti: ‘Kodi zocita zanga zimaonetsa kuti nimam’dziŵadi Yehova? Kodi cikhulupililo canga cimanilimbikitsa kutsatila mfundo zolungama za Mulungu na kuphunzitsakonso ena mfundozo?’ Mayankho anu pa mafunsowa adzaonetsa ngati inu, mofanana ndi Nowa, ‘mumayenda ndi Mulungu woona’ kapena ai.

DANIELI ANAONETSA NZELU YAUMULUNGU MUMZINDA WOIPA WA BABULO

11. (a) Kodi kukonda zinthu zauzimu kwa Danieli pamene anali wacicepele kuonetsa kuti analeledwa bwanji? (b) Ni makhalidwe ati a Danieli amene mufuna kutengela?

11 Mmene Danieli anadziŵila Yehova. Mwacidziŵikile, Danieli anaphunzitsidwa bwino na makolo ake. Anamuphunzitsa kukonda Yehova na Mau ake. Danieli anapitiliza kukonda Mulungu na Malemba kwa moyo wake wonse. Ngakhale pamene anakalamba, iye anapitiliza kuŵelenga Malemba mwakhama. (Dan. 9:1, 2) Danieli anali kum’dziŵa bwino Mulungu, kuphatikizapo mmene anali kucitila zinthu ndi Aisiraeli. Umboni wa zimenezi ni pemphelo lake lolapa locokela pansi pa mtima, lolembedwa pa Danieli 9:3-19. Bwanji osapatula kanthawi koŵelenga na kusinkha-sinkha mau a m’pemphelo limenelo, na kuganizila zimene likutiuza ponena za Danieli?

12-14. (a) Kodi Danieli anaonetsa bwanji nzelu yaumulungu? (b) Nanga anadalitsidwa bwanji cifukwa ca kulimba mtima na kukhulupilika kwake kwa Mulungu?

12 Kodi kudziŵa Mulungu molondola kunam’thandiza bwanji Danieli? Kwa Ayuda okhulupilika, umoyo unali wovuta kwambili ku Babulo. Mwacitsanzo, Yehova anauza Ayuda kuti: “Mzinda umene ndakucititsani kukhalamo monga akapolo, muziufunila mtendele.” (Yer. 29:7) Koma pa nthawi imodzi-modziyo anawalamula kuti akhale odzipeleka kwa iye yekha cabe. (Eks. 34:14) N’ciani cinam’thandiza Danieli kutsatila malamulo onse aŵiliwa mokhulupilika? Nzelu yaumulungu ni imene inam’thandiza kudziŵa kuti ayenela kugonjela olamulila a dziko kupatulapo ngati apeleka lamulo losemphana na malamulo a Mulungu. Zaka zambili pambuyo pake, Yesu anaphunzitsanso mfundo yomweyi.—Luka 20:25.

13 Ganizilani zimene Danieli anacita pamene kunakhazikitsidwa lamulo la boma lakuti kwa masiku 30, anthu asapemphele kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense, koma kwa mfumu cabe. (Ŵelengani Danieli 6:7-10.) Akanakhala wina, Danieli sembe anakamba kuti, ‘Masiku 30 cabe osapemphela kwa Mulungu, ni ocepa!’ Koma iye sanalole lamulo la mfumu kumulepheletsa kukwanilitsa udindo wake wa M’malemba wopemphela. N’zoona kuti akanatha kupemphela cam’seli kuti ena asamuone. Koma anadziŵa kuti anthu anali kucidziŵa bwino cizoloŵezi cake copemphela. Conco, Danieli sanasinthe cizoloŵezi cake olo kuti izi zinaika moyo wake paciopsezo. Iye sanafune kucita zinthu zoonetsa ngati kuti wayamba kugonja pa kulambila kwake.

14 Cifukwa cakuti Danieli analimba mtima na kutsatila cikumbumtima cake, Yehova anam’dalitsa mwa kumupulumutsa mozizwitsa kuti asadyewe na nkhalamu. Komanso, izi zinacititsa kuti Yehova adziŵike m’madela onse a Ufumu wa Mediya ndi Peresiya, ngakhale ku madela akutali kwambili.—Dan. 6:25-27.

15. Tingacite ciani kuti tikhale na cikhulupililo monga ca Danieli?

15 Tingatengele bwanji cikhulupililo ca Danieli? Cimene cingatithandize kukhala na cikhulupililo colimba si kuŵelenga Baibo cabe. Tifunikanso “kuzindikila tanthauzo” la zimene taŵelenga. (Mat. 13:23) Timafuna kuona zinthu mmene Yehova amazionela na kumvetsetsa mfundo za m’Baibo. Conco, tifunika kumasinkha-sinkha zimene taŵelenga. Cina cofunika kwambili ni kupemphela nthawi zonse mocokela pansi pa mtima, maka-maka tikakumana na mayeselo kapena mavuto ena. Ngati tipempha nzelu na mphamvu kwa Yehova tili na cikhulupililo, iye adzatipatsa zimenezi mooloŵa manja.—Yak. 1:5.

YOBU ANASEŴENZETSA MFUNDO ZA MULUNGU M’NTHAWI YA MTENDELE NDI YOVUTA

16, 17. Kodi Yobu anadziŵa bwanji coonadi ponena za Mulungu?

16 Mmene Yobu anadziŵila Yehova. Yobu sanali Mwiisiraeli. Koma anali wacibululu wapatali wa Abulahamu, Isaki na Yakobo, anthu amene anali kudziŵa coonadi ponena za Yehova na colinga cake kwa anthu. Yobu anaphunzila coonadi ca mtengo wapatali cimeneci, koma Baibo siikamba mmene anaciphunzilila. (Yobu 23:12) Yobu iye mwini anakamba kuti anamvapo za Mulungu. (Yobu 42:5) Komanso, Yehova ananena kuti zimene Yobu anakamba ponena za Mulunguyo zinali zoona.—Yobu 42:7, 8.

Cikhulupililo cathu cimalimba tikadziŵa makhalidwe a Mulungu osaoneka mwa kuona cilengedwe cake (Onani palagilafu 17)

17 Kuwonjezela apo, Yobu anadziŵa makhalidwe a Mulungu osaoneka mwa kuyang’ana cilengedwe cake. (Yobu 12:7-9, 13) Pa nthawi ina, onse aŵili, Elihu na Yehova, anaseŵenzetsa zacilengedwe pokumbutsa Yobu kuti Mulungu ni wamkulu kwambili poyelekezela na ise anthu. (Yobu 37:14; 38:1-4) Mau a Yehova anam’khudza mtima Yobu cakuti anakamba modzicepetsa kwa Mulungu kuti: “Ndadziŵa kuti inu mumatha kucita zinthu zonse, ndipo palibe zimene simungakwanitse. . . . ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.”—Yobu 42:2, 6.

18, 19. Kodi Yobu anaonetsa bwanji kuti anali kum’dziŵa bwino Yehova?

18 Kodi kudziŵa Mulungu molondola kunam’thandiza bwanji Yobu? Yobu anali kudziŵa bwino mfundo za Mulungu. Analinso kum’dziŵa bwino Yehova, ndipo izi zinam’limbikitsa kucita zinthu zoyenela. Mwacitsanzo, Yobu anali kudziŵa kuti sangakambe kuti amakonda Mulungu ngati sakomela mtima anthu anzake. (Yobu 6:14) Komanso, iye sanali kudzikweza pamaso pa ena, koma anali kudela nkhawa anthu onse, kaya olemela kapena osauka. Yobu anati: “Kodi amene anandipanga m’mimba si amene anapanganso iyeyo?” (Yobu 31:13-22) Inde, ngakhale pamene anali wochuka ndi wolemela, iye anali wodzicepetsa ndipo anali kulemekeza ena. Ndithudi, Yobu anali munthu wosiyana ngako ndi anthu ambili olemekezeka na olemela a m’dzikoli!

19 Yobu anapewelatu kulambila mafano kwa mtundu uliwonse, ngakhale kwa mumtima cabe. Anadziŵa kuti kulambila konama, kuphatikizapo kukonda cuma, ‘n’kukana Mulungu woona wakumwamba.’ (Ŵelengani Yobu 31:24-28) Yobu analinso kuona kuti banja ni mgwilizano wopatulika pakati pa mwamuna na mkazi. Ndiye cifukwa cake anacita pangano na maso ake kuti asayang’ane namwali mom’khumbila. (Yobu 31:1) Koma kumbukilani kuti pa nthawiyo, Mulungu anali kulolela anthu kukwatila cipali. Conco, Yobu akanafuna, sembe anakwatila mkazi wina. * Komabe, mwacidziŵikile iye anatengela dongosolo la cikwati limene Mulungu anakhazikitsa mu Edeni, n’kulipanga monga lamulo loyenela kulitsatila. (Gen. 2:18, 24) Zaka 1,600 pambuyo pake, Yesu Khristu anaphunzitsa ophunzila ake kuti ayenela kutsatila mfundo zolungama zimenezi, zokhudza cikwati na kugonana.—Mat. 5:28; 19:4, 5.

20. Kodi kudziŵa coonadi ponena za Yehova na mfundo zake kumatithandiza bwanji kusankha anzathu abwino na zosangalatsa zoyenela?

20 Tingatengele bwanji cikhulupililo ca Yobu? Monga takambila kale, cinsinsi cake ni kuphunzila coonadi ponena za Yehova na kulola zimene taphunzilazo kutitsogolela pa zocita zathu zonse. Mwacitsanzo, wamasalimo Davide anakamba kuti Yehova “amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa.” Iye anakambanso kuti sitiyenela kuyanjana ndi “anthu obisa umunthu wawo.” (Ŵelengani Salimo 11:5; 26:4.) Kodi malemba amenewa atiphunzitsa ciani ponena za mmene Mulungu amaonela zinthu? Nanga kudziŵa zimenezi kuyenela kukhudza bwanji zinthu zimene timaika patsogolo, mmene timaseŵenzetsela Intaneti, ndi mmene timasankhila anzathu na zosangalatsa? Mayankho anu pa mafunsowa angakuthandizeni kuona ngati mumam’dziŵa bwino Yehova kapena ayi. Kuti tikhalebe osalakwa m’dziko loipali, tifunika kuphunzitsa ‘mphamvu zathu za kuzindikila’ kuti tizikwanitsa kusiyanitsa zoyenela na zosayenela komanso zanzelu na zopanda nzelu.—Aheb. 5:14; Aef. 5:15.

21. Tingacite ciani kuti ‘timvetsetse ciliconse’ cofunikila kuti tikondweletse Atate wathu wakumwamba?

21 Popeza kuti Nowa, Danieli, na Yobu anafuna-funa Yehova na mtima wawo wonse, iye analola kuti iwo am’peze. Anawathandiza ‘kumvetsa ciliconse’ cimene cinali cofunikila kuti am’kondweletse. N’cifukwa cake anakhala zitsanzo zabwino za anthu a cilungamo, ndipo zinthu zinawayendela bwino mu umoyo wawo. (Sal. 1:1-3) Cotelo, dzifunseni kuti, ‘Kodi nimam’dziŵa Yehova monga mmene Nowa, Danieli, na Yobu anali kum’dziŵila?’ Masiku ano, kuwala kwa coonadi kwaonjezeka, ndipo ise tingathe kum’dziŵa bwino kwambili Mulungu kuposa mmene amuna amenewa anam’dziŵila. (Miy. 4:18) Conco, muziphunzila Mau a Mulungu mozama. Muziwasinkha-sinkha. Muzipempha mzimu woyela. Mukatelo, mudzamuyandikila kwambili Atate wanu wakumwamba. Ndipo mudzacita zinthu mozindikila ndi mwanzelu m’dziko loipali.—Miy. 2:4-7.

^ par. 5 Nayenso Inoki, ambuye awo a atate ake a Nowa, “anayenda ndi Mulungu woona.” Koma kukali zaka 69 kuti Nowa abadwe, ‘Mulungu anam’tenga” Inoki.—Gen. 5:23, 24.

^ par. 19 N’cimodzi-modzi na Nowa. Nayenso anali na mkazi mmodzi, ngakhale kuti kukwatila cipali kunayamba kale-kale anthu atangopanduka kumene mu Edeni.—Gen. 4:19.