Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauzanji?

Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauzanji?

“Mulungu . . . acititse nonsenu kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.”—AROMA 15:5.

NYIMBO: 17, 13

1, 2. (a) Kodi anthu ambili amakuona bwanji kukhala munthu wauzimu? (b) Kodi tidzakambilana mafunso ofunika ati okhudza kukhala munthu wauzimu?

“KUKHALA munthu wauzimu kwanithandiza kukhala wosangalala. Kwanithandizanso kuti nikwanitse kupilila mavuto amene nimakumana nawo tsiku na tsiku,” anatelo mlongo wina wa ku Canada. M’bale wina wa ku Brazil anakamba kuti, “Pa zaka 23 zimene takhala m’cikwati, takhala na umoyo wosangalala kwambili cifukwa ine na mkazi wanga timakonda zinthu zauzimu.” Komanso, m’bale wina wa ku Philippines anati: “Kukhala munthu wauzimu kwanithandiza kukhala na mtendele wa m’maganizo. Kwanicititsanso kuti nizikwanitsa kukhala bwino na abale a zikhalidwe zosiyana-siyana.”

2 Zimene abale amenewa anakamba zionetsa kuti kukhala munthu wauzimu kumabweletsa madalitso. Conco, tingadzifunse kuti, ‘Ningacite ciani kuti nikhale munthu wauzimu n’colinga cakuti nipeze madalitso monga amene abalewa anafotokoza?’ Tisanayankhe funso limeneli, tifunika kumvetsetsa zimene Baibo imakamba ponena za anthu auzimu, kapena kuti okonda zauzimu. M’nkhani ino, tidzakambilana mafunso atatu ofunika kwambili. (1) Kodi kukhala munthu wauzimu kumatanthauzanji? (2) N’zitsanzo ziti zimene zingatithandize kukula mwauzimu? (3) Kodi kuyetsetsa kukhala na “maganizo a Khristu” kungatithandize bwanji kukhala anthu auzimu?

KODI MUNTHU WAUZIMU AMAKHALA WOTANI?

3. Malinga n’zimene Baibo imakamba, kodi munthu wakuthupi na munthu wauzimu amasiyana bwanji?

3 Pofuna kutithandiza kumvetsetsa mmene munthu wauzimu amakhalila, mtumwi Paulo anafotokoza kusiyana pakati pa “munthu wauzimu” na “munthu wakuthupi.” (Ŵelengani 1 Akorinto 2:14-16 mau amunsi.) Kodi amasiyana bwanji? Iye anafotokoza kuti “munthu wakuthupi salandila zinthu za mzimu wa Mulungu, cifukwa amaziona ngati zopusa ndipo sangathe kuzidziŵa.” Ku mbali ina, “munthu wauzimu amafufuza zinthu zonse,” ndipo amakhala na “maganizo a Khristu.” Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kukhala anthu auzimu. Kodi munthu wakuthupi na munthu wauzimu amasiyana m’njila zina ziti?

4, 5. Kodi munthu wakuthupi tingam’dziŵe bwanji?

4 Coyamba, onani maganizo amene munthu wakuthupi amakhala nawo. Anthu ambili m’dzikoli amaika maganizo awo onse pa kukhutilitsa zilakolako za thupi. Paulo anakamba kuti mzimu umenewu, kapena kuti ‘kaganizidwe kameneka tsopano kakugwila nchito mwa ana a kusamvela.’ (Aef. 2:2) Mzimu umenewu umasonkhezela anthu kumangotsatila zimene anthu ambili amaona kuti ndiye zabwino. Conco, ambili amakonda kucita zinthu zimene amaona kuti n’zoyenela kwa iwo, ndipo safuna kutsatila miyezo ya Mulungu. Nthawi zambili, munthu wakuthupi amafunitsitsa kukhala wochuka, amakonda kufuna-funa zinthu zakuthupi, ndiponso amaumilila kuteteza ufulu wake.

5 N’ciani cina cimene cimaonetsa kuti munthu ni wakuthupi? Aliyense amene amacita “ntchito za thupi” ni munthu wakuthupi. (Agal. 5:19-21) M’kalata yoyamba imene Paulo analembela mpingo wa ku Korinto, iye anafotokoza makhalidwe ena amene anthu akuthupi amakhala nawo. Makhalidwewo amaphatikizapo kulimbikitsa magaŵano, kukhalila mbali, kutengelana ku makhoti, kusagonjela umutu, ndi kukondetsa kudya na kumwa. Munthu wakuthupi akakumana na ciyeso, amagonja mosavuta. (Miy. 7:21, 22) Yuda anafotokoza za anthu amene adzafooka mpaka kufika pokhala opanda “mzimu wa Mulungu.”—Yuda 18, 19.

6. Kodi munthu wauzimu tingam’dziŵe bwanji?

6 Nanga kodi kukhala “munthu wauzimu” kumatanthauza ciani? Mosiyana ndi munthu wakuthupi, munthu wauzimu amakonda kucita zimene Mulungu amafuna. Anthu okonda zauzimu amayesetsa ‘kutsanzila Mulungu.’ (Aef. 5:1) Izi zitanthauza kuti iwo amayesetsa kuphunzila mmene Yehova amaonela zinthu, ndipo amayamba kuziona mmene iye amazionela. Mulungu ni weni-weni kwa iwo. Mosiyana ndi anthu akuthupi, anthu auzimu amayesetsa kutsatila miyezo ya Yehova pa zocita zawo zonse. (Sal. 119:33; 143:10) Munthu wokonda zinthu zauzimu sacita nchito za thupi, koma amayesetsa kukhala na “makhalidwe amene mzimu woyela” umabala. (Agal. 5:22, 23) Kuti timveketse bwino tanthauzo la mau akuti “munthu wokonda zinthu zauzimu,” ganizilani citsanzo ici: Ngati munthu amadziŵa kwambili zamalonda, tingakambe kuti ni wokonda bizinesi. Nayenso munthu amene amaona zinthu zauzimu kukhala zofunika, amadziŵika monga munthu wokonda zinthu zauzimu.

7. Kodi Baibo imakamba ciani ponena za anthu okonda zinthu zauzimu?

7 Baibo imaonetsa kuti anthu okonda zinthu zauzimu ali na mwayi. Pa Mateyu 5:3 pamati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu, cifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.” Nalonso lemba la Aroma 8:6 limafotokoza ubwino wokhala munthu wauzimu. Limati: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweletsa imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa moyo ndi mtendele.” Ngati tiika maganizo athu pa zinthu zauzimu, timakhala pa mtendele na Mulungu. Timakhalanso na mtendele wa mumtima komanso ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha m’tsogolo.

8. N’cifukwa ciani pamafunika khama kuti tikhale auzimu na kuteteza uzimu wathu?

8 Komabe, tikukhala m’dziko loipa. Anthu ambili ni okonda zakuthupi. Conco, tifunika kucita khama kuti tikhale anthu auzimu na kuteteza uzimu wathuwo. Ngati munthu wataikilidwa uzimu wake, amapeleka mpata wakuti “mpweya” woipa kapena kuti mzimu wa dzikoli uloŵe mwa iye. N’ciani cimene tingacite kuti zaconco zisaticitikile? Nanga tingacite ciani kuti tikule mwauzimu?

ZITSANZO ZIMENE TIYENELA KUTENGELA

9. (a) N’ciani cingatithandize kuti tikule mwauzimu? (b) Kodi tidzakambilana zitsanzo za anthu ati auzimu?

9 Mwana amayamba kukhwima m’maganizo mwa kuona zimene makolo ake amacita na kutengela citsanzo cawo cabwino. Mofananamo, tingakule mwauzimu pamene tiona zimene anthu acikulile kuuzimu amacita na kutengela citsanzo cawo. Koma anthu akuthupi ni zitsanzo zoticenjeza. (1 Akor. 3: 1-4) M’Baibo muli zitsanzo za anthu auzimu komanso za anthu akuthupi. Koma popeza kuti colinga cathu n’kukhala anthu auzimu, tiyeni lomba tikambilaneko za anthu angapo amene ni zitsanzo zabwino zoyenela kutengela. Tidzakambilana za Yakobo, Mariya, na Yesu.

Kodi tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Yakobo? (Onani palagilafu 10)

10. Kodi Yakobo anaonetsa bwanji kuti anali munthu wauzimu?

10 Coyamba, ganizilani citsanzo ca Yakobo. Zinthu zinali zovuta mu umoyo wake, mofanana ndi mmene zilili kwa ambili a ise masiku ano. Iye anapilila khalidwe loipa la mkulu wake, Esau, amene anali kufuna kumupha. Kuwonjezela apo, Yakobo anavutika na zocita za apongozi ake acinyengo, amene mobweleza-bweleza anayesa kumudyela masuku pa mutu. Olo kuti Yakobo anali kukhala na anthu amaganizo “akuthupi,” iye anali munthu wauzimu. Yakobo anali kukhulupilila zimene Mulungu analonjeza Abulahamu, ndipo anayesetsa kusamalila banja lake limene Yehova anasankha kuti adzaligwilitsila nchito pokwanilitsa colinga cake. (Gen. 28:10-15) Mwa zokamba na zocita zake, Yakobo anaonetsa kuti anali kuganizila kwambili za miyezo ya Mulungu na cifunilo cake. Mwacitsanzo, ataopsezedwa na Esau, Yakobo anapempha Mulungu kuti: “Ndapota nanu [conde], ndipulumutseni . . . Inuyotu munanena kuti, ‘Mosakayikila m’pang’ono pomwe ndidzakusamalila, ndipo ndidzaculukitsa mbewu yako ngati mcenga wa kunyanja.’” (Gen. 32:6-12) Mwacidziŵikile, iye anali kukhulupilila zimene Yehova anamulonjeza na zimene analonjeza makolo ake, ndipo anali kufuna kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu.

Kodi tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Mariya? (Onani palagilafu 11)

11. N’ciani cionetsa kuti Mariya anali munthu wauzimu?

11 Lomba ganizilani citsanzo ca Mariya. N’cifukwa ciani Yehova anasankha Mariya kuti akhale mayi wa Yesu? Mwacionekele, n’cifukwa cakuti anali munthu wauzimu. Tidziŵa bwanji zimenezi? Cimene cionetsa kuti anali munthu wauzimu ni mau abwino acitamando amene iye anakamba pamene anakacezela abululu ake, Zakariya na Elizabeti. (Ŵelengani Luka 1:46-55.) Zimene anakamba zionetsa kuti anali munthu wokonda kwambili Mau a Mulungu, ndipo anali kuwadziŵa bwino Malemba Aciheberi. (Gen. 30:13; 1 Sam. 2:1-10; Mal. 3:12) Cinanso, ngakhale kuti iye na Yosefe anali atakwatilana kumene, sanakhaleko malo amodzi mpaka Yesu atabadwa. Kodi izi zionetsa ciani? Zionetsa kuti onse aŵili anali kuona kuti kucita cifunilo ca Yehova ndiye kunali kofunika kwambili kuposa kukhutilitsa zilakolako zawo. (Mat. 1: 25) Pamene zaka zinali kupita, Mariya anali kuganizila mosamala zimene zinali kucitika mu umoyo wa Yesu, ndiponso anali kumvetsela mosamala mau ake anzelu. Komanso, Mariya ‘anasunga mosamala kwambili mawu onsewo mumtima mwake.’ (Luka 2:51) N’zoonekelatu kuti iye anali kuganizila kwambili za mmene Mulungu adzakwanilitsila colinga cake cokhudza Mesiya. Citsanzo ca Mariya ciyenela kutilimbikitsa kuganizila zimene tingacite, kuti tionetse kuti timaika cifunilo ca Mulungu patsogolo mu umoyo wathu.

12. (a) Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anatengela Atate ake? (b) Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu? (Onani pikica kuciyambi.)

12 Pa anthu onse amene anakhalapo pa dziko, Yesu ndiye citsanzo cabwino ngako ca munthu wauzimu. Mu umoyo na utumiki wake wonse, iye anaonetsa kuti anatengela Yehova, Atate ake. Anali kuganiza na kucita zinthu motengela Yehova. Komanso anali kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu na miyezo yake. (Yoh. 8:29; 14:9; 15:10) Mwacitsanzo, ganizilani mmene mneneli Yesaya anafotokozela cifundo ca Yehova. Ndiyeno, yelekezelani zimenezo na zimene wolemba Uthenga Wabwino, Maliko, analemba zoonetsa mmene Yesu anamvelela ataona khamu la anthu. (Ŵelengani Yesaya 63:9; Maliko 6:34.) Kodi inu mumayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu mwa kukhala wokonzeka kucitila cifundo anthu amene afunika thandizo? Cinanso, Yesu anadzipeleka kwambili pa nchito yolalikila na kuphunzitsa anthu uthenga wabwino. (Luka 4:43) Zonse zimenezi ni zizindikilo za munthu wauzimu.

13, 14. (a) Tingaphunzile ciani pa zitsanzo zamakono za anthu okonda zinthu zauzimu? (b) Fotokozani citsanzo.

13 Kuwonjezela pa zitsanzo za m’Malemba, pali zitsanzo zina zambili zamakono za atumiki a Mulungu okonda zinthu zauzimu, amene amayesetsa kutengela makhalidwe a Khristu. Iwo ni acangu kwambili mu ulaliki, oceleza, acifundo, ndipo ali na makhalidwe enanso abwino. Olo kuti ali na zofooka ndipo amalakwitsa zinthu zina monga ife tonse, amayesetsa kukulitsa makhalidwe abwino. Mlongo wina wa ku Brazil, dzina lake Rachel, anati: “N’nali kukonda kwambili mafashoni a kudziko, ndipo sin’nali kuvala mwaulemu. Koma kuphunzila coonadi kunanilimbikitsa kusintha na kukhala munthu wauzimu. Kusintha sikunali kopepuka, koma n’tasintha n’napeza cimwemwe ndipo lomba nimaona kuti moyo wanga uli na colinga.”

14 Nayenso Reylene wa ku Philippines anali na copinga cinacake. Anaika mtima wake wonse pa kucita maphunzilo apamwamba kuti akapeze nchito yabwino ndi kukhala na umoyo wapamwamba. Iye anati: “N’nayamba kunyalanyaza zolinga zanga zauzimu. Koma pambuyo pake n’nazindikila kuti cinacake cofunika kwambili kuposa nchito cinali kusoŵeka mu umoyo wanga. Mwa ici, n’naganiza zoyambanso kutumikila Yehova na mtima wanga wonse.” Kucokela nthawi imeneyo, Reylene wakhala citsanzo cabwino pa nkhani yokhulupilila lonjezo la Yehova la pa Mateyu 6:33, 34. Iye anakamba kuti: “Sinikayikila olo pang’ono kuti Yehova adzanisamalila.” Mwina mu mpingo mwanu mulinso abale na alongo a zitsanzo zabwino ngati amenewa. Tiyenela kuyesetsa kutengela zitsanzo za Akhristu okhulupilika amenewa, pamene nawonso akutsatila Khristu.—1 Akor. 11:1; 2 Ates. 3:7.

KHALANI NA “MAGANIZO A KHRISTU”

15, 16. (a) Kuti tikhale monga Khristu, kodi tifunika kucita ciani? (b) Tingacite ciani kuti tidziŵe bwino “maganizo a Khristu”?

15 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Khristu aliyense payekha? Pa 1 Akorinto 2:16, Baibo imaonetsa kuti tiyenela kukhala na “maganizo a Khristu.” Nalonso lemba la Aroma 15:5 limanena kuti tifunika kukhala na “maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.” Conco, kuti tikhale monga Khristu, tifunika kudziŵa bwino maganizo na makhalidwe ake onse. Kenako, tiyenela kutsatila mapazi ake. Nthawi zonse, Yesu anali kuganizila zinthu zimene zikanalimbitsa ubwenzi wake na Mulungu. Motelo, kutsatila citsanzo Yesu kumatithandiza kumuyandikila kwambili Yehova. Izi zionetsa kuti kuphunzila mmene Yesu anali kuganizila n’kofunika kwambili.

16 Kodi tingacite bwanji zimenezi? Ophunzila a Yesu anaona zozizwitsa zimene iye anacita, anamvetsela maulaliki ake, komanso anaona mmene anali kucitila zinthu ndi anthu osiyana-siyana. Iwo anaonanso mmene Yesu anali kuseŵenzetsela mfundo za Mulungu. Ophunzilawo anati: “Ife ndife mboni za zinthu zonse zimene anacita.” (Mac. 10:39) Koma ise sitingaone zocita za Yesu mwacindunji. Ngakhale n’conco, Yehova mwacikondi anatipatsa mabuku a Uthenga Wabwino amene amatithandiza kudziŵa bwino makhalidwe a Yesu. Mwa kuŵelenga na kusinkha-sinkha mabuku a m’Baibo a Mateyu, Maliko, Luka, na Yohane, tingathe kudziŵa bwino kwambili maganizo a Khristu. Tikatelo, tidzatha ‘kutsatila mapazi ake mosamala kwambili’ na ‘kudzikonzekeletsa ndi maganizo’ amenenso Khristu anali nawo.—1 Pet. 2:21; 4:1.

17. Kodi kuganiza monga Khristu kumatithandiza bwanji?

17 Kodi kuphunzila kuti tiziganiza monga Khristu kungatithandize bwanji? Monga mmene kudya cakudya copatsa thanzi kumalimbitsila thupi, kuphunzila kaganizidwe ka Khristu kumalimbitsa uzimu wathu. Pang’ono m’pang’ono, timayamba kudziŵa zimene Khristu angacite pa cocitika ciliconse. Izi zimatithandiza kupanga zosankha zokondweletsa Mulungu, zimenenso zingatisiye na cikumbumtima coyela. Kuganizila mapindu amenewa kuyenela kutilimbikitsa kuyesetsa ‘kuvala Ambuye Yesu Khristu.’—Aroma 13:14.

18. Kodi inu pacanu mwaphunzila ciani m’nkhani ino ponena za kukhala munthu wauzimu?

18 M’nkhani ino, takambilana zimene kukhala munthu wauzimu kumatanthauza. Takambilananso kuti tiyenela kutengela zitsanzo zabwino za anthu auzimu. Comalizila, taona mmene kukhala na “maganizo a Khristu” kungatithandizile kukhala munthu wauzimu. Komabe, pa nkhani imeneyi ya kukhala munthu wauzimu, palinso zina zimene tiyenela kukambilana. Mwacitsanzo, kodi tingadziŵe bwanji kuti ndise okhwima mwauzimu? N’ciani cina cimene tingacite kuti tikhale munthu wauzimu? Nanga kodi kukhala munthu wauzimu kungakhudze bwanji umoyo wathu wa tsiku na tsiku? Nkhani yotsatila idzayankha mafunso amenewa.