Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauza Chiyani?

Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauza Chiyani?

‘Mulungu achititse nonsenu kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.’​—AROMA 15:5.

NYIMBO: 17, 13

1, 2. (a) Kodi anthu ambiri amakhala ndi maganizo otani pa nkhani yokhala munthu wauzimu? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

MLONGO wina wa ku Canada ananena kuti: “Kukhala munthu wauzimu kwandithandiza kukhala wosangalala komanso kulimbana bwinobwino ndi mayesero amene ndimakumana nawo tsiku ndi tsiku.” M’bale wina wa ku Brazil anati: “Takhala m’banja mosangalala kwa zaka 23 ndipo timaona kuti kuyesetsa kukhala anthu auzimu n’kumene kwatithandiza.” M’bale wina wa ku Philippines anati: “Kukhala munthu wauzimu kwandithandiza kuti ndizikhala ndi mtendere mumtima komanso ndizigwirizana ndi abale azikhalidwe zosiyanasiyana.”

2 Mawu ngati amenewa amasonyeza kuti kukhala munthu wauzimu n’kothandiza kwambiri. Ndipo mwina tingadzifunse kuti: ‘Ndingatani kuti ndikhale munthu wauzimu ndipo zinthu zizindiyendera bwino ngati abale ndi alongo amene atchulidwawa?’ Koma tisanayankhe funsoli tiyenera kukambirana zimene Baibulo limanena zokhudza munthu wauzimu. Munkhaniyi tikambirana mafunso atatu awa: (1) Kodi kukhala munthu wauzimu kumatanthauza chiyani? (2) Kodi ndi zitsanzo za anthu ati zimene zingatithandize kukhala anthu auzimu? (3) Kodi kuyesetsa kukhala ndi “maganizo a Khristu” kungatithandize bwanji kukhala anthu auzimu?

KODI KUKHALA MUNTHU WAUZIMU KUMATANTHAUZA CHIYANI?

3. Kodi Baibulo limafotokoza bwanji kusiyana pakati pa munthu wakuthupi ndi munthu wauzimu?

3 Zimene mtumwi Paulo ananena zingatithandize kudziwa tanthauzo la munthu wauzimu. Iye anafotokoza kusiyana pakati pa “munthu wauzimu” ndi “munthu wakuthupi” kapena kuti “munthu wokonda zinthu za m’dziko.” (Werengani 1 Akorinto 2:14-16; mawu a m’munsi) Kodi anthu amenewa amasiyana bwanji? Paulo ananena kuti munthu wakuthupi “salandira zinthu za mzimu wa Mulungu, chifukwa amaziona ngati zopusa ndipo sangathe kuzidziwa.” Koma “munthu wauzimu” ndi amene “amafufuza zinthu zonse” ndipo ali ndi “maganizo a Khristu.” Paulo anatilimbikitsa kukhala anthu auzimu. Koma kodi munthu wakuthupi amasiyana ndi munthu wauzimu m’njira zinanso ziti?

4, 5. Kodi munthu wakuthupi amachita zotani?

4 Choyamba, tiyeni tikambirane maganizo a munthu wakuthupi. Anthu ambiri m’dzikoli amaganizira kwambiri zofuna zawo. Pofotokoza za maganizo amenewa, Paulo ananena kuti “kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” (Aef. 2:2) Kaganizidweka kamachititsa kuti anthu ambiri azingotengera zimene anzawo akuchita. Iwo amangochita zimene akuona kuti n’zabwino ndipo saganizira mfundo za Mulungu. Munthu wakuthupi amaganizira kwambiri za kutchuka, chuma komanso kulimbana ndi aliyense amene iyeyo akuganiza kuti akumuphwanyira ufulu.

5 Kodi munthu wakuthupi amachitanso zotani? Munthu wotereyu amakonda kuchita “ntchito za thupi.” (Agal. 5:19-21) M’kalata yoyamba imene Paulo analembera mpingo wa ku Korinto, anatchulanso makhalidwe ena amene anthuwa amakhala nawo. Mwachitsanzo, iwo amalimbikitsa magawano, amatengera anzawo kukhoti, salemekeza anthu amene akuwatsogolera ndiponso amakonda kudya kapena kumwa mopitirira malire. Anthu oterewa akakumana ndi mayesero sachedwa kugonja. (Miy. 7:21, 22) Yuda anafotokoza za anthu ena amene amayamba kukonda kwambiri za m’dzikoli moti sakhalanso ndi mzimu wa Mulungu.​—Yuda 18, 19.

6. Kodi munthu wauzimu tingamudziwe bwanji?

6 Ndiye kodi kukhala munthu wauzimu kumatanthauza chiyani? Mosiyana ndi munthu wakuthupi, munthu wauzimu amaganizira kwambiri za ubwenzi wake ndi Mulungu. Amayesetsanso kuti ‘azitsanzira Mulungu.’ (Aef. 5:1) Apa tikutanthauza kuti amayesetsa kudziwa maganizo a Mulungu n’kumaona zinthu mmene Mulunguyo amazionera. Amadalira kwambiri Mulungu ndipo amayesetsa kutsatira mfundo zake pa zonse zimene amachita. (Sal. 119:33; 143:10) Munthu wotereyu sachita “ntchito za thupi” koma amakhala ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Kuti timvetse nkhaniyi tiyeni tiyerekezere chonchi: Munthu amene ali ndi luso pochita bizinezi anthu amangomunena kuti wabizinezi. N’chimodzimodzi ndi munthu amene amaganizira kwambiri zinthu zauzimu kapena kuti zokhudza kulambira Mulungu. Amatchedwa munthu wauzimu.

7. Kodi Baibulo limati chiyani ponena za anthu auzimu?

7 Yesu anasonyeza kuti anthu auzimu amakhala osangalala. Paja pa Mateyu 5:3 ananena kuti “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.” Pofotokozanso za ubwino wokhala munthu wauzimu, lemba la Aroma 8:6 limanena kuti: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.” Munthu akamaika maganizo pa zinthu zauzimu amakhala pa mtendere ndi Mulungu, amakhala ndi mtendere mumtima komanso amakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.

8. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama kuti tikhale anthu auzimu komanso tisabwerere m’mbuyo?

8 Koma dziko limene tikukhalamoli ndi loipa kwambiri. Popeza anthu osaopa Mulungu ali ponseponse, tiyenera kuchita khama kwambiri kuti tikhale auzimu komanso kuti tisabwerere m’mbuyo. Munthu akasiya kuganizira kwambiri za Mulungu amapereka mpata m’maganizo mwake kuti mpweya woipa wa m’dzikoli ulowemo. Ndiye kodi tingatani kuti zimenezi zisatichitikire? Nanga tingatani kuti tizikula mwauzimu?

ANTHU AMENE ANAPEREKA CHITSANZO CHABWINO

9. (a) N’chiyani chingatithandize kuti tikule mwauzimu? (b) Kodi tikambirana chitsanzo cha anthu ati?

9 Mwana amayamba kuchita zinthu ngati munthu wamkulu akamatengera chitsanzo chabwino cha makolo ake. Nafenso tikhoza kukula mwauzimu tikamatsanzira anthu olimba mwauzimu. Koma tiyenera kupewa kutsanzira anthu okonda za m’dzikoli. (1 Akor. 3:1-4) M’Baibulo muli zitsanzo za anthu auzimu ndiponso za anthu akuthupi. Koma poti cholinga chathu n’chakuti tikhale anthu auzimu, tiyeni tikambirane za anthu amene anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Tikambirana chitsanzo cha Yakobo, Mariya ndi Yesu.

Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yakobo? (Onani ndime 10)

10. Kodi Yakobo anasonyeza bwanji kuti anali munthu wauzimu?

10 Choyamba tiyeni tikambirane za Yakobo. Mofanana ndi ifeyo, Yakobo ankakumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, ankafunika kupirira zochita za mkulu wake yemwe ankafunanso kumupha. Apongozi akenso anamuchitira zinthu zachinyengo kambirimbiri. Koma ngakhale kuti ankakhala ndi anthu okonda za m’dziko, Yakobo anakhalabe munthu wauzimu. Iye ankakhulupirira kwambiri zimene Mulungu analonjeza Abulahamu ndipo ankayesetsa kusamalira bwino banja lake podziwa kuti lidzathandiza pokwaniritsa cholinga cha Yehova. (Gen. 28:10-15) Zolankhula komanso zochita za Yakobo zinkasonyeza kuti ankaganizira mfundo za Mulungu komanso cholinga chake. Mwachitsanzo, pa nthawi imene ankaopa kuphedwa ndi Esau, iye anapempha Mulungu kuti: “Ndapota nanu, ndipulumutseni . . . Inuyotu munanena kuti, ‘Mosakayikira m’pang’ono pomwe ndidzakusamalira, ndipo ndidzachulukitsa mbewu yako ngati mchenga wa kunyanja.’” (Gen. 32:6-12) Apa zikuonekeratu kuti Yakobo ankakhulupirira kwambiri zimene Yehova analonjeza iyeyo komanso makolo ake ndipo ankachita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulunguyo.

Kodi tikuphunzira chiyani kwa Mariya? (Onani ndime 11)

11. N’chiyani chikusonyeza kuti Mariya anali munthu wauzimu?

11 Tsopano tiyeni tikambirane chitsanzo cha Mariya. N’chifukwa chiyani Yehova anasankha Mariya kuti akhale mayi a Yesu? N’zosakayikitsa kuti anamusankha chifukwa anali munthu wauzimu. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Zinthu zabwino zimene iye ananena poyamikira Mulungu, pamene anali kunyumba ya Zekariya ndi Elizabeti, zimasonyeza kuti anali wauzimu. (Werengani Luka 1:46-55.) Zimene ananenazo zimasonyeza kuti ankakonda kwambiri Mawu a Mulungu komanso ankadziwa bwino Malemba Achiheberi. (Gen. 30:13; 1 Sam. 2:1-10; Mal. 3:12) Kumbukiraninso kuti iye ndi Yosefe atakwatirana sanagonane mpaka pamene Yesu anabadwa. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Zikusonyeza kuti onse ankaganizira kwambiri za cholinga cha Mulungu osati kuchita zimene ankalakalaka. (Mat. 1:25) Mariya ankaonetsetsa zimene zinkachitika pa moyo wa Yesu ndipo ankamvetsera mawu anzeru amene ankalankhula. Baibulo limanenanso kuti iye “anasunga mosamala kwambiri mawu onsewa mumtima.” (Luka 2:51) Iye ankachita chidwi kwambiri kuti aone mmene Mulungu akukwaniritsira malonjezo ake okhudza Mesiya. Kunena zoona, chitsanzo cha Mariya chimatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tiziika cholinga cha Mulungu pamalo oyamba.

12. (a) Kodi Yesu ankatsanzira bwanji Atate wake? (b) Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji Yesu? (Onani chithunzi choyambirira.)

12 Pa anthu onse amene anakhalapo, kodi ndi ndani amene anapereka chitsanzo chabwino kwambiri chokhala munthu wauzimu? Palibenso wina koma Yesu. Pa moyo wake komanso utumiki wake anasonyeza kuti ankafunitsitsa kutsanzira Atate wake Yehova. Iye ankatsanzira maganizo komanso mtima wa Yehova. Zonse zimene ankachita zinali zogwirizana ndi cholinga cha Mulungu komanso mfundo zake. (Yoh. 8:29; 14:9; 15:10) Mwachitsanzo, tayerekezerani zimene Yesaya analemba zokhudza chifundo cha Yehova ndi zimene Maliko analemba zokhudza chifundo cha Yesu. (Werengani Yesaya 63:9; Maliko 6:34.) Kodi ifeyo timatsanzira Yesu n’kumakhala okonzeka kuthandiza anthu ovutika? Yesu ankachitanso khama kwambiri pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu uthenga wabwino. (Luka 4:43) Zonse zimene Yesu ankachitazi zimasonyeza kuti ndi wauzimu.

13, 14. (a) Kodi tingaphunzire chiyani kwa abale ndi alongo auzimu amasiku ano? (b) Perekani chitsanzo.

13 Masiku ano, palinso abale ndi alongo auzimu amene amayesetsa kutsanzira Yesu. Mwina inunso mwaonapo Akhristu amene amayesetsa kulalikira mwakhama, kulandira bwino alendo, kuchitira anthu chifundo komanso kusonyeza makhalidwe ena abwino. Mofanana ndi ifeyo, nawonso amalakwitsa zinthu zina koma amayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku Brazil dzina lake Rachel. Iye anati: “Poyamba ndinkatengeka kwambiri ndi mafashoni. Izi zinkachititsa kuti ndisamavale mwaulemu. Koma kuphunzira choonadi kwandithandiza kuti ndiyesetse kusintha n’kukhala munthu wauzimu. Sizinali zophweka koma panopa ndimakhala wosangalala.”

14 Nayenso mlongo wina wa ku Philippines dzina lake Reylene anali ndi vuto lina. Iye ankafunitsitsa kuphunzira kwambiri kuti apeze ntchito yapamwamba. Mlongoyu anati: “Zolinga zanga zauzimu zinayamba kutha. Koma ndinazindikira kuti ndikusoweka chinthu china chofunika kwambiri kuposa ntchito yanga. Choncho ndinasintha maganizo ndipo ndinayamba kuona kuti chofunika kwambiri ndi kutumikira Yehova.” Kungoyambira pamene anasintha, wakhala akupereka chitsanzo chabwino pokhulupirira lonjezo la Yehova la pa Mateyu 6:33, 34. Mlongoyu anati: “Sindikayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova adzandisamalira.” Mwina inunso mwaona anthu ena mumpingo wanu amene akuperekanso chitsanzo chabwino. Kunena zoona ndi nzeru kutsanzira anthu ngati amenewa omwe akutsanzira Khristu.​—1 Akor. 11:1; 2 Ates. 3:7.

YESETSANI KUKHALA NDI “MAGANIZO A KHRISTU”

15, 16. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizitsanzira Khristu? (b) Kodi tingatani kuti tizindikire “maganizo a Khristu”?

15 Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji Khristu? Pa 1 Akorinto 2:16, Baibulo limasonyeza kuti tiyenera kukhala ndi “maganizo a Khristu.” Lemba la Aroma 15:5 limanenanso kuti tiyenera kukhala ndi “maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.” Choncho kuti titsatire mapazi a Khristu, tiyenera kudziwa bwino maganizo komanso makhalidwe ake. Nthawi zonse Yesu amaganizira ubwenzi wake ndi Mulungu. Choncho tikamatsanzira Yesu timakhala kuti tikutsanziranso Yehova. N’chifukwa chake tiyenera kuyesetsa kuti tiziganiza ngati mmene Yesu amaganizira.

16 Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Ophunzira a Yesu anamuona akuchita zozizwitsa, akukamba nkhani, akuchita zinthu ndi anthu osiyanasiyana komanso akutsatira mfundo za Mulungu. Iwo anafika ponena kuti: “Ife ndife mboni za zinthu zonse zimene anachita.” (Mac. 10:39) Koma ifeyo sitingamuone Yesu mwachindunji. Koma Yehova watipatsa nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zomwe zingatithandize kumvetsa makhalidwe a Yesu. Tikamawerenga komanso kusinkhasinkha mabuku a Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane timazindikira maganizo a Khristu. Zimenezi zimatithandiza kuti ‘titsatire mapazi ake mosamala kwambiri’ komanso kuti ‘tikhale ndi maganizo’ a Khristu.​—1 Pet. 2:21; 4:1.

17. Kodi kukhala ndi maganizo a Khristu kungatithandize bwanji?

17 Kodi kukhala ndi maganizo a Khristu kungatithandize bwanji? Munthu akamadya chakudya chabwino thupi lake limakhala lamphamvu. Mofanana ndi zimenezi, munthu akamaphunzira kuti adziwe maganizo a Khristu amakhala wolimba mwauzimu. Zimenezi zimamuthandiza kudziwa zimene Khristu akanachita pa nkhani iliyonse. Zikatero, munthu amasankha zinthu zimene zimasangalatsa Mulungu komanso zimamuthandiza kukhala ndi chikumbumtima chabwino. Zimenezitu ndi zifukwa zabwino zomwe zingatilimbikitse ‘kuvala Ambuye Yesu Khristu.’​—Aroma 13:14.

18. Kodi inuyo mwaphunzira mfundo ziti pa nkhani ya kukhala munthu wauzimu?

18 Nkhaniyi yatithandiza kudziwa bwino munthu wauzimu. Yatithandizanso kuona zimene tingaphunzire kwa anthu amene anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Pomaliza taona mmene kukhala ndi “maganizo a Khristu” kungatithandizire kuti tikule mwauzimu. Koma pali mfundo zinanso zimene tiyenera kukambirana pa nkhaniyi. Mwachitsanzo, kodi tingadziwe bwanji ngati ndifedi olimba mwauzimu? Tingatani kuti tizikula mwauzimu? Nanga kukhala munthu wauzimu kungatithandize bwanji pa zochita zathu za tsiku ndi tsiku? Munkhani yotsatira tidzakambirana mafunso amenewa.