Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZA M’NKHOKWE YATHU

Kufalitsa Uthenga Wabwino ku Ireland mwa Nkhani Zapoyela

Kufalitsa Uthenga Wabwino ku Ireland mwa Nkhani Zapoyela

TSIKU lina m’maŵa pamene boti inayandikila doko lochedwa Belfast Lough ku Ireland, kagulu ka anthu amene anaimilila pamwamba pa botilo kanaona mapili obiliwila bwino. Umu munali m’mwezi wa May, 1910. Pakati pawo panali munthu wina dzina lake Charles T. Russell. Uwu unali ulendo wake wacisanu wopita ku Ireland. Kutsogolo kwawo, M’bale Russell anaona sitima ziŵili zikulu-zikulu zapamadzi zimene zinali mkati momangidwa. Sitima yoyamba inali kuchedwa Titanic, ndipo inayo Olympic. * Kofikila sitima zapamadzi kunali kutaimilila Ophunzila Baibo 12, amene anabwela kudzalandila M’bale Russell.

Zaka 20 m’mbuyomo, M’bale Russell anaganiza zoyamba kuyenda m’maiko osiyana-siyana a kunja kwa dziko la America, pofuna kupeza njila yabwino yofalitsila uthenga wabwino padziko lonse. Pa ulendo wake woyamba, iye anayambila kucezela dziko la Ireland. Umu munali mu July, 1891. Sitima imene m’Bale Russell anakwela yochedwa City of Chicago itayandikila tauni yochedwa Queenstown, iye anaona dzuŵa likuloŵa ca ku gombe la nyanja. Mwacionekele, anakumbukila zimene makolo ake anali kumuuza zokhudza kukongola kwa dziko lawo. Pamene M’bale Russell na anzake anali kudutsa cakufupi ndi matauni na midzi yokongola, anazindikila kuti mbeu za m’munda wauzimu kumeneko zinali “zitaca kale ndipo zinali kuyembekezela okolola.”

M’bale Russell anayendela dziko la Ireland maulendo 7. Cidwi cimene anadzutsa paulendo woyamba, mwacionekele n’cimene cinacititsa kuti pa maulendo ake otsatila, anthu mahandiledi, ndipo nthawi zina masausande, azibwela kudzamvetsela nkhani zake. Paulendo wake waciŵili mu May 1903, misonkhano yapoyela imene inali kucitikila ku Belfast ndi ku Dublin, inali kulengezedwa m’manyuzipepala. M’bale Russell anakamba kuti “anthu anali kumvetsela mwachelu” pamene anali kukamba nkhani yofotokoza za cikhulupililo ca Abulahamu na madalitso amene anthu adzalandila m’tsogolo.

Cifukwa cakuti anthu ambili anali acidwi kumeneko, M’bale Russell anayendelanso dziko la Ireland paulendo wake wacitatu wopita ku Ulaya. Tsiku lina m’maŵa mu April 1908, abale 5 anamulandila atafika pa doko la ku Belfast. Nkhani yapoyela imene inali italengezedwa, ya mutu wakuti “Kugwetsedwa kwa Ulamulilo wa Satana,” inakoka “anthu acidwi pafupi-fupi 300.” Wotsutsa wina pa gululo sanapite patali na mtsutso wake atamuyankha mafunso ake poseŵenzetsa Malemba mwaluso. Mu mzinda wa Dublin, munali mwamuna wina wotsutsa kwambili dzina lake O’Connor, amene anali kalembela wa kagulu ka cipembedzo kochedwa YMCA. Iye anayesa kukopa anthu opitilila 1,000 amene anali kumvetsela kuti ayambe kutsutsa Ophunzila Baibo. Kodi zotulukapo zake zinali zotani?

Tiyeni tiyelekezele kuti tikuona m’maganizo mwathu zimene zinacitika pa nthawiyo. Mwamuna wina wofunitsitsa kudziŵa coonadi ca m’Baibo, wabwela kudzamvetsela nkhani yapoyela imene inalengezedwa m’nyuzipepala ya The Irish Times. Movutikila, iye akupeza malo okhala mu holo imene mukukambidwila nkhaniyo. Mwamunayo akumvetsela mwachelu kwa M’bale Russell, mkambi wa imvi ndi ndevu zambili, amene wavala jekete yaitali yakuda. Pamene mkambiyo akamba nkhani yake, akuyenda uku na uku pa pulatifomu, kwinaku akucita magesica. Iye akulumikiza malemba na kuwafotokoza mwaluso cakuti mwamuna wacidwi uja wayamba kumvetsetsa coonadi ca m’Baibo. Olo kuti palibe maikolofoni, mau a mkambiyo akumveka mu holo yonseyo, cakuti anthu akumvetsela mwachelu nkhaniyo kwa ola limodzi na hafu. Ndiyeno, panthawi ya mafunso na mayankho, O’Connor uja ndi anzake akufunsa M’bale Russell mafunso amtsutso, koma iye akuikila kumbuyo uthengawo poseŵenzetsa Baibo. Omvetselawo akuomba m’manja poonetsa kuti akuvomeleza zimene m’baleyo wakamba. Pambuyo pa zonsezo, mwamuna wacidwi uja akupita kwa abalewo kukafunsila zoonjezeleka. Malinga ndi umboni wa anthu amene analipo pa nthawiyo, ambili anaphunzila coonadi mwa njila imeneyi.

Ponyamuka mumzinda wa New York, pa ulendo wake wacinayi, M’bale Russell anakwela sitima yapamadzi yochedwa Mauretania. Umu munali m’mwezi wa May 1909. Pa ulendowo, iye anatenga M’bale Huntsinger, amene anali kalembela. Anam’tenga n’colinga cakuti paulendo wautaliwo, azim’thandiza kulemba nkhani za mu Nsanja ya Mlonda. Pa nkhani yapoyela imene M’bale Russell anakamba m’holo ina ku Belfast, panapezeka anthu 450, ndipo pafupi-fupi 100 mwa anthuwo anaimilila cifukwa cosoŵa pokhala.

M’bale C. T. Russell ali pa sitima yapamadzi yochedwa Lusitania

Paulendo wacisanu umene tauchula kuciyambi, M’bale Russell anayankhanso mafunso a otsutsa. Russell atakamba nkhani yapoyela ku Dublin, katswili wina wa zacipembedzo amene O’Connor anam’bweletsa anayamba kufunsa mafunso. Koma M’bale Russell anamuyankha poseŵenzetsa Malemba, ndipo omvetsela anakondwela kwambili. Tsiku lotsatila, Ophunzila Baibo anakwela boti ya melo kupita ku Liverpool. Kumeneko, anakwela sitima ya pamadzi yochedwa Lusitania kupita ku New York. *

Nkhani yapoyela yolengezedwa m’nyuzipepala ya The Irish Times, pa May 20, 1910

Mu 1911, paulendo wa namba 6 na 7 wa M’bale Russell, nkhani za poyela zimene zinalengezedwa zija nazonso zinakambidwa. Mu April 1911, Ophunzila Baibo 20 a ku Belfast analandila alendo 2,000 amene anabwela kudzamvetsela nkhani yakuti “Moyo Pambuyo pa Imfa.” O’Connor anabwelanso ku Dublin ndi mnzake wacipembedzo, amene anayambanso kufunsa mafunso otsutsa. Koma omvetselawo anali kuombela m’manja povomeleza mayankho ocokela m’Malemba a M’bale Russell. Mu October caka cimeneco, M’bale Russell anakambanso nkhani m’matauni ena, ndipo kumeneko kunalinso anthu ambili omvetsela. O’Connor na anthu 100 acipongwe anayesa kusokoneza msonkhano wina umene m’baleyu anacititsa ku Dublin, koma omvetsela anacita zotheka pomuikila kumbuyo mlankhuliyo.

Olo kuti M’bale Russell ndiye anali kukamba nkhani kaŵili-kaŵili, anazindikila kuti “Gulu la Mulungu silidalila munthu mmodzi” cifukwa “iyi si nchito ya munthu, koma ya Mulungu.” Nkhani zapoyela zimenezo, zimene masiku ano timati Msonkhano wa Anthu Onse, zinapeleka mipata yabwino yophunzitsa anthu coonadi ca m’Malemba. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Nkhanizo zinathandizila kufalitsa uthenga wabwino, ndipo mipingo inabadwa m’mizinda yambili m’dziko lonse la Ireland.—Za m’nkhokwe yathu ku Britain.

^ par. 3 Patapita zaka ziŵili, sitima ya Titanic inasweka n’kumila m’madzi.

^ par. 9 Sitima yapamadzi ya Lusitania inamizidwa mu May, 1915, ku gombe la kum’mwela kwa dziko la Ireland.