Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani si zololeka kuika pawebusaiti ina kapena pamalo ochezera a pa intaneti zinthu zimene a Mboni za Yehova amafalitsa?

Popeza a Mboni za Yehovafe timapereka mabuku ndi zinthu zina kwaulere, anthu ena amaganiza kuti palibe vuto ngati atakopera zinthu zina n’kukaziika pawebusaiti kapena pamalo ena ochezera pa intaneti. Koma kuchita zimenezi n’kuphwanya mfundo zoyenera kutsatira pogwiritsa ntchito webusaiti yathu ndipo kungayambitse mavuto aakulu. * Malinga ndi mfundo zoyenera kutsatira pogwiritsa ntchito webusaiti yathu, si zololeka kutenga zithunzi, mabuku, zizindikiro, nyimbo, mavidiyo ndiponso nkhani n’kukaziika pawebusaiti ina kapena pamalo pamene anthu amachezera. N’chifukwa chiyani sitilola zimenezi?

Si zololeka kukopera zinthu zathu n’kukaziika pa intaneti

Pali lamulo loletsa kufalitsa zinthu zimene munthu wakopera pawebusaiti yathu. Anthu ampatuko amatenga zinthu m’mabuku athu n’kuziika m’mawebusaiti awo n’cholinga choti akope a Mboni za Yehova komanso anthu ena. Koma zimene amalemba kapena kuika m’mawebusaiti ngati amenewa zimachititsa anthu kuyamba mtima wokayikira. (Sal. 26:4; Miy. 22:5) Anthu ena amatsatsa malonda awo pogwiritsa ntchito zinthu zimene timaika pawebusaiti ndipo ena amagwiritsa ntchito molakwika zinthu zathu m’zipangizo zawo zamakono. Malamulo oletsa kufalitsa zinthu zapawebusaitiyi amathandiza kuti zoterezi zisamachitike. (Miy. 27:12) Koma tikalola kuti anthu azingotenga zinthu pawebusaitiyi kapena chizindikiro cha jw.org n’kumazigwiritsa ntchito potsatsa malonda, makhoti sangatithandize kukhwimitsa chitetezo chathu kwa anthu otsutsa kapena amalonda.

Kuchita dawunilodi pawebusaiti ina zinthu zimene timafalitsa m’malo mochita dawunilodi pa jw.org n’koopsa. Yehova wapatsa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” udindo wopereka chakudya chauzimu. (Mat. 24:45) ‘Kapoloyu’ amagwiritsa ntchito webusaiti yovomerezeka popereka chakudya chauzimuchi moti tingachipeze pa www.pr418.com, tv.pr418.com, ndiponso pa wol.pr418.com. Tilinso ndi mapulogalamu ovomerezeka atatu okha a pa zipangizo zamakono omwe ndi JW Language, JW Library ndi JW Library Sign Language. Sitikayikira kuti ngati munthu atafika m’malo ngati amenewa sadzapezapo zamalonda ndipo sipapezeka zinthu zoipa za m’dziko la Satanali. Koma ngati zinthuzi zitadzera kumawebusaiti ena, sitingakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti zilibe vuto lililonse.​—Sal. 18:26; 19:8.

Tizikumbukiranso kuti ngati titaika zinthu zathu pawebusaiti pamene anthu akhoza kulembapo maganizo awo, tingapereke mpata kwa anthu ampatuko komanso otsutsa kuti achititse anthu kukayikira gulu la Yehova. Zikuoneka kuti abale ndi alongo ena amayamba kutsutsana ndi anthu pamalo ochezera pa intaneti ndipo zimenezi zimanyozetsa dzina la Yehova. Tisaiwale kuti malo ngati amenewa sangatipatse mpata “wolangiza mofatsa anthu otsutsa.” (2 Tim. 2:23-25; 1 Tim. 6:3-5) Zikuonekanso kuti anthu ena atsegula maakaunti pa intaneti komanso mawebusaiti okhala ndi dzina la gulu la Yehova, Bungwe Lolamulira kapena anthu amene ali m’Bungwe Lolamulira. Koma dziwani kuti palibe m’bale wa m’Bungwe Lolamulira amene ali ndi webusaiti yakeyake kapena malo ochezera pa intaneti.

Kulimbikitsa anthu kuti azipita pa jw.org kumathandiza kufalitsa “uthenga wabwino.” (Mat. 24:14) Zinthu za pa intaneti zimene timagwiritsa ntchito mu utumiki zimasinthidwa pafupipafupi. Timachita izi n’cholinga choti anthu ambiri azipindula nazo. Choncho malinga ndi mfundo zoyenera kutsatira pogwiritsa ntchito webusaiti yathu, palibe vuto ngati munthu atatumizira munthu wina buku kapena linki yoti apitire pa jw.org. Tikamalimbikitsa anthu kuti azipita pawebusaiti yathu yovomerezeka timawathandiza kuti afike pamalo amene angapeze chakudya chauzimu chenicheni chimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka.

^ ndime 1 Ngati mukufuna kudziwa mfundo zoyenera kutsatira pogwiritsa ntchito webusaiti yathu, pitani m’munsi mwenimweni pa jw.org pamene alemba kuti Zoyenera Kutsatira. Zinthu zimene talemba kuti simuyenera kuchita zikukhudza chilichonse chimene timaika pawebusaitiyi.