Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Tiyeni Tilimbikitsane, Ndipo Tiwonjezele Kucita Zimenezi”

“Tiyeni Tilimbikitsane, Ndipo Tiwonjezele Kucita Zimenezi”

“Tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” —AHEB. 10:24, 25.

NYIMBO: 90, 87

1. N’cifukwa ciani mtumwi Paulo analangiza Akhristu oyambilila aciheberi kuti awonjezele mzimu wolimbikitsana?

N’CIFUKWA CIANI tiyenela kuwonjezela zimene timacita polimbikitsa ena? M’kalata yopita kwa Akhristu aciheberi, mtumwi Paulo anafotokoza cifukwa cake. Anawauza kuti: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena acizoloŵezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” (Aheb. 10:24, 25) Panali patatsala zaka 5 cabe kuti Akhristu aciyuda okhala mu Yerusalemu aone cizindikilo cimene Yesu anawapatsa coonetsa kuti “tsiku . . , la Yehova” layandikila, ndipo anafunika kuthaŵa mu mzindawo kuti apulumutse miyoyo yawo. (Mac. 2:19, 20; Luka 21:20-22) Tsiku la Yehova limenelo linafika mu 70 C.E. pamene Aroma anawononga Yerusalemu mogwilizana na ciweluzo ca Yehova.

2. N’cifukwa ciani tiyenela kuona nkhani ya kulimbikitsana kukhala yofunika kwambili masiku ano?

2 Masiku ano, tili na cifukwa comveka cokhulupilila kuti ‘tsiku la Yehova lalikulu ndi locititsa mantha’ lili pafupi. (Yow. 2:11) Mneneli Zefaniya anati: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwela mofulumila kwambili.” (Zef. 1:14) Mau aulosi ocenjeza amenewa akhudzanso ise masiku ano. Popeza kuti tsiku la Yehova layandikila, Paulo anatilangiza kuti, “tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.” (Aheb. 10:24) Conco, tiyenela kumaganizila kwambili za umoyo wa abale na alongo athu kuti tiwalimbikitse pamene kuli kofunikila.

N’NDANI AMAFUNIKILA CILIMBIKITSO?

3. Kodi mtumwi Paulo anakamba ciani pa nkhani ya kulimbikitsana? (Onani pikica kuciyambi.)

3 Baibo imati: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauwelamitsa, koma mau abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miy. 12:25) Izi zimacitikila aliyense wa ise. Conco, tonse timafunika kulimbikitsiwa nthawi na nthawi. Paulo anaonetsa kuti anthu amene ali na udindo wolimbikitsa ena, nawonso amafunikila cilimbikitso. Iye analembela Akhristu a ku Roma kuti: “Ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugaŵileni mphatso inayake yauzimu kuti mukhale olimba, kapena kuti tidzalimbikitsane mwa cikhulupililo, canu ndi canga.” (Aroma 1:11, 12) Ndithudi, olo kuti Paulo anali kulimbikitsa kwambili Akhristu anzake, nayenso nthawi zina anafunika kulimbikitsidwa.—Ŵelengani Aroma 15:30-32.

4, 5. N’ndani amene tingawalimbikitse masiku ano? Nanga n’cifukwa ciani?

4 Abale na alongo amene ali na umoyo wodzimana, tifunika kumawayamikila. Ena a iwo ni apainiya okhulupilika. Akhristu oculuka adzimana zambili mu umoyo wawo kuti akhale na mpata wocita upainiya. N’cimodzi-modzinso ndi amishonale, atumiki a pa Beteli, oyang’anila dela na azikazi awo, komanso abale amene akutumikila m’maofesi omasulila mabuku. Onsewa amadzimana zinthu zina mu umoyo wawo kuti azithela nthawi yambili pocita utumiki wopatulika. Kaamba ka ici, iwo amafunika kulimbikitsiwa. Palinso abale na alongo ena amene pa zifukwa zina analeka kucita utumiki wa nthawi zonse, koma akali kuulaka-laka. Nawonso angayamikile ngati tiwalimbikitsa.

5 Enanso amene amafunikila cilimbikitso ni abale na alongo amene sali pa banja cifukwa cofuna kumvela lamulo lakuti tiyenela kukwatila kokha “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Nawonso akazi amene amagwila nchito mwakhama pa banja amayamikila kumvela tumau tolimbikitsa tocokela kwa amuna awo. (Miy. 31:28, 31) Komanso, Akhristu amene akupilila mokhulupilika cizunzo kapena matenda, amafunika kulimbikitsidwa. (2 Ates. 1:3-5) Yehova na Mwana wake amalimbikitsa Akhristu onse okhulupilika amenewa.—Ŵelengani 2 Atesalonika 2:16, 17.

AKULU AMAYESETSA KULIMBIKITSA ENA

6. Malinga n’zimene zili pa Yesaya 32:1, 2, kodi akulu ali na udindo wanji?

6 Ŵelengani Yesaya 32:1, 2. M’nthawi yovuta ino, Yesu Khristu amapeleka cilimbikitso na citsogozo kwa abale na alongo olefuka na opsinjika maganizo. Amacita izi kupitila mwa abale ake odzozedwa ndi “akalonga,” amene ni akulu a m’gulu la nkhosa zina. Akulu amenewa si “olamulila” cikhulupililo ca ena, koma ni ‘antchito anzathu’ amene amatithandiza kukhala na cimwemwe.—2 Akor. 1:24.

7, 8. Kuwonjezela pa kukamba mau olimbikitsa, kodi akulu angalimbikitse bwanji ena?

7 Mtumwi Paulo anatisiila citsanzo cimene tiyenela kutengela. Polembela kalata Akhristu a ku Tesalonika amene anali kukumana na cizunzo, iye anati: “Popeza timakukondani kwambili, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeni-yeniyo, cifukwa tinakukondani kwambili.”—1 Ates. 2:8.

8 Pokamba na akulu a mu mpingo wa ku Efeso, Paulo anaonetsa kuti kulimbikitsa ena na mau cabe, nthawi zina sikukhala kokwanila. Iye anawauza kuti: “Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukila mau a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.’” (Mac. 20:35) Paulo sanangolimbikitsa abale ake na mau cabe, koma ‘anagwilitsila nchito zinthu zake zonse ndi kupeleka moyo wake wonse cifukwa ca miyoyo yawo.’ (2 Akor. 12:15) N’cimodzi-modzinso na akulu. Sayenela kulimbikitsa ndi kutonthoza Akhristu anzawo na mau cabe, koma afunikanso kuwalimbikitsa mwa kuwaonetsa cidwi ceni-ceni.—1 Akor. 14:3.

9. Kodi akulu angapeleke bwanji uphungu m’njila yolimbikitsa?

9 Nthawi zina, kulimbikitsana kungaphatikizepo kupeleka uphungu. Pa mbali imeneyinso, akulu ayenela kutengela citsanzo ca m’Baibo ca mmene tingapelekele uphungu m’njila yolimbikitsa. Citsanzo cabwino ngako pa nkhaniyi ni cimene Yesu anapeleka pambuyo pa imfa na kuukitsidwa kwake. Iye anapeleka uphungu wamphamvu ku mipingo ina ya m’cigawo ca Asia Minor. Kodi anaupeleka motani? Asanapeleke uphungu ku mpingo wa ku Efeso, Pegamo, na wa ku Tiyatira, coyamba anaiyamikila mipingoyo. (Chiv. 2:1-5, 12, 13, 18, 19) Iye anauza mpingo wa ku Laodikaya kuti: “Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Conco, khala wodzipeleka ndipo ulape.” (Chiv. 3:19) Akulu angacite bwino kutengela citsanzo ca Khristu pamene apeleka uphungu.

KULIMBIKITSA ENA SI UDINDO WA AKULU CABE

Makolo, kodi mumaphunzitsa ana anu kuti azilimbikitsa ena? (Onani palagilafu 10)

10. Kodi tonse tingacite ciani kuti tizilimbikitsana wina na mnzake?

10 Kulimbikitsa ena si udindo wa akulu cabe. Paulo analangiza Akhristu kuti azikamba mau “olimbikitsa monga mmene kungafunikile, kuti asangalatse owamva.” (Aef. 4:29) Aliyense wa ise ayenela kukhala chelu kuti adziŵe zimene ena ‘akufunikila.’ Komanso, polangiza Akhristu aciheberi, Paulo anati: “Limbitsani manja amene ali lende ndi mawondo olobodoka, ndipo pitilizani kuwongola njila zimene mapazi anu akuyendamo, kuti ciwalo cimene cavulala cisaguluke polumikizila, koma cicilitsidwe.” (Aheb. 12:12, 13) Ise tonse, kuphatikizapo acicepele, tingalimbikitse Akhristu anzathu mwa kukamba mau olimbikitsa.

11. Kodi Marthe analimbikitsiwa bwanji pa nthawi imene anali kuvutika maganizo?

11 Marthe, * mlongo amene anavutika maganizo kwa nthawi itali, analemba kuti: “Tsiku lina pamene n’napemphela kuti nipeze cilimbikitso, n’nakumana na mlongo wina wacikulile amene ananionetsa cikondi na cifundo. Izi n’zimene n’nali kufunikila kwambili pa nthawiyo. Mlongoyo ananiuza kuti nayenso anakumanapo na vuto monga limene ine n’nali nalo. Conco, n’nayamba kuona kuti si ine nekha amene n’nali na vutolo.” N’kutheka kuti mlongo wacikulileyo sanazindikile mmene mau ake analimbikitsila Marthe.

12, 13. Kodi tingaseŵenzetse bwanji malangizo a pa Afilipi 2:1-4?

12 Paulo analangiza Akhristu a mu mpingo wa Filipi kuti: “Cotelo, ngati pakati panu pali kulimbikitsana kulikonse mwa Khristu, kaya kutonthozana kulikonse kwa cikondi, kaya mzimu woganizilana, kaya cikondi cacikulu ciliconse ndi cifundo, cititsani cimwemwe canga kusefukila pokhala ndi maganizo amodzi, ndi cikondi cofanana. Mukhalenso ogwilizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi. Musacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzicepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.”—Afil. 2:1-4.

13 Ndithudi, tonse tiyenela kuyesetsa kumaganizila zofuna za ena. Tiyenela ‘kumatonthozana mwacikondi,’ kuonetsa “mzimu woganizilana,” komanso kusonyeza ‘cikondi cacikulu ndi cifundo’ kuti tilimbikitse abale na alongo athu.

ZINTHU ZINA ZIMENE ZINGATILIMBIKITSE

14. Chulani cinthu cimodzi cimene cingatilimbikitse.

14 Tikamva kuti anthu amene tinawathandiza kuphunzila coonadi akutumikila Mulungu mokhulupilika, timalimbikitsidwa ngako, monga mmene mtumwi Yohane analimbikitsidwila. Iye analemba kuti: “Palibe cimene cimandisangalatsa kwambili kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’coonadi.” (3 Yoh. 4) Apainiya ambili amalimbikitsiwa kwambili akadziŵa kuti ena mwa anthu amene iwo anawaphunzitsa coonadi akali kutumikila Yehova mokhulupilika, mwinanso kuti akucita upainiya. Conco ngati mpainiya wafooka, tingamulimbikitse mwa kum’kumbutsa zabwino zimene wakhala akucita pothandiza ena.

15. Ni njila ina iti imene tingalimbikitsile Akhristu amene akutumikila mokhulupilika?

15 Oyang’anila dela ambili amakamba kuti iwo na azikazi awo amalimbikitsiwa ngako akalandila kakalata kowayamikila pambuyo pocezela mpingo. Ni mmenenso akulu, apainiya, na atumiki a pa Beteli amamvelela akayamikilidwa cifukwa cotumikila mokhulupilika.

MMENE ALIYENSE WA ISE ANGALIMBIKITSILE MNZAKE

16. N’zinthu monga ziti zosavuta zimene tingacite polimbikitsa ena?

16 N’kulakwa kuganiza kuti sitingakwanitse kulimbikitsa ena cifukwa cakuti ndise osamasuka kweni-kweni na ŵanthu. Kulimbikitsa ena sikulila zambili. Mwina mungangomwetulila popatsa moni munthu. Ngati iye sakumwetulila, ndiye kuti mwina pali cinacake cimene cikumuvutitsa maganizo, ndipo kungomumvetsela pamene akamba nkhawa zake kungamulimbikitse.—Yak. 1:19.

17. Kodi m’bale wina wacicepele analimbikitsiwa bwanji pa nthawi yovuta?

17 M’bale wina wacicepele, dzina lake Henri, cinamuŵaŵa kwambili mu mtima pamene abululu ake anasiya coonadi, kuphatikizapo atate ŵake, amene anali mkulu wodziŵika. Henri analimbikitsiwa na woyang’anila dela amene anapita naye ku lesitilanti kukamwa naye tiyi. Kumeneko, anamulola kufotokoza momasuka mmene anali kumvelela. Pambuyo pa makambilanowo, Henri anazindikila kuti njila yokha imene akanathandizila a m’banja lake kubwelela m’coonadi ni kupilila ciyeso cimeneco mokhulupilika. Iye analimbikitsiwa ngako mwa kuŵelenga Salimo 46; Zefaniya 3:17; na Maliko 10:29, 30.

Ise tonse tingalimbikitsane wina na mnzake (Onani palagilafu 18)

18. (a) Kodi Mfumu Solomo inalemba ciani pa nkhani ya kulimbikitsana? (b) Kodi mtumwi Paulo anaonetsa kuti n’ciani cina cimene cingatilimbikitse?

18 Zitsanzo zimene takambilana, ca Marthe ndi ca Henri, zionetsa kuti tingakwanitse kulimbikitsa m’bale kapena mlongo wathu amene afunikila citonthozo. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili. Maso owala amapangitsa mtima kusangalala. Uthenga wabwino umanenepetsa mafupa.” (Miy. 15:23, 30) Kuwonjezela apo, kuŵelenga Nsanja ya Mlonda kapena zofalitsa za pa webusaiti yathu kungalimbikitse munthu wopanikizika m’maganizo. Komanso, Paulo anaonetsa kuti kuimba nyimbo za Ufumu capamodzi kungakhale kolimbikitsa. Iye analemba kuti: “Pitilizani kuphunzitsana ndi kulangizana mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwila mtima. Pitilizani kuimbila Yehova m’mitima yanu.”—Akol. 3:16; Mac. 16:25.

19. N’cifukwa ciani kulimbikitsana kudzakhala kofunika ngako m’tsogolomu? Nanga tifunika kucita ciani?

19 Pamene tsiku la Yehova “likuyandikila,” kulimbikitsana kudzakhala kofunika ngako. (Aheb. 10:25) Monga mmene Paulo anakambila kwa Akhristu a m’nthawi yake, na ise tikuti: “Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukucitila.”—1 Ates. 5:11.

^ par. 11 Maina ena asinthidwa.