Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cifukwa Cake ‘Timapitiliza Kubala Zipatso’

Cifukwa Cake ‘Timapitiliza Kubala Zipatso’

“Atate amalemekezeka mukapitiliza kubala zipatso zambili ndi kusonyeza kuti mulidi ophunzila anga.”—YOH. 15:8

NYIMBO: 53, 60

1, 2. (a) Atatsala pang’ono kuphedwa, kodi Yesu anawauza ciani ophunzila ake? (Onani pikica pamwambapa.) (b) N’cifukwa ciani kukumbukila zifukwa zimene timagwilila nchito yolalikila n’kofunika? (c) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

USIKU wakuti maŵa adzaphedwa, Yesu anakambilana na atumwi ake kwa nthawi yaitali, ndipo anawatsimikizila kuti amawakonda ngako. Komanso, iye anawafotokozela fanizo la mtengo wa mpesa, limene tinakambilana m’nkhani yapita. M’fanizolo, Yesu analimbikitsa ophunzila ake ‘kupitiliza kubala zipatso zambili,’ kutanthauza kupilila polalikila uthenga wabwino wa Ufumu.—Yoh. 15:8.

2 Yesu sanangouza ophunzila ake kuti azilalikila, koma anawauzanso zifukwa zake anafunika kucita zimenezo. N’cifukwa ciani kukambilana zifukwa zimenezo n’kofunika? Cifukwa cakuti ngati nthawi zonse tikumbukila zifukwa zake tiyenela kupitiliza kulalikila, timalimbikitsidwa kupilila pocitila “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:13, 14) Conco, tiyeni tikambilane zifukwa zinayi za m’Malemba zimene timagwilila nchito yolalikila. Komanso, tidzakambilana mphatso zinayi zocokela kwa Yehova zimene zimatithandiza kupilila pogwila nchito imeneyi.

TIMALEMEKEZA YEHOVA

3. (a) Kodi lemba la Yohane 15:8 limafotokoza cifukwa citi cimene tiyenela kugwilila nchito yolalikila? (b) Kodi mpesa za m’fanizo la Yesu ziimila ciani? Nanga n’cifukwa ciani kuyelekezela mwanjila imeneyi n’koyenelela?

3 Cifukwa cacikulu kwambili cimene timalalikilila n’cakuti, timafuna kulemekeza na kuyeletsa dzina la Yehova pakati pa anthu. (Ŵelengani Yohane 15:1, 8.) Onani kuti Yesu anayelekezela Atate ake, Yehova, na mlimi wa mpesa. Iye anadziyelekezela na mtengo wa mpesa, ndipo ophunzila ake anawayelekezela na nthambi za mtengowo. (Yoh. 15:5) Conco, mpesa ziimila zipatso za Ufumu zimene otsatila a Khristu amabala. Kuyelekezela mwanjila imeneyi n’koyenela. Kumbukilani kuti Yesu anauza atumwi kuti: “Atate amalemekezeka mukapitiliza kubala zipatso zambili.” Monga mmene mitengo ya mpesa yobala zipatso zabwino imacititsila kuti mlimi alemekezeke, na ise tikamalalikila uthenga wa Ufumu mwakhama, timacititsa kuti Yehova alemekezeke na kupatsiwa ulemelelo.—Mat. 25:20-23.

4. (a) Kodi dzina la Mulungu timaliyeletsa m’njila ziti? (b) Kodi mumamvela bwanji mukaganizila mwayi umene muli nawo woyeletsa dzina la Mulungu?

4 Kodi nchito yolalikila imayeletsa bwanji dzina la Mulungu? Sikuti ise tingacititse dzina la Mulungu kukhala loyela kwambili kuposa mmene lilili. Ilo n’loyela kale mokwanila kapena kuti n’lopatulika. Koma onani zimene mneneli Yesaya anakamba. Anati: “Yehova wa makamu ndi amene muyenela kumuona kuti ndi woyela.” (Yes. 8:13) Conco, njila zina zimene timayeletsela dzina la Mulungu ni mwa kuliona kukhala lapadela kwambili kuposa maina ena onse, komanso kuthandiza anthu ena kuti aziliona mwanjila imeneyi. (Mat. 6:9) Mwacitsanzo, pamene tiuzako ena coonadi ponena za makhalidwe abwino a Yehova na colinga cake cosasinthika kwa anthu, timakhalila kumbuyo dzina la Mulungu potsutsa mabodza a Satana na zinenezo zake. (Gen. 3:1-5) Cinanso, timayeletsa dzina la Mulungu mwa kuyesetsa kuthandiza anthu a m’gawo lathu kuona kuti Yehova ni woyenelela “kulandila ulemelelo ndi ulemu” ndi mphamvu. (Chiv. 4:11) Rune, mpainiya amene watumikila kwa zaka 16, anati: “Nimayamikila ngako mwayi umene nili nawo wocitila umboni za Mlengi wa cilengedwe conse. Zimenezi zimanilimbikitsa kupitiliza kulalikila.”

TIMAKONDA YEHOVA NA MWANA WAKE

5. (a) Kodi lemba la Yohane 15:9, 10 limachula cifukwa cina citi cogwilila nchito yolalikila? (b) Kodi Yesu anagogomeza bwanji kufunika kokhala opilila?

5 Ŵelengani Yohane 15:9, 10. Cifukwa cina cacikulu cimene timalalikilila uthenga wa Ufumu n’cakuti timakonda Yehova na Yesu ndi mtima wonse. (Maliko 12:30; Yoh. 14:15) Yesu sanangouza ophunzila ake kuti akhale m’cikondi cake. Koma anawauzanso kuti “akhalebe m’cikondi [cake].” N’cifukwa ciani anawauza conco? Cifukwa cakuti munthu amafunika kupilila kuti apitilize kukhala wotsatila woona wa Khristu. Pa Yohane 15:4-10, Yesu anagogomeza kufunika kwa khalidwe la kupilila mwa kuseŵenzetsa mau angapo otanthauza “kukhalabe.”

6. Kodi timaonetsa bwanji kuti tifuna kukhalabe m’cikondi ca Khristu?

6 Kodi timaonetsa bwanji kuti tifuna kukhalabe m’cikondi ca Khristu? Timacita izi mwa kusunga malamulo ake. Mwacidule, Yesu amafuna kuti tizimumvela. Zilizonse zimene Yesu anatilamula kucita ni zimenenso iye anali kucita. Ndiye cifukwa cake anakamba kuti tifunika kusunga malamulo ake ‘monga mmene iye anasungila malamulo a Atate ake ndi kukhalabe m’cikondi cake.’ Inde, Yesu anatisiila citsanzo.—Yoh. 13:15.

7. Kodi pali kugwilizana kwanji pakati pa kumvela na cikondi?

7 Pa nthawi ina, Yesu anauza atumwi ake mau oonetsa kugwilizana pakati pa kumvela na cikondi. Iye anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda.” (Yoh. 14:21) Kuwonjezela apo, pamene timvela lamulo la Yesu lakuti tizilalikila, timaonetsanso kuti timakonda Mulungu, cifukwa malamulo a Yesu ni ogwilizana ndi cifunilo ca Atate ŵake. (Mat. 17:5; Yoh. 8:28) Ngati timvela malamulo a Yehova na Yesu, iwo adzapitiliza kutikonda.

TIMACENJEZA ANTHU

8, 9. (a) N’cifukwa cina citi cimene timagwilila nchito yolalikila? (b) Kodi mau a Yehova a pa Ezekieli 3:18, 19 na pa caputa 18:23 amatilimbikitsa bwanji kupitiliza kulalikila?

8 Tilinso na cifukwa cina copitilizila kugwila nchito yolalikila. Timalalikila pofuna kucenjeza anthu. Baibo imakamba kuti Nowa anali “mlaliki.” (Ŵelengani 2 Petulo 2:5.) Mwacionekele, nchito yolalikila imene iye anagwila Cigumula cisanafike, inaphatikizapo kucenjeza anthu za ciwonongeko cimene cinali kubwela. Tidziŵa bwanji zimenezi? Kumbukilani kuti Yesu anati: “M’masiku amenewo cigumula cisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatila ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analoŵa m’cingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka cigumula cinafika n’kuwaseselatu onsewo. Zidzatelonso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.” (Mat. 24:38, 39) Olo kuti anthu analibe cidwi, Nowa anapitiliza kulengeza mokhulupilika uthenga wocenjeza umene anapatsidwa.

9 Masiku ano, timalalikila uthenga wa Ufumu pofuna kupatsa anthu mwayi wodziŵa colinga ca Mulungu kwa anthu. Mofanana ndi Yehova, timafunitsitsa kuti anthu amvetsele uthenga wathu na “kukhalabe ndi moyo.” (Ezek. 18:23) Pa nthawi imodzi-modzi, pamene tilalikila ku nyumba ndi nyumba komanso pa malo ena aliwonse, timacenjeza anthu ambili kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela ndi kuwononga dziko loipali.—Ezek. 3:18, 19; Dan. 2:44; Chiv. 14:6, 7.

TIMAKONDA ANTHU ANZATHU

10. (a) Kodi pa Mateyu 22:39 pali cifukwa canji cimene tiyenela kugwilila nchito yolalikila? (b) Fotokozani mmene Paulo na Sila anathandizila woyang’anila ndende ku Filipi.

10 Cifukwa cina cacikulu cimene timapitilizila kulalikila n’cakuti timakonda anthu anzathu. (Mat. 22:39) Cikondi cimeneci cimatilimbikitsa kupitiliza kugwila nchitoyi, podziŵa kuti anthu ena angayambe kumvetsela uthenga wathu pamene zinthu zasintha mu umoyo wawo. Onani zimene zinacitika m’nthawi ya mtumwi Paulo na mnzake Sila. Ali mu mzinda wa Filipi, anthu otsutsa anawaponya m’ndende. Ndiyeno, pakati pa usiku, mwadzidzidzi kunacitika civomezi cimene cinagwedeza ndendeyo na kucititsa kuti zitseko za ndendeyo zitseguke. Woyang’anila ndende anacita mantha poganiza kuti akaidi athaŵa. Kaamba ka ici, iye anatenga lupanga kuti adziphe. Koma Paulo anafuula mokweza kuti: “Usadzivulaze!” Woyang’anila ndendeyo anati: “Ndicite ciani kuti ndipulumuke?” Iwo anamuuza kuti: “Khulupilila mwa Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka.”—Mac. 16: 25-34.

Kukonda Yehova, Yesu, na anthu anzathu kumatilimbikitsa kulalikila (Onani palagilafu 5, 10)

11, 12. (a) Kodi nkhani ya woyang’anila ndende igwilizana bwanji na nchito yathu yolalikila? (b) Kodi pamene tigwila nchito yolalikila, timakhala okonzeka kucita ciani?

11 Kodi nkhani ya woyang’anila ndende igwilizana bwanji na nchito yathu yolalikila? Onani kuti woyang’anila ndende uja anamvetsela na kupempha thandizo pambuyo pakuti civomezi cacitika. N’cimodzi-modzi masiku ano. Anthu ena amene poyamba sanali kulabadila uthenga wathu wa m’Baibo, angayambe kumvetsela na kusakila thandizo pambuyo pokumana ndi mavuto aakulu mosayembekezeleka. Mwacitsanzo, anthu ena m’gawo lathu angakhale kuti anacotsedwa nchito mosayembekezela ndipo ni othedwa nzelu. Enanso angakhale opwetekedwa mtima cifukwa cakuti cikwati cawo cinasila posacedwa. Komanso, ena angakhale na nkhawa kwambili pambuyo powapeza na matenda aakulu, kapena angakhale na cisoni cacikulu cifukwa ca imfa ya munthu amene anali kum’konda. Zinthu ngati zimenezi zikawacitikila, anthu angayambe kudzifunsa mafunso okhudza colinga ca moyo, amene poyamba sanali kuwaganizila. Mwina angadzifunse kuti, ‘Kodi ningacite ciani kuti nikapulumuke?’ Ndipo tikakumana nawo mu ulaliki, kwa nthawi yoyamba mu umoyo wawo, angafune kumvetsela uthenga wathu wopatsa ciyembekezo.

12 Conco, pamene tipitiliza kugwila nchito yolalikila mokhulupilika, timakhala okonzeka kupeleka cilimbikitso kwa anthu panthawi imene akufunikila thandizo. (Yes. 61:1) Mlongo Charlotte, amene watumikila mu utumiki wanthawi zonse kwa zaka 38, anati: “Anthu masiku ano ni osocela. Iwo amafunikila kumva uthenga wabwino.” Nayenso Ejvor, mpainiya amene watumikila kwa zaka 34, anakamba kuti: “Masiku ano kuposa kale lonse, anthu ambili amafuna cilimbikitso. Nimafunitsitsa kuwathandiza. Ndipo izi zimanilimbikitsa kugwila nchito yolalikila.” Ndithudi! Kukonda anthu anzathu ni cifukwa cabwino cimene cimatilimbikitsa kupitiliza kulalikila.

MPHATSO ZIMENE ZIMATITHANDIZA KUPILILA

13, 14. (a) Ni mphatso yanji imene imachulidwa pa Yohane 15:11? (b) Kodi cimwemwe ca Yesu cingakhale bwanji mwa ise? (c) Nanga cimakhudza bwanji utumiki wathu?

13 Pa usiku wakuti maŵa Yesu adzaphedwa, iye anafotokozelanso atumwi ake mphatso zosiyana-siyana zimene zikanawathandiza kupitiliza kubala zipatso. Kodi mphatso zimene anakamba ni ziti? Nanga timapindula bwanji na mphatso zimenezi?

14 Mphatso ya cimwemwe. Kodi kugwila nchito yolalikila imene Yesu anatilamula n’kolemetsa? Kutalitali! Pambuyo pofotokoza fanizo la mpesa, Yesu anakamba kuti tikamagwila nchito yolalikila za Ufumu, tidzakhala acimwemwe. (Ŵelengani Yohane 15:11) Ndipo iye anatitsimikizila kuti cimwemwe cake cidzakhala mwa ise. Motani? Monga taonela kale, Yesu anadziyelekezela na mtengo wa mpesa, ndipo ophunzila ake anawayelekezela na nthambi. Mtengo wa mpesa umacilikiza nthambi zake. Malinga ngati nthambi n’zolumikizika kumtengo wa mpesawo, zimalandila madzi na cakudya kucokela kumtengowo. Na ise n’cimodzi-modzi. Malinga ngati tikhalabe ogwilizana na Khristu mwa kutsatila mapazi ake mosamala, tidzakhala na cimwemwe monga cimene iye amakhala naco pocita cifunilo ca Atate ake. (Yoh. 4:34; 17:13; 1 Pet. 2:21) Hanne, mpainiya amene watumikila kwa zaka zoposa 40, anati: “Cimwemwe cimene nimakhala naco pambuyo pogwila nchito yolalikila cimanilimbikitsa kupitiliza kum’tumikila Yehova.” Inde, cimwemwe coculuka cimene timapeza, cimatipatsa mphamvu yopitiliza kulalikila ngakhale m’magawo ouma.—Mat. 5:10-12.

15. (a) Ni mphatso yanji imene imachulidwa pa Yohane 14:27? (b) Kodi mtendele umatithandiza bwanji kupitiliza kubala zipatso?

15 Mphatso ya mtendele. (Ŵelengani Yohane 14:27.) M’madzulo, pa tsiku lakuti maŵa adzaphedwa, Yesu anauza atumwi kuti: “Ndikupatsani mtendele wanga.” Kodi mphatso ya mtendele imeneyi imatithandiza bwanji kubala zipatso? Pamene tipilila pa nchito yolalikila, timakhala na mtendele waukulu wa mumtima, umene umabwela cifukwa codziŵa kuti ndise oyanjidwa na Yehova na Yesu. (Sal. 149:4; Aroma 5:3, 4; Akol. 3:15) M’bale Ulf, amene watumikila mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 45, anati: “Nimalema ngako nikagwila nchito yolalikila, koma nchitoyi imanithandiza kukhala wokhutila komanso kuona kuti umoyo wanga uli na phindu.” Kodi sitiyamikila kuti Mulungu watidalitsa mwa kutipatsa mtendele waukulu wa mumtima?

16. (a) Ni mphatso iti imene yachulidwa pa Yohane 15:15? (b) Kodi atumwi anafunika kucita ciani kuti akhalebe mabwenzi a Yesu?

16 Mphatso yokhala pa ubwenzi na Yesu. Pambuyo pouza atumwi ake kuti afuna ‘cimwemwe cawo cisefukile,’ Yesu anawafotokozelanso za kufunika koonetsa cikondi codzimana. (Yoh. 15:11-13) Kenako, anawauza kuti: “Ndakuchani mabwenzi.” Ndithudi! Kukhala pa ubwenzi na Yesu ni mphatso ya mtengo wapatali. Nanga n’ciani cimene atumwiwo anafunika kucita kuti akhalebe mabwenzi ake? Anafunika ‘kupitiliza kubala zipatso zoculuka.’ (Ŵelengani Yohane 15:14-16.) Zaka ziŵili m’mbuyomo, Yesu anali atalamula atumwi ake kuti: “Pitani ndi kulalikila kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikila.’” (Mat. 10: 7) Conco, pa usiku womaliza uja, iye anawalimbikitsa kuti ayenela kupilila pa nchito imene anawapatsa. (Mat. 24:13; Maliko 3:14) Kugwila nchito imene Yesu anawapatsa kunali na zovuta zake. Koma iwo anakwanitsa kugwila nchitoyo na kukhalabe mabwenzi ake. Nanga anakwanitsa bwanji? Pali mphatso inanso imene inawathandiza.

17, 18. (a) Ni mphatso yanji imene lemba la Yohane 15:16 limachula? (b) Kodi mphatso imeneyo inawathandiza bwanji ophunzila a Yesu? (c) Ni mphatso ziti zimene zimatilimbikitsa masiku ano?

17 Mphatso ya kuyankhidwa kwa mapemphelo. Yesu anati: ‘Ciliconse cimene mungapemphe Atate m’dzina langa adzakupatsani.’ (Yoh. 15:16) Mwacionekele, mau amenewa anawalimbikitsa ngako atumwi. * Pa nthawiyo, Mtsogoleli wawo Khristu anali atatsala pang’ono kuphedwa, koma iwo sanali kumvetsetsa zimenezi. Olo zinali conco, atumwiwo sakanasiyidwa opanda thandizo lililonse. Yehova anali wokonzeka kuyankha mapemphelo awo, na kuwapatsa thandizo lililonse lofunikila kuti akwanitse kugwila nchito yolalikila uthenga wa Ufumu imene anapatsiwa. Ndipo mogwilizana ndi mau a Yesu, posapita nthawi, iwo anadzionela okha mmene Yehova anayankhila mapemphelo awo.—Mac. 4:29, 31.

Timakhulupilila kuti Yehova amayankha mapemphelo athu opempha thandizo (Onani palagilafu 18)

18 Ni mmenenso zilili masiku ano. Pamene tipitiliza kubala zipatso mopilila, timakhala pa ubwenzi na Yesu. Komanso, timakhulupilila kuti Yehova ni wokonzeka kuyankha mapemphelo athu tikamupempha kuti atithandize kupilila mavuto aliwonse amene tingakumane nawo polalikila uthenga wabwino wa Ufumu. (Afil. 4:13) Kukamba zoona, ndise oyamikila ngako kuti mapemphelo athu amayankhidwa, komanso kuti tili na mwayi wokhala pa ubwenzi na Yesu. Mphatso zimenezi zocokela kwa Yehova zimatilimbikitsa kupitiliza kubala zipatso.—Yak. 1:17.

19. (a) N’cifukwa ciani timapitiliza kugwila nchito yolalikila? (b) N’ciani cimatithandiza kupitiliza kugwila nchito ya Mulungu?

19 Monga takambila m’nkhani ino, timapitiliza kugwila nchito yolalikila kuti tilemekeze Yehova na kuyeletsa dzina lake, komanso pofuna kuonetsa kuti timakonda Yehova na Yesu. Cinanso, timalalikila pofuna kucenjeza anthu na kuonetsa kuti timawakonda. Kuwonjezela apo, mphatso ya cimwemwe, mtendele, kukhala pa ubwenzi na Yesu, komanso kuyankhidwa kwa mapemphelo, zimatilimbikitsa kupitiliza kugwila nchito ya Mulungu. Zoonadi, Yehova amakondwela ngako poona kuti tikuyesetsa na mtima wonse ‘kubala zipatso zambili.’

^ par. 17 Pamene Yesu anali kukambilana ndi atumwi ake, anawatsimikizila mobweleza-bweleza kuti Mulungu adzayankha mapemphelo awo.—Yoh. 14:13; 15:7, 16; 16:23.