Kodi Mumamudziwa Bwino Mdani Wanu?

Kodi Mumamudziwa Bwino Mdani Wanu?

“Tikudziwa bwino ziwembu za [Satana].”​2 AKOR. 2:11.

NYIMBO: 150, 32

1. Kodi Yehova anafotokoza zinthu ziti zokhudza mdani wathu m’munda wa Edeni?

N’ZOSAKAYIKITSA kuti Adamu ankadziwa zoti njoka sizilankhula. Choncho ayenera kuti anazindikira kuti pali winawake wauzimu amene anagwiritsa ntchito njokayo polankhula ndi Hava. (Gen. 3:1-6) Adamu ndi Hava sankadziwa chilichonse chokhudza mdani ameneyu. Ngakhale zinali choncho, Adamu anasankha kusamvera Atate wake wachikondi ndipo anagwirizana ndi mdani wosadziwikayo pochita zinthu zosemphana ndi cholinga cha Mulungu. (1 Tim. 2:14) Nthawi yomweyo, Yehova anayamba kuulula za mdani amene anasokoneza Adamu ndi Havayu ndipo analonjeza kuti adzawonongedwa. Koma Yehova anasonyezanso kuti kwa kanthawi ndithu, mdaniyo adzakhala ndi mphamvu zolimbana ndi anthu amene amakonda Mulungu.​—Gen. 3:15.

2, 3. Kodi mwina n’chifukwa chiyani Yehova sanafotokoze zambiri zokhudza Satana, Mesiya asanafike?

2 Popeza Yehova ndi wanzeru, sanatiuze dzina lenileni la mngelo amene anamugalukirayu. * Ndipo Mulungu sanatchulenso dzina limene anapatsidwa loti Satana mpaka panadutsa zaka pafupifupi 2,500 kuchokera pamene anapusitsa anthu oyambirira. (Yobu 1:6) M’Malemba Achiheberi muli mabuku atatu okha amene amatchula dzina loti Satana, lomwe limatanthauza “Wotsutsa.” Mabuku ake ndi 1 Mbiri, Yobu ndi Zekariya. N’chifukwa chiyani Yehova sanafotokoze kwambiri za mdaniyu Mesiya asanafike?

3 Zikuoneka kuti Yehova sankafuna kutchukitsa Satana polola kuti zinthu zambiri zokhudza iyeyo zilembedwe m’Malemba Achiheberi. Cholinga chachikulu chimene anauzira anthu kuti alembe Malembawo chinali kuthandiza anthu kuzindikira Mesiya ndiponso kutsogolera anthu a Mulungu kwa Mesiyayo. (Luka 24:44; Agal. 3:24) Mesiya atafika, Yehova anamugwiritsa ntchito limodzi ndi ophunzira ake kufotokoza zambiri zokhudza Satana komanso angelo amene ali kumbali yake. * Zimenezi n’zomveka chifukwa Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu yemweyo limodzi ndi olamulira anzake kuti aphwanye Satana ndi otsatira ake.​—Aroma 16:20; Chiv. 17:14; 20:10.

4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa kwambiri Mdyerekezi?

4 Mtumwi Petulo anati Satana ndi “mkango wobangula” pomwe Yohane anamufotokoza pogwiritsa ntchito mawu oti “njoka” komanso “chinjoka.” (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:9) Koma sitiyenera kuopa kwambiri Mdyerekezi chifukwa mphamvu zake zili ndi malire. (Werengani Yakobo 4:7.) Ndipo kumbali yathu kuli Yehova, Yesu ndi angelo okhulupirika. Iwo angatithandize kulimbana ndi mdani wathuyu. Komabe tiyenera kupeza mayankho a mafunso atatu ofunika kwambiri awa: Kodi Satana ali ndi mphamvu zotani? Kodi iye amachita bwanji zinthu pofuna kutilamulira? Nanga alibe mphamvu zochita zinthu ziti? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa komanso zimene tikuphunzirapo.

KODI SATANA ALI NDI MPHAMVU ZOTANI?

5, 6. N’chifukwa chiyani maboma a anthu sangathetse mavuto onse a anthu?

5 Angelo ambiri anakhala kumbali ya Satana poukira Mulungu. Chigumula chisanafike, Satana anakopa angelo ena kuti agone ndi akazi padzikoli. Baibulo limatsimikizira zimenezi pofotokoza Satana monga chinjoka chimene chinakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba. (Gen. 6:1-4; Yuda 6; Chiv. 12:3, 4) Pamene angelowo anachoka m’banja la Mulungu, anayamba kulamuliridwa ndi Satana. Koma sikuti angelowa amangokhala ngati gulu la anthu osokoneza basi. Tikutero chifukwa chakuti Satana wakhazikitsa ufumu motsanzira Ufumu wa Mulungu, ndipo iye ndi mfumu yake. Mu ufumu wake wosaonekawu, Satana wakhazikitsanso maboma ndipo waika ziwanda zake kuti zizilamulira.​—Aef. 6:12.

6 Satana amagwiritsa ntchito ufumu wake kuti azilamulira maboma a anthu. Zimenezi zinaonekeratu pamene Satana anaonetsa Yesu “maufumu onse a padziko lapansi” n’kumuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.” (Luka 4:5, 6) Ngakhale kuti Satana amalamulira mabomawa, maboma ambiri amachita zinthu zina zabwino kwa anthu awo. Ndipo olamulira ena amakhala ndi zolinga zabwino. Koma palibe boma la anthu kapena munthu aliyense wolamulira amene angathetse mavuto onse a anthu.​—Sal. 146:3, 4; Chiv. 12:12.

7. Kuwonjezera pa maboma a anthu, kodi Satana amagwiritsanso ntchito bwanji zipembedzo zonyenga komanso mabungwe a zamalonda? (Onani chithunzi choyambirira.)

7 Kuwonjezera pa maboma a anthu, Satana ndi ziwanda zake amagwiritsanso ntchito zipembedzo zonyenga ndiponso mabungwe a zamalonda kuti azisocheretsa “dziko lonse lapansi.” (Chiv. 12:9) Iye amagwiritsa ntchito zipembedzo zonyenga kuti azifalitsa mabodza okhudza Yehova. Zikuoneka kuti amafunitsitsanso kuti anthu aiwale dzina la Mulungu. (Yer. 23:26, 27) Izi zimachititsa kuti anthu omwe akufuna kuchita zabwino aziganiza kuti akulambira Mulungu koma akulambira ziwanda. (1 Akor. 10:20; 2 Akor. 11:13-15) Satana amagwiritsanso ntchito mabungwe a zamalonda kuti azifalitsa mabodza. Mwachitsanzo, mabungwewo amachititsa anthu kuganiza kuti akhoza kukhala osangalala pokhapokha ngati atapeza ndalama komanso zinthu zambiri. (Miy. 18:11) Anthu amene amakhulupirira bodza limeneli, amangokhalira kufunafuna chuma m’malo motumikira Mulungu. (Mat. 6:24) Pakapita nthawi, kukonda chuma kumawasokoneza kwambiri moti amasiyiratu kukonda Mulungu.​—Mat. 13:22; 1 Yoh. 2:15, 16.

8, 9. (a) Kodi nkhani ya Adamu ndi Hava komanso ya angelo oipa imatiphunzitsa mfundo ziwiri ziti? (b) Kodi kudziwa mphamvu zimene Satana ali nazo kumatithandiza bwanji?

8 Nkhani ya Adamu ndi Hava komanso ya angelo oipa imatiphunzitsa mfundo ziwiri zofunika. Choyamba, tiyenera kusankha kukhala kumbali ya Yehova kapena ya Satana ndipo palibe malo a pakati. Munthu akalephera kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndiye kuti amakhala kumbali ya Satana. (Mat. 7:13) Chachiwiri, mapindu amene munthu amapeza akakhala kumbali ya Satana amakhala ochepa. Paja Adamu ndi Hava anapeza mwayi wodzisankhira okha zabwino ndi zoipa ndipo ziwanda zinapatsidwa mphamvu zolamulira maboma a anthu. (Gen. 3:22) Koma mavuto amene munthu angakumane nawo akakhala kumbali ya Satana, nthawi zonse amakhala aakulu kwambiri kuposa mapindu amene angapeze.​—Yobu 21:7-17; Agal. 6:7, 8.

9 Kodi kudziwa mphamvu zimene Satana ali nazo kumatithandiza bwanji? Kumatithandiza kuona moyenera olamulira a m’dzikoli komanso kumatilimbikitsa kugwira mwakhama ntchito yolalikira. Timadziwa kuti Yehova amafuna kuti tizilemekeza maboma. (1 Pet. 2:17) Amafunanso kuti tizimvera malamulo a mabomawa kupatulapo ngati akusemphana ndi malamulo a Mulungu. (Aroma 13:1-4) Koma timadziwa kuti sitiyenera kuchita nawo zandale. Si bwino kukondera chipani chinachake kapena wolamulira winawake. (Yoh. 17:15, 16; 18:36) Popeza timaona kuti Satana akuyesetsa kuipitsa kwambiri dzina la Yehova, timafunitsitsa kuphunzitsa anthu mfundo zoona zokhudza Mulungu wathu. Timanyadira kudziwika ndi dzina lake komanso kuligwiritsa ntchito. Timadziwanso kuti kukonda Mulungu n’kothandiza kwambiri kuposa kukonda ndalama kapena chuma.​—Yes. 43:10; 1 Tim. 6:6-10.

KODI SATANA AMACHITA ZOTANI POFUNA KUTILAMULIRA?

10-12. (a) Kodi Satana ayenera kuti ananyengerera bwanji angelo ena? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira angelo amenewa?

10 Satana ali ndi njira zimene amagwiritsa ntchito pofuna kulamulira anthu ndipo njirazo zimamuthandiza. Mwachitsanzo, nthawi zina amakhala ngati msodzi amene amaperekera nyambo kuti akole nsomba. Koma nthawi zina amaopseza kapena kuzunza anthu n’cholinga choti azimumvera.

11 Satana anagwiritsa ntchito njira yonyengererayi pofuna kukopa angelo kuti akhale kumbali yake ndipo zinatheka. Iye ayenera kuti anayamba n’kuona mmene angelowo ankachitira zinthu kwa nthawi yaitali, kenako n’kupeza njira yowakopera. Angelowo atakopeka n’kukagona ndi akazi padzikoli, anabereka zimphona zimene zinkapondereza anthu. (Gen. 6:1-4) N’kutheka kuti Satana anawanyengerera powauza kuti agone ndi akaziwo komanso kuti akachita zimenezo adzayamba kulamulira anthu. Mwina anachita izi pofuna kusokoneza kubwera kwa ‘mbewu ya mkazi.’ (Gen. 3:15) Kaya zinthu zinalidi choncho kapena ayi, Yehova analepheretsa zolinga zake. Anabweretsa Chigumula chimene chinalepheretsa mapulani a Satana ndi ziwanda zakezo.

Satana amatinyengerera pogwiritsa ntchito msampha wa chiwerewere, kudzikuza ndiponso kukhulupirira mizimu (Onani ndime 12, 13)

12 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Tiyenera kusamala kwambiri ndi msampha wa chiwerewere komanso kudzikuza. Tizikumbukira kuti angelo amene anapusitsidwa ndi Satana anatumikira pamaso pa Mulungu kwa zaka zambirimbiri. Koma ngakhale kuti ankakhala pafupi ndi Mulungu, iwo analola kuti maganizo oipa akhazikike komanso akule mumtima mwawo. Mwina nafenso tatumikira kwa zaka zambiri m’gulu la Yehova. Koma ngakhale tili m’gulu momwemu, maganizo oipa akhoza kuyamba n’kukula m’mitima yathu. (1 Akor. 10:12) Choncho tiyenera kudzifufuza moona mtima n’kumachotseratu maganizo achiwerewere komanso odzikuza.​—Agal. 5:26; werengani Akolose 3:5.

13. Kodi Satana amagwiritsanso ntchito chiyani popusitsa anthu, nanga tingapewe bwanji msampha umenewu?

13 Satana amapusitsanso anthu pogwiritsa ntchito nkhani zokhudza kukhulupirira mizimu. Amagwiritsa ntchito zipembedzo zonyenga komanso zinthu zosangalatsa pofuna kuti anthu azichita chidwi ndi ziwanda. Zinthu monga mafilimu ndi masewera apakompyuta zimachititsa kuti anthu azisangalala ndi zamatsenga. Kodi tingapewe bwanji msampha umenewu? Sitingayembekezere kuti gulu la Yehova lizitipatsa mndandanda wa zosangalatsa zoyenera ndi zosayenera. Aliyense ayenera kuphunzitsa chikumbumtima chake kuti azisankha zinthu mogwirizana ndi mfundo za Mulungu. (Aheb. 5:14) Tikhoza kusankha zinthu mwanzeru tikamatsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti ‘chikondi chathu chisakhale cha chiphamaso.’ (Aroma 12:9) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda zingandichititse kukhala munthu wachinyengo? Ngati anthu amene ndimawalalikira ataona zinthu zimene ndimasangalala nazo, kodi angaganize kuti ndimatsatira zimene ndimaphunzitsa?’ Zochita zathu zikamagwirizana ndi zolankhula zathu tikhoza kupewa misampha ya Satana.​—1 Yoh. 3:18.

Satana amatiopseza pochititsa kuti maboma aletse ntchito yathu, anzathu akusukulu azitivutitsa komanso kuti achibale azititsutsa (Onani ndime 14)

14. Kodi Satana angagwiritse ntchito njira ina iti kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova, nanga n’chiyani chingatithandize?

14 Kuwonjezera pa kunyengerera anthu, nthawi zina Satana amaopseza anthu kapena kuwazunza kuti asiye kukhala okhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, angachititse kuti maboma aletse ntchito yathu yolalikira. Apo ayi akhoza kuchititsa anzathu akuntchito kapena kusukulu kuti azitinyoza chifukwa choti timatsatira mfundo za m’Baibulo. (1 Pet. 4:4) Akhozanso kuchititsa kuti achibale athu azitiletsa kupita kumisonkhano. (Mat. 10:36) Kodi n’chiyani chingatithandize ngati zimenezi zitatichitikira? Choyamba, sitiyenera kudabwa ndi zimenezi chifukwa Baibulo limasonyeza kuti Satana akulimbana nafe. (Chiv. 2:10; 12:17) Chachiwiri, tiyenera kukumbukira nkhani yaikulu. Paja Satana amanena kuti anthufe timatumikira Yehova pokhapokha ngati zinthu zikutiyendera bwino. Iye amanena kuti tikhoza kusiya kumutumikira ngati tapanikizika ndi zinazake. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Pomaliza, tiyenera kudalira Yehova kuti azitithandiza. Tizikumbukira lonjezo lake lakuti sadzatisiya ngakhale pang’ono.​—Aheb. 13:5.

KODI SATANA ALIBE MPHAMVU YOCHITA ZINTHU ZITI?

15. Kodi Satana angatikakamize kuchita zimene sitikufuna? Fotokozani.

15 Satana sangatikakamize kuchita zimene sitikufuna. (Yak. 1:14) M’dzikoli anthu ambiri amachita zofuna za Satana mosazindikira. Koma akaphunzira mfundo za m’Baibulo, amasankha amene akufuna kumutumikira, kaya ndi Yehova kapena Satana. (Mac. 3:17; 17:30) Ngati tatsimikiza mumtima mwathu kuti tizimvera Yehova, palibe zimene Satana angachite kuti atilepheretse.​—Yobu 2:3; 27:5.

16, 17. (a) Kodi Satana ndi ziwanda alibe mphamvu yochita zinthu ziti? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa kupemphera mokweza kwa Yehova?

16 Koma pali zinthu zinanso zimene Satana ndi ziwanda zake sangathe kuchita. Mwachitsanzo, palibe paliponse m’Malemba pamene pamasonyeza kuti iwo angathe kuzindikira zimene zili m’maganizo kapena mumtima mwa munthu. Koma Malemba amasonyeza kuti Yehova ndi Yesu ndi amene angathe kuchita zimenezi. (1 Sam. 16:7; Maliko 2:8) Nanga bwanji pa nkhani ya kulankhula kapena kupemphera mokweza. Kodi tiyenera kuopa kuti Satana ndi ziwanda angamve zimene tikunena m’pemphero n’kusokoneza zimene tikufuna? Ayi. Tikutero chifukwa choti sitisiya kuchita zinthu zabwino potumikira Yehova poopa kuti Mdyerekezi angatione. N’chimodzimodzi ndi nkhani yopemphera mokweza. M’Baibulo muli zitsanzo za atumiki a Mulungu amene anapemphera mokweza ndipo Baibulolo silisonyeza kuti pali amene ankaopa kuti Mdyerekezi angamve zimene akunena. (1 Maf. 8:22, 23; Yoh. 11:41, 42; Mac. 4:23, 24) Tikamayesetsa kulankhula komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna, tizidziwa kuti Yehova sangalole kuti Satana atibweretsere mavuto amene sangathetsedwe.​—Werengani Salimo 34:7.

17 Ndi zoona kuti tiyenera kudziwa bwino mdani wathu koma sitiyenera kumuopa. Ngakhale anthu amene si angwiro akhoza kugonjetsa Satana akamathandizidwa ndi Yehova. (1 Yoh. 2:14) Tikamatsutsa Mdyerekezi, adzatithawa. (Yak. 4:7; 1 Pet. 5:9) Komatu Satana amapezerera kwambiri achinyamata. Ndiye kodi achinyamatawo angatani kuti Satana asawagonjetse? Munkhani yotsatira tidzakambirana yankho la funso limeneli.

^ ndime 2 Baibulo limasonyeza kuti angelo ena ali ndi mayina awo enieni. (Ower. 13:18; Dan. 8:16; Luka 1:19; Chiv. 12:7) Koma popeza Yehova amatchula dzina nyenyezi iliyonse, (Sal. 147:4) n’zomveka kunena kuti angelo onse, kuphatikizapo amene anadzakhala Satana, ali ndi mayina.

^ ndime 3 Dzina lakuti Satana limatchulidwa maulendo 18 okha m’Malemba Achiheberi koma m’Malemba Achigiriki limatchulidwa maulendo oposa 30.