Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Msonkhano wacigawo ku Nyzhnya Apsha, Ukraine, 2012

Zokolola Zoculuka!

Zokolola Zoculuka!

YESU anakambilatu kuti otsatila ake adzakolola zokolola zoculuka m’nthawi ya mapeto ino. (Mat. 9:37; 24:14) Onani mmene mau ake akwanilitsidwila mocititsa cidwi m’dela la Transcarpathia, ku Ukraine. M’matauni atatu cabe a m’delali, muli mipingo 50 na ofalitsa oposa 5,400. * Inde, n’zocititsa cidwi kuona kuti pa anthu 4 alionse m’matauni amenewa, mmodzi ni Mboni ya Yehova.

Kodi gawo lake n’lotani? M’bale wina wa kumeneko, dzina lake Vasile, anati: “Anthu a kuno amalemekeza Baibo, amakonda cilungamo, ali na mabanja ogwilizana, komanso amayesetsa kuthandizana.” Anakambanso kuti: “Sikuti nthawi zonse amagwilizana ndi ziphunzitso zathu. Koma ukawalongoza mfundo inayake m’Baibo, amamvetsela mwachelu.”

Komabe, abale na alongo athu amene amalalikila m’madela okhala na Mboni zambili conco amakumana na mavuto ena apadela. Mwacitsanzo, mpingo wina uli na ofalitsa 134, koma gawo lawo lili cabe na nyumba 50. Kodi ofalitsa amacita bwanji na vuto limeneli la kucepa kwa gawo?

Abale na alongo ambili amadzipeleka kukalalikila ku madela kumene kuli ofalitsa ocepa. M’bale wina wa zaka 90, dzina lake Ionash, anati: “Gawo la mpingo wathu n’locepa ngako cakuti wofalitsa mmodzi amagaŵilidwa nyumba ziŵili cabe zolalikilamo. Lomba nimalalikila m’mudzi mwathu. Koma pamene thanzi yanga inali bwino n’nali kupitanso kukalalikila ku gawo lopanda ofalitsa, limene lili pa mtunda wa makilomita 160. Kumeneko, n’nali kulalikila m’citundu ca Cihangare.” Ofalitsa amafunika kukhala na mtima wodzipeleka kuti akwanitse kukalalikila ku magawo ena. M’bale Ionash anati: “Kuti nipeze sitima, n’nali kuuka 04:00hrs kuseni-seni, ndipo n’nali kulalikila mpaka 18:00hrs, nthawi imene sitima inali kubwelela kwathu. N’nali kucita izi kaŵili kapena katatu pa wiki.” Kodi khama lake linabweletsa mapindu anji? Iye anati: “N’napeza cimwemwe cacikulu mu utumiki umenewu. N’nakhala na mwayi wothandiza banja lina kuphunzila coonadi m’gawo limene kunalibe mpingo.”

N’zoona kuti si aliyense m’mipingo ya m’delali amene amakwanitsa kuyenda misenga itali-itali kukalalikila. Koma onse, kuphatikizapo ofalitsa okalamba, amayesetsa kulalikila paliponse m’gawo la mpingo wawo. Zotulukapo zake n’zakuti, mu 2017, anthu amene anapezeka pa Cikumbutso m’matauni atatu amenewa anali ambili kuŵilikiza kaŵili ciŵelengelo ca ofalitsa, kapena kuti hafu ya anthu onse a m’matauniwa. Zoonadi, kaya titumikila ku dela liti, tikali na “zocita zambili . . . mu nchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.

^ par. 2 Matauni amenewo ni Hlybokyy Potik, Serednye Vodyane, na Nyzhnya Apsha.