Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumafuna Kukhala Wodziŵika kwa Ndani?

Kodi Mumafuna Kukhala Wodziŵika kwa Ndani?

“Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake.”—AHEB. 6:10.

NYIMBO: 39, 30

1. Kodi mwacibadwa, ise tonse timafuna ciani? Nanga zimenezo ziphatikizapo ciani?

KODI mumamvela bwanji ngati munthu amene mumam’dziŵa na kum’lemekeza waiŵala dzina lanu, kapena ngati wakamba kuti sakudziŵani? Zingakhale zovutitsa maganizo. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti mwacibadwa, ise tonse timafuna kuti anthu ena azitidziŵa. Izi zimaphatikizapo zambili osati kudziŵa cabe dzina lathu. Timafunanso kuti azidziŵa kuti ndise anthu abwanji na kuti tacita zotani mu umoyo wathu.—Num. 11:16; Yobu 31:6.

2, 3. Kodi cilako-lako cofuna kukhala wodziŵika kwa ena cingatisoceletse bwanji? (Onani pikica pamwambapa.)

2 Mofanana na zilako-lako zina zacibadwa zimene tili nazo, cilako-lako cofuna kukhala wodziŵika kwa ena cingatisoceletse. Izi zingacitike cifukwa ndise opanda ungwilo. Tingayambe kudzifunila ulemu wopambanitsa. Dziko la Satanali limasonkhezela anthu kukhala na mtima wofuna kuchuka na kulemekezedwa kwambili, m’malo mopeleka ulemelelo kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, amene ndiye woyenela kulambilidwa na kulandila ulemelelo.—Chiv. 4:11.

3 M’nthawi ya Yesu, atsogoleli ena acipembedzo anali na mtima wofuna kukhala odziŵika kwambili kwa ena. Yesu anacenjeza otsatila ake kuti: “Cenjelani ndi alembi. Iwo amakonda kuyendayenda atavala mikanjo. Amakonda kupatsidwa moni m’misika ndi kukhala m’mipando yakutsogolo [kapena kuti “yapamwamba”] m’masunagoge. Amakondanso malo olemekezeka kwambili pa cakudya camadzulo.” Kenako Yesu anati: “Anthu amenewa adzalandila ciweluzo camphamvu.” (Luka 20:46, 47) Mosiyana ndi zimenezi, Yesu anayamikila mkazi wamasiye wosauka, amene anapeleka copeleka cocepa kwambili, cimene mwina ena sanacione ngati kanthu. (Luka 21:1-4) Conco, pa nkhani ya kukhala wodziŵika kwa ena, Yesu anali na maganizo osiyana kwambili ndi a anthu ena. Nkhani ino idzatithandiza kukhala na maganizo oyenela, amene Yehova Mulungu amavomeleza, pa nkhani yofuna kukhala wodziŵika kwa ena.

KODI COFUNIKA KWAMBILI N’KUKHALA WODZIŴIKA KWA NDANI?

4. Kodi cofunika kwambili ni kukhala wodziŵika kwa ndani? Nanga n’cifukwa ciani zili conco?

4 Kodi cofunika kwambili ni kuyesetsa kukhala wodziŵika kwa ndani? Anthu m’dzikoli amafuna kukhala odziŵika kwambili kwa ena pa zamaphunzilo, bizinesi, kapena pa zamaseŵela. Koma ise timafuna kukhala odziŵika kwa Mulungu, monga mmene Paulo anakambila, pamene anati: “Tsopano pamene mwadziŵa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano pamene mwadziŵidwa ndi Mulungu, mukubwelelanso bwanji ku mfundo zacibwanabwana, zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake, n’kumafuna kukhalanso akapolo ake?” (Agal. 4:9) Ndithudi! Ni mwayi waukulu kwambili ‘kudziŵidwa ndi Mulungu,’ Wolamulila Wamkulu wa cilengedwe conse. Iye ni wokonzeka kupanga ubwenzi wabwino na ise. Monga mmene katswili wina anakambila, tikakhala mabwenzi ake, iye “amationa kukhala ofunika kwambili na kutikonda.” Komanso, tikakhala mabwenzi a Yehova, m’pamene timaona kuti umoyo wathu uli na phindu.—Mlal. 12:13, 14.

5. Tingacite ciani kuti Mulungu atidziŵe?

5 Mose ni mmodzi mwa anthu amene anadalitsidwa mwanjila imeneyi. Nthawi ina, pamene iye anapempha Yehova kuti amuthandize kudziŵa bwino njila zake, Yehova anamuyankha kuti: “Ndidzacita izinso zimene wanena, cifukwa ndakukomela mtima ndipo ndikukudziŵa bwino, ndi dzina lako lomwe.” (Eks. 33:12-17) Na ise tingalandile madalitso ambili ngati Yehova amatidziŵa bwino. Koma kodi tingacite ciani kuti iye atidziŵe? Tiyenela kumukonda na kudzipatulila kwa iye.—Ŵelengani 1 Akorinto 8:3.

6, 7. N’ciani cingaticititse kuwononga ubwenzi wathu na Yehova?

6 Koma tifunika kusungabe ubwenzi wathu wamtengo wapatali na Atate wathu wakumwamba. Mofanana ndi Akhristu a ku Galatiya amene Paulo anawalembela kalata, na ise tifunika kupewa kukhala akapolo a zinthu “zacibwanabwana, zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake” za m’dzikoli. Izi zingaphatikizepo mtima wofuna kutamandidwa na ena. (Agal. 4:9) Akhristu a m’nthawi ya atumwi amenewo, anali atapita kale patsogolo mwauzimu mpaka kufika pokhala odziŵika kwa Mulungu. Komabe, Paulo anakamba kuti abalewo anayamba ‘kubwelelanso’ ku zinthu zopanda pake. Zili ngati kuti Paulo anali kuwauza kuti: “Anthu inu mwapita kale patsogolo, nanga n’cifukwa ciani mukubwelelanso ku zinthu zacabecabe zimene munasiya m’mbuyo?”

7 Kodi na ise zaconco zingaticitikile? Inde. Pamene tinadziŵa Yehova, ise mofanana ndi Paulo, tinasiya zinthu zina zimene zikanaticititsa kukhala wodziŵika kwambili m’dziko la Satanali. (Ŵelengani Afilipi 3:7, 8.) Mwina tinali na mwayi wocita maphunzilo apamwamba, wokwezedwa pa nchito, kapena wopeza ndalama zambili pocita bizinesi inayake. Mwinanso tinali na luso la zoimbaimba kapena la zamaseŵela, limene likanaticititsa kukhala wochuka komanso wolemela m’dzikoli. Koma zonsezo tinazisiya. (Aheb. 11:24-27) Kukamba zoona, kungakhale kupanda nzelu kuyamba kuganiza kuti ‘tinataya mwayi.’ Maganizo aconco angapangitse kuti tiyambenso kufuna-funa zinthu za m’dzikoli, zimene tinaziona kale kuti ‘n’zacibwanabwana ndi zosathandiza.’ *

KHALANI WOFUNITSITSA KUKHALA WODZIŴIKA KWA YEHOVA

8. N’ciani cingatithandize kukhala na mtima wofunitsitsa kudziŵika kwa Yehova?

8 N’ciani cingatithandize kukhala na mtima wofunitsitsa kudziŵika kwa Yehova osati ku dziko? Tiyenela kukumbukila mfundo ziŵili zofunika kwambili. Yoyamba, Yehova nthawi zonse amadziŵa anthu amene amam’tumikila mokhulupilika. (Ŵelengani Aheberi 6:10; 11:6.) Iye amayamikila zimene mtumiki wake aliyense amacita, ndipo amaona kuti kunyalanyaza atumiki ake okhulupilika kungakhale kupanda cilungamo. Malemba amati, Yehova “amadziŵa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Iye “amadziŵa njila za olungama,” komanso amawapulumutsa akakhala pa mayeselo.”—Sal. 1:6; 2 Pet. 2:9.

9. Fotokozani zitsanzo za mmene Yehova waonetsela kuti amawayanja anthu ake.

9 Kale, nthawi zina Yehova anali kucita zozizwitsa pofuna kuonetsa kuti anthu ake amawayanja. (2 Mbiri 20:20, 29) Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yehova anapulumutsila anthu ake pa Nyanja Yofiila pamene anali kuthamangitsidwa na asilikali amphamvu a Farao. (Eks. 14:21-30; Sal. 106:9-11) Zimene zinacitikazo zinali zodabwitsa kwambili cakuti ngakhale pambuyo pa zaka 40, anthu anali kukambabe za cocitikaco. (Yos. 2:9-11) Zocitika zimenezi zimaonetsa kuti Yehova ali na mphamvu ndipo amatikonda. Kukumbukila zocitika ngati zimenezi n’kolimbikitsa ngako pamene tikuyang’anizana ndi kuukila kwa Gogi wa Magogi, kumene Malemba anakambilatu. (Ezek. 38:8-12) Pa nthawiyo, tidzakhala wokondwa kwambili podziŵa kuti tinayesetsa kukhala wodziŵika kwa Mulungu osati ku dzikoli.

10. Ni mfundo iti imene tifunika kukumbukila pa nkhani ya kukhala wodziŵika kwa Yehova?

10 Tifunikanso kukumbukila mfundo yaciŵili yofunika kwambili yakuti, Yehova angaonetse kuti amatidziŵa mwa kuticitila zinthu zimene sitinali kuyembekezela. Malemba amaonetsa kuti anthu amene amacita zabwino n’colinga cakuti anthu ena awaone, sadzalandila mphoto iliyonse yocokela kwa Yehova. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anthu akawatamanda, ndiye kuti akulandililatu mphoto yawo yonse. (Ŵelengani Mateyu 6:1-5.) Koma Yesu anakamba kuti Atate ŵake amayang’ana anthu amene amacitila anzawo zabwino, olo kuti anthu ena sanaone. Akaona zimene acita, amawadalitsa mogwilizana ndi nchito zawozo. Komabe, nthawi zina Yehova amatidalitsa m’njila imene sitinali kuyembekezela. Tiyeni tikambilane zitsanzo zingapo.

MTSIKANA WODZICEPETSA ANADALITSIDWA M’NJILA YAPADELA

11. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anali kuona zimene Mariya anali kucita?

11 Pamene nthawi inafika yakuti Mwana wa Mulungu abadwe monga munthu, Yehova anasankha namwali wodzicepetsa Mariya, kuti adzakhale mayi wa mwana wapadela ameneyu. Mariya anali kukhala mu mzinda waung’ono wa Nazareti, kutali na Yerusalemu na kacisi wake waulemelelo. (Ŵelengani Luka 1:26-33.) N’cifukwa ciani Mulungu anasankha Mariya kuti adzakhale mayi wa Yesu? Mngelo Gabirieli anauza Mariyayo kuti Mulungu ‘anamukomela mtima.’ Patapita nthawi, zimene Mariya anakamba kwa wacibale wake Elizabeti zionetsa kuti anali munthu wauzimu kwambili. (Luka 1:46-55) Zoonadi, Yehova anali kuona zimene Mariya anali kucita, ndipo cifukwa ca kukhulupilika kwake anam’patsa mwayi wapadela umene sanali kuuyembekezela.

12, 13. Kodi Yesu analemekezedwa bwanji pa nthawi ya kubadwa kwake komanso pamene anapita naye ku kacisi pambuyo pa masiku 40?

12 Mariya atabeleka Yesu, Yehova sanapatse mtsogoleli aliyense wochuka kapena olamulila a mu Yerusalemu ndi Betelehemu mwayi wodziŵa za kubadwa kwa Yesu. Koma angelo anaonekela kwa abusa amene anali kuŵeta nkhosa kuchile, kunja kwa Betelehemu. (Luka 2:8-14) Kenako, abusawo anapita kukaona mwanayo. (Luka 2:15-17) Mariya na Yosefe ayenela kuti anakondwela kwambili kuona Yesu akulemekezedwa mwanjila imeneyi. Koma onani kusiyana pakati pa mmene Yehova amacitila zinthu na mmene Mdyelekezi amacitila. Satana atatuma openda nyenyezi kuti akaone Yesu na makolo ake, Yerusalemu yense anagwedezeka anthu atamva za kubadwa kwa Yesu. (Mat. 2:3) Nkhani ya kubadwa kwa Yesu inafala kwambili. Ndipo izi zinacititsa kuti ana ambili osalakwa aphedwe.—Mat. 2:16.

13 Pambuyo pa masiku 40 Yesu atabadwa, Mariya anapita ku kacisi ku Yerusalemu kukapeleka nsembe kwa Yehova. Uwu unali ulendo wa makilomita 9 kucokela ku Betelehemu. (Luka 2:22-24) Pamene Mariya anali kupita ku kacisi pamodzi na Yosefe komanso Yesu, mwina anali kuganiza kuti akafika kumeneko, wansembe adzakamba mau ena ake oonetsa kuti anali kudziŵa udindo umene Yesu adzakhala nawo m’tsogolo. Iwo atafika ku kacisiko, Yesu analemekezedwadi mwapadela. Koma zimene zinacitika mwina zinali zosiyana na zimene Mariya anali kuyembekezela. Yehova anaseŵenzetsa Simiyoni, mwamuna “wolungama ndi woopa Mulungu,” komanso mneneli Anna, mkazi wamasiye wa zaka 84, potsimikizila kuti Yesu adzakhala Mesiya wolonjezedwa, kapena kuti Khristu.—Luka 2:25-38.

14. Kodi Yehova anam’dalitsa bwanji Mariya?

14 Nanga bwanji Mariya? Kodi Yehova anam’dalitsa bwanji cifukwa colela Mwana wake mokhulupilika? Mulungu anaonetsetsa kuti mau na zocita zake zalembedwa m’Baibo. Cioneka kuti zinali zosatheka kwa Mariya kuyenda na Yesu mu utumiki wake wa zaka zitatu na hafu. Mariya anatsala ku Nazareti, mwina cifukwa cakuti anali mayi wamasiye. Mwa ici, iye sanakhale na mwayi woona zocitika zambili zocititsa cidwi zimene ena anaona. Olo zinali conco, anakwanitsa kupezekapo pa nthawi ya imfa ya Yesu. (Yoh. 19:26) Patapita nthawi, Mariya anapezeka ku Yerusalemu pamodzi na ophunzila ena, patatsala masiku angapo kuti ophunzilawo adzozedwe na mzimu woyela pa Pentekosite. (Mac. 1:13, 14) Mwacionekele, nayenso anadzozedwa pamodzi na ophunzila ena amene analipo. Ngati zinalidi conco, ndiye kuti iye anapatsidwa mwayi wokakhala na Yesu kumwamba kwamuyaya. Ndithudi! Yehova anam’dalitsa kwambili Mariya cifukwa com’tumikila mokhulupilika.

YEHOVA ANAONETSA KUTI ANALI KUM’DZIŴA MWANA WAKE

15. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anali kumuyanja?

15 Yesu sanali kulakalaka kulemekezedwa na atsogoleli acipembedzo kapena andale a m’nthawi yake. Koma iye ayenela kuti analimbikitsidwa ngako pamene Yehova anakamba mau katatu konse kucokela kumwamba oonetsa kuti anali kumudziŵa. Koyamba, Yesu atangobatizika mu mtsinje wa Yorodano, Yehova anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.” (Mat. 3:1-17) Mwacidziŵikile, kuwonjezela pa Yesu, Yohane M’batizi yekha ndiye anamvako mau amenewa. Kaciŵili, patatsala pafupi-fupi caka cimodzi kuti Yesu aphedwe, ophunzila ake atatu anamva Yehova akukamba za Yesu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwela naye, muzimumvela.” (Mat. 17:5) Kothela, patangotsala masiku oŵelengeka kuti Yesu aphedwe, Yehova anakambanso naye kucokela kumwamba.—Yoh. 12:28.

Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Yehova anaonetsela kuti anali kum’dziŵa Mwana wake na mmene anamudalitsila? (Onani palagilafu 15-17)

16, 17. Kodi Yehova anam’dalitsa bwanji Yesu m’njila yapadela?

16 Yesu anali kudziŵa kuti anthu adzamunamizila kuti ni munthu wonyoza Mulungu. Anali kudziŵanso kuti adzafa imfa yonyozeka. Olo zinali conco, iye anapemphela kuti cifunilo ca Yehova cicitike osati cake. (Mat. 26:39, 42) Yesu “anapilila mtengo wozunzikilapo,” ndipo “sanasamale kuti zocititsa manyazi zimucitikila.” Iye sanafune kukhala wodziŵika m’dzikoli, koma anafuna kukhala wodziŵika kwa Atate wake. (Aheb. 12:2) Kodi Yehova anam’dalitsa bwanji?

17 Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu anakamba kuti anali kulakalaka kukhalanso na ulemelelo umene anali nawo poyamba, pamene anali ndi Atate wake kumwamba. (Yoh. 17:5) Palibe cimene cionetsa kuti iye anali kuyembekezela zoposa pamenepa. Iye sanali kuyembekezela kukwezedwa pa udindo, titelo kukamba kwake. Koma kodi Yehova anacita ciani? Anam’dalitsa Yesu m’njila imene iye sanali kuyembekezela. Anamuukitsa n’kumuika “pamalo apamwamba” ndipo anamupatsa cinthu cimene aliyense anali asanalandilepo. Anamupatsa moyo wosafa. * (Afil. 2:9; 1 Tim. 6:16) Zoonadi! Pamenepa Mulungu anaonetsa m’njila yapadela kwambili kuti anayamikila utumiki wokhulupilika wa Yesu.

18. N’ciani cingatithandize kupewa mtima wofuna kuyanjidwa na dzikoli?

18 N’ciani cingatithandize kupewa mtima wofuna kuyanjidwa na dzikoli? Tizikumbukila kuti Yehova nthawi zonse amadziŵa atumiki ake okhulupilika, komanso kuti nthawi zambili amawadalitsa m’njila imene iwo sanali kuyembekezela. Na ise sitingadziŵe madalitso onse amene Yehova adzatipatsa m’tsogolo. Koma pali pano, pamene tikupilila mavuto na mayeselo m’dziko loipali, tiyeni nthawi zonse tizikumbukila kuti dzikoli na ulemelelo umene limapeleka, zikupita. (1 Yoh. 2:17) Atate wathu wakumwamba, Yehova, ‘si wosalungama woti angaiwale nchito yathu ndi cikondi cimene timacisonyeza pa dzina lake.’ (Aheb. 6:10) Ndipo iye adzationetsa kukoma mtima kwake, mwina ngakhale m’njila imene sitinali kuyembekezela.

^ par. 7 M’ma Baibo ena, liu limene linamasulidwa kuti “zosathandiza,” analimasulila kuti “zacabecabe,” “zopanda phindu,” na “zotha nchito.”

^ par. 17 Mwina Yesu sanali kuyembekezela kulandila mphatso imeneyi cifukwa cakuti moyo wosafa suchulidwako paliponse m’Malemba Aciheberi.