Kodi Maso Anu Amayang’ana kwa Ndani?
“Ndakweza maso anga kuyang’ana inu, kuyang’ana inu amene mukukhala kumwamba.”—SAL. 123:1.
1, 2. Kodi kuyang’ana kwa Yehova kumaphatizikizapo kucita ciani?
TIKUKHALA m’nthawi “yapadela komanso yovuta,” ndipo mavuto adzapitiliza kuwonjezeka mpaka pamene Yehova adzawononga dziko loipali na kubweletsa mtendele weni-weni. (2 Tim. 3:1) Conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimayang’ana kwa ndani nikafuna thandizo na citsogozo?’ Mwacionekele, tingayankhe kuti, “Kwa Yehova,” ndipo imeneyi ni yankho yabwino.
2 Kodi kuyang’ana kwa Yehova kumaphatikizapo ciani? Nanga tingacite ciani kuti maso athu akhalebe pa iye pamene takumana na mavuto aakulu mu umoyo wathu? Zaka zambili m’mbuyomo, wamasalimo anakamba kuti tifunika kuyang’ana kwa Yehova pamene tifuna thandizo. (Ŵelengani Salimo 123:1-4.) Iye anayelekezela kuyang’ana kwa Yehova na mmene mtumiki amayang’anila kwa mbuye wake. Kodi wamasalimo anatanthauza ciani pamenepa? Mtumiki amayang’ana kwa mbuye wake kuti am’patse cakudya na kum’teteza. Komanso amafuna kudziŵa zimene mbuye wakeyo afuna kuti iye acite, ndipo akadziŵa amacita zimenezo. Mofananamo, tifunika kuphunzila Mau a Mulungu tsiku lililonse kuti tidziŵe zimene Yehova afuna kuti ticite. Ndipo tikadziŵa, tifunika kucita zimenezo. Tikatelo, m’pamene Yehova adzatikomela mtima tikafuna thandizo.—Aef. 5:17.
3. N’ciani cimene cingatilepheletse kupitiliza kuyang’ana kwa Yehova?
3 Timadziŵa kuti kuyang’ana kwa Yehova nthawi zonse n’kofunika. Komabe, nthawi zina zinthu zina zingaticenjeneke. Izi n’zimene zinacitikila bwenzi la Yesu, Marita. Iye “anatanganidwa ndi nchito zoculuka.” (Luka 10:40-42) Ngati munthu wokhulupilika Marita anatangwanika na zinthu zina pamene Yesu analipo, ndiye kuti na ise zaconco zingaticitikile. Kodi n’ciani cingatilepheletse kuikabe maso athu pa Yehova? M’nkhani ino, tidzakambilana mmene zocita za ena zingatilepheletsele kuyang’anabe kwa Yehova. Tidzaphunzilanso zimene tingacite kuti tipitilizebe kuyang’ana kwa Yehova.
MWAMUNA WOKHULUPILIKA ANATAYA MWAYI
4. N’cifukwa ciani tingadabwe kuti Mose anataya mwayi woloŵa m’Dziko Lolonjezedwa?
4 Mose anali kukonda kuyang’ana kwa Yehova kuti am’patse malangizo. Baibo imati iye “anapitiliza kupilila moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Ŵelengani Aheberi 11:24-27.) Komanso Malemba amati “mu Isiraeli simunakhalebe mneneli aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova anali kumudziwa pamasom’pamaso.” (Deut. 34:10) Olo kuti Mose anali pa ubwenzi wolimba na Yehova, iye anataya mwayi woloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:12) Kodi n’ciani cinacititsa kuti ataye mwayi umenewu?
5-7. N’ciani cinacitika Aisiraeli atangotuluka kumene mu Iguputo? Nanga Mose anacita ciani pa cocitikaco?
5 Pasanathe miyezi iŵili kucokela pamene Aisiraeli anacoka ku Iguputo, komanso asanafike ngakhale pa Phiri la Sinai, pakati pawo panabuka vuto lalikulu. Anthuwo anayamba kudandaula cifukwa ca kusowa kwa madzi. Iwo anayamba kudandaulila Mose, ndipo vutolo linakula kwambili cakuti Mose anafuulila Yehova kuti: “Nditani nawo anthuwa? Angotsala pang’ono kundiponya miyala!” (Eks. 17:4) Poona zimenezi, Yehova anapatsa Mose malangizo omveka bwino. Anamuuza kuti atenge ndodo yake na kukamenya thanthwe ku Horebe, kuti madzi akatuluke m’thanthwelo. Nkhaniyo imati: “Mose anacitadi zomwezo, pamaso pa akulu a Isiraeli.” Aisiraeli anamwa madzi, ndipo vuto la kusoŵa madzi linatha.—Eks. 17:5, 6.
6 Nkhani youzilidwa imeneyi imakamba kuti Mose “anacha malowo Masa ndi Meriba, cifukwa ana a Isiraeli anakangana ndi Mose, komanso cifukwa ca kuyesa Yehova kuti: ‘Kodi pakati pathu pano, Yehova alipo kapena ayi?’” (Eks. 17:7) Maina amenewa anali oyenelela cifukwa amatanthauza “Kuyesa” ndi “Kukangana.”
7 Kodi Yehova anamva bwanji na zimene zinacitika ku Meriba? Iye anaona kuti zimene Aisiraeli anacita kunali kum’pandukila komanso kutsutsa ulamulilo wake, osati kutsutsa Mose cabe. (Ŵelengani Salimo 95:8, 9.) Zimene Aisiraeli anacita zinali zolakwika kwambili. Pa cocitikaco, Mose anacita zinthu mwanzelu mwa kuyang’ana kwa Yehova na kutsatila malangizo ake mosamala.
8. Ni vuto lanji limene linabuka pakati pa Aisiraeli cakumapeto kwa ulendo wawo wa zaka 40 wa m’cipululu?
8 Koma patapita zaka 40, vuto lofanana ndi limeneli linabukanso pakati pa Aisiraeli, cakumapeto kwa ulendo wawo wa m’cipululu. Kodi n’ciani cinacitika pa nthawiyo? Aisiraeli anafika pa malo amene pambuyo pake anachedwanso Meriba. Koma awa * Kumeneko, Aisiraeli anayambanso kudandaula cifukwa cosoŵa madzi. (Num. 20:1-5) Koma panthawiyi, zinthu sizinamuyendele bwino Mose.
anali malo ena, a kufupi na ku Kadesi, kumalile na Dziko Lolonjezedwa.9. Kodi Yehova anam’patsa malangizo anji Mose? Nanga iye anacita ciani? (Onani pikica kuciyambi.)
9 Kodi Mose anacita ciani Aisiraeli atapanduka pa nthawiyi? Molingana ndi poyamba paja, iye anayang’ananso kwa Yehova kuti am’patse malangizo. Koma pa nthawiyi, Yehova sanamuuze kuti amenye thanthwe. Anamuuza kuti atenge ndodo yake, asonkhanitse anthu pafupi na thanthwe, na kukamba nalo thanthwelo kuti litulutse madzi. (Num. 20:6-8) Koma Mose sanakambe nalo thanthwelo. M’malomwake, mwaukali anauza anthuwo kuti: “Tsopano tamvelani anthu opanduka inu! Kodi ticite kukutulutsilani madzi m’thanthweli?” Ndiyeno anamenya thanthwelo, osati kamodzi cabe koma kaŵili.—Num. 20:10, 11.
10. Kodi Yehova anamvela bwanji na zimene Mose anacita?
10 Yehova anamukwiyila kwambili Mose. (Deut. 1:37; 3:26) N’cifukwa ciani anakwiya? Payenela kukhala zifukwa zingapo. Monga takambila m’ndime yapita, mwina Yehova anakwiya cifukwa Mose sanatsatile malangizo atsopano amene anapatsiwa.
11. N’cifukwa ciani tingakambe kuti pamene Mose anamenya thanthwe, mwina anacititsa Aisiraeli kukayikila kuti Yehova wacita cozizwitsa?
11 Pangakhalenso cifukwa cina. Matanthwe a ku Meriba woyamba ni a nsangalabwi (kapena kuti olimba kwambili). Olo munthu atawamenya bwanji, sangatulutse madzi. Koma matanthwe a ku Meriba waciŵili ni ofooka. Matanthwe aconco amakhala na tumphako mkati, ndipo amasunga madzi cakuti anthu angathe kuwabowola kuti apeze madzi. Conco, mwina n’kutheka kuti pamene Mose anamenya thanthwe lofookalo kaŵili, anthu anaganiza kuti iye wangobooleza madzi m’thanthwelo, osati kuti Yehova ndiye watulutsa madziwo. Kodi n’kutheka kuti pamene Mose anamenya thanthwe m’malo mongokamba nalo, anapangitsa anthu kukayikila kuti Yehova wacita cozizwitsa? * Mwina, koma sitingakambe motsimikiza.
MMENE MOSE ANAPANDUKILA
12. Kodi Yehova anakwiyila Mose na Aroni mwina pa cifukwa cina citi?
12 Palinso cifukwa cina cimene ciyenela kuti cinacititsa Yehova kukwiyila Mose na Aroni. Onani zimene Mose anauza anthuwo. Iye anati: “Kodi ticite kukutulutsilani madzi m’thanthweli?” Mwa kukamba mau akuti “ticite,” mwacionekele Mose anali kutanthauza kuti wotulutsa madzi adzakhala iye na Aroni. Zimene Mose anakamba sizinali zopeleka ulemu kwa Yehova, Gwelo leni-leni la cozizwitsaco. Mogwilizana na mfundo imeneyi, lemba la Salimo 106:32, 33 limati: “Iwo anaputa mkwiyo [wa Mulungu] pa madzi a ku Meriba, moti Mose sizinamuyendele bwino cifukwa ca anthu amenewa. Iwo anamukwiyitsa ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalila bwino.” * (Num. 27:14) Mulimonse mmene zinakhalila, cimene tidziŵa n’cakuti zimene Mose anacita zinapangitsa kuti Yehova asapatsidwe ulemu womuyenelela. Pokamba ndi Mose na Aroni, Yehova anati: “Amuna inu munapandukila malangizo anga.” (Num. 20:24) Cimeneci cinalidi colakwa cacikulu!
13. N’cifukwa ciani tikamba kuti zimene Yehova anacita poweluza Mose cinali cilungamo?
13 Monga atsogoleli a anthu a Yehova, Mose ndi Aroni anali na udindo waukulu wopeleka citsanzo cabwino kwa anthuwo. (Luka 12:48) M’mbuyomo, Yehova anaweluza mtundu wonse wa Isiraeli kuti sudzaloŵa m’dziko la Kanani cifukwa ca kupanduka kwawo. (Num. 14:26-30, 34) Conco, zimene Yehova anacita poweluza Mose kuti sadzaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa cinali cilungamo, cifukwa nayenso Mose anaonetsa mzimu wopanduka.
CIMENE CINABWELETSA VUTO
14, 15. N’ciani cinacititsa Mose kupandukila Mulungu?
14 N’ciani cinacititsa Mose kupandukila Yehova? Onaninso zimene Salimo 106:32, 33 imakamba. Imati: “Iwo anaputa mkwiyo [wa Mulungu] pa madzi a ku Meriba, moti Mose sizinamuyendele bwino cifukwa ca anthu amenewa. Iwo anamukwiyitsa ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalila bwino.” Ngakhale kuti Aisiraeli anaputa mkwiyo wa Yehova, Mose ndiye anakwiya. Cifukwa colephela kudziletsa, iye analankhula mosasamala popanda kuganizila zotulukapo zake.
15 Mose analola zocita za ena kumulepheletsa kuyang’anabe kwa Yehova. Pa cocitika coyamba, iye anacita zinthu moyenela. (Eks. 7:6) Koma n’kutheka kuti pambuyo potsogolela Aisiraeli opanduka kwa zaka zambili, iye analema komanso anakhumudwa na zocita zawo. Ndipo mwina Mose anayamba kuganizila kwambili za mmene anali kumvelela, m’malo moganizila za mmene angapelekele ulemelelo kwa Yehova.
16. N’cifukwa ciani kuganizila mosamala zimene Mose anacita n’kofunika?
16 Ngati mneneli wokhulupilika Mose anacenjenekewa mpaka kulakwila Mulungu, na ise zaconco zingaticitikile mosavuta. Mofanana ndi Mose, tatsala pang’ono kuloŵa m’dziko latsopano limene Yehova anatilonjeza. (2 Pet. 3:13) Palibe aliyense amene angafune kuphonya mwayi wapadela umenewu. Koma kuti mwayi umenewu usakatiphonye, tifunika kuikabe maso athu pa Yehova na kumumvela nthawi zonse. (1 Yoh. 2:17) Kodi tiphunzilapo ciani pa colakwa ca Mose?
MUSALOLE ZOCITA ZA ENA KUKULEPHELETSANI KUIKABE MASO ANU PA YEHOVA
17. N’ciani cingatithandize kuti tisalole mkwiyo kutilamulila?
17 Musalole mkwiyo kukulamulilani. Ngakhale kuti mwina takhala tikulimbana na mavuto amodzi-modzi kwa nthawi yaitali, “tisaleke kucita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.” (Agal. 6:9; 2 Ates. 3:13) Ngati takumana na zokhumudwitsa kapena ngati timasemphana maganizo kaŵili-kaŵili na munthu wina cifukwa cosiyana zibadwa, kodi timatha kulamulila milomo yathu na kuugwila mtima? (Miy. 10:19; 17:27; Mat. 5:22) Ngati ena atikwiyitsa, tifunika ‘kusiila malo mkwiyo.’ Mkwiyo wa ndani? Wa Yehova. (Ŵelengani Aroma 12:17-21.) Ngati timayang’anabe kwa Yehova, tidzaonetsa kuti timamulemekeza mwa kusiila malo mkwiyo wake ndi kumuyembekezela moleza mtima kuti adzacitepo kanthu pa nthawi yake yoyenela. Ngati tingabwezele mwanjila ina iliyonse, ndiye kuti sitikulemekeza Yehova.
18. Kodi tifunika kukumbukila ciani pa nkhani ya kutsatila malangizo?
Aheb. 13:17) Komanso, tidzacita zinthu mosamala kuti ‘tisapitilile zinthu zolembedwa.’ (1 Akor. 4:6) Ngati ticita zimenezi, ndiye kuti tikuikabe maso athu pa Yehova.
18 Muzitsatila malangizo atsopano mosamala. Kodi timatsatila mokhulupilika malangizo atsopano ocokela kwa Yehova? Ngati n’conco, tidzapewa cizoloŵezi cocita zinthu mongotsatila zimene takhala tikucita m’mbuyomu. M’malomwake, tidzayesetsa kutsatila mwamsanga malangizo aliwonse atsopano amene Yehova amapeleka kupitila m’gulu lake. (19. Tingacite ciani kuti zolakwa za ena zisatipangitse kuwononga ubwenzi wathu na Yehova?
19 Musalole kuti zophophonya za ena zikupangitseni kuwononga ubwenzi wanu na Yehova. Ngati mophiphilitsila tiikabe maso athu pa Yehova, sitidzalola zocita za ena kutikhumudwitsa kapena kuticititsa kuwononga ubwenzi wathu na iye. Kucita zimenezi n’kofunika kwambili maka-maka ngati, mofanana ndi Mose, tili na udindo m’gulu la Mulungu. N’zoona kuti aliyense wa ise afunika ‘kupitiliza kukonza cipulumutso cake, mwamantha ndi kunjenjemela.’ (Afil. 2:12) Ngati munthu ali na udindo waukulu, Yehova amayembekezelanso zambili kwa iye. (Luka 12:48) Komabe, ngati timakonda Yehova na mtima wonse, palibe cimene cidzatipunthwitsa kapena kutilekanitsa na cikondi cake.—Sal. 119:165; Aroma 8:37-39.
20. Kodi tifunika kukhala wotsimikiza mtima kucita ciani?
20 M’masiku ovuta ano, tiyeni tipitilizebe kuyang’ana kwa Yehova Mulungu, ‘amene amakhala kumwamba,’ n’colinga cakuti tikwanitse kuzindikila cifunilo cake. Tisalole ubwenzi wathu na iye kusokonezeka cifukwa ca zocita za ena. Zimene zinacitikila Mose ni cenjezo lamphamvu kwa ise pa nkhani imeneyi. M’malo mokhumudwa na zophophonya za abale athu, tiyeni tikhale wotsimikiza mtima ‘kuyang’anabe kwa Yehova Mulungu wathu, kufikila atatikomela mtima.”—Sal. 123:1, 2.
^ par. 8 Meriba uyu ni wina osati uja wa kufupi na ku Refidimu. Mosiyana ndi Meriba woyamba uja, Meriba waciŵiliyu anali kufupi na ku Kadesi, osati ku Masa. Komabe, madela onse aŵili anachedwa Meriba cifukwa ca mikangano imene inacitika kumeneko.—Onani mapu 7, pa peji 38, m’kabuku kakuti Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu.
^ par. 11 Pa nkhani imeneyi, pulofesa John A. Beck anati: “Malinga n’zimene Ayuda amakhulupilila, Aisiraeli opanduka anamutsutsa Mose na kukamba kuti: ‘Mose wamenya thanthwe ili cifukwa adziŵa kuti n’lofooka. Ngati afuna kuti tikhulupilile kuti alidi na mphamvu yocita zozizwitsa, atitulutsile madzi m’thanthwe lina ili.’” Izi n’zimene Ayuda akhala akukhulupilila, koma zilibe umboni.
^ par. 12 Onani “Mafunso Ochokera kwa Owelenga” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1987.