Kodi Maso Anu Amayang’ana kwa Ndani?

Kodi Maso Anu Amayang’ana kwa Ndani?

“Ndakweza maso anga kuyang’ana inu, kuyang’ana inu amene mukukhala kumwamba.”​—SAL. 123:1.

NYIMBO: 143, 124

1, 2. Kodi tingatani kuti tiziyang’ana kwa Yehova nthawi zonse?

PANOPA tili m’masiku ovuta kwambiri. Ndipo mavutowa aziwonjezereka pamene nthawi yoti padzikoli pakhalenso mtendere ikuyandikira. (2 Tim. 3:1) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimadalira ndani kuti andithandize ndiponso kundilangiza?’ Mwina tayankha kuti, “Yehova,” ndipo limeneli ndi yankho labwino kwambiri.

2 Koma kodi ndi zinthu ziti zimene zimasonyeza kuti tikuyang’ana kwa Yehova? Nanga tingatani kuti maso athu asamachoke kwa Yehova tikamakumana ndi mavuto osiyanasiyana? M’mbuyomo, wolemba masalimo wina anasonyeza kuti tiyenera kuyang’ana kwa Yehova pa nthawi imene tapanikizika ndi mavuto. (Werengani Salimo 123:1-4.) Iye anayerekezera kuyang’ana kwa Yehova ndi zimene kapolo amachita poyang’ana kwa mbuye wake. Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? N’zoona kuti kapolo amayang’ana kwa mbuye wake kuti amupatse chakudya komanso azimuteteza. Koma amayang’ananso mbuyeyo kuti adziwe zimene akufuna kenako n’kuchita zimene akufunazo. Ifenso tiyenera kufufuza m’Mawu a Mulungu tsiku lililonse kuti tidziwe zimene Yehova akufuna kenako n’kumachita zimene akufunazo. Tikamachita zimenezi sitingakayikire ngakhale pang’ono kuti iye adzatithandiza tikapanikizika ndi mavuto.​—Aef. 5:17.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatichititse kuti tisiye kuyang’ana kwa Yehova?

3 Koma nthawi zina tikhoza kusokonezedwa ndi zinthu zina ngakhale kuti timadziwa ubwino woyang’ana kwa Yehova. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Marita, yemwe anali mnzake wa Yesu. Baibulo limanena kuti nthawi ina iye anasokonezedwa “ndi ntchito zochuluka.” (Luka 10:40-42) Ngati zimenezi zinachitikira munthu wokhulupirikayu ali ndi Yesu, kuli bwanji ifeyo? Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene zingatichititse kuti tisiye kuyang’ana kwa Yehova? Munkhaniyi tikambirana mmene zochita za anthu ena zingatisokonezere. Tionanso zimene zingatithandize kuti tisasiye kuyang’ana kwa Yehova.

MUNTHU WOKHULUPIRIKA ANATAYA MWAYI WAUKULU

4. N’chifukwa chiyani zingakhale zodabwitsa kuti Mose analephera kulowa m’Dziko Lolonjezedwa?

4 Mose ankayang’ana kwa Yehova kuti amupatse malangizo. Paja Baibulo limati iye “anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Werengani Aheberi 11:24-27.) Limanenanso kuti “mu Isiraeli simunakhalebe mneneri aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova anali kumudziwa pamasom’pamaso.” (Deut. 34:10) Koma ngakhale kuti Mose anali pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Yehova, iye anataya mwayi wolowa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:12) Kodi chinamuchititsa n’chiyani?

5-7. Kodi panachitika vuto lotani Aisiraeli atangochoka ku Iguputo, ndipo kodi Mose anathana nalo bwanji vutoli?

5 Pasanathe miyezi iwiri kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, anakumana ndi vuto lalikulu. Asanafike n’komwe kuphiri la Sinai, anayamba kudandaula za kusowa kwa madzi. Iwo anayamba kung’ung’udzira Mose ndipo zinafika povuta moti Mose anadandaulira Yehova kuti: “Nditani nawo anthuwa? Angotsala pang’ono kundiponya miyala!” (Eks. 17:4) Yehova atamva, anauza Mose zoyenera kuchita. Anamuuza kuti atenge ndodo yake n’kumenya mwala ku Horebe n’cholinga choti madzi atuluke. Baibulo limati: “Mose anachitadi zomwezo, pamaso pa akulu a Isiraeli.” Zitatero Aisiraeli anayamba kumwa moti ludzu lawo linatheratu.​—Eks. 17:5, 6.

6 Nkhani ya m’Baibuloyi imapitiriza kuti Mose “anatcha malowo Masa ndi Meriba, chifukwa ana a Isiraeli anakangana ndi Mose, komanso chifukwa cha kuyesa Yehova kuti: ‘Kodi pakati pathu pano, Yehova alipo kapena ayi?’” (Eks. 17:7) Mayinawa anali oyenerera chifukwa amatanthauza “Kuyesa” ndi “Kukangana.”

7 Kodi zimene zinachitika ku Meriba zinamukhudza bwanji Yehova? Iye anaona kuti Aisiraeli ankalimbana ndi iyeyo osati Mose yekha. (Werengani Salimo 95:8, 9.) Apa Aisiraeli analakwitsa kwambiri. Koma pa nthawi imeneyi, Mose anachita zinthu mwanzeru kwambiri chifukwa anayang’ana kwa Yehova kenako n’kutsatira malangizo ake mosamala kwambiri.

8. Kodi Aisiraeli anakumana ndi vuto lotani atatsala pang’ono kufika m’Dziko Lolonjezedwa?

8 Vuto lofananali linachitikanso Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Pa nthawiyi n’kuti patapita zaka 40 ndipo anafika kudera lomwe pambuyo pake linayamba kutchedwanso kuti Meriba. Malowa anali osiyana ndi oyamba aja ndipo anali pafupi ndi dera la Kadesi lomwe linali loyandikana ndi malire a Dziko Lolonjezedwa. * Aisiraeli anadandaulanso za vuto la kusowa kwa madzi. (Num. 20:1-5) Koma pa nthawiyi Mose anachita zinthu mosiyana ndi poyamba.

9. Kodi Yehova anapatsa Mose malangizo otani, koma iye anachita chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)

9 Kodi Mose anachita zotani pa nthawi imeneyi? Iye anayang’ananso kwa Yehova kuti amupatse malangizo. Koma ulendo umenewu Yehova sanamuuze kuti amenye mwala. Iye anauza Mose kuti atenge ndodo yake, kuuza anthu kuti asonkhane pafupi ndi mwala, kenako alankhule ndi mwalawo. (Num. 20:6-8) Koma Mose sanalankhule ndi mwalawo. M’malomwake analankhula ndi anthu amene anasonkhanawo mokwiya kuti: “Tsopano tamverani anthu opanduka inu! Kodi tichite kukutulutsirani madzi m’thanthweli?” Kenako iye anamenya mwalawo osati kamodzi, koma kawiri.​—Num. 20:10, 11.

10. Kodi Yehova anatani Mose atalephera kutsatira malangizo?

10 Zitatero, Yehova anakwiyira Mose kwambiri. (Deut. 1:37; 3:26) N’chifukwa chiyani anakwiya? Payenera kuti panali zifukwa zingapo. Monga tanena kale, Yehova ayenera kuti anakwiya chifukwa Mose sanatsatire malangizo atsopano amene analandira.

11. Kodi zimene Mose anachita mwina zikanapangitsa bwanji anthu kuganiza kuti Yehova sanachite chozizwitsa?

11 Koma n’kutheka kuti panali chifukwa chinanso. Miyala yakudera la ku Meriba koyamba kuja ndi yolimba kwambiri. Ngakhale munthu ataimenya kwambiri, singatulutse madzi. Koma miyala yakudera la ku Meriba kwachiwiriku ndi yofewa. Chifukwa cha zimenezi, miyala yambiri inkakhala ndi akasupe amadzi moti zinali zotheka kuwabooleza. N’kutheka kuti Mose atamenya mwalawu kawiri, zinapangitsa kuti anthu aganize zoti iyeyo ndi amene wabooleza osati Yehova ndi amene wawapatsa madziwo mozizwitsa. Kumenya kawiri m’malo mongolankhula ndi mwalawu mwina kukanachititsa kuti anthu asaganize kuti chinali chozizwitsa. * Kaya zinalidi choncho kapena ayi sitikudziwa.

KODI CHIMENE MOSE ANALAKWITSA N’CHIYANI?

12. Kodi n’kutheka kuti Yehova anakwiyira Mose ndi Aroni pa chifukwa china chiti?

12 Koma pali chifukwa chinanso chomveka chimene chinachititsa kuti Yehova akwiyire Mose ndi Aroni. Kumbukirani kuti Mose anauza anthu aja kuti: “Kodi tichite kukutulutsirani madzi m’thanthweli?” Ponena kuti “tichite” kukutulutsirani, Mose ayenera kuti ankatanthauza iyeyo ndi Aroni. Ponena zimenezi, iye sanalemekeze Yehova monga wochititsa zozizwitsazo. Tikhoza kutsimikizira kuti mfundoyi ndi yoona tikaganizira zimene lemba la Salimo 106:32, 33 limanena. Paja limati: “Iwo anaputa mkwiyo pa madzi a ku Meriba, moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa. Iwo anamukwiyitsa ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalira bwino.” * (Num. 27:14) Kaya zinthu zinali bwanji, koma zimene Mose anachitazi zinachititsa kuti anthu asapereke ulemu woyenerera kwa Yehova. Choncho Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Amuna inu munapandukira malangizo anga.” (Num. 20:24) Apa zikuonekeratu kuti tchimo lawoli linali lalikulu kwambiri.

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chiweruzo chimene Yehova anapereka kwa Mose chinali choyenera komanso chachilungamo?

13 Popeza Mose ndi Aroni anali ndi udindo wotsogolera anthu a Yehova, iwo ankayenera kuyankha pamaso pa Yehovayo. (Luka 12:48) Yehova anali atanena kale kuti m’badwo wonse wa Aisiraeli sudzalowa m’dziko la Kanani chifukwa chosamumvera. (Num. 14:26-30, 34) Choncho Yehova anachita zinthu moyenera komanso mwachilungamo popereka chiweruzo chomwecho kwa Mose pamene nayenso sanamumvere. Mofanana ndi Aisiraeli ena osamverawo, iye sanaloledwe kulowa m’Dziko Lolonjezedwa.

KODI N’CHIYANI CHINACHITITSA KUTI MOSE ALAKWE?

14, 15. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Mose asamvere Yehova?

14 Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Mose asamvere Yehova? Paja lemba la Salimo 106:32, 33 lija limanena kuti: “Iwo anaputa mkwiyo pa madzi a ku Meriba, moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa. Iwo anamukwiyitsa ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalira bwino.” Ngakhale kuti Aisiraeliwo anaputa mkwiyo wa Yehova, Mose ndi amene anakwiya. Kusadziletsa kwake kunachititsa kuti alankhule mosaganizira mavuto amene angakumane nawo.

15 Mose analola kuti zochita za anthu ena zimulepheretse kuyang’anabe kwa Yehova. Iye atakumana ndi vutoli pa ulendo woyamba anachita zinthu bwinobwino. (Eks. 7:6) Koma n’kutheka kuti atakhala zaka zambiri ndi Aisiraeli, omwe nthawi zambiri sankamvera, iye anakhumudwa komanso kutopa nawo. Mwina Mose ankaganizira kwambiri mmene Aisiraeliwo ankamukhumudwitsira m’malo moganizira mmene iyeyo angalemekezere Yehova.

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira kwambiri zimene zinachitikira Mose?

16 Ngati Mose, yemwe anali mneneri wokhulupirika, analephera kuyang’anabe kwa Yehova, ndiye kuti ifenso zikhoza kutichitikira. Mofanana ndi Mose, nafenso tangotsala pang’ono kulowa m’dziko latsopano limene Yehova watilonjeza. (2 Pet. 3:13) Palibe amene angafune kutaya mwayi ngati umenewu. Koma kuti zimenezi zitheke, tonsefe tiyenera kuyang’anabe kwa Yehova kuti tidziwe zimene akufuna n’kumachita zomwezo. (1 Yoh. 2:17) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mose analakwitsa?

MUSAMALOLE KUTI ZOCHITA ZA ENA ZIKUSOKONEZENI

17. N’chiyani chingatithandize kuti tisamakhumudwe ndi zochita za anthu ena?

17 Musamakhumudwe chifukwa cha zochita za ena. Mwina panopa pali vuto lina limene limakusowetsani mtendere mobwerezabwereza. Koma chofunika n’chakuti “tisaleke kuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.” (Agal. 6:9; 2 Ates. 3:13) Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapewa kupsa mtima kapena kulankhula mawu oipa ndikapanikizika ndi mavuto kapena anthu ena akamandikhumudwitsa mobwerezabwereza?’ (Miy. 10:19; 17:27; Mat. 5:22) Anthu ena akatiputa, tiyenera ‘kusiyira malo mkwiyo wa Yehova.’ (Werengani Aroma 12:17-21.) Tikamadalirabe Yehova tidzasonyeza kuti timamulemekeza n’kupereka mpata woti asonyeze mkwiyo wake. Tingati timadekha n’kumayembekezera kuti iye akonze zinthu pa nthawi imene akuona kuti ndi yoyenera. Koma ngati tingafune kubwezera tokha zingatanthauze kuti sitilemekeza Yehova.

18. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikalandira malangizo atsopano?

18 Tizitsatira mosamala malangizo atsopano. Kodi timayesetsa kutsatira mokhulupirika malangizo atsopano amene Yehova watipatsa? Ngati timatero tidzapewa mtima wongofuna kuchita zinthu m’njira imene tinazolowera. M’malomwake tiziyesetsa kutsatira malangizo atsopano alionse amene Yehova angatipatse kudzera m’gulu lake. (Aheb. 13:17) Komanso tidzapewa ‘kupitirira zinthu zolembedwa.’ (1 Akor. 4:6) Tikamatero ndiye kuti tikuyang’anabe kwa Yehova.

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mose anachita ena atalakwitsa zinthu? (Onani ndime 19)

19. Kodi tingatani kuti zochita za anthu ena zisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova?

19 Musalole kuti zolakwa za anthu ena zisokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. Ngati timayang’ana kwa Yehova nthawi zonse, sitidzalola kuti zochita za anthu ena zitikwiyitse kapena zisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri makamaka kwa anthu amene ali ndi udindo m’gulu la Yehova. N’zoona kuti tonsefe tiyenera ‘kukonza chipulumutso chathu, mwamantha ndi kunjenjemera.’ (Afil. 2:12) Koma tizikumbukira kuti Yehova saweruza tchimo lililonse mofanana. Iye amayembekezera zambiri kwa anthu amene ali ndi udindo ngati mmene zinalili ndi Mose. (Luka 12:48) Ngati timakonda Yehova ndi mtima wonse, sitidzalola chilichonse kutipunthwitsa kapena kutisiyanitsa ndi chikondi chake.​—Sal. 119:165; Aroma 8:37-39.

20. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani nthawi zonse?

20 M’masiku ovuta ano, tiyenera kuyesetsa kuti nthawi zonse tiziyang’ana kwa ‘amene akukhala kumwamba’ n’cholinga choti tidziwe zimene akufuna kuti tichite. Tisalole kuti ubwenzi wathu ndi Yehova usokonezedwe ndi zochita za anthu ena. Nkhani ya Mose imatitsimikizira kufunika kwa mfundo imeneyi. M’malo mofulumira kukwiya chifukwa cha zolakwa za ena, tiyenera ‘kuyang’ana kwa Yehova Mulungu wathu nthawi zonse kufikira atatikomera mtima.’​—Sal. 123:1, 2.

^ ndime 8 Ku Meriba uku ndi kosiyana ndi ku Meriba komwe kunayandikana ndi dera la Refidimu. Malowa anali ku Kadesi osati ku Masa. Koma malo onsewa anatchedwa Meriba chifukwa cha kukangana komwe kunachitikako.​—Onani kabuku kakuti Onani Dziko Lokoma, patsamba 9 kapena Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu, mutu 7.

^ ndime 11 Pulofesa wina dzina lake John A. Beck ananena kuti Ayuda ena amakhulupirira kuti: “Anthu otsutsana ndi Mose anati: ‘Mose wadziwa kuti mumwalawu muli madzi. Ngati akufuna kuchitadi zozizwitsa, bwanji osatulutsa madzi pamwala winawu?’” Koma izi n’zimene anthu ena amangokhulupirira basi.

^ ndime 12 Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya October 15, 1987.