Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Ngati mwamuna ndi mkazi amene sali pa banja atakhala limodzi usiku wonse popanda zifukwa zomveka, kodi tingati achita tchimo lofunika komiti yoweruza?

Inde. Ngati anthuwo akhala limodzi popanda zifukwa zomveka, komiti yoweruza mlandu ikhoza kupangidwa chifukwa umenewu ungakhale umboni wosonyeza kuti anthuwo achita dama.​—1 Akor. 6:18.

Bungwe la akulu liyenera kufufuza bwino nkhaniyo kuti lidziwe ngati pangafunike komiti yoweruza kapena ayi. Mwachitsanzo, kodi anthuwo akhala ali pa chibwenzi? Kodi m’mbuyomo anapatsidwapo malangizo pa nkhani ya mmene amachitira zinthu pa chibwenzi chawo? N’chifukwa chiyani anakhala limodzi usiku wonse? Kodi anachita kukonzeratu kuti akakhale limodzi usikuwo? Nanga panali njira ina imene akanatsatira kuti asakhale limodzi? Kapena panali vuto linalake ladzidzidzi limene linachititsa kuti asachitire mwina koma akhale limodzi usikuwo? (Mlal. 9:11) Kodi anagona bwanji? Popeza zochitika zimasiyana pa nkhani iliyonse, akulu ayenera kufufuza bwino n’kumaganizira zifukwa zonse zimene zinachititsa.

Pambuyo pofufuza zifukwa zonse, bungwe la akulu lingaone ngati pangafunike kupanga komiti yoweruza.