Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

“Muziopa Yehova Mulungu wanu. Muzim’tumikila, kum’mamatila.”—DEUT. 10:20.

NYIMBO: 28, 32

1, 2. (a) N’cifukwa ciani n’cinthu canzelu kukhala ku mbali ya Yehova? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

KUMAMATILA kwa Yehova n’cinthu canzelu. Palibe wina wamphamvu, wanzelu kapena wacikondi kuposa Mulungu wathu. N’ndani wa ise amene sangakonde kukhala ku mbali yake? (Sal. 96:4-6) Komabe, olambila ena a Mulungu alephela kukhala okhulupilika kwa iye ndipo acoka kumbali yake.

2 M’nkhani ino, tidzakambilana zitsanzo za anthu ena amene anali kudziona kuti ali kumbali ya Yehova, koma panthawi imodzi-modzi anali kucita zinthu zom’khumudwitsa. Pa nkhani za anthu amenewa, tidzaphunzilapo mfundo zofunika zimene zingatithandize kukhalabe okhulupilika kwa Yehova pa ciliconse.

YEHOVA AMASANTHULA MTIMA

3. N’cifukwa ciani Yehova anayesa kum’thandiza Kaini? Ndipo anamuuza ciani?

3 Ganizilani za Kaini. Iye anali kulambila Yehova, osati mulungu wina aliyense. Komabe, Mulungu sanakondwele na kulambila kwake, cifukwa maganizo oipa anayamba kuzika mizu mu mtima mwake. (1 Yoh. 3:12) Yehova anayesa kum’thandiza Kaini mwa kumuuza kuti: “Ukasintha n’kucita cabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti ucite cabwino, ucimo wamyata pakhomo kukudikilila, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?” (Gen. 4:6, 7) Mwanjila ina, tingakambe kuti Yehova anali kuuza Kaini kuti: “Ukalapa na kukhalabe ku mbali yanga, na ine nidzakhala ku mbali yako.”

4. N’ciani cimene Kaini anacita atapatsidwa mwayi wokhala kumbali ya Yehova?

4 Kaini akanasintha maganizo ake oipa, Yehova akanamuyanja. Koma iye sanamvele uphungu wa Mulungu. Maganizo oipa komanso cilako-lako coipa zinam’sonkhezela kucita chimo. (Yak. 1:14, 15) Pamene anali wacicepele, mwina Kaini anali kuona kuti sangapandukile Yehova. Koma m’kupita kwa nthawi, iye anapandukila Mulungu na kupha m’bale wake.

5. Ni maganizo anji amene angacititse kuti Yehova aleke kutiyanja?

5 Mofanana ndi Kaini, Mkhristu masiku ano angakambe kuti amalambila Yehova, koma n’kumacita zinthu zina zimene iye amazonda. (Yuda 11) Mwacitsanzo, iye angalole maganizo a ciwelewele ndi a dyela kuzika mizu mu mtima mwake. Kapena angayambe kusungila Mkhristu mnzake cidani. (1 Yoh. 2:15-17; 3:15) Maganizo aconco angapangitse Mkhristuyo kucita chimo. Koma pa nthawi imodzi-modzi, iye angakhale kuti ni wacangu mu ulaliki ndipo amapezeka pa misonkhano nthawi zonse. Mwina anthu ena sangadziŵe maganizo athu na zocita zathu, koma Yehova amaona zonse ndipo amadziŵa ngati timam’tumikiladi mokhulupilika kapena ayi.—Ŵelengani Yeremiya 17:9, 10.

6. Ngati tikhalabe ku mbali ya Yehova, kodi iye angatithandize bwanji ‘kugonjetsa’ zilakolako za ucimo?

6 Ngakhale n’conco, Yehova amayesetsabe kutithandiza. Ngati munthu wayamba kuyenda njila yolakwika, Yehova amam’langiza kuti: ‘Bwelela kwa ine ndipo ine ndibwelela kwa iwe.’ (Malaki 3:7) Maka-maka ngati tikulimbana ndi zofooka zinazake, Yehova amafuna kuti tiziyesetse kukana zoipa. (Yes. 55:7) Tikacita zimenezi, iyenso adzakhala ku mbali yathu mwa kutilimbikitsa na kutipatsa mphamvu zimene zingatithandize ‘kugonjetsa’ zilakolako zathu za ucimo.—Gen. 4:7.

“MUSASOCELETSEDWE”

7. Kodi Solomo anawononga bwanji ubwenzi wake na Yehova?

7 Tingaphunzile zambili pa nkhani ya Mfumu Solomo. Pamene anali wacicepele, Solomo anali kuyang’ana kwa Yehova kuti am’patse malangizo. Mulungu anam’patsa nzelu zambili komanso udindo womanga kacisi waulemelelo ku Yerusalemu. Koma Solomo anawononga ubwenzi wake wabwino na Yehova. (1 Maf. 3:12; 11:1, 2) M’Cilamulo ca Mulungu, munali lamulo lacindunji loletsa mfumu ya Isiraeli ‘kudziculukitsila akazi kuti mtima wake ungapatuke.’ (Deut. 17:17) Koma Solomo sanamvele lamulo limeneli cakuti m’kupita kwa nthawi anakwatila akazi 700. Komanso anatenga akazi ena apambali 300. (1 Maf. 11:3) Akazi ake ambili sanali Aisiraeli, ndipo anali kulambila mafano. Conco pamenepa, Solomo anaphwanyanso lamulo la Mulungu loletsa kukwatila akazi a mitundu ina.—Deut. 7:3, 4.

8. Kodi Solomo anam’kwiyitsa bwanji Yehova?

8 Cifukwa cakuti Solomo anali kunyalanyaza malamulo a Yehova, m’kupita kwa nthawi anacita macimo aakulu kwambili. Iye anamangila guwa la nsembe mulungu wamkazi wochedwa Asitoreti ndi guwa lina la mulungu wochedwa Kemosi. Ndipo anayamba kulambila mafano pamodzi ndi azikazi ake. Iye anacita kumanga maguwa ansembewo pa phili loyang’anana ndi mzinda wa Yerusalemu, kumene anamangako kacisi wa Yehova. (1 Maf. 11:5-8; 2 Maf. 23:13) Mwina Solomo anaganiza kuti Yehova adzanyalanyaza zolakwa zake malinga ngati apitiliza kupeleka nsembe pa kacisi.

9. Kodi mtima wonyalanyaza malamulo a Mulungu umene Solomo anali nawo unabweletsa mavuto anji?

9 Koma Yehova sanyalanyaza macimo. Baibo imati: “Yehova anamukwiyila kwambili Solomo cifukwa mtima wake unapatuka kwa Yehova. . . , amene anamuonekela kaŵili konse. Pa nkhani imeneyi, Mulungu anali atamulamula kuti asatsatile milungu ina, koma iye sanasunge zimene Yehova analamula.” Pamapeto pake, Mulungu analeka kumuyanja na kum’cilikiza. Komanso iye atafa, ufumu wa Isiraeli unagaŵikana moti mafumu obwela pambuyo pake anakumana na mavuto ambili kwa zaka zoculuka.—1 Maf. 11:9-13.

10. N’ciani cingaike ubwenzi wathu na Yehova paciopsezo?

10 Molingana ndi zimene zinacitikila Solomo, vuto limodzi lalikulu limene lingaike umoyo wathu wauzimu paciopsezo ni kukhala pa ubwenzi ndi anthu amene sadziŵa kapena kulemekeza miyezo ya Yehova. Ena angakhale kuti amagwilizana na mpingo, koma ni ofooka mwauzimu. Enanso angakhale acibululu, maneba, ndiponso anzathu a kunchito kapena akusukulu amene salambila Yehova. Kaya mabwenzi athu ni a mumpingo kapena ayi, ngati iwo salemekeza miyezo ya Yehova, m’kupita kwa nthawi angaticititse kuwononga ubwenzi wathu na Mulungu.

Kodi mabwenzi anu amakhudza bwanji unansi wanu na Yehova? (Onani palagilafu 11)

11. Tingam’dziŵe bwanji munthu amene si bwenzi labwino?

11 Ŵelengani 1 Akorinto 15:33. Anthu ambili aliko na makhalidwe ena abwino. Ngakhale anthu amene si Mboni sikuti nthawi zonse amacita zoipa. Ngati anthu amene mumadziŵana nawo ali conco, kodi ndiye kuti angakhale mabwenzi abwino? Ayi. Coyamba dzifunseni kuti, ‘Kodi kugwilizana nawo kudzakhudza bwanji ubwenzi wanga na Yehova? Kodi adzanithandiza kuulimbitsa? Kodi iwo amakonda kuganizila ciani? Mwacitsanzo, kodi amakonda kukamba za mafashoni, ndalama, zipangizo zamakono, zosangalatsa, kapena zolinga zakuthupi? Kodi zokamba zawo nthawi zambili zimaphatikizapo mijedo kapena nthabwala zotukwana?’ Kumbukilani kuti Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima.” (Mat. 12:34) Ngati mwaona kuti zocita za anzanu zikuika ubwenzi wanu na Yehova paciopsezo, citamponi kanthu mofulumila mwa kupewa kugwilizana nawo kwambili kapena kungothetsa ubwenziwo.—Miy. 13:20.

YEHOVA AMAFUNA KUTI TIKHALE ODZIPELEKA KWA IYE YEKHA

12. (a) Kodi Yehova anawauza ciani Aisiraeli atangotuluka mu Iguputo? (b) Nanga iwo anayankha bwanji Mulungu atawalamula kuti ayenela kukhala okhulupilika kwa iye yekha?

12 Palinso mfundo zina zimene tingaphunzilepo pa zimene zinacitika Aisiraeli atangotuluka mu Iguputo. Iwo atasonkhana pa Phili la Sinai, Yehova anacita zizindikilo zazikulu zoonetsa kukhalapo kwake. Mtambo wakuda unawonekela modabwitsa. Yehova anapangitsa kuti kucite mabingu, mphenzi, na utsi, ndipo panamveka kulila kwamphamvu kwambili kokhala ngati kwa lipenga. (Eks. 19:16-19) Pa cocitikaco, Yehova anauza Aisiraeli kuti iye ni ‘Mulungu wofuna kuti anthu azidzipeleka kwa iye yekha.’ Anawatsimikizila kuti adzakhala wokhulupilika kwa anthu amene amam’konda na kusunga malamulo ake. (Ŵelengani Ekisodo 20:1-6.) Apa tingakambe kuti Yehova anali kuuza anthu ake kuti, “Ngati mudzakhalabe ku mbali yanga, na ine nidzakhalabe ku mbali yanu.” Kodi mukanakhala inu mukanacita ciani mutamva lonjezo la Yehova Mulungu limeneli? Mwacionekele, mukanacita monga mmene Aisiraeli anacitila. Iwo “anayankhila pamodzi kuti: “Mau onse amene Yehova wanena tidzacita.’” (Eks. 24:3) Komabe, pasanapite nthawi, panacitika zinthu zina zimene zinayesa kukhulupilika kwawo kwa Yehova.

13. N’zocitika ziti zimene zinayesa kukhulupilika kwa Aisiraeli?

13 Aisiraeli anacita mantha na mtambo wakuda, mphenzi, na zizindikilo zina zocititsa mantha zocokela kwa Mulungu. Kaamba ka ici, iwo anapempha kuti Mulungu asakambe nawo mwacindunji, koma kuti Mose aziwauza zilizonse zimene Mulunguyo adzakamba naye pa Phili la Sinai. Ndipo Mose anacitadi zimenezo. (Eks. 20:18-21) Mose anakwela m’phililo, ndipo anakhalamo kwa nthawi yaitali. Aisiraeli anayamba kuona ngati kuti ali okha-okha m’cipululumo popanda mtsogoleli aliyense. Zioneka kuti cikhulupililo ca anthuwo cinali kudalila kwambili pa Mose, mtsogoleli wawo waumunthu. Conco iwo anada nkhawa, ndipo anauza Aroni kuti: “Tipangile mulungu woti atitsogolele, cifukwa sitikudziŵa zimene zacitikila Mose, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.”—Eks. 32:1, 2.

14. Kodi Aisiraeli anakhala na maganizo anji odzinamiza? Nanga Yehova anamvela bwanji cifukwa ca zocita zawo?

14 Aisiraeli anali kudziŵa kuti kulambila mafano ni chimo lalikulu pamaso pa Yehova. (Eks. 20:3-5) Ngakhale n’conco, iwo anayamba kulambila mwana wa ng’ombe. Olo kuti anali atacita chimo, Aisiraeli ayenela kuti anali kuganiza kuti akali ku mbali ya Yehova. Izi zionekela bwino pa zimene Aroni anakamba. Iye ananena kuti kulambila mwana wa ng’ombeko cinali “cikondwelelo ca Yehova.” Kodi Yehova anamvela bwanji? Anaona kuti anthuwo am’pandukila. Yehova anauza Mose kuti iwo ‘anacita zinthu zowawonongetsa’ komanso kuti ‘anapatuka mofulumila panjila imene iye anawalamula kuyendamo.’ Yehova anakwiya kwambili cakuti anafuna kufafaniza mtundu wonse wa Isiraeli.—Eks. 32:5-10.

15, 16. Kodi Mose na Aroni anaonetsa bwanji kuti anaimabe zolimba ku mbali ya Yehova? (Onani pikica kuciyambi.)

15 Yehova anaganiza zakuti asawononge mtundu wonse wa Aisiraeli. Cifundo cake cinapatsa Aisiraeli okhulupilika mwayi woimabe zolimba ku mbali yake. (Eks. 32:14) Mose ataona zinthu zonyansa zimene anthuwo anali kucita, monga kukuwa, kuimba, na kuvina patsogolo pa fano, anatenga mwana wa ng’ombeyo na kumuphwanya-phwanya mpaka kukhala fumbi lokha-lokha. Kenako anati: “Ndani ali kumbali ya Yehova? Abwele kwa ine! Ndipo ana onse aamuna a Levi anayamba kusonkhana kwa Mose.”—Eks. 32:17-20, 26.

16 Olo kuti Aroni ndiye anapanga fanolo, iye analapa na kukhala ku mbali ya Yehova pamodzi na alevi anzake. Anthu okhulupilika amenewa anasankha kukhala ku mbali ya Yehova, komanso anadzipatula kwa anthu ocita zoipa. Zimene anacitazo zinali zanzelu cifukwa pa tsikulo Aisiraeli masauzande anaphedwa cifukwa ca kulambila fano. Koma amene anali ku mbali ya Yehova analonjezedwa kuti adzadalitsidwa.—Eks. 32:27-29.

17. Kodi tiphunzilapo ciani pa zimene Paulo anakamba zokhudza kulambila mwana wa ng’ombe?

17 Mtumwi Paulo atafotokoza za kulambila fano la mwana wa ng’ombe anati: “Zinthu zimenezi zinakhala zitsanzo kwa ife, kuti ifenso. . . tisapembedze mafano, mmene ena mwa iwo anacitila. Zinthu zimenezi . . . zinalembedwa kuti ziticenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikila. N’cifukwa cake amene akuyesa kuti ali cilili asamale kuti asagwe.” (1 Akor. 10:6, 7, 11, 12) Monga mmene Paulo anakambila, ngakhale olambila oona angayambe makhalidwe ena oipa. Anthu ena amene amacita chimo, angakhale akumvabe kuti ali pa ubwenzi wolimba na Yehova. Komabe, kumvela cabe mu mtima kuti tili pa ubwenzi na Yehova kapena kudzionetsela kuti ndise okhulupilika kwa iye, sikutanthauza kuti Yehova akutiyanja.—1 Akor. 10:1-5.

18. N’ciani cingatipangitse kucoka pang’ono-pang’ono kwa Yehova ? Nanga pangakhale zotulukapo zanji?

18 Monga mmene Aisiraeli anakhalila na nkhawa cifukwa ca kucedwa kwa Mose pa Phili la Sinai, Akhristu ena masiku ano angakhale na nkhawa cifukwa coona ngati kuti tsiku la Yehova laciweluzo ndi dziko latsopano zacedwa. Iwo angayambe kuganiza kuti kukali nthawi yaitali kuti zimenezi zidzacitike, kapenanso kuti sizidzacitika n’komwe. Ngati sitingacitepo kanthu, maganizo amenewa angacititse kuti tiyambe kuika patsogolo zolinga zakuthupi m’malo moika patsogolo cifunilo ca Yehova. Ndipo tingayambe kutengeka pang’ono-pang’ono n’kucoka kwa Yehova. M’kupita kwa nthawi, tingayambe kucita zinthu zoipa zimene poyamba sitinali kuganiza kuti tingazicite.

19. Ni mfundo yofunika iti imene sitiyenela kuiiŵala? Nanga n’cifukwa ciani?

19 Tisamaiŵale kuti Yehova amafuna kuti tizimumvela na mtima wonse na kukhala wodzipeleka kwa iye yekha. (Eks. 20:5) Tikangoleka kucita cifunilo ca Yehova, ndiye kuti tayamba kucita cifunilo ca Satana, ndipo zimenezi zingatibweletsele mavuto aakulu. Ndiye cifukwa cake Paulo anati: “Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova komanso za m’kapu ya ziwanda. Sizingatheke kuti muzidya patebulo la Yehova komanso patebulo la ziwanda.”—1 Akor. 10:21.

MAMATILANI KWA YEHOVA

20. Kodi Yehova amatithandiza bwanji ngati tayamba kuyenda njila yolakwika?

20 Nkhani ya Kaini, Solomo, ndi ya Aisiraeli pa Phili la Sinai, zonse zili na mbali inayake yofanana. Anthu onsewa anali na mwayi ‘wolapa na kutembenuka.’ (Mac. 3:19) N’zoonekelatu kuti Yehova saleka mwamsanga kuthandiza anthu amene ayamba kuyenda njila yolakwika. Mwacitsanzo, Yehova anam’khululukila Aroni pa zimene anacita. Masiku ano, Yehova amaticenjeza kupitila m’Nkhani za m’Baibo, zofalitsa, komanso kupyolela m’malangizo ocokela kwa Akhristu anzathu. Tikamvela malangizo amenewa, iye amaticitila cifundo.

21. Kodi mudzacita ciani ngati mwayesedwa kuti musakhale wokhulupilika kwa Yehova?

21 Kukoma mtima kwa Yehova kuli na colinga. (2 Akor. 6:1) Kumatipatsa mwayi ‘wokana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko.’ (Ŵelengani Tito 2:11-14.) Popeza tikali “m’nthawi” yovuta, tidzapitiliza kukumana na mavuto amene adzayesa kukhulupilika kwathu kwa Yehova. Koma tiyeni tiimebe zolimba ku mbali yake, cifukwa ‘Yehova Mulungu wathu’ ndi amene tiyenela ‘kumuopa, kum’tumikila, ndi kum’mamatila’!—Deut. 10:20.