Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzichitira Chifundo Anthu “Kaya Akhale a Mtundu Wotani”

Muzichitira Chifundo Anthu “Kaya Akhale a Mtundu Wotani”

PAMENE Yesu ankaphunzitsa ophunzira ake ntchito yolalikira anawauza kuti anthu ena sadzawalandira bwino. (Luka 10:3, 5, 6) Choncho tikakhala mu utumiki tikhoza kukumana ndi anthu amene angatiyankhe mwachipongwe. Zoterezi zikachitika, zimakhala zovuta kuti tichitire chifundo anthu amene tikuwalalikira.

Munthu wachifundo amazindikira mavuto a anthu ena, kuwamvera chisoni komanso amayesetsa kuwathandiza. Choncho ngati tingasiye kuchitira chifundo anthu mu utumiki, tikhoza kuyamba mphwayi n’kusiya kulalikira mogwira mtima. Tikhoza kuyerekezera khama lathu mu utumiki ndi moto. Pamafunika kuwonjezera nkhuni kuti moto uziyakabe. N’chimodzimodzi ndi zimene tiyenera kuchita mu utumiki. Kuti tipitirize kuchita khama tiyenera kuwonjezera chifundo chimene timasonyeza anthu.​—1 Ates. 5:19.

Ndiye kodi tingatani kuti tizikhalabe achifundo ngakhale kuti nthawi zina zimavuta? Tiyeni tikambirane zitsanzo zabwino zitatu zimene tingatengere. Zitsanzo zake ndi za Yehova, Yesu komanso mtumwi Paulo.

TIZITSANZIRA CHIFUNDO CHA YEHOVA

Yehova wakhala akunyozedwa kwa zaka masauzande ambiri koma amakhalabe “wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.” (Luka 6:35) Iye amasonyeza chifundo chake pokhala woleza mtima. Yehova amafuna kuti “anthu kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke.” (1 Tim. 2:3, 4) Ngakhale kuti Mulungu amadana ndi zoipa, iye amaona kuti munthu aliyense ndi wamtengo wapatali moti safuna kuti afe.​—2 Pet. 3:9.

Yehova amadziwanso kuti Satana wachititsa khungu anthu ambiri. (2 Akor. 4:3, 4) Anthu ena akhala akuphunzitsidwa zinthu zabodza komanso maganizo oipa kuyambira ali aang’ono ndipo zimakhala zovuta kuti ayambe kuphunzira choonadi. Koma iye amafunitsitsa kuthandiza anthu ngati amenewo. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

Taganizirani mmene Yehova ankaonera anthu a ku Nineve. Ngakhale kuti anthuwo anali ankhanza, Yehova anauza Yona kuti: “Kodi ine sindikuyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Nineve, mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziwa kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere? Kodi sindiyenera kumveranso chisoni ziweto zambiri zimene zili mmenemo?” (Yona 4:11) Yehova ankaona kuti anthu a ku Nineve analibe mwayi womva uthenga wake choncho anawamvera chisoni n’kutuma Yona kuti akawachenjeze.

Nafenso tiyenera kuona kuti anthu onse ndi amtengo wapatali. Tizitsanzira Yehova n’kumafunitsitsa kuthandiza anthu ngakhale amene amaoneka kuti ndi ovuta.

TIZITSANZIRA CHIFUNDO CHA YESU

Mofanana ndi Yehova, Yesu ankamvera chisoni anthu amene analibe mwayi wophunzitsidwa za Yehova. Baibulo limanena kuti Yesu ataona “chikhamu cha anthu, iye anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Yesu ankaona mumtima mwa anthu ndipo anazindikira kuti anthu amene anabwera kudzamvetsera uthenga wake ankaphunzitsidwa zabodza komanso kuchitiridwa nkhanza ndi atsogoleri awo achipembedzo. Yesu ankadziwa kuti anthuwo sangalandire bwino uthenga wake pa zifukwa zosiyanasiyana koma sanasiye “kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”​—Maliko 4:1-9.

Tisamakhumudwe ngati munthu sanatilandire bwino pa ulendo woyamba

Anthu akhoza kumvetsera uthenga wathu zinthu zikasintha pa moyo wawo

Choncho anthu akatiyankha mwachipongwe mu utumiki tiyenera kuganizira zimene zawachititsa. Ena amakhala ndi maganizo olakwika okhudza Baibulo kapena Chikhristu chifukwa chakuti aona zinthu zoipa zimene anthu ena amene amati ndi Akhristu amachita. Pomwe ena amakhala atauzidwa zinthu zabodza zokhudza zimene timakhulupirira. Palinso ena amene satilandira bwino chifukwa choopa kunyozedwa ndi achibale awo kapena anzawo.

Anthu enanso amene timakumana nawo mu utumiki satilandira bwino chifukwa choti anakumana ndi vuto linalake limene likuwavutitsabe maganizo. Chitsanzo ndi mmishonale wina dzina lake Kim. Iye anati: “M’dera lina limene timalalikira muli anthu ambiri amene katundu wawo yense anawonongeka pa nthawi ya nkhondo. Iwo amaona kuti palibenso chabwino pa moyo wawo. Popeza anakhumudwa kwambiri, sakhulupirira aliyense. M’dera limeneli anthu ambiri samvetsera uthenga wabwino. Tsiku lina ndikulalikira munthu wina anandimenya.”

N’chiyani chimathandiza mlongoyu kuti azichitirabe chifundo anthu? Iye anati: “Anthu ena akandichitira zachipongwe mu utumiki ndimangokumbukira lemba la Miyambo 19:11 lomwe limati: ‘Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake.’ Kukumbukira zimene zinachitikira anthu a m’dera lathu kumandithandiza kuti ndiziwachitirabe chifundo. Komanso sikuti aliyense amene timakumana naye amakhala wolusa. M’dera lomweli tili ndi maulendo obwereza abwino kwambiri.”

Nthawi zina ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikanakhala iwowo ndikanatani munthu atabwera kudzandilalikira?’ Mwachitsanzo, tikanatani tikanakhala kuti tamva zinthu zambirimbiri zabodza zokhudza Mboni za Yehova? Mwina nafenso bwenzi tikukana kulalikiridwa ndipo tikanafunika kuchitiridwa chifundo. Tiyenera kukumbukira malangizo a Yesu akuti zimene tikufuna kuti anthu atichitire, ifenso tiziwachitira zomwezo. (Mat. 7:12) Tikatero tidzachitira chifundo anthu ngakhale pamene zili zovuta kwambiri.

TIZITSANZIRA CHIFUNDO CHA PAULO

Mtumwi Paulo ankachitira chifundo anthu ngakhale amene anali otsutsa komanso ankhanza. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Iye ankakumbukira zimene nayenso anachita m’mbuyomo. Paja iye analemba kuti: “Kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe. Komabe anandichitira chifundo chifukwa ndinali wosadziwa ndi wopanda chikhulupiriro.” (1 Tim. 1:13) Iye ankazindikira kuti Yehova ndi Yesu anamusonyeza chifundo chachikulu. Choncho akaona anthu ena akuvuta powalalikira ankangokumbukira zimene nayenso ankachita.

Nthawi zina Paulo ankakumana ndi anthu amene ankakhulupirira kwambiri mfundo zabodza. Ndiye kodi anatani? Lemba la Machitidwe 17:16 limafotokoza mmene Paulo anamvera atafika ku Atene. Limati: “Mtima unamuwawa kwambiri poona kuti mumzindawo mwadzaza mafano.” Ngakhale kuti zinkamupweteka, Paulo anawalalikirabe ndipo anawauza mokoma mtima za mafano amene ankalambirawo. (Mac. 17:22, 23) Iye ankasintha ulaliki wake kuti ugwirizane ndi anthu osiyanasiyana n’cholinga choti ‘mulimonse mmene zingakhalire apulumutseko ena.’​—1 Akor. 9:20-23.

Tingatsanzire Paulo pokhala omvetsa ngati anthu akukhulupirira zinthu zolakwika, kenako n’kuwafotokozera mwaluso “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yes. 52:7) Mlongo wina dzina lake Dorothy anati: “Anthu ambiri m’gawo lathu anaphunzitsidwa kuti Mulungu ndi wankhanza komanso wokonda kuweruza anthu. Ndikakumana ndi anthu oterewa ndimawayamikira chifukwa chokhulupirira kuti kuli Mulungu. Kenako ndimawauza zimene Baibulo limanena zoti Yehova ndi wachikondi ndipo watilonjeza zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo.”

“PITIRIZANI KUGONJETSA CHOIPA MWA KUCHITA CHABWINO”

Pamene mapeto akuyandikira, tiyenera kudziwa kuti makhalidwe a anthu ena amene timawalalikira “adzaipiraipirabe.” (2 Tim. 3:1, 13) Koma sitiyenera kulola zimenezi kutilepheretsa kukhala osangalala kapena kusonyeza chifundo. Yehova akhoza kutipatsa mphamvu kuti tipitirize “kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:21) Mpainiya wina dzina lake Jessica ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimakumana ndi anthu onyada omwe amatinyoza komanso kunyoza uthenga wathu. Zimenezi zikhoza kukhala zokhumudwitsa. Choncho ndisanayambe kukambirana ndi munthu ndimapemphera chamumtima kuti Yehova andithandize kumuona munthuyo mmene iye amamuonera. Izi zimandithandiza kuti ndisakwiye naye koma ndiziganizira mmene ndingamuthandizire.”

Tisasiye kufufuza anthu amene ali ndi maganizo oyenera moyo wosatha

Tikakhala oleza mtima, ena amayamba kumvetsera uthenga wathu

Tiyeneranso kuganizira mmene tingalimbikitsire atumiki anzathu. Jessica uja anati: “Wina wa ife akakumana ndi zinthu zokhumudwitsa mu utumiki sindikonda kulankhula kwambiri za zimenezo. Ndimangosintha nkhani kuti tizikamba zina zolimbikitsa. Mwachitsanzo, ndimangofotokoza zabwino zimene zimatheka chifukwa cholalikira ngakhale kuti anthu amatitsutsa.”

Yehova amadziwa bwino mavuto amene timakumana nawo mu utumiki. Ndipo amasangalala kwambiri tikamatsanzira chifundo chake. (Luka 6:36) Koma chifundo cha Yehova chili ndi malire ake. Choncho tisamakayikire kuti akudziwa bwino nthawi yoyenera kuwononga dziko loipali. Chofunika panopa n’kumalalikira mwakhama basi. (2 Tim. 4:2) Tiyeni tipitirize kugwira ntchito yathu mwakhama komanso tizichitira chifundo “anthu kaya akhale a mtundu wotani.”