Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzicitila Cifundo Anthu “Kaya Akhale a Mtundu Wotani”

Muzicitila Cifundo Anthu “Kaya Akhale a Mtundu Wotani”

PAMENE Yesu anali kuphunzitsa ophunzila ake kulalikila uthenga wabwino, anadziŵa kuti si anthu onse amene adzalabadila uthengawo. (Luka 10:3, 5, 6) Anthu ena amene timakumana nawo mu ulaliki amakhala aukali kapena acipongwe. Zinthu ngati zimenezi zingacititse kuti cikhale covuta kupitiliza kuonetsa cifundo kwa anthu amene timawalalikila.

Munthu wacifundo amaona zosoŵa za ena na mavuto awo, amawamvela cisoni, ndipo amafuna kuwathandiza. Ngati cifundo cimene tili naco pa anthu amene timawalalikila cayamba kucepa, cangu na luso lathu mu ulaliki zimayambanso kucepa. Koma ngati tiyesetsa kukulitsa khalidwe la cifundo, zimakhala ngati tikuwonjezela nkhuni pa moto. Cangu cathu mu ulaliki cimapitiliza kuyaka ngati moto.—1 Ates. 5:19.

Kodi tingakulitse bwanji khalidwe la cifundo olo kuti nthawi zina zimakhala zovuta kutelo? Tiyeni tikambilane zitsanzo zitatu zimene tiyenela kutengela—ca Yehova, Yesu, na mtumwi Paulo.

TENGELANI CIFUNDO CA YEHOVA

Kwa zaka masauzande ambili, Yehova wakhala akupilila kunyozedwa kwa dzina lake. Komabe, iye amaonetsabe ‘cifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.’ (Luka 6:35) Yehova waonetsa cifundo cake mwa kukhala woleza mtima. Iye amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani”, akapulumuke. (1 Tim. 2:3, 4) Olo kuti Mulungu amazonda zoipa, amaona anthu kukhala amtengo wapatali kwambili ndipo safuna kuti aliyense akawonongeke.—2 Pet. 3:9.

Yehova amadziŵa kuti Satana wacititsa khungu anthu osakhulupilila. (2 Akor. 4:3, 4) Ambili a iwo akhala akuphunzitsidwa zikhulupililo zabodza na makhalidwe oipa kungoyambila ali ana. Izi zacititsa kuti cikhale covuta kwa iwo kulandila coonadi. Koma Yehova ni wofunitsitsa kuwathandiza. Tidziŵa bwanji zimenezi?

Ganizilani mmene Yehova anali kuonela anthu a ku Nineve. Olo kuti anthu a kumeneko anali aciwawa kwambili, Yehova anauza Yona kuti: “Kodi ine sindikuyenela kumvela cisoni mzinda waukulu wa Nineve, mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziŵa kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzele?” (Yona 4:11) Yehova anadziŵa kuti Anineve sanali kudziŵa coonadi ponena za iye, ndipo powamvela cifundo, anatuma Yona kuti akawacenjeze.

Mofanana na Yehova, na ise timaona anthu kukhala amtengo wapatali. Ndipo tingatengele citsanzo cake mwa kuyesetsa kulalikila kwa aliyense, olo amene aoneka kuti sangalabadile.

TENGELANI CIFUNDO CA YESU

Mofanana ndi Atate wake, Yesu nayenso anali kumvela cifundo anthu amene anali na njala yauzimu. Malemba amati: “Poona cikhamu ca anthu, iye anawamvela cisoni, cifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Yesu anadziŵa cifukwa cake anthuwo anali otayika ndi onyukanyuka mwauzimu. Atsogoleli awo acipembedzo anali kuwaphunzitsa mabodza na kuwapondeleza. Ngakhale kuti Yesu anali kudziŵa kuti ambili mwa iwo sadzalabadila uthenga wake, iye anapitilizabe “kuwaphunzitsa zinthu zambili.”—Maliko 4:1-9.

Musakhumudwe ngati munthu sanaonetse cidwi pa ulendo woyamba

Munthu amene poyamba sanalabadile coonadi, m’kupita kwa nthawi angalabadile cifukwa ca kusintha kwa zinthu mu umoyo wake

Ngati anthu sanalabadile uthenga wathu, tiyenela kuganizila zimene zawacititsa kuti asamvetsele. Ena salabadila kaamba kakuti amakayikila Baibo na Cikhristu cifukwa cokhumudwa na zinthu zoipa zimene anthu ena odzicha Akhristu amacita. Enanso samvetsela cifukwa cakuti anauzidwa mabodza ponena za zikhulupililo zathu. Komanso, ena salandila uthenga wathu poopa kunyozedwa ndi anthu a m’dela lawo kapena abululu awo.

Anthu ena amene timakumana nawo mu ulaliki amakana kumvetsela cifukwa cakuti m’mbuyomo anakumanapo na mavuto ena aakulu. Mmishonale wina, dzina lake Kim, anati: “Mbali ina m’gawo lathu, anthu ambili anakumana na mavuto aakulu cifukwa ca nkhondo moti anatayikilidwa katundu wawo yense. Iwo amadziona kuti alibe ciyembekezo ciliconse. Ni aukali ndipo amakayikila munthu aliyense. M’dela limenelo, nthawi zambili timakumana ndi anthu otsutsa uthenga wathu. Tsiku lina, n’namenyedwa pamene n’nali kulalikila.”

N’ciani cimathandiza Kim kupitiliza kuonetsa cifundo mosasamala kanthu za mavuto amenewa? Iye anati: “Nikakumana ndi anthu aukali, nimayesetsa kukumbukila lemba la Miyambo 19:11, imene imati: ‘Kuzindikila kumacititsa munthu kubweza mkwiyo wake.’ Kukumbukila mavuto amene anthu m’dela lathu apitamo, kumanithandiza kupitiliza kuwaonetsa cifundo. Koma sikuti anthu onse amene timakumana nawo ni aukali. M’dela limodzi-modzilo, muli anthu acidwi amene timacitako maulendo obwelelako.”

Tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Nikanakhala kuti si ndine Mboni ndipo anthu abwela kudzanilalikila, kodi nikanamvetsela uthenga wa Ufumu?’ Mwacitsanzo, kodi mukanamvetsela mukanakhala kuti munauzidwa mabodza mobweleza-bweleza okhudza Mboni za Yehova? Mwina sitikanamvetsela, ndipo pakanafunika kuti olalikilawo aticitile cifundo. Conco, tizikumbukila lamulo la Yesu lakuti tiyenela kucitila anthu zimene tifuna kuti iwo aticitile. Kukumbukila lamuloli kudzatilimbikitsa kuonetsa cifundo ngakhale pamene zinthu zili zovuta.—Mat. 7:12.

TENGELANI CIFUNDO CA PAULO

Mtumwi Paulo anali kucitila cifundo ngakhale anthu amene anali kum’tsutsa mwaciwawa. Cifukwa ciani? Cifukwa sanaiŵale mmene iye analili poyamba. Paulo anati: “Kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wacipongwe. Komabe anandicitila cifundo cifukwa ndinali wosadziŵa ndi wopanda cikhulupililo.” (1 Tim. 1:13) Iye anali kudziŵa kuti Yehova na Yesu anamuonetsa cifundo cacikulu. Paulo anaona kuti ena mwa anthu amene anali kuwalalikila anali na makhalidwe monga amene iye anali nawo poyamba.

Nthawi zina, Paulo anali kulalikila anthu okhala na zikhulupililo zabodza zozika mizu kwambili. Kodi iye anali kumvela bwanji? Lemba la Machitidwe 17:16 limati, pamene Paulo anali ku Atene, ‘mtima unamuwawa kwambili poona kuti mumzindawo munali modzala mafano.’ Komabe, kuyambila pa zinthu zomwezo zimene zinam’pweteka mtima, Paulo anacitila umboni mogwila mtima. (Mac. 17:22, 23) Anali kusintha-sintha ulaliki wake kuti ugwilizane ndi anthu amene anali kuwalalikila, n’colinga cakuti ‘mulimonse mmene zikanakhalila apulumutseko ena.’—1 Akor. 9:20-23.

Tingatengele citsanzo ca Paulo mwa kuvomeleza maganizo olakwika na zikhulupililo zabodza za anthu amene tawafikila, kenako mwaluso tingayambe kuwalalikila “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yes. 52:7) Mlongo wina, dzina lake Dorothy, anati: “M’gawo lathu, ambili amaphunzitsidwa kuti Mulungu ni wankhanza komanso wokonda kupeza ena zifukwa. Coyamba, nimawayamikila anthu aconco cifukwa cokhulupilila Mulungu. Ndiyeno nimawaonetsa zimene Baibo imakamba zosonyeza kuti Yehova ni wacikondi. Nimawafotokozelanso zimene iye walonjeza.”

“PITILIZANI KUGONJETSA COIPA MWA KUCITA CABWINO”

Pamene tikuyandikila ku mapeto kwa “masiku otsiliza,” makhalidwe a anthu ena amene timawalalikila “adzaipilaipilabe.” (2 Tim. 3:1, 13) Koma tisalole zimenezi kutilepheletsa kukhala acifundo kapena kutilanda cimwemwe cathu. Yehova angatipatse mphamvu kuti tipitilize “kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino.” (Aroma 12:21) Mpainiya wina, dzina lake Jessica, anati: “Nthawi zambili nimakumana ndi anthu odzitukumula, amene amatinyoza komanso kusuliza uthenga wathu. Izi zingakhale zokhumudwitsa. Conco, nikayamba kulalikila, nimapemphela ca mumtima kwa Yehova. Nimam’pempha kuti anithandize kuona munthuyo mmene iye amamuonela. Izi zimanithandiza kuti nisamangoganizila zinthu zokhumudwitsa zimene angacite, koma kuti niziganizila za mmene ningamuthandizile.”

Sitileka kufuna-funa anthu a maganizo oyenela amene angawathandize kukapeza moyo wosatha

Anthu ena angalabadile tikapitiliza kuwalalikila moleza mtima

Tiyenelanso kuganizila mmene tingalimbikitsile ofalitsa anzathu. Jessica anati: “Wina wa ise akakumana na zinthu zosakondweletsa mu ulaliki, nimapewa kukamba kwambili pa zimenezo. M’malomwake, nimayamba kukamba nkhani zina zolimbikitsa. Mwacitsanzo, nimakamba zinthu zabwino zimene utumiki wathu umakwanilitsa ngakhale kuti anthu ena salabadila.”

Yehova amadziŵa bwino mavuto amene timakumana nawo mu ulaliki. Iye amakondwela ngako akaona kuti tikutengela cifundo cake. (Luka 6:36) Koma sikuti Yehova adzapitiliza kucitila cifundo anthu oipa mpaka kale-kale. Tili na cikhulupilillo cakuti, pa nthawi yake yoyenela, iye adzawononga dongosolo loipali. Koma pali pano, tiyenela kugwila nchito yathu yolalikila mwacangu. (2 Tim. 4:2) Inde, tiyeni tipitilize kugwila nchito yathu mokangalika, ndipo tizicitila cifundo “anthu, kaya akhale a mtundu wotani.”