Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Opatsa Mowoloŵa Manja Amakhala Acimwemwe

Opatsa Mowoloŵa Manja Amakhala Acimwemwe

“Kupatsa kumabweletsa cimwemwe.”—MAC. 20:35.

NYIMBO: 76, 110

1. Kodi zolengedwa zimaonetsa bwanji kuti Yehova ni wowolowa manja?

YEHOVA anali yekha-yekha asanayambe kulenga zinthu. Kenako analenga angelo na anthu, nowapatsa mphatso ya moyo. Yehova, “Mulungu wacimwemwe,” amakonda kupatsa ena zinthu zabwino. (1 Tim. 1:11; Yak. 1:17) Ndipo popeza kuti amafuna kuti na ise tizikhala acimwemwe, amatiphunzitsa kukhala owoloŵa manja.—Aroma 1:20.

2, 3. (a) N’cifukwa ciani kupatsa kumabweletsa cimwemwe? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

2 Mulungu analenga anthu m’cifanizilo cake. (Gen. 1:27) Izi zitanthauza kuti tinalengedwa kuti tizitha kuonetsa makhalidwe monga ake. Conco, kuti tikhale acimwemwe, tiyenela kutengela Yehova mwa kukhala oganizila ena ndi opatsa mowolowa manja. (Afil. 2:3, 4; Yak. 1:5) N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa ni mmene Yehova anatilengela. Olo kuti ndise opanda ungwilo, tingatengele khalidwe la Yehova la kuwolowa manja.

3 Baibo imafotokoza mmene tingakhalile owolowa manja. Lomba tiyeni tikambilane mfundo zina zimene Malemba amaphunzitsa pankhaniyi. Tidzakambilananso mmene kukhala owolowa manja kumathandizila kuti Mulungu atiyanje, komanso mmene kumatithandizila pa nchito imene iye watipatsa. Tidzaonanso mmene kuwolowa manja kumatithandizila kukhala acimwemwe, komanso cifukwa cake tifunika kupitiliza kukulitsa khalidwe limeneli.

ZIMENE TINGACITE KUTI MULUNGU ATIYANJE

4, 5. Kodi Yehova na Yesu anatipatsa citsanzo canji pa nkhani ya kuwolowa manja?

4 Yehova amafuna kuti tizitengela citsanzo cake. Iye amakondwela tikakhala owolowa manja. (Aef. 5:1) Tikaona mmene Mulungu anatilengela, komanso zinthu zambili zokongola zimene analenga, n’zosacita kufunsa kuti iye amafuna kuti tizikhala acimwemwe. (Sal. 104:24; 139:13-16) Conco, Mulungu amalemekezeka ngati tiyesetsa kucita zinthu zokondweletsa ena.

5 Akhristu oona amatengela Khristu, amene anatipatsa citsanzo cabwino ngako pankhani ya kuwolowa manja. Yesu anakamba kuti: “Mwana wa munthu sanabwele kudzatumikilidwa, koma kudzatumikila ndi kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.” (Mat. 20:28) N’cifukwa cake mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo . . . Anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo.” (Afil. 2:5, 7) Ndiyeno tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi n’ciani cina cimene ningacite coonetsa kuti nikutsatila citsanzo ca Yesu mosamala kwambili?’—Ŵelengani 1 Petulo 2:21.

6. Kodi fanizo la Yesu la Msamariya wacifundo limatiphunzitsa ciani? (Onani pikica kuciyambi.)

6 Yehova angatiyanje ngati titengela citsanzo cake cabwino, komanso ca Khristu pankhani ya kuwolowa manja. Tingacite izi mwa kukhala oganizila ena na kupeza njila zowathandizila pa zosoŵa zawo. Zimene Yesu anakamba m’fanizo la Msamariya wacifundo, zionetselatu kuti ophunzila ake ayenela kukhala odzipeleka pothandiza anthu ena, kaya akhale a mtundu wotani. (Ŵelengani Luka 10:29-37.) Kodi mukumbukila funso imene inacititsa Yesu kukamba fanizo la Msamariya wacifundo? Myuda wina anamufunsa kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenela kumukonda ndani kwenikweni?” Yankho imene Yesu anapeleka ionetsa kuti ngati tifuna kuti Mulungu atiyanje, tiyenela kukhala ofunitsitsa kuthandiza ena mmene Msamariya wacifundo anacitila.

7. Ni nkhani yanji imene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni? Nanga tingaonetse bwanji kuti timakhulupilila kuti zimene Mulungu amatiuza ndiye zabwino koposa?

7 Akhristu ali na zifukwa zambili zabwino zokhalila owolowa manja. Mwacitsanzo, khalidwe limeneli limakhudzana ndi nkhani imene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni. Motani? Satana anaonetsa kuti Adamu na Hava, kuphatikizapo anthu onse, angakhale na umoyo wacimwemwe ngati aika zofuna zawo patsogolo m’malo momvela Mulungu. Hava anacimwa cifukwa ca mtima wadyela wofuna kukhala wofanana na Mulungu. Komanso Adamu anaonetsa mtima wadyela mwa kuphwanya lamulo la Mulungu kuti akondweletse Hava, mkazi wake. (Gen. 3:4-6) Zotulukapo zake n’zosacita kufunsa. Kukhala na mtima wadyela kumabweletsa mavuto, osati cimwemwe. Koma tikakhala owolowa manja, timaonetsa kuti timakhulupilila kuti zimene Mulungu amatiuza kucita ndiye zabwino koposa.

TIZIGWILA NCHITO IMENE MULUNGU WATIPATSA

8. N’cifukwa ciani mwamuna na mkazi oyambilila anafunika kucita zinthu moganizila ena?

8 Mulungu anapatsa mwamuna na mkazi oyambilila malangizo amene akanawathandiza kucita zinthu moganizila ena. N’zoona kuti panthawiyo anali aŵili cabe m’munda wa Edeni. Koma Yehova anawadalitsa na kuwauza kuti abalane, adzadze dziko lapansi, na kuliyang’anila. (Gen. 1:28) Mlengi wathu anaonetsa kuti anali kuganizila za ubwino wa zolengedwa zake. Conco, nawonso makolo athu oyambilila anafunika kuganizila tsogolo la ana awo amene anali kudzabadwa m’tsogolo. Mulungu anali kufuna kuti dziko lonse lidzakhale paradaiso kuti Adamu ndi ana ake adzakhalemo mosangalala. Adamu na Hava akanakwanitsa kugwila nchito yopanga dziko lonse kukhala Paradaiso, mothandizidwa ndi ana awo amene anali kudzabadwa m’tsogolo.

9. Kodi kugwila nchito yopanga dziko lonse kukhala Paradaiso kukanathandiza bwanji anthu kukhala acimwemwe?

9 Adamu na Hava akanapanda kucimwa, dziko lapansi likanadzala na anthu angwilo okha-okha. Anthu angwilo amenewo akanafunika kucita zinthu mogwilizana kwambili na Yehova kuti akwanilitse colinga cake copanga dziko lonse kukhala paradaiso. Kucita izi kukanawapatsa mwayi woloŵa mu mpumulo wa Mulungu. (Aheb. 4:11) Ndithudi, nchito imeneyo ikanakhala yopatsa cimwemwe ngako. Ndipo Yehova akanawadalitsa kwambili cifukwa ca mtima wawo wopanda dyela ndi woganizila ena.

10, 11. Tingacite ciani kuti tikwanitse kugwila nchito yolalikila na kupanga ophunzila imene tinapatsidwa?

10 Masiku ano, Yehova wapatsa anthu ake nchito yolalikila na kupanga ophunzila. Kuti tikwanitse kugwila nchitoyi, tiyenela kukhala na mtima woganizila ena. Tingapitilize kugwila nchitoyi mwakhama kokha ngati timakondadi Mulungu na anthu anzathu.

11 M’nthawi ya atumwi, Paulo anakamba kuti iye na Akhristu anzake anali “anchito anzake a Mulungu” cifukwa ca nchito yawo yofesa na kuthilila mbeu za coonadi. (1 Akor. 3:6, 9) Na ise masiku ano, tingaonetse kuti ndise “anchito anzake a Mulungu” mwa kuseŵenzetsa mowolowa manja nthawi yathu, cuma, na mphamvu zathu pa nchito yolalikila imene tapatsidwa. Kukamba zoona, umenewu ni mwayi waukulu ngako!

Kuthandiza anthu oona mtima kumvetsetsa coonadi ca m’Baibo n’kokondweletsa kwambili (Onani palagilafu 12)

12, 13. Kodi muona kuti nchito yopanga ophunzila imabweletsa madalitso anji?

12 Kuseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu mowolowa manja pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila kumabweletsa cimwemwe coculuka. Ofalitsa ambili amene anakhalapo na mwayi wotsogoza maphunzilo a Baibo opita patsogolo, angakuuzeni kuti kucita zimenezi n’kokondweletsa kwambili. Cimakhala cokondweletsa ngako kuona nkhope za anthu oona mtima zikuwala na cimwemwe, pambuyo pomvetsetsa mfundo za coonadi ca m’Baibo. Zimakondweletsanso kuwaona akukula m’cikhulupililo, akusintha umoyo wawo, na kuyamba kuuzako ena coonadi cimene aphunzila. Yesu nayenso anakondwela kwambili pamene ophunzila 70 amene anawatumiza kukalalikila “anabwelela ali osangalala,” cifukwa utumiki wawo unayenda bwino.—Luka 10:17-21.

13 Ofalitsa padziko lonse amakondwela akaona mmene uthenga wabwino ukuthandizila anthu mu umoyo wawo. Ganizilani citsanzo ca mlongo wina wacicepele, dzina lake Anna. Iye anawonjezela utumiki wake mwa kukukila ku dziko lina la ku Eastern Europe, kumene kuli ofalitsa ufumu ocepa. * Mlongoyo anati: “Kuno tili na mwayi wotsogoza maphunzilo a Baibo ambili, ndipo izi zimanikondweletsa maningi. Nimasangalala kwambili na utumiki kuno. Nikakomboka mu ulaliki na kupita ku nyumba sinikhala na nthawi yomangoganizila zofuna zanga. Koma nimaganizila za anthu amene nimaphunzila nawo Baibo. Nimaganizila za mavuto awo na nkhawa zawo. Ndiyeno nimayesetsa kuganizila zimene ningacite kuti niwalimbikitse nowathandiza. Lomba natsimikiza kuti ‘kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.’”—Mac. 20:35.

Ngati tiyesetsa kulalikila pa nyumba iliyonse m’gawo lathu, timapatsa anthu mwayi wolabadila uthenga wa Ufumu (Onani palagilafu 14))

14. Ngati ni anthu ocepa amene amalabadila uthenga wathu, tingacite ciani kuti tizikhalabe acimwemwe mu ulaliki?

14 Timapeza cimwemwe cifukwa copatsa anthu mwayi wolabadila uthenga wabwino, olo kuti ena safuna kumvetsela. Nchito yathu masiku ano ni yolingana na imene mneneli Ezekieli anapatsidwa. Yehova anamuuza kuti: “Ukawauze mau anga, kaya akamva kapena ayi.” (Ezek. 2:7; Yes. 43:10) Kaya anthu amvetsele uthenga wathu kapena ayi, Yehova amayamikila khama lathu. (Ŵelengani Aheberi 6:10.) M’bale wina anaonetsa kuti ali na maganizo abwino pa nkhaniyi. Pokamba za utumiki wake, iye analemba kuti: “Timafesa mbeu za coonadi, kuthilila, na kupemphela tili na cikhulupililo cakuti Yehova adzakulitsa cidwi ca anthu amene tawalalikila.”—1 Akor. 3:6.

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUKHALA ACIMWEMWE

15. Kodi tiyenela kukhala owolowa manja kokha ngati anthu amayamikila? Fotokozani.

15 Yesu amafuna kuti tipeze cimwemwe mwa kukhala owolowa manja. Anthu ambili amayamikila tikawapatsa mowolowa manja. Yesu anati: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani. Adzakhuthulila m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendeleka, wokhuchumuka ndi wosefukila.” (Luka 6:38) N’zoona kuti si onse amene amayamikila tikawapatsa mowolowa manja. Koma akakhala na mtima woyamikila, nawonso amasonkhezeleka kukhala owolowa manja. Conco, khalani owolowa manja, kaya anthu aoneke kuti ayamikila kapena ayi. Simungadziŵe mmene kuwolowa manja kwanu kungakhudzile ena.

16. Kodi tifunika kuonetsa kuwolowa manja kwa ndani? Ndipo n’cifukwa ciani?

16 Anthu owolowa manja sapatsa ena zinthu n’colinga cakuti anthuwo adzawabwezele zinazake m’tsogolo. Yesu anali kuganizila mfundo imeneyi pamene anati: “Ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu. Ukatelo udzakhala wodala, cifukwa alibe coti adzabweze kwa iwe.” (Luka 14:13, 14) Lemba lina limati: “Wa diso labwino [“munthu wowolowa manja”, NWT] adzadalitsidwa.” Linanso limati: “Wodala ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka.” (Miy. 22:9; Sal. 41:1) Conco, tiyenela kukhala opatsa cifukwa cakuti kuthandiza ena kumatikondweletsa.

17. Kupatsa kumabweletsa cimwemwe. Koma kumaphatikizapo kupatsa ciani?

17 Pa nthawi ina, mtumwi Paulo anagwila mau a Yesu akuti “kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” Pa nthawiyo, iye sanali kukamba za kupatsa ena zinthu zakuthupi cabe, koma anali kukambanso za kupatsa ena cilimbikitso, malangizo, komanso thandizo kwa amene akufunikila zinthu zimenezi. (Mac. 20:31-35) Mwa mau na citsanzo cake, mtumwiyu anatiphunzitsa kuti tiyenela kudzipeleka pothandiza ena mwa kuseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu, komanso kuwalimbikitsa na kuwaonetsa cikondi.

18. Kodi akatswili ena anakamba ciani pa nkhani ya kuwolowa manja?

18 Akatswili a za cikhalidwe ca anthu nawonso azindikila kuti kupatsa kumathandiza anthu kukhala acimwemwe. Nkhani ina inati, “anthu amakhala acimwemwe kwambili akacitila ena zabwino.” Akatswiliwo amakamba kuti kuthandiza ena n’kofunika kuti munthu akhale na umoyo “waphindu na wokhutilitsa, cifukwa kumakwanilitsa zosoŵa zazikulu za anthu.” Ndiye cifukwa cake nthawi zambili akatswili amalimbikitsa anthu kuti azidzipeleka pa nchito zacitukuko kuti akhale na thanzi labwino komanso acimwemwe. Izi n’zosadabwitsa kwa ise amene timakhulupilila Baibo, imene ni Mau a Mlengi wathu wacikondi, Yehova.—2 Tim. 3:16, 17.

KHALANIBE OWOLOWA MANJA

19, 20. Kodi mwatsimikiza mtima kukhala owolowa manja? Cifukwa ciani?

19 Zingakhale zovuta kukhala owolowa manja cifukwa anthu ambili amene timakhala nawo amaika zofuna zawo patsogolo, osati za ena. Koma Yesu anakamba kuti lamulo lalikulu kwambili limene tifunika kutsatila ni kukonda Yehova na mtima wathu wonse, moyo, nzelu, na mphamvu zathu zonse. Ndipo lina lolingana nalo ni kukonda anzathu monga mmene timadzikondela tekha. (Maliko 12:28-31) M’nkhani ino, taphunzila kuti anthu amene amakonda Yehova amatengela citsanzo cake. Yehova na Yesu ni owolowa manja. Ndipo amafuna kuti na ise tikhale owolowa manja. Kucita zimenezi kudzatibweletsela cimwemwe ceni-ceni. Ngati tiyesetsa kukhala owolowa manja potumikila Mulungu, komanso pothandiza anthu anzathu, Yehova adzalemekezeka. Kuwonjezela apo, tidzapindula na kupindulitsanso ena.

20 Mwacionekele, na imwe mumayesetsa kuthandiza ena, maka-maka Akhristu anzanu. (Gal. 6:10) Mukapitiliza kucita zimenezi, anthu adzakuyamikilani komanso adzakukondani. Ndipo mudzakhala acimwemwe. Miyambo 11:25 imati: “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandila mphoto, ndipo wothilila ena mosaumila nayenso adzathililidwa mosaumila.” Inde, kuwolowa manja na kukoma mtima tingakuonetse m’njila zambili mu utumiki wathu, komanso mu umoyo wathu wacikhristu. Ndipo tikatelo, tidzapeza madalitso ambili. M’nkhani yokonkhapo, tidzakambilana njila zina zimene tingaonetsele kuwolowa manja.

^ par. 13 Dzina lasinthidwa.