Anthu Opatsa Amakhala Osangalala

Anthu Opatsa Amakhala Osangalala

“Kupatsa kumabweretsa chimwemwe.”​—MAC. 20:35.

NYIMBO: 76, 110

1. Kodi zinthu zimene Yehova analenga zimasonyeza bwanji kuti iye ndi wopatsa?

YEHOVA asanayambe kulenga zinthu anali yekhayekha. Koma sikuti ankangoganiza za iye yekha basi. Tikutero chifukwa anapereka mphatso ya moyo kwa anthu komanso angelo. Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe,” amakonda kupatsa ena zinthu zabwino. (1 Tim. 1:11; Yak. 1:17) Iye amafuna kuti nafenso tizisangalala, choncho amatiphunzitsa kuti tizikhala opatsa.​—Aroma 1:20.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani timasangalala tikakhala opatsa? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake. (Gen. 1:27) Izi zikutanthauza kuti iye anatilenga mwanjira yakuti tizitha kusonyeza makhalidwe ake. Choncho kuti tizikhala osangalala, tikuyenera kutsatira chitsanzo cha Yehova poganizira za anthu ena komanso kukhala opatsa. (Afil. 2:3, 4; Yak. 1:5) Zili choncho chifukwa umu ndi mmene Yehova anatilengera. Ngakhale kuti si ife angwiro, tikhoza kutsanzira Yehova pa nkhani yopatsa.

3 Baibulo limanena zimene tingachite kuti tikhale opatsa. Tiyeni tikambirane zimene Malemba amaphunzitsa pa nkhaniyi. Tiona chifukwa chake kukhala opatsa kumachititsa kuti Mulungu azisangalala nafe komanso mmene kungatithandizire kukwaniritsa udindo umene Mulungu anatipatsa. Tionanso mmene kupatsa kumatithandizira kukhala osangalala ndiponso chifukwa chake tikuyenera kuyesetsabe kusonyeza khalidweli.

KODI TINGATANI KUTI TIZISANGALATSA MULUNGU?

4, 5. Kodi Yehova ndi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani yopatsa?

4 Yehova amafuna kuti anthufe tizimutsanzira, choncho amasangalala tikakhala opatsa. (Aef. 5:1) Timadziwa kuti Mulungu amafuna kuti anthu azikhala osangalala tikaganizira mmene anatilengera komanso tikaona zinthu zambiri zokongola ndiponso zodabwitsa zimene analenga. (Sal. 104:24; 139:13-16) Choncho timasonyeza kuti timamulemekeza tikamayesetsa kuthandiza ena kukhala osangalala.

5 Akhristu enieni amatsanzira Khristu yemwe anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yopatsa. Paja Yesu ananena kuti: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mat. 20:28) N’chifukwa chake mtumwi Paulo anauza Akhristu kuti: ‘Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo. Iye anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo, ndi kukhala wofanana ndi anthu.’ (Afil. 2:5, 7) Tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndizitsanzira kwambiri Yesu?’​—Werengani 1 Petulo 2:21.

6. Kodi Yesu anatiphunzitsa chiyani m’fanizo la Msamariya wachifundo? (Onani chithunzi choyambirira.)

6 Yehova amasangalala nafe tikamatsatira chitsanzo chake komanso cha Khristu pokhala ndi mtima woganizira anthu ena ndiponso wofunitsitsa kuwathandiza. Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la Msamariya wachifundo posonyeza kuti otsatira ake ayenera kudzipereka pothandiza anthu ena, ngakhale amene amasiyana nawo mtundu. (Werengani Luka 10:29-37.) Kodi mukukumbukira funso limene linachititsa Yesu kuti afotokoze fanizoli? Myuda wina anamufunsa kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?” Yankho la Yesu limasonyeza kuti tiyenera kukhala ofunitsitsa kuthandiza anthu ngati mmene anachitira Msamariyayo kuti Mulungu azisangalala nafe.

7. Kodi kuchita zinthu modzikonda kumagwirizana bwanji ndi nkhani imene Satana anayambitsa?

7 Pali zifukwa zomveka zochititsa Akhristu kuti azikhala opatsa. Mwachitsanzo, khalidweli likugwirizana ndi nkhani imene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni. Tikutero chifukwa chakuti Satana anasonyeza kuti Adamu ndi Hava, komanso anthu onse, akhoza kukhala osangalala ngati atamangoganizira zofuna zawo osati za Mulungu. Hava anachita zinthu modzikonda chifukwa chofuna kufanana ndi Mulungu. Nayenso Adamu anachita zinthu modzikonda chifukwa chongofuna kusangalatsa Hava. (Gen. 3:4-6) Tonsefe timaona zotsatira za zimene anachitazo. Choncho n’zosachita kufunsa kuti munthu akamachita zinthu modzikonda sakhala wosangalala. Koma tikamakhala opatsa timasonyeza kuti timakhulupirira ndi mtima wonse kuti kuchita zimene Mulungu amafuna n’kothandiza kwambiri.

TIZIKWANIRITSA UDINDO UMENE MULUNGU WATIPATSA

8. N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava anafunika kukhala ndi mtima wopatsa?

8 Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava malangizo amene akanawathandiza kuganizira za ena ngakhale kuti pa nthawiyo anali awiriwiri m’munda wa Edeni. Yehova anawadalitsa n’kuwauza kuti aberekane, adzaze dziko lapansi ndi kuliyang’anira. (Gen. 1:28) Popeza Yehova ankaganizira anthu amene anawalenga, Adamu ndi Hava anafunikanso kuchita zinthu moganizira ana amene adzabereke. Yehova anafuna kuti dziko lonse likonzedwe kuti likhale paradaiso n’cholinga choti ana onse a Adamu adzakhale osangalala. Kuti zimenezi zitheke panafunika kuti banja lonse lizichita zinthu mogwirizana.

9. Kodi kukonza dziko kuti likhale paradaiso kukanathandiza bwanji kuti anthu akhale osangalala?

9 Anthu angwirowa anayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi Yehova kuti akwaniritse cholinga chake komanso akonze dziko kuti likhale paradaiso. Zimenezi zikanawathandizanso kuti alowe mu mpumulo wake. (Aheb. 4:11) Kunena zoona akanasangalala kwambiri kugwira ntchito imeneyi. Mtima wofuna kuthandiza enawu ukanawathandiza kuti adalitsidwe komanso azikhala osangalala.

10, 11. Kodi tingatani kuti tizigwira bwino ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu?

10 Masiku ano, Yehova watipatsa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Kuti tigwire bwino ntchitoyi tiyenera kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza anthu ena. Kukonda Mulungu komanso anzathu n’kumene kungatithandize kuti tipitirize kugwira ntchitoyi.

11 Paulo ananena kuti iye ndi anzake anali “antchito anzake a Mulungu” chifukwa chakuti ankagwira ntchito yodzala komanso kuthirira mbewu za Ufumu. (1 Akor. 3:6, 9) Ifenso tingakhale “antchito anzake a Mulungu” tikamagwiritsa ntchito nthawi yathu, zinthu zathu komanso mphamvu zathu pa ntchito yolalikira imene Mulungu watipatsa. Kunena zoona umenewu ndi mwayi waukulu kwambiri.

Timasangalala kwambiri tikamathandiza anthu ena kuti amvetse mfundo za m’Baibulo (Onani ndime 12)

12, 13. N’chifukwa chiyani mumaona kuti ntchito yolalikira ndi yosangalatsa?

12 Timasangalala kwambiri tikamagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu polalikira ndi kuphunzitsa anthu. Abale ndi alongo amene akhala akuphunzitsa anthu n’kumawaona akusintha akhoza kukuuzani zinthu zosangalatsa zimene zimachitika pogwira ntchitoyi. Zimakhala zosangalatsa kwambiri kuona anthu akumvetsa mfundo za m’Baibulo, kuzikhulupirira kwambiri, kusintha moyo wawo komanso kuyamba kuuza ena zimene amaphunzira. Yesu anasangalala kwambiri ataona kuti anthu 70 amene anawatumiza kukalalikira abwera “ali osangalala” chifukwa choti ntchito yawo inayenda bwino.​—Luka 10:17-21.

13 Abale ndi alongo padziko lonse amasangalala kwambiri kuona kuti uthenga wabwino ukuthandiza anthu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wachitsikana dzina lake Anna. * Mlongoyu anasamukira kudera lina lakum’mawa kwa Europe, komwe kukufunika ofalitsa ambiri. Iye analemba kuti: “Ndimasangalala kwambiri kutumikira kuno chifukwa kuli anthu ambiri amene amafuna kuphunzira Baibulo. Ndikafika kunyumba ndimaganizira kwambiri za mavuto a anthu amene ndimaphunzira nawo moti sindikhala ndi nthawi yambiri yomangoganizira mavuto anga. Ndimayesetsa kupeza njira zowathandizira komanso kuwalimbikitsa. Panopa ndazindikira kuti ‘kupatsa kumabweretsadi chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.’”​—Mac. 20:35.

Tikamapita kunyumba iliyonse m’gawo lathu timapatsa anthu mwayi womva uthenga wa Ufumu (Onani ndime 14)

14. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalalabe ngakhale pamene anthu sakumvetsera uthenga wathu?

14 Zimakhala zosangalatsa tikamapereka mwayi kwa anthu woti amve uthenga wabwino ngakhale kuti nthawi zina amakana. Ndipotu ntchito yathu masiku ano ikufanana ndi ya Ezekieli amene anauzidwa ndi Yehova kuti: “Ukawauze mawu anga, kaya akamva kapena ayi.” (Ezek. 2:7; Yes. 43:10) Kaya anthu amvetsere kapena ayi, Yehova amayamikira zimene timachita. (Werengani Aheberi 6:10.) Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi wofalitsa wina amene analemba kuti: “Takhala tikudzala, kuthirira komanso kupempha Yehova kuti akulitse chidwi cha anthu amene timawalalikira.”​—1 Akor. 3:6.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIKHALA OSANGALALA

15. Kodi anthu ena amatani akathandizidwa kapena kupatsidwa zinthu, nanga kodi zimenezi ziyenera kutipangitsa kusiya kukhala opatsa?

15 Yesu amafuna kuti tizikhala osangalala choncho anatilimbikitsa kuti tikhale opatsa. Anthu ambiri akapatsidwa zinthu nawonso amachita zabwino. Iye anati: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani. Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.” (Luka 6:38) N’zoona kuti anthu ena sayamikira tikawapatsa zinthu kapena kuwathandiza. Koma akayamikira, zimathandiza kuti nawonso akhale opatsa. Choncho muziyesetsa kukhala opatsa ngakhale kuti anthu ena sayamikira. Zimene mungapatse ena zikhoza kuthandiza kwambiri ngakhale mutangowapatsa kamodzi kokha.

16. Kodi cholinga chathu popereka zinthu sichiyenera kukhala chiyani?

16 Anthu amene amapereka zinthu kuchokera pansi pa mtima sakhala ndi cholinga choti adzapezepo kenakake. Yesu ankaganizira mfundo imeneyi pamene ananena kuti: “Ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu. Ukatero udzakhala wodala, chifukwa alibe choti adzabweze.” (Luka 14:13, 14) Wolemba Baibulo wina ananena kuti munthu wopatsa “adzadalitsidwa.” Winanso ananena kuti: “Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.” (Miy. 22:9; Sal. 41:1) Choncho, tiyenera kukhala opatsa chifukwa timasangalala tikamathandiza anthu.

17. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale osangalala?

17 Kodi pamene Paulo anagwira mawu a Yesu akuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira,” ankangonena za kupatsa anthu zinthu? Ayi. Ankatanthauzanso kupereka malangizo, kuthandiza anthu amene akuvutika komanso kuwalimbikitsa. (Mac. 20:31-35) Zolankhula komanso zochita za Paulo zimatithandiza kudziwa zimene tiyenera kuchita pa nkhani imeneyi. Tiyenera kukonda kwambiri anthu, kuwaganizira komanso kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu kuti tiwathandize.

18. Kodi anthu ochita kafukufuku apeza zotani pa nkhani yopatsa?

18 Anthu ochita kafukufuku apezanso kuti anthu opatsa amakhala osangalala. Nkhani ina imanena kuti “anthu akathandiza anzawo amayamba kumva bwino kwambiri komanso kusangalala.” Ochita kafukufukuwo ananena kuti munthu akamathandiza ena “amaona kuti moyo wake uli ndi cholinga.” Zili choncho chifukwa chakuti tinalengedwa m’njira yoti tizisangalala tikamathandiza ena. Chifukwa cha zimenezi, akatswiri amalimbikitsa anthu kuti azidzipereka kugwira ntchito zothandiza ena n’cholinga choti azimva bwino komanso azikhala osangalala. Zimenezi n’zosadabwitsa kwa anthu amene amaona kuti Baibulo ndi mphatso imene Mlengi wathu Yehova anatipatsa.​—2 Tim. 3:16, 17.

TIZIYESETSA KUKHALABE OPATSA

19, 20. N’chifukwa chiyani inuyo mumafunitsitsa kukhala opatsa?

19 Zingakhale zovuta kuti tikhalebe opatsa chifukwa tikukhala m’dziko limene anthu ambiri saganizira zofuna za anzawo. Koma Yesu ananena kuti lamulo lalikulu kwambiri ndi loti tizikonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndi mphamvu zathu zonse. Lachiwiri lake ndi loti tizikonda anzathu ngati mmene timadzikondera tokha. (Maliko 12:28-31) Munkhaniyi taona kuti anthu amene amakonda Yehova amamutsanzira. Yehova komanso Yesu ali ndi mtima wopatsa. Ndiye amatiuza kuti tizichitanso zomwezo chifukwa zingatithandize kukhala osangalala. Tiyeni tiziyesetsa kukhala opatsa kwa Mulungu komanso anzathu. Tikamatero, tidzalemekeza Yehova, kuthandiza anthu ena ndipo tidzakhala osangalala.

20 Muyenera kuti mumayesetsa kuthandiza anthu, makamaka Akhristu anzanu. (Agal. 6:10) Mukamapitiriza kuchita zimenezi, anthu azikukondani komanso mudzakhala osangalala. Lemba la Miyambo 11:25 limati: “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto, ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.” Koma pali njira zambiri zimene tingasonyezere kuti ndife opatsa komanso okoma mtima mu utumiki ndiponso pa moyo wathu. Ndipo tikamachita zimenezi timapeza madalitso ambiri. Munkhani yotsatira tidzakambirana zina mwa njira zimenezi.

^ ndime 13 Dzina lasinthidwa.