Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?

Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?

“Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.”​—MIY. 18:13.

NYIMBO: 126, 95

1, 2. (a) Kodi tiyenera kuyesetsa kukhala ndi luso lotani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi luso limenelo? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

AKHRISTUFE tiyenera kukhala ndi luso loganizira bwino nkhani iliyonse n’cholinga choti tizindikire zoona zake pa nkhaniyo. (Miy. 3:21-23; 8:4, 5) Ngati tilibe luso limeneli, zingakhale zosavuta kuti tisokonezedwe ndi Satana komanso anthu a m’dziko loipali. (Aef. 5:6; Akol. 2:8) Choncho kuti tidziwe zoona zake pa nkhani inayake, tiyenera kudziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo. M’pake kuti lemba la Miyambo 18:13 limanena kuti: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.”

2 Munkhaniyi tikambirana zinthu zimene zingatilepheretse kudziwa mfundo zonse pa nkhani inayake komanso kuzindikira ngati nkhaniyo ndi yoona kapena ayi. Tikambirananso mfundo komanso zitsanzo za m’Baibulo zomwe zingatithandize kukhala ndi luso lozindikira zoona pa nkhani iliyonse.

MUSAMAKHULUPIRIRE “MAWU ALIONSE”

3. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mfundo ya pa Miyambo 14:15? (Onani chithunzi choyambirira.)

3 Masiku ano, timawerenga kapena kumva nkhani zambirimbiri. Tikhoza kupeza mfundo zankhaninkhani pa zinthu monga intaneti ndi TV. Anthu amalandiranso maimelo, mameseji kapena nkhani zambirimbiri kuchokera kwa anzawo. Popeza anthu ena amakonda kufalitsa nkhani zabodza kapena kupotoza mfundo zina, tiyenera kukhala osamala kwambiri. Kodi ndi mfundo iti ya m’Baibulo imene ingatithandize pa nkhaniyi? Lemba la Miyambo 14:15 limanena kuti: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”

4. Kodi lemba la Afilipi 4:8, 9 lingatithandize bwanji posankha zimene timawerenga, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kupeza mfundo zoona? (Onaninso bokosi lakuti “ Zinthu Zina Zotithandiza Kudziwa Zoona.”)

4 Kuti tisankhe zochita mwanzeru pa nkhani inayake, timayenera kudziwa mfundo zoona. Choncho tiyenera kusankha bwino zimene timawerenga. (Werengani Afilipi 4:8, 9.) Sitiyenera kuwononga nthawi powerenga zinthu zokayikitsa pa intaneti kapena nkhani zopanda umboni zimene timalandira m’maimelo. Koma chofunika kwambiri ndi kupewa mawebusaiti a anthu ampatuko. Tikutero chifukwa chakuti cholinga cha anthuwo ndi kusokoneza anthu a Mulungu komanso kupotoza choonadi. Ngati mfundo zimene tikudziwa pa nkhani inayake ndi zokayikitsa, sitingasankhe bwino zochita. Komanso musaiwale kuti ngati nkhani ili ndi mfundo zina zabodza ikhoza kusokoneza kwambiri maganizo anu komanso mtima wanu.​—1 Tim. 6:20, 21.

5. Kodi Aisiraeli anakhulupirira nkhani iti yabodza, nanga zotsatira zake zinali zotani?

5 Kukhulupirira nkhani yabodza n’koopsa kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika mu nthawi ya Mose. Pa anthu 12 amene anakaona Dziko Lolonjezedwa, anthu 10 anafotokoza zinthu zoipa. (Num. 13:25-33) Iwo anakokomeza zinthu moti anthu a Yehova anakhala ndi mantha komanso anataya mtima. (Num. 14:1-4) Mwina Aisiraeliwo ankaganiza kuti popeza ambiri mwa anthu amene anakaona dzikolo anafotokoza zoipa ndiye kuti zimene ankanenazo zinali zoona. Iwo anakana kumvetsera zinthu zabwino zokhudza Dziko Lolonjezedwa zimene Yoswa ndi Kalebe, omwe anali anthu odalirika, ankafotokoza. (Num. 14:6-10) Aisiraeliwo anachita zinthu zopusa kwambiri. Iwo anasankha kukhulupirira zinthu zabodzazo m’malo moyesetsa kudziwa nkhani yonse komanso kukhulupirira Yehova.

6. Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa tikamva nkhani zabodza zokhudza anthu a Yehova?

6 Tiyenera kusamala kwambiri tikapeza nkhani zokhudza anthu a Yehova. Tisaiwale kuti Satana amaneneza atumiki a Mulungu okhulupirika. (Chiv. 12:10) M’pake kuti Yesu anachenjeza kuti adani athu ‘adzatinamizira zoipa zilizonse.’ (Mat. 5:11) Tikamakumbukira chenjezoli sitingadabwe tikamva nkhani zabodza zokhudza anthu a Yehova.

7. Kodi muyenera kudzifunsa mafunso ati musanatumize maimelo kapena mameseji?

7 Kodi inuyo mumakonda kutumiza maimelo ndiponso mameseji kwa anzanu? Ngati zili choncho, mwina mukamva nkhani inayake yatsopano mungafune kukhala ngati mtolankhani amene amayesetsa kukhala woyamba kufalitsa nkhaniyo. Komabe musanatumize meseji kapena imeloyo, muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndatsimikizira kuti nkhaniyi ndi yoona? Kodi ndikudziwadi mfundo zonse?’ Ngati simunatsimikizire, mukhoza kufalitsa nkhani zabodza kwa abale ndi alongo. Ndipo ngati mukukayikira, mungachite bwino osatumiza.

8. Kodi adani athu amachita zotani m’mayiko ena, nanga tingawathandize bwanji mosazindikira?

8 Kutumiza maimelo ndiponso mameseji mopupuluma ndi koopsa pa chifukwa chinanso. M’mayiko ena, ntchito yathu ndi yoletsedwa. Ndipo adani athu m’mayikowa akhoza kufalitsa nkhani n’cholinga choti atiopseze kapena kutichititsa kuti tizikayikirana. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika ku Soviet Union. Apolisi amene ankadziwika kuti KGB anafalitsa mabodza okhudza abale ena amene ankatsogolera m’gulu. * N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri anakhulupirira mabodzawa moti anachoka m’gulu la Yehova. Chosangalatsa n’chakuti ambiri mwa anthuwo anabwerera koma ena sanabwerere ndipo ‘chikhulupiriro chawo chinasweka ngati ngalawa.’ (1 Tim. 1:19) Kodi tingapewe bwanji mavuto ngati amenewa? Tiyenera kupewa kufalitsa nkhani zoipa kapena zimene zilibe umboni. Komanso sitiyenera kukhulupirira nkhani ngati sitikudziwa mfundo zake zonse.

KODI MUKUDZIWA ZONSE?

9. Kodi n’chiyani chingachititsenso kuti tisadziwe zoona pa nkhani inayake?

9 Anthu amathanso kupotoza kapena kungofotokoza mfundo zochepa zokhudza nkhani inayake ndipo zimenezi zingachititse kuti tisadziwe zonse pa nkhaniyo. Tizikumbukira kuti nkhani ya ziganizo 10 imene ili ndi chiganizo chimodzi chokha cholakwika ikhoza kusokonezeratu munthu. Ndiye kodi tingapewe bwanji kusokonezedwa ndi nkhani zabodza ngati zimenezo?​—Aef. 4:14.

10. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ena ankafuna kumenyana ndi abale awo, nanga nkhaniyi inatha bwanji?

10 Chitsanzo ndi zimene zinachitikira Aisiraeli amene ankakhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano m’masiku a Yoswa. (Yos. 22:9-34) Iwo anamva kuti Aisiraeli amene ankakhala kum’mawa (afuko la Rubeni ndi Gadi komanso hafu ya fuko la Manase) anamanga guwa lalikulu pafupi ndi mtsinje wa Yorodano. Zimene anamvazi zinali zoona. Koma popeza sankadziwa zonse zokhudza nkhaniyi, anaganiza kuti abale awowo asiya kulambira Yehova. Choncho Aisiraeli akumadzulowo anatengana kuti apite kukamenyana ndi abale awowo. (Werengani Yoswa 22:9-12.) Koma mwamwayi, anaganiza zotumiza kaye anthu odalirika kuti akafufuze zoona zake. Kodi anapeza zotani? Abale awowo sanamange guwalo kuti aziperekapo nsembe koma kuti chingokhala chikumbutso. Ankafuna kuti anthu odzabadwa m’tsogolo adzazindikire kuti nawonso anali atumiki a Yehova okhulupirika. Aisiraeli akumadzulowo ayenera kuti anasangalala kwambiri kuti sanapupulume n’kupha abale awo koma anafufuza kaye n’kudziwa zoona zenizeni.

11. (a) Fotokozani zinthu zopanda chilungamo zimene zinachitikira Mefiboseti. (b) Kodi Davide akanapewa bwanji zimenezi?

11 Ifenso tikhoza kuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo chifukwa choti anthu ena afalitsa nkhani yokhudza ifeyo koma sanafotokoze mfundo zonse kapena anafotokoza mfundo zina zabodza. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira Davide ndi Mefiboseti. Davide anakomera mtima Mefiboseti pomupatsa malo onse a Sauli, yemwe anali agogo ake. (2 Sam. 9:6, 7) Koma patapita nthawi, Davide anamva zinthu zoipa zokhudza Mefiboseti. Iye asanafufuze n’komwe nkhaniyi, analanda Mefiboseti zinthu zake zonse. (2 Sam. 16:1-4) Koma kenako Davide analankhula ndi Mefiboseti n’kuzindikira kuti analakwitsa ndipo anamubwezera zinthu zake zina. (2 Sam. 19:24-29) Davide akanayamba wafufuza kaye kuti adziwe zonse, zinthu zopanda chilungamozi sizikanachitika.

12, 13. (a) Kodi Yesu anatani atanenezedwa zinthu zabodza? (b) Kodi ifeyo tingatani ngati munthu wina watinenera zinthu zabodza?

12 Koma kodi mungatani ngati anthu akunenerani zinthu zabodza? Zoterezi zinachitikiranso Yesu ndi Yohane M’batizi. (Werengani Mateyu 11:18, 19.) Kodi Yesu anatani? Iye sanataye nthawi ndi kuyankha zimene anthu ankamunenazo. M’malomwake analimbikitsa anthu kuti azingoona zimene akuchita komanso kuphunzitsa kuti adziwe zoona zake. Iye anati: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.”​—Mat. 11:19.

13 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene anachitazi? Ngati anthu atinenera zinthu zoipa, tikhoza kufunitsitsa kuti chilungamo chichitike komanso tikonze zinthu kuti mbiri yathu isaipe. Koma pali zinthu zina zimene tingachite. Anthu akatinenera zinthu zabodza, zochita zathu n’zimene zingathandize anthu ena kuti asakhulupirire mabodzawo. Zimene Yesu anachita zikusonyeza kuti khalidwe lathu labwino lingachititse kuti anthu aiwale zoipa zimene anthu ena anatinena.

KODI MUMADZIDALIRA KWAMBIRI?

14, 15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kudalira kwambiri luso lathu lomvetsa zinthu kungakhale msampha?

14 Tonsefe si angwiro ndipo zimenezi zingachititsenso kuti tizivutika kudziwa mfundo zonse za nkhani inayake. Mwina takhala tikutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri ndipo tili ndi luso loganiza komanso lomvetsa zinthu. Mwinanso anthu amatilemekeza chifukwa choti ndife oganiza bwino. Komatu umenewunso ukhoza kukhala msampha.

15 Zimenezi zingakhale msampha ngati tayamba kudalira kwambiri luso lathu lomvetsa zinthu. Tikhoza kupezeka kuti tikungochita zinthu motsatira mtima ndi maganizo athu. Tingayambe kuganiza kuti tikangoona pang’ono zinthu zina tingadziwiretu nkhani yonse. Koma maganizo amenewa ndi oopsa. Paja Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti sitiyenera kudalira luso lathu lomvetsa zinthu.​—Miy. 3:5, 6; 28:26.

16. Munkhani yoyerekezerayi, kodi n’chiyani chinachitika kulesitilanti, nanga Tom anafulumira kuganiza chiyani?

16 Kuti timvetse nkhaniyi, tiyerekeze kuti m’bale wina dzina lake Tom, yemwe ndi mkulu, anapita kulesitilanti. Ali komweko anaona mkulu mnzake dzina lake John akudya limodzi ndi mkazi wina yemwe sanali wake. Ankaoneka kuti akusangalala kwambiri ndipo potsanzikana anahagana. Tom anakhumudwa kwambiri n’kuyamba kuganiza kuti, Koma banja la mkulu ameneyu silitha? Kodi mkazi wake zimukhudza bwanji? Nanga ana ake ziwathera bwanji? Tom anaonapo zinthu ngati zimenezi zitachitika komanso mavuto amene anatsatirapo. Kodi inuyo mukanaona zimene zinachitika kulesitilantiko mukanamva bwanji?

17. Munkhani yoyerekezerayi, kodi Tom anazindikira chiyani, nanga ife tikuphunzirapo chiyani?

17 Koma funso n’kumati, Kodi Tom ankadziwa zonse pa nkhaniyi kuti afulumire kuganiza zoti John ndi wosakhulupirika kwa mkazi wake? Tiyerekeze kuti madzulo a tsikulo, Tom akuimbira foni John ndipo akumva kuti mkaziyo ndi mchemwali wake ndipo ankangodutsa m’tauniyo. Awiriwo anali asanakumane kwa zaka zambiri. Popeza anali ndi nthawi yochepa, sakanatha kufika kunyumba kwawo koma kungokumana kulesitilantiko n’kudyera limodzi chakudya. Mkazi wa John analephera kufika kuti acheze nawo. Kodi mukuganiza kuti Tom angamve bwanji? Mwinatu mtima wake ukhoza kukhala m’malo. Ubwino wake ndi wakuti sanauze anthu ena zimene ankaganizazo. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Nkhaniyitu ikusonyeza kuti kaya timadziwa zinthu zochuluka bwanji, timafunikabe kufufuza kuti tidziwe zonse pa nkhani inayake.

18. Kodi kusagwirizana ndi anzathu kungabweretse mavuto otani?

18 Ngati sitigwirizana ndi Mkhristu mnzathu tikhozanso kulephera kuona zinthu moyenera. Tikamangoganizira zinthu zokhudza m’baleyo zimene sizitisangalatsa, tingayambe kumukayikira. Ndiye tikangomva nkhani yoipa yokhudza m’baleyo tikhoza kuikhulupirira nthawi yomweyo. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kusagwirizana ndi abale athu kungachititse kuti tiziwaganizira zoipa tilibe umboni wokwanira. (1 Tim. 6:4, 5) Kuti tipewe zimenezi, tiyenera kuyesetsa kuti tisakhale ndi nsanje kapena kaduka mumtima mwathu. M’malomwake tiziyesetsa kukonda abale athu komanso kuwakhululukira ndi mtima wonse.​—Werengani Akolose 3:12-14.

MFUNDO ZA M’BAIBULO ZINGATITETEZE

19, 20. (a) Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zingatithandize kumvetsa bwino nkhani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

19 Popeza nkhani zabodza zimapezeka paliponse masiku ano komanso anthufe si angwiro, timavutika kudziwa mfundo zonse pa nkhani inayake ndiponso kuzimvetsa bwino. Koma n’chiyani chingatithandize? Tiyenera kudziwa mfundo za m’Baibulo komanso kuzitsatira. Mfundo ina yofunika ndi yakuti munthu akayankhira nkhani asanaimvetsetse amapusa komanso amachita manyazi. (Miy. 18:13) Palinso mfundo ina ya m’Baibulo imene imatikumbutsa kuti tisamangokhulupirira mawu aliwonse. (Miy. 14:15) Mfundo inanso ndi yakuti kaya timadziwa zambiri bwanji, tiyenera kupewa kudalira luso lathu lomvetsa zinthu. (Miy. 3:5, 6) Mfundo za m’Baibulo zingatiteteze ngati timayesetsa kupeza mfundo zoona pa nkhani inayake, kuziganizira bwino komanso kusankha zochita mwanzeru.

20 Koma palinso vuto lina. Vuto lake ndi lakuti anthufe timakonda kuweruza potengera maonekedwe a zinthu. Munkhani yotsatira tidzakambirana mavuto ena amene tingakumane nawo pa nkhaniyi komanso zimene zingatithandize kuwapewa.

^ ndime 8 Onani Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2004 lachingelezi, tsamba 111-112 komanso Buku Lapachaka la 2008 lachingelezi, tsamba 133-135.