Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuleza Mtima Ndi Kupirira Kokhala ndi Cholinga

Kuleza Mtima Ndi Kupirira Kokhala ndi Cholinga

‘M’MASIKU OTSIRIZA’ ano, mavuto akuchulukirachulukira. Choncho anthu a Yehova ayenera kukhala oleza mtima kwambiri kuposa kale. (2 Tim. 3:1-5) Anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda, osafuna kugwirizana ndi anzawo komanso osadziletsa. Anthu oterewa sakhala oleza mtima ngakhale pang’ono. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nanenso ndatengera kusaleza mtima kwa anthu a m’dzikoli? Kodi kuleza mtima n’kutani? Nanga ndingatani kuti ndizikhala woleza mtima nthawi zonse?’

KODI KULEZA MTIMA N’KUTANI?

Kodi m’Baibulo, mawu oti kuleza mtima amatanthauza chiyani? Sikuti amatanthauza kungopirira vuto. Munthu woleza mtima amapirira ali ndi cholinga kapena kuti amayembekezera kuti zinthu zikhala bwino. Samangoganizira zimene akufuna koma amafunira zabwino anthu amene akuchititsa kuti azivutika. Choncho munthu woleza mtima akaputidwa sataya mtima n’kumaganiza kuti sangagwirizanenso ndi munthu amene wamuputayo. M’pake kuti Baibulo limayamba n’kutchula ‘kuleza mtima’ pofotokoza makhalidwe amene munthu wachikondi amakhala nawo. * (1 Akor. 13:4) Mawu a Mulungu amasonyezanso kuti “kuleza mtima” ndi limodzi mwa “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Koma kodi tingatani kuti tikhale oleza mtima?

KODI TINGATANI KUTI TIKHALE OLEZA MTIMA?

Choyamba, tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake. Paja iye amapereka mzimuwo kwa anthu amene amamudalira. (Luka 11:13) Ngakhale kuti mzimu woyera ndi wamphamvu, tifunikabe kuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu. (Sal. 86:10, 11) Izi zikutanthauza kuti tiyenera kuyesetsa kuchita zinthu moleza mtima tsiku lililonse kuti khalidweli likhazikike mumtima mwathu. Komatu pali zinthu zinanso zimene tingachite kuti tizikhalabe oleza mtima. Kodi zinthu zake ndi ziti?

Tiyenera kuphunzira za Yesu n’kumatsatira chitsanzo chake. Pofotokoza za umunthu watsopano, womwe umaphatikizapo kuleza mtima, mtumwi Paulo ananena kuti “mtendere wa Khristu ulamulire m’mitima yanu.” (Akol. 3:10, 12, 15) Mtendere wa Khristu ukhoza ‘kulamulira’ m’mitima yathu tikamatsanzira chikhulupiriro chimene anali nacho choti Mulungu adzakonza pa nthawi yoyenera zinthu zimene zimatidetsa nkhawa. Tikamatsanzira Yesu, sitingasiye kuleza mtima ngakhale patachitika zinthu zopsetsa mtima kwambiri.​—Yoh. 14:27; 16:33.

Tonsefe timafuna dziko latsopano litafika msanga. Koma kuganizira mmene Yehova amatilezera mtima kumatithandiza kuti nafenso tizidikira moleza mtima. Paja Malemba amatitsimikizira kuti: “Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake, ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Tikamaganizira mmene Yehova amalezera nafe mtima, timalimbikitsidwa kuti nafenso tizilezera mtima anzathu. (Aroma 2:4) Koma kodi tiyenera kukhala oleza mtima pa zinthu ziti?

KODI TIYENERA KULEZA MTIMA PA ZINTHU ZITI?

Tsiku lililonse pamachitika zinthu zimene zingatilepheretse kukhala oleza mtima. Mwachitsanzo, ngati mukuona kuti pali mfundo inayake yofunika kuinena, kodi mumaleza mtima n’kumapewa kudula mawu anzanu? (Yak. 1:19) Tiyeneranso kukhala oleza mtima tikamachita zinthu ndi Akhristu amene khalidwe lawo silitisangalatsa kwenikweni. M’malo mokwiya ndi zinthu ngati zimenezi, ndi bwino kuganizira zimene Yehova ndi Yesu amachita ifeyo tikalakwitsa zinazake. Sikuti amangokhalira kufufuza tinthu ting’onoting’ono timene talakwitsa. M’malomwake amaona zabwino zimene tikuchita n’kumayembekezera moleza mtima pamene tikuyesetsa kusintha zimene sitichita bwino.​—1 Tim. 1:16; 1 Pet. 3:12.

Timafunikanso kuleza mtima ngati munthu wina wanena kuti zimene tinalankhula kapena kuchita n’zolakwika. Zoterezi zikachitika, anthufe timakonda kukhumudwa kapena kudziikira kumbuyo. Komatu izi si zimene Baibulo limatiuza kuti tizichita. Paja limatiuza kuti: “Munthu woleza mtima ndi wabwino kuposa munthu wodzikuza. Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.” (Mlal. 7:8, 9) Choncho ngakhale zimene munthuyo akunena zitakhala kuti ndi bodza lenileni, tiyenera kukhalabe oleza mtima n’kuyamba taganizira tisanayankhe. Izi n’zimene Yesu anachita atalankhulidwa mawu achipongwe popanda chifukwa.​—Mat. 11:19.

Makolo ayeneranso kukhala oleza mtima kwambiri akamathandiza ana awo kuti asinthe mtima kapena maganizo amene ali nawo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Mattias amene amatumikira ku Beteli ya ku Scandinavia. M’baleyu ali pasukulu ankanyozedwa kwambiri ndi anzake chifukwa cha zimene amakhulupirira. Poyamba makolo ake sankadziwa zimenezi. Koma ankangoona kuti mwana wawo wayamba kukayikira zimene ankakhulupirirazo. Bambo ake omwe ndi a Gillis anati: “Tinafunika kuleza mtima kwambiri.” Nthawi zina Mattias ankafunsa kuti: “Kodi Mulungu ndi ndani? Nanga ngati si zoona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu? Kodi tingatsimikizire bwanji kuti Mulungu amafunadi kuti tizichita izi osati izi?” Ankafunsanso bambo ake kuti: “Bwanji mumandiweruza ngati sindikugwirizana ndi maganizo anu kapena zimene mumakhulupirira?”

Bambowo anati: “Nthawi zina mwana wathu ankafunsa mafunso atakwiya kwambiri. Sikuti ankakwiyira makolofe koma ankapsa mtima ndi choonadi chifukwa ankaona kuti chikuchititsa kuti azizunzika.” Kodi bambo a m’baleyu anatani? “Nthawi zina ine ndi mwana wanga tinkakambirana kwa nthawi yaitali. Nthawi zambiri ndinkangomvetsera n’kumafunsa mafunso mwa apa ndi apo kuti ndimvetse bwino maganizo ake. Nthawi zina ndinkamufotokozera mfundo inayake n’kumuuza kuti aiganizire kwa tsiku limodzi kapena angapo kenako n’kudzakambirananso. Masiku ena ndinkamuuza kuti andidikire masiku angapo kuti ndiganizire zimene wanena. Pang’ono ndi pang’ono Mattias anayamba kumvetsa komanso kukhulupirira kwambiri mfundo zokhudza dipo, ulamuliro wa Mulungu komanso chikondi chake. Zinali zovuta ndipo zinatenga nthawi koma kenako anayamba kukonda kwambiri Yehova. Ine ndi mkazi wanga timasangalala kuti tinaleza naye mtima pamene ankakula ndipo tinakwanitsa kumufika pamtima ndi choonadi.”

Gillis ndi mkazi wake ankakhulupirira kuti Yehova awathandiza pamene ankathandiza mwana wawo moleza mtima. Akamakumbukira zimene zinachitika, Gillis amati: “Nthawi zambiri ndinkamuuza Mattias kuti ine ndi mayi ake timamukonda kwambiri ndipo timamupempherera kuchokera pansi pa mtima kuti Yehova amuthandize kumvetsa zinthu.” Makolowa akusangalala kwambiri kuti anasonyeza khalidwe labwino kwambiri la kuleza mtima.

Akhristu amafunikanso kuleza mtima akamasamalira wachibale kapena mnzawo amene akudwala kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Ellen * amene amakhalanso ku Scandinavia.

Pafupifupi zaka 8 zapitazo, mwamuna wake wa Ellen anachita sitiroko kawiri moti ubongo wake unawonongeka. Izi zinachititsa kuti mwamuna wakeyo asamathe kumva chisoni, chifundo kapena kusangalala. Ellen amavutika kwambiri kuti amusamalire bwino. Iye anati: “Ndimafunika kuleza mtima kwambiri komanso kupemphera mosalekeza. Lemba limene limandilimbikitsa kwambiri ndi la Afilipi 4:13 lomwe limati: ‘Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.’” Chifukwa cha mphamvu imene Mulungu amapereka, Ellen amapirira vuto lakeli moleza mtima ndipo sakayikira kuti Yehova apitiriza kumuthandiza.​—Sal. 62:5, 6.

TSANZIRANI YEHOVA PA NKHANI YOLEZA MTIMA

Kunena zoona, Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yoleza mtima. (2 Pet. 3:15) M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kuti Yehova ndi woleza mtima kwambiri. (Neh. 9:30; Yes. 30:18) Mwachitsanzo, kodi Yehova anatani Abulahamu atamufunsa mafunso okhudza mzinda wa Sodomu? Choyamba Yehova sanamudule mawu Abulahamu. Koma anamumvetsera moleza mtima pamene ankafunsa mafunso onse komanso kufotokoza zimene zinkamudetsa nkhawa. Yehova anasonyeza kuti ankamva zimene Abulahamu ankanena chifukwa pomuyankha ankabwereza zimene wanena kenako n’kumutsimikizira kuti sangawononge mzindawo ngakhale atangopezamo anthu 10 okha olungama. (Gen. 18:22-33) Apatu Yehova anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yomvetsera moleza mtima popanda kuchita zinthu mopupuluma.

Kuleza mtima ndi mbali yofunika kwambiri ya umunthu watsopano umene Mkhristu aliyense ayenera kuuvala. Tikamayesetsa kuti tikhale ndi khalidweli, timalemekeza Yehova yemwe ndi Atate wathu wachikondi. Komanso tidzakhala m’gulu la anthu amene “mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.”​—Aheb. 6:10-12.

^ ndime 4 Khalidwe la chikondi linafotokozedwa mu nkhani yoyambirira yonena za makhalidwe 9 amene mzimu wa Mulungu umatulutsa.

^ ndime 15 Dzina lasinthidwa.