Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuleza mtima Kumatanthauza Kupilila Tili na Colinga

Kuleza mtima Kumatanthauza Kupilila Tili na Colinga

CIFUKWA ca kuculuka kwa mavuto ‘m’masiku otsiliza’ ano, anthu a Yehova ayenela kukhala oleza mtima kuposa kale lonse. (2 Tim. 3:1-5) Anthu ambili amene timakhala nawo m’dzikoli ni odzikonda, osafuna kugwilizana na anzawo, komanso osadziletsa. Anthu aconco, nthawi zambili sacita zinthu moleza mtima. Conco, Mkhristu aliyense ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi nayamba kutengela khalidwe la anthu a m’dzikoli la kusaleza mtima? Kodi kuleza mtima kwa zoona kumatanthauza ciani? Nanga ningacite ciani kuti khalidwe labwino limeneli likhale mbali ya umunthu wanga?’

TANTHAUZO LA KULEZA MTIMA

M’Baibo, kuleza mtima kumatanthauza zambili osati cabe kupilila mavuto. Munthu woleza mtima amapilila ali na colinga, kutanthauza kuti amakhala na ciyembekezo cakuti zinthu zidzakhala bwino. Munthu waconco saganizila zofuna zake zokha, koma amaganizilanso zabwino zokhudza munthu amene wacita zinthu zosamukondweletsa. Ndiye cifukwa cake, ngati munthu woleza mtima walakwilidwa, amakhalabe na ciyembekezo cakuti ubwenzi wake na munthu amene wam’lakwila udzakhala bwino. M’pake kuti Baibo imayambila kuchula khalidwe la “kuleza mtima” pa makhalidwe amene munthu wacikondi amakhala nawo. * (1 Akor. 13:4) Mau a Mulungu amachulanso “kuleza mtima” monga limodzi mwa “makhalidwe amene mzimu woyela” umabala. (Agal. 5:22, 23) Koma kodi tingacite ciani kuti tikhale na khalidwe locokela kwa Mulungu limeneli?

MMENE TINGAKULITSILE KHALIDWE LA KULEZA MTIMA

Kuti tikulitse khalidwe la kuleza mtima, tifunika kumapempha mzimu woyela, umene Yehova amaupeleka kwa anthu amene amam’khulupilila na kum’dalila. (Luka 11:13) N’zoona kuti mzimu wa Mulungu ni wamphamvu kwambili. Koma kuti utithandize, tifunika kucita mbali yathu, komanso kucita zinthu mogwilizana na mapemphelo athu. (Sal. 86:10, 11) Izi zitanthauza kuti tifunika kuyesetsa kucita zinthu moleza mtima tsiku lililonse kuti khalidweli likhale mbali ya umunthu wathu. Koma pali zinanso zimene tifunika kucita. Ziti?

Tingakulitse khalidwe la kuleza mtima mwa kuphunzila na kutengela citsanzo cabwino ca Yesu. Mouzilidwa, mtumwi Paulo anafotokoza za “umunthu watsopano,” umene umaphatikizapo “kuleza mtima.” Ndiyeno, iye anatilimbikitsa kulola ‘mtendele wa Khristu kulamulila m’mitima yathu.’ (Akol. 3:10, 12, 5) Tingalole mtendele umenewu ‘kulamulila’ m’mitima yathu mwa kukhala na cikhulupililo colimba ngati ca Yesu, coti pa nthawi yake Mulungu adzakonza zinthu zimene zimatisowetsa mtendele. Ngati titengela citsanzo ca Yesu, tidzakhalabe oleza mtima, olo zinthu zifike poipa bwanji.—Yoh. 14:27; 16:33.

Timafunitsitsa kuti dziko latsopano la Mulungu libwele. Komabe, ngati tisinkha-sinkha mmene Yehova waonetsela kuleza mtima kwa ise, timalimbikitsidwa kukhala oleza mtima kwambili. Malemba amatitsimikizila kuti: “Yehova sakucedwa kukwanilitsa lonjezo lake, ngati mmene anthu ena amaonela kuti akucedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Tikamaganizila kuleza mtima kumene Yehova wationetsa, kodi sitilimbikitsidwa kukhala oleza mtima ndi anthu ena? (Aroma 2:4) Tili na mfundo imeneyi m’maganizo, kodi ni pa zocitika zanji pamene timafunika kukhala oleza mtima?

ZOCITIKA ZIMENE ZIMAFUNA KULEZA MTIMA

Tsiku lililonse pamacitika zinthu zambili zimene zimafuna kuleza mtima. Mwacitsanzo, ngati pali nkhani yofunika imene mufuna kuuza munthu, koma iye akukambilana na ena, mungafunike kukhala oleza mtima kuti musasokoneze makambilano awo. (Yak. 1:19) Mungafunikenso kukhala oleza mtima poceza na Akhristu anzanu amene ali na zizoloŵezi zimene simukondwela nazo. M’malo mokhumudwa na zocita zawozo, mungacite bwino kuganizila mmene Yehova na Yesu amaonela zofooka zathu. Iwo sayang’ana kwambili pa zophophonya zathu. Koma amayang’ana pa makhalidwe athu abwino, ndipo amayembekezela moleza mtima kuti tiwongolele zimene siticita bwino.—1 Tim. 1:16; 1 Pet. 3:12.

Tingafunikenso kukhala oleza mtima ngati wina watiuza kuti zimene takamba kapena kucita n’zolakwika. Nthawi zambili timathamangila kukhumudwa kapena kukamba modzikhululukila. Koma Mau a Mulungu amati: “Munthu woleza mtima ndi wabwino kuposa munthu wodzikuza. Usamafulumile kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sacedwa kupsa mtima.” (Mlal. 7:8, 9) Conco, olo kuti zimene munthu wakamba si zoona, tiyenela kucitabe zinthu moleza mtima. N’zimene Yesu anacita pamene anthu anamunyoza popanda cifukwa.—Mat. 11:19.

Makolo afunika kukhala oleza mtima kwambili maka-maka pamene akuthandiza mwana wawo amene wayamba kukhala na maganizo olakwika, zilakolako, kapena zizoloŵezi zoipa. Ganizilani za Mattias, amene amatumikila pa nthambi ya ku Scandinavia. Pamene anali wacicepele, tsiku lililonse iye anali kusekewa na anzake ku sukulu cifukwa ca cikhulupililo cake. Poyamba, makolo ake sanadziŵe zimenezo. Koma m’kupita kwa nthawi, iwo anakhudzidwa kwambili cifukwa cakuti citsutsoco cinapangitsa mwanayo kuyamba kukayikila coonadi. M’bale Gillis, tate wake wa Mattias, anakamba kuti iye na mkazi wake anafunika kukhala oleza mtima kwambili. Nthawi zina Mattias anali kuwafunsa kuti: “Kodi Mulungu ndani? Ningatsimikizile bwanji kuti Baibo ni Mau a Mulungu? Tingatsimikizile bwanji kuti Mulungu amafunadi kuti tizicita zimenezi?” Nthawi zinanso anali kufunsa atate wake kuti: “Kodi n’kulakwa kukhala na maganizo osiyana ndi anu, kapena kusakhulupilila zimene imwe mumakhulupilila?”

M’bale Gillis anakambanso kuti: “Nthawi zina, mwana wathu anali kutifunsa mafunso mwaukali, osati cifukwa coipidwa na ine kapena amake, koma kaamba kozonda coonadi. Anali kuona kuti cinali kupangitsa umoyo wake kukhala wovuta.” Kodi m’bale Gillis anamuthandiza bwanji mwanayo? Iye anati: “Ine na mwana wanga tinali kukhala pansi nokambilana kwa maola angapo. N’nali kumumvetsela na kumufunsako mafunso mwa apo na apo kuti nidziŵe bwino maganizo ake na mmene anali kumvelela. Nthawi zina n’nali kumufotokozela mfundo inayake na kumupatsa tsiku kapena masiku angapo kuti anganizilepo tisanakambilanenso. Nthawi zinanso, akafunsa funso n’nali kumuuza kuti anipatse masiku angapo kuti niganizilepo. Kukambilana mwanjila imeneyi kunathandiza kuti mwapang’ono-pang’ono, Mattias ayambe kumvetsetsa na kukhulupilila za dipo, ulamulilo wa Mulungu, na cikondi cake. Zinatenga nthawi, ndipo nthawi zambili zinali zovuta. Koma pang’ono m’pang’ono, cikondi pa Yehova cinakula mu mtima mwake. Ine na mkazi wanga ndise okondwa kuti khama lathu pothandiza Mattias moleza mtima pamene anali wacicepele silinapite pacabe, ndipo tinam’fika pa mtima.”

M’bale Gillis na mkazi wake anadalila Yehova pamene anali kuthandiza mwana wawo moleza mtima. Pokumbukila nthawiyo, m’bale Gillis anati: “Nthawi zambili n’nali kumuuza Mattias kuti cifukwa comukonda, ine na amayi ake tinali kum’pemphelela kwa Yehova mocondelela kuti amuthandize kumvetsetsa coonadi.” Makolo amenewa ni okondwa ngako kuti anayesetsa kuonetsa khalidwe lofunika limeneli la kuleza mtima.

Kuphatikiza popeleka thandizo lauzimu, Akhristu oona afunika kukhala odzicepetsa pamene asamalila abululu awo kapena anzawo amene akudwala matenda osathelapo. Ganizilani za Ellen, * amenenso amakhala ku Scandinavia.

Pafupi-fupi zaka 8 zapitazo, mwamuna wa Ellen anadwala sitroko kaŵili, ndipo izi zinacititsa kuti ubongo wake usamaseŵenze bwino. Pa cifukwa ici, mwamunayo lomba sakwanitsa kumvela cifundo, sasangalala na ciliconse, kapena kumva cisoni. Zinthu n’zovuta kwambili kwa Ellen. Iye anati: “Canithandiza ni kuyesetsa kukhala woleza mtima na kupemphela kaŵili-kaŵili.” Ellen anakambanso kuti: “Lemba langa lapamtima, limene limanitonthoza ni Afilipi 4:13, limene limati: ‘Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.’” Mwa mphamvu zimenezo, Ellen wapilila moleza mtima ali na cidalilo colimba cakuti Yehova adzapitiliza kumuthandiza.—Sal. 62:5, 6.

TENGELANI KULEZA MTIMA KWA YEHOVA

Pa nkhani ya kuleza mtima, Yehova ndiye citsanzo cabwino kwambili cimene tiyenela kutengela. (2 Pet. 3:15) M’Mau a Mulungu muli nkhani zambili zosonyeza mmene Yehova anaonetsela kuleza mtima kwakukulu. (Neh. 9:30; Yes. 30:18) Mwacitsanzo, kodi Yehova anacitanji pamene Abulahamu anam’funsa mafunso pa colinga cake cofuna kuwononga Sodomu? Iye sanam’dule mau Abulahamu pamene anali kukamba. M’malomwake, anamvetsela moleza mtima funso lililonse limene Abulahamu anafunsa, komanso nkhawa zake. Ndiyeno Yehova anaonetsa kuti anamvetsa nkhawa za Abulahamu, ndipo anamutsimikizila kuti sakanawononga mzinda wa Sodomu, olo mukanapezeka cabe anthu 10 olungama. (Gen. 18:22-33) Ndithudi! Yehova ni citsanzo cabwino ngako pa nkhani yomvetsela moleza mtima na kusakwiya msanga.

Inde, kuleza mtima ni mbali yofunika kwambili ya umunthu watsopano umene ise tonse Akhristu tiyenela kuvala. Ngati tiyesetsa kukulitsa khalidwe lofunika limeneli, timaonetsa kuti timalemekeza Atate wathu wakumwamba, amene ni wacikondi komanso woleza mtima. Tikatelo, tidzakhala m’gulu la anthu “amene, mwa cikhulupililo ndi kuleza mtima, akulandila zinthu zimene Mulungu analonjeza monga colowa cawo.”—Aheb. 6:10-12.

^ par. 4 Khalidwe la cikondi linafotokozedwa m’nkhani yoyamba pa nkhani 9 zimenezi zofotokoza makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala.

^ par. 15 Dzina lasinthidwa.