Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Yehova Anan’dalitsa Kwambili Cifukwa ca Zimene N’nasankha

Yehova Anan’dalitsa Kwambili Cifukwa ca Zimene N’nasankha

Kunja kunali kutangoyamba kuca pamene tinali kutsiliza kuika tumapepa twauthenga munsi mwa zitseko za nyumba m’gawo lathu. Umu munali mu 1939. Pa tsikulo, tinacoka ku nyumba ca pakati pa usiku na kuyenda ulendo wa pa motoka wa ola limodzi, kupita ku tauni ina yaing’ono yochedwa Joplin, kum’mwela cakumadzulo kwa Missouri, ku America. Titangotsiliza kuika tumapepato, tinakwela m’motoka yathu na kupita ku malo amene tinapangana kuti tikakumane. Kumeneko, tinayamba kuyembekezela anzathu. Koma mwina mungadabwe kuti n’cifukwa ciani tinapita mu ulaliki usiku na kucokako m’matandakuca. Nidzakufotokozelani pambuyo pake.

NIMAYAMIKILA kuti n’naleledwa na makolo a Mboni, a Fred ndi a Edna Molohan. Iwo ananiphunzitsa kukonda Yehova. Pamene n’nabadwa, mu 1934, iwo anali atatumikila kale Mulungu kwa zaka 20 monga Ophunzila Baibo (Mboni za Yehova). Banja lathu linali kukhala ku Parsons, tauni yaing’ono kum’mwela cakum’maŵa kwa mzinda wa Kansas. Pafupi-fupi ofalitsa onse mu mpingo mwathu anali Akhristu odzozedwa. Banja lathu linali kukonda misonkhano, komanso kulalikila coonadi ca Mau a Mulungu. Nthawi zambili, pa ciŵelu madzulo tinali kucita ulaliki wa mu msewu, umene manje timaucha ulaliki wa poyela. Masiku ena, tinali kutopa ngako. Koma nthawi zonse tikatsiliza kulalikila, atate anali kutitenga nokatigulila aizikilimu.

Mpingo wathu unali waung’ono. Koma unali na gawo lalikulu, limene linaphatikizapo matauni angapo ang’ono-ang’ono, komanso mafamu amene anali pafupi. Polalikila alimi, nthawi zambili tinali kusinthanitsa mabuku athu na ndiyo zamasamba, mazila (ocotsa kumene pa fuka), ngakhalenso nkhuku zamoyo. Popeza atate anali kupelekelatu zopeleka kuti alandile mabuku, cakudya cimene tinali kusinthitsa na mabukuwo, tinali kudya pa nyumba.

MAKAMPENI AULALIKI

Makolo anga anagula galamafoni, imene anali kuiseŵenzetsa mu ulaliki. Popeza n’nali mwana, sin’nali kukwanitsa kuiliza. Koma n’nali kukonda kuthandiza atate na amayi, pamene anali kulizila anthu nkhani za M’bale Rutherford, pa maulendo obwelelako na ku maphunzilo a Baibo.

Nili na atate na amayi titaimilila pambali pa motoka yathu yokhala na zokuzila mau

Atate anamanga masipika akulu-akulu pamwamba pa motoka yathu ya mtundu wa Ford, ndipo tinayamba kuiseŵenzetsa mu ulaliki. Motokayo inathandiza kwambili pofalitsa uthenga wa Ufumu. Poyamba, anali kuliza nyimbo kuti akope cidwi ca anthu. Kenako, anali kuliza nkhani ya Baibo. Nkhani ikasila, tinali kugaŵila mabuku kwa anthu acidwi.

Mtauni yaing’ono ya Cherryvale, ku Kansas, apolisi anauza atate kuti aleke kulalikila na motoka ya zokuzila mau m’paki ya tauni, cifukwa n’kumene anthu ambili anali kupumulila pa Sondo. Koma anawalola kucita zimenezo kunja kwa pakiyo. Atate anamvela, ndipo anaika motoka pa malo ena oyang’anana ndi pakiyo, n’colinga cakuti anthu m’pakiyo azikwanitsabe kumvetsela uthengawo. M’masiku amenewo, zinali zokondweletsa ngako kulalikila pamodzi na atate komanso mkulu wanga, Jerry.

Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1930, tinayamba makampeni apadela, n’colinga cakuti titsilize mofulumula kulalikila m’magawo amene munali citsutso kwambili. Monga nafotokozela kuciyambi, tinali kuuka kuseni-seni. Ndiyeno mwakacetecete, tinali kuika tumapepa twauthenga na tumabuku kunsi kwa zitseko pa nyumba za anthu. Pambuyo pake, tinali kukumana kunja kwa tauniyo kuti tione ngati wina wa ise wagwidwa kapena kumangiwa na apolisi.

M’zaka zimenezo, tinali kusangalalanso na ulaliki umene tinali kuucha kuti ndaŵala ya ulaliki. Polengeza uthenga wa Ufumu, tinali kukoloŵeka m’khosi zikwangwani zokhala na mau ena ake, n’kumayenda m’tauni mondondozana. Nikumbukila kuti pa ndaŵala ina imene inacitika m’tauni yathu, abale ananyamula zikwangwani zokhala na mau akuti “Cipembedzo ni Msampha Komanso Cinyengo.” Iwo ananyamuka ku nyumba kwathu na kuyenda msenga wa makilomita 1.6 m’tauni, kenako n’kubwelela. Mwamwayi, sanakumane na otsutsa aliwonse. Koma anakumana na anthu ambili acidwi amene anali kupenyelela.

MISONKHANO YACIGAWO YAKALE

Nthawi zambili, banja lathu linali kucoka ku Kansas kupita ku Texas kukapezeka pa msonkhano wacigawo. Atate anali kuseŵenza ku kampani yokonza njanji. Conco, tinali kukwela mahala sitima popita ku misonkhano yacigawo kapena kukaona acibululu. Amalume, a Fred Wismar, na akazi awo a Eulalie, anali kukhala ku Temple, mu mzinda wa Texas. Iwo anaphunzila coonadi ali acicepele, kuciyambi-yambi kwa m’ma 1900. Atabatizika, anaphunzitsako abululu awo coonadi, kuphatikizapo amayi. Iwo anatumikilako ku Texas monga mtumiki wa dela (amene masiku ano timati woyang’anila dela), ndipo abale ambili kumeneko anali kuwadziŵa bwino. Anali m’bale wokoma mtima, wansangala, ndi wocezeka. Anali wokonda coonadi, ndipo ananisonkhezela kukhala na zolinga zabwino pamene n’nali wacicepele.

Mu 1941, tinayenda ulendo wa pa sitima kupita ku msonkhano waukulu wacigawo ku St. Louis, mu mzinda wa Missouri. Ana tonse tinauzidwa kuti tikhale pa malo amodzi, kuti timvetsele nkhani ya M’bale Rutherford ya mutu wakuti, “Ana a Mfumu.” Nkhaniyo itatha, tonse ana okwana 15,000 tinasangalala kulandila mphatso yapadela, buku latsopano lakuti, Ana. M’bale Rutherford na abale ena ndiwo anatigaŵila mabukuwo.

Mu April 1943, tinasangalala na msonkhano wadela waung’ono, koma wosaiŵalika. Unali na mutu wakuti “Tigwile Nchito Mwakhama,” ndipo unacitikila m’tauni ya Coffeyville, ku Kansas. Pa msonkhanowu m’pamene panayambila Sukulu ya Ulaliki. Komanso panatulutsidwa kabuku kokhala na maphunzilo 52 oseŵenzetsa pa sukuluyo. Kumapeto kwa caka cimeneco, n’nakamba nkhani yanga yoyamba m’sukuluyo. Msonkhanowo unalinso wapadela kwa ine cifukwa m’pamene n’nabatizika. Ine pamodzi na abale ena, anatibatizila m’dziŵe linalake la pa famu, limene munali madzi ozizila kwambili.

N’NALI KULAKALAKA UTUMIKI WA PA BETELI

N’tatsiliza sukulu mu 1951, n’nafunika kusankha zimene n’dzacita mu umoyo wanga. N’nali kufunitsitsa kukatumikilako ku Beteli, kumene mkulu wanga anali kutumikila m’mbuyomo. Posakhalitsa, fomu yanga yofunsila utumikiwu inatumizidwa ku ofesi ya nthambi ku Brooklyn. Cosankha cimeneci cinanibweletsela madalitso ambili auzimu. Patapita cabe nthawi yocepa, ananiitana kuti nikayambe utumiki wa pa Beteli pa March 10, 1952.

N’nali kulakalaka kukaseŵenzela ku fakitale yopulintila mabuku, kuti nikathandize pa nchito yopulinta magazini na mabuku. Koma n’tafika, n’napatsidwa nchito yopelekela zakudya. Patapita nthawi, n’nayamba kuseŵenzela m’khichini, ndipo kumeneko n’naphunzila zambili. Conco, sin’nakhaleko na mwayi woseŵenzela ku fakitale yopulintila mabuku. Nchito ya m’khichini tinali kugwila mosinthana-sinthana. Izi zinali zothandiza kwa ine, cifukwa masana n’nali kukhala na mpata wocita phunzilo laumwini m’laibulali yaikulu ya pa Beteli. Izi zinanithandiza kukula mwauzimu na kulimba m’cikhulupililo. Komanso, zinanilimbikitsa kupitiliza kutumikila Yehova pa Beteli kwa nthawi yaitali mmene ningathele. Mkulu wanga Jerry anacoka pa Beteli mu 1949 na kukwatila mlongo Patricia. Koma anali kukhala pafupi na Beteli ku Brooklyn. Iwo ananithandiza kwambili na kunilimbikitsa m’zaka zoyambilila za utumiki wanga wa pa Beteli.

N’tafika kumene pa Beteli, panayamba kucitika mayeso pofuna kuwonjezela ciŵelengelo ca abale otumidwa na nthambi kukakamba nkhani pa misonkhano. Abale amenewo anali kutumidwa kuti akakambe nkhani za anthu onse m’mipingo ya mu Brooklyn, imene inali pa msenga wosapitilila makilomita 322 kucokela pa Beteli. Pambuyo pake, anali kuyenda mu ulaliki pamodzi na mpingo. Inenso n’nasankhidwa kuti nikhale m’gulu la abale amenewo. Mwamantha, n’nayamba kukamba nkhani yanga yoyamba ya anthu onse, imene pa nthawiyo inali kutenga ola lathunthu. Nthawi zambili, n’nali kuyenda pa sitima popita ku mipingo. Nikumbukila zimene zinacitika tsiku lina m’nyengo yozizila. Panali pa Sondo m’zuŵa, mu 1954. N’nakwela sitima yopita ku New York, ndipo n’nali kuyembekezela kukafika ku Beteli ca m’ma 17:00hrs kapena 19:00hrs madzulo. Koma kunacita cimphepo camphamvu, komanso kunazizila maningi mpaka kunagwa sinoo. Pa cifukwa ici, mainjini a sitima anali kungozimazima m’njila. Sitimayo inafika ku New York ca m’ma 05:00hrs, pa Monday kuseni. N’tafika kumeneko, n’nakwela sitima yopita ku Brooklyn, ndipo n’nangofikila m’khichini kukaseŵenza. N’nali n’tacedwako pang’ono, komanso n’nali wotopa kwambili cifukwa usiku wonse sin’nagone pa ulendowo. Koma zonsezo zinaiŵalika cifukwa ca cimwemwe cimene n’napeza kaamba kotumikila abale, ndiponso kupeza mabwenzi ambili atsopano m’mipingo imene n’nali kutumikila.

Tikukonzekela kuulutsa pulogilamu pa wailesi ya WBBR

M’kati mwa zaka zoyambilila za utumiki wanga pa Beteli, n’nauzidwa kuti niziulutsa nawo mapulogilamu pa wailesi ya WBBR. Panthawiyo, studiyo ya wailesiyi inali m’nyumba yochedwa 124 Columbia Heights, pa nsanjika yaciŵili. N’nali mmodzi wa abale na alongo amene anali kucita pulogilamu ya wiki iliyonse ya phunzilo la Baibo pa wailesiyo. M’bale A. H. Macmillan, mmodzi wa amkhalakale pa Beteli, kaŵili-kaŵili anali kutengako mbali pa pulogilamuyo. Tinali kungowachula kuti M’bale Mac. Iwo anali citsanzo cabwino ngako kwa ise atumiki acinyamata a pa Beteli, pa nkhani ya kupilila potumikila Yehova.

Tinali kugaŵila tumapepa tolimbikitsa anthu kumvetsela wailesi ya WBBR

Mu 1958, n’nauzidwa kuti nizitumikila ku Sukulu ya Giliyadi. Nchito yanga inali yothandiza abale na alongo otsiliza maphunzilo a Giliyadi kupeza mapasipoti, komanso kuwakonzela mayendedwe opita ku maiko kumene auzidwa kukatumikila. M’zaka zimenezo, maulendo a pa ndeke anali odula ngako. Conco, ni amishonale ocepa cabe amene anali kuyenda pa ndeke. Amishonale ambili amene anatumizidwa ku Africa na ku East Asia, anali kuyenda pa sitima zonyamula katundu. Pamene makampani a ndeke zonyamula anthu anayamba, mitengo ya ulendo wa pa ndeke inatsika kwambili. Ndipo amishonale ambili anayamba kuyenda pa ndeke popita ku maiko kumene anauzidwa kukatumikila.

Nikulongedza masatifiketi ya abale na alongo otsiliza maphunzilo a Giliyadi

MAULENDO A KU MISONKHANO YACIGAWO

Nchito yanga inakula mu 1960, pamene kunapangiwa makonzedwe ocita haya ndeke, kuti zikanyamule abale ocoka ku United States kupita ku Europe, kukacita misonkhano ya maiko mu 1961. N’nakwela ndeke pamodzi na abale ena, kucoka ku New York kupita ku msonkhano wa maiko umene unacitikila ku Hamburg, ku Germany. Msonkhanowo utatha, ine na abale ena atatu a pa Beteli tinabweleka motoka na kupita ku Italy, kukaona ofesi ya nthambi ku Rome. Titacoka kumeneko, tinapita ku France, kupitila ku mapili ochedwa Pyrenees Mountains, ndipo tinakafika mpaka ku Spain, kumene nchito yathu yolalikila inali yoletsedwa. Titafika ku Barcelona, mzinda waukulu wa dzikolo, tinakwanitsa kusiila abale mabuku. Tinawakulunga bwinobwino monga mphatso kuti a boma asadziŵe kuti tanyamula mabuku. Tinakondwela kwambili kukumana na abale athu kumeneko! Pambuyo pake, tinapita ku Amsterdam, kumene tinakakwela ndeke yopita ku New York.

Patapita pafupi-fupi caka cimodzi, utumiki wanga wa pa Beteli unaphatikizapo kukonzela mayendedwe abale ena amene anatumidwa ku msonkhano wapadela wa maiko, umene unacitikila m’maiko osiyana-siyana pa dziko lonse. Msonkhanowo unali na mutu wakuti, “Uthenga Wabwino Wosatha,” ndipo unacitika mu 1963. Panapangiwa makonzedwe akuti abale na alongo 583 apite kukapezeka pa msonkhanowu ku Europe, Asia, na ku South Pacific. Ulendo wawo unakathela ku Honolulu, m’cigawo ca Hawaii, na ku Pasadena, m’cigawo ca California. Pa ulendowo, anafunikanso kuima ku Lebanon na ku Jordan, kuti akaone malo osiyana-siyana ochulidwa m’Baibo. Kuwonjezela pa kukonzela abalewa mayendedwe komanso kogona, dipatimenti yathu inawathandizanso kutenga mapasipoti ongenela m’maikowo.

MNZANGA WATSOPANO WOYENDA NAYE

Caka ca 1963 cinali capadela kwa ine pa cifukwa cinanso. Pa June 29, n’nakwatila Lila Rogers wocokela ku Missouri, amene anali atabwela pa Beteli zaka zitatu m’mbuyomo. Patapita wiki imodzi kucokela pamene tinacita cikwati, ine na Lila tinayamba kupita nawo ku misonkhano ya maiko. Ndipo tinapita ku Greece, Egypt, na ku Lebanon. Pambuyo pake, tinayenda ulendo wa pa ndeke kucoka ku Beirut, mzinda waukulu wa Lebanon, kupita ku eyapoti inayake yaing’ono ya ku Jordan. Pa nthawiyo, nchito yathu inali yoletsedwa ku Jordan, ndipo tinauzidwa kuti Mboni za Yehova sizinali kuloledwa kungena m’dzikolo. Conco, tinada nkhawa kuti cidzacitika n’ciani ngati tangena m’dzikolo. Koma pamene tinafika, tinacita cidwi kwambili cifukwa tinaona gulu la anthu pa eyapoti, atanyamula cikwangwani cokhala na mau akuti, “Takulandilani a Mboni za Yehova”! Komanso, tinakondwela ngako kudzionela tekha madela ochulidwa m’Baibo! Tinaona kumene kunali kukhala makolo akale ochulidwa m’Baibo, komanso kumene Yesu na atumwi anali kulalikila. Tinaonanso kumene Cikhristu cinayambila kufalikila mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.—Mac. 13:47.

Kwa zaka 55, Lila wakhala akunithandiza mokhulupilika m’mautumiki onse amene takhala tikucita. Tinakwanitsa kupita ku Spain na ku Portugal maulendo angapo, m’nthawi imene nchito yathu inali yoletsedwa m’maiko amenewa. Tinalimbikitsa abale komanso kuwapatsa mabuku na zinthu zina zimene anali kufunikila. Tinakhalanso na mwayi wokaona abale athu amene anali m’jele pa malo ena ake amene kale kunali kukhala asilikali, ku Cádiz, m’dziko la Spain. N’nakondwela kukhala na mwayi wowalimbikitsa mwa kukamba nkhani ya m’Baibo.

Tili na Patricia na Jerry Molohan, pa ulendo wopita ku msonkhano wacigawo wa mu 1969, wa mutu wakuti “Mtendele pa Dziko”

Zaka zambili pambuyo pa caka ca 1963, n’nali na mwayi wokonzela abale na alongo mayendedwe opita ku misonkhano ya maiko ku Africa, Australia, Central na South America, Europe, East Asia, Hawaii, New Zealand, na ku Puerto Rico. Ine na Lila tinapezeka ku misonkhano yambili yosaiŵalika, monga wa ku Warsaw, m’dziko la Poland, mu 1989. Abale ambili a ku Soviet Union anapezekapo, ndipo kwa iwo unali msonkhano waukulu woyamba kupezekapo. Ena mwa iwo anali atakhala m’jele kwa zaka zambili m’mbuyomo ku Soviet Union, cifukwa ca cikhulupililo cawo.

Utumiki wina wokondweletsa umene n’nacitapo unali woyendela nthambi m’maiko osiyana-siyana, kukalimbikitsa atumiki a pa Beteli na amishonale. Pa ulendo wathu wotsiliza woyendela nthambi, tinapita ku South Korea. Kumeneko, tinali na mwayi woonana na abale 50 m’ndende ya ku Suwon. Onse anali na nkhope zacimwemwe, ndipo anali kuyembekezela mwacidwi kukayambanso kulalikila akadzatuluka m’ndende. Kuonana nawo cinali cinthu colimbikitsa kwambili!—Aroma 1:11, 12.

KUWONJEZEKA KWA GULU KUMANIBWELETSELA CIMWEMWE

M’zaka zapitazi, naona mmene Yehova wadalitsila anthu ake. Pamene n’nali kubatizika mu 1943, ofalitsa pa dziko lonse anali pafupi-fupi 100,000. Koma tsopano pali ofalitsa oposa 8 miliyoni amene akutumikila Yehova m’maiko 240. Nchito yaikulu imene abale na alongo otsiliza maphunzilo a Giliyadi amagwila yathandiza kwambili kuti pakhale kupita patsogolo kumeneku. Ndipo kwa ine, unali mwayi waukulu kuthandiza amishonale amenewa, mwa kuwakonzela zinthu zofunikila kuti akwanitse kupita ku maiko kumene anauzidwa kukatumikila.

Nimaona kuti n’nacita bwino kuwonjezela utumiki wanga mwa kufunsila utumiki wa pa Beteli pamene n’nali wacicepele. Yehova wanidalitsa kwambili pa zonse zimene nakhala nikucita pom’tumikila. Kuwonjezela pa cimwemwe cimene tapeza mu utumiki wa pa Beteli, ine na Lila tinali na mwayi wolalikila pamodzi na abale na alongo m’mipingo yosiyana-siyana ya ku Brooklyn. Ndipo tinapeza mabwenzi ambili okhalitsa.

Masiku yano, nikutumikilabe pa Beteli pamodzi na Lila. Olo kuti nili na zaka 84, nimakondwelabe na utumiki wanga. Tsopano nimathandiza pa nchito yoyankha makalata amene abale amalembela ku Sosaite.

Ine pamodzi na Lila masiku yano

Ndithudi, ni mwayi waukulu kwambili kukhala m’gulu la Yehova, komanso kuona kusiyana kwakukulu kumene kulipo pakati pa anthu amene amatumikila Yehova na amene sam’tumikila. Tsopano tikumvetsetsa mfundo ya pa Malaki 3:18, yakuti: “Anthu inu mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikila Mulungu ndi amene sanatumikilepo Mulungu.” Tsiku lililonse m’dziko la Satanali, timaona kuwonjezeka kwa magaŵano pakati pa anthu. Ndipo ambili alibe ciyembekezo ciliconse kapena cimwemwe mu umoyo wawo. Koma anthu amene amakonda Yehova na kum’tumikila, amakhala acimwemwe, olo kuti tikukhala m’nthawi zovuta. Alinso na ciyembekezo codalilika cam’tsogolo. Ha! Ni mwayi waukulu cotani nanga kugwila nawo nchito yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu! (Mat. 24:14) Ndithudi, tikuyembekezela mwacidwi zimene zidzacitika posacedwa, pamene Ufumu wa Mulungu udzawononga dziko loipali na kubweletsa dziko latsopano. Ufumuwo udzabweletsanso madalitso onse amene takhala tikuyembekezela, kuphatikizapo thanzi labwino na moyo wosatha. Pa nthawiyo, atumiki a Yehova okhulupilika pano pa dziko lapansi adzakondwela na moyo wamuyaya.