Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

N’ciani cinathandiza wophunzila wa Yesu, Sitefano, kukhalabe wodekha pamene anali kuzunzidwa?

SITEFANO anaweluzidwa na oweluza 71 oipa mtima kwambili. Pokhala oweluza a khoti lalikulu la ayuda, kapena kuti Sanihedirini, amuna amenewo anali na ulamulilo wamphamvu kwambili m’dziko la Isiraeli. Iwo anasonkhanitsidwa na Kayafa, Mkulu wa Ansembe, amenenso anatsogolela khoti la Sanihedirini miyezi ingapo m’mbuyomo poweluza Yesu kuti aphedwe. (Mat. 26:57, 59; Mac. 6:8-12) Oweluzawo anabweletsa mboni zonama, ndipo zinayamba kumuneneza Sitefano. Pamene anali kucita izi, iwo anadabwa kuona kuti nkhope yake inayamba kuoneka “ngati nkhope ya mngelo.”—Mac. 6:13-15.

N’ciani cinamuthandiza Sitefano kukhala na mtendele wa mumtima komanso kukhala wodekha pa nthawi yovuta kwambili imeneyi? Asanam’tengele ku khoti ya Sanihedirini, Sitefano anali kucita utumiki wake modzipeleka motsogoleledwa na mzimu wamphamvu wa Mulungu. (Mac. 6:3-7) Pamene anali kuzengedwa mlandu, mzimuwo unapitiliza kugwila nchito pa iye. Unali kum’tonthoza na kumukumbutsa zimene anaphunzila. (Yoh. 14:16) Pamene Sitefano anali kudziteteza molimba mtima, mzimu woyela unam’kumbutsa malemba 20 kapena kuposelapo ocokela m’Malemba Aciheberi. Zimene anakamba zinalembedwa mu caputa 7 ca Machitidwe. (Yoh. 14:26) Komanso cikhulupililo cake cinalimba kwambili pamene anaona masomphenya a Yesu ataimilila ku dzanja lamanja la Mulungu.—Mac. 7:54-56, 59, 60.

Na ise nthawi zina tingakumane na cizunzo kapena tingaopsezedwe na anthu. (Yoh. 15:20) Ngati tiŵelenga Mau a Mulungu nthawi zonse na kugwila nchito yolalikila mokangalika, timalola mzimu wa Yehova kugwila nchito pa ise. Komanso, timapeza mphamvu zimene zingatithandize kupilila citsutso tili na mtendele wa mu mtima.—1 Pet. 4:12-14.