Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Dalilani Yehova Kuti Mukhalebe na Moyo!

Dalilani Yehova Kuti Mukhalebe na Moyo!

“Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu.”—MIY. 3:5.

NYIMBO: 3, 8

1. N’cifukwa ciani tonse timafunikila citonthozo?

TONSE timafunikila citonthozo. N’kutheka kuti umoyo wathu wangodzala na mavuto, nkhawa, na zofooketsa. Mwina tikuvutika na ukalamba, kudwala, kapena kutaikilidwa munthu amene tinali kum’konda. Ndipo ena a ise timavutitsiwa na anthu ena. Cinanso, khalidwe la ciwawa likukula pakati pa anthu amene timakhala nawo. Mavuto amenewa ni umboni wakuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza,’ ndipo masiku akamapita timakhala tikuyandikila kwambili dziko latsopano. (2 Tim. 3:1) Komabe, mwina tayembekezela malonjezo a Yehova kwa nthawi yaitali, koma tikuona kuti mavuto athu akungowonjezeleka. Kodi tingapeze kuti citonthozo?

2, 3. (a) Kodi tidziŵako ciani za mneneli Habakuku? (b) N’cifukwa ciani tidzakambilana mfundo za m’buku la Habakuku?

2 Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambilane mfundo za m’buku la Habakuku. Olo kuti Malemba safotokoza zambili zokhudza nchito na umoyo wa Habakuku, m’buku la Habakuku muli mfundo zolimbikitsa kwambili. Zioneka kuti dzina lakuti Habakuku limatanthauza “Kukumbatila Mwacikondi.” Mwina mawuwa amakamba za mmene Yehova amatitonthozela. Iye amatitonthoza mokoma mtima, monga kuti watifukata mwacikondi. N’kuthekanso kuti amakamba za mmene olambila ake amamamatilila kwa iye cifukwa com’dalila. Habakuku anafunsa Yehova mafunso ambili, ndipo iye anamuyankha. Mulungu anamuuza kuti alembe zimene anakambilanazo, cifukwa anadziŵa kuti zidzakhala zothandiza kwa ise.—Hab. 2:2.

3 Malemba sakamba zambili zokhudza Habakuku, kupatulapo zimene iye anakambilana na Yehova, pa nthawi imene anali wovutika maganizo. Koma buku lake ni mbali ya “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale” m’Mawu a Mulungu Baibo, zimene “zimatipatsa ciyembekezo cifukwa malembawa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.” (Aroma 15:4) Kodi mfundo za m’buku la Habakuku zingatithandize bwanji? Zingatithandize kumvetsetsa tanthauzo la kudalila Yehova. Cinanso, ulosi wa Habakuku umatitsimikizila kuti n’zotheka kukhalabe na mtendele wa mu mtima ngakhale pamene tikukumana na mavuto. Tili na zimenezi m’maganizo, tiyeni manje tikambilane zambili zokhudza mfundo za m’buku la Habakuku.

TIZIPEMPHA THANDIZO KWA YEHOVA

4. N’cifukwa ciani Habakuku anavutika maganizo?

4 Ŵelengani Habakuku 1:2, 3. M’nthawi ya Habakuku, zinthu zinali zovuta kwambili. Iye anakhumudwa kwambili cifukwa anthu ambili pa nthawiyo anali na makhalidwe oipa komanso aciwawa. Iye anayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi zoipa zonsezi zidzatha liti? N’cifukwa ciani Yehova sakucitapo kanthu mwamsanga?’ Habakuku anaona kuti kulikonse mu Yuda, anthu anali kupondeleza anzawo na kucita zinthu zopanda cilungamo. Iye anafika pothedwa nzelu. Pa nthawi yovuta imeneyi, Habakuku anapempha Yehova kuti acitepo kanthu. N’kutheka kuti iye anayamba kuganiza kuti Yehova sakuwaganizilanso anthu ake. Anaona ngati kuti Mulungu sadzacitapo kanthu mwamsanga. Kodi na imwe nthawi zina mumamvela monga mmene mtumiki wa Mulungu ameneyu anamvelela?

5. Ni mfundo yofunika kwambili iti imene taphunzila m’buku la Habakuku? (Onani pikica kuciyambi.)

5 Kodi Habakuku analeka kudalila Yehova? Kodi analeka kukhulupilila malonjezo a Mulungu? Kutalitali! Kumbukilani kuti iye anauza Yehova nkhawa zake na mavuto ake. Izi zionetsa kuti sanaleke kudalila Yehova. Komabe, Habakuku anavutika maganizo posamvetsetsa cifukwa cake Yehova sanagwepo mwamsanga. Komanso sanamvetsetse cifukwa cimene analolela kuti iye akumane na mavuto aakulu. Yehova anauzila Habakuku kulemba nkhawa zake. Izi zitiphunzitsa mfundo yofunika kwambili yakuti: Tisamaope kumuuza Yehova ngati tili na nkhawa, kapena ngati cikhulupililo cathu cayamba kufooka. Ndipo iye mokoma mtima amatipempha kuti tizimukhuthulila za mu mtima mwathu kupitila m’pemphelo. (Sal. 50:15; 62:8) Miyambo 3:5 imatilimbikitsa kuti “tizikhulupilila Yehova ndi mtima [wathu] wonse,” na kuti “tisamadalile luso [lathu] lomvetsa zinthu.” Habakuku ayenela kuti anali kuwadziŵa bwino mawu amenewa, ndipo anawagwilitsila nchito.

6. N’cifukwa ciani kupemphela n’kofunika kwambili?

6 Habakuku anacitapo kanthu kuti alimbitse ubwenzi wake na Yehova, amene anali Tate komanso Bwenzi lake lokhulupilika. Iye sanangokhala n’kumadandaula za mavuto ake, kapena kuyesa kuthetsa yekha mavutowo. M’malomwake, anauza Yehova nkhawa zake, ndipo mwa ici, anatisiila citsanzo cabwino. Kuwonjezela apo, Yehova, amene ni Wakumva pemphelo, amatipempha kuti tizionetsa kuti timamukhulupilila mwa kumuuza nkhawa zathu m’pemphelo. (Sal. 65:2) Tikacita zimenezi, iye adzayankha mapemphelo athu. Adzatitonthoza mwacikondi na kutitsogolela. (Sal. 73:23, 24) Adzatithandiza kudziŵa mmene amaonela mavuto athu, olo akhale aakulu bwanji. Kupemphela mocokela pansi pa mtima ni njila imodzi yofunika kwambili yoonetsela kuti timadalila Mulungu.

TIZIMVETSELA KWA YEHOVA

7. Kodi Yehova anacita ciani Habakuku atamuuza nkhawa zake?

7 Ŵelengani Habakuku 1:5-7. Pambuyo pouza Yehova nkhaŵa zake, n’kutheka kuti Habakuku anayamba kudela nkhawa kuti mwina Yehova adzamudzudzula. Koma pokhala Tate wacifundo ndi woganizila ena, Yehova sanam’dzudzule cifukwa cofotokoza madandaulo ake moona mtima. Mulungu anadziŵa kuti Habakuku anali kucondelela thandizo cifukwa covutika mtima na zoipa zimene zinali kucitika. Conco, Yehova anauza Habakuku zimene zinali pafupi kucitikila Ayuda osamvela. N’kutheka kuti Habakuku ndiye anali woyamba kuuziwa na Yehova kuti kwatsala kanthawi kocepa kuti Ayuda aciwawa awonongedwe.

8. N’cifukwa ciani Habakuku sanayembekezele kuti Yehova adzamuyankha mmene anacitila?

8 Yehova anatsimikizila Habakuku kuti anali wokonzeka kucitapo kanthu. Anamuuza kuti adzaseŵenzetsa Akasidi, kapena kuti Ababulo polanga Ayuda oipa ndi aciwawa amenewo. Pamene Yehova anaseŵenzetsa mawu akuti “m’masiku anu,” iye anaonetsa kuti ciweluzoco cidzabwela mneneli Habakuku akali moyo, kapena Aisiraeli ena amene analipo pa nthawiyo asanafe. Habakuku sanayembekezele kuti Yehova angamuyankhe mwanjila imeneyi. Zimene Yehova anamuuza, zakuti adzaseŵenzetsa Ababulo polanga anthu ake, zinaonetsa kuti mavuto adzawonjezeka pakati pa Ayuda. * Ababulo anali anthu opanda cifundo komanso ankhanza. Iwo anali aciwawa kwambili kuposa Ayuda a m’nthawi ya Habakuku, omwe anali kudziŵa malamulo a Yehova. Mwina Habakuku anadzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciani Yehova afuna kuseŵenzetsa mtundu wacikunja wankhanza umenewu polanga anthu ake?’ Sembe munali imwe, kodi mukanamvela bwanji pambuyo pa kumva yankho ya Mulungu imeneyi?

9. Kodi Habakuku ayenela kuti anafunsa Mulungu mafunso monga ati?

9 Ŵelengani Habakuku 1:12-14, 17. Habakuku anadziŵa kuti Yehova adzaseŵenzetsa Ababulo poweluza na kulanga anthu ocita zoipa a mtundu wake. Koma panali zina zimene sanali kumvetsetsa pa nkhaniyo. Ngakhale n’conco, iye anakhala wodzicepetsa ndipo anatsimikiza mtima kupitiliza kudalila Yehova. Komanso anakamba kuti Yehova anakhalabe “thanthwe” lake. (Deut. 32:4; Yes. 26:4) Habakuku anapitiliza kukhulupilila kuti Yehova ni Mulungu wacikondi komanso wokoma mtima. N’cifukwa cake anakhala womasuka kucondelelanso kwa Yehova. Anam’funsa mafunso monga akuti, ‘N’cifukwa ciani mwalola kuti zinthu ziipile-ipile mu Yuda? N’cifukwa ciani simunaloŵelelepo mwamsanga? N’cifukwa ciani inu Wamphamvuzonse mukulola kuti mavuto awonjezeleke? N’cifukwa ciani ‘mukukhala cete’ pamene zoipa zikuculukila-culukila?’ Habakuku anafunsa mafunso amenewa cifukwa anali kudziŵa kuti Mulungu ni ‘woyela kwambili moti sangaonelele zinthu zoipa.’

10. Mofanana ndi Habakuku, kodi nthawi zina na ise tingamvele bwanji?

10 Nthawi zina, isenso tingamvele monga mmene Habakuku anamvelela. Timamvetsela kwa Yehova. Timam’khulupilila, ndipo timaŵelenga na kuphunzila Mawu ake, amene amatipatsa ciyembekezo. Timamva za malonjezo ake kupitila m’zimene gulu lake limatiphunzitsa. Komabe, tingadzifunse kuti, ‘Kodi mavuto amene tikukumana nawo adzatha liti?’ Lekani tsopano tikambilane zimene Habakuku anacita pambuyo pomvetsela kwa Mulungu. Kenako, tiona zimene tingaphunzilepo.

TIZIYEMBEKEZELA PA YEHOVA

11. Kodi Habakuku anatsimikiza mtima kucita ciani pambuyo pomvetsela kwa Yehova?

11 Ŵelengani Habakuku 2:1. Zimene Habakuku anakambilana na Yehova zinam’khazika mtima pansi. Ndipo anatsimikiza mtima kupitiliza kuyembekezela Yehova. Patapita nthawi, Habakuku anakambanso mawu ena oonetsa kuti anatsimikiza mtima kuyembekezela pa Mulungu. Anati: “Ndidzayembekezela mofatsa tsiku la nsautso.” (Hab. 3:16) Atumiki a Mulungu enanso okhulupilika anali na mtima woyembekezela pa Yehova. Izi zitilimbikitsa kuti sitiyenela kulema poyembekezela pa Yehova.—Mika 7:7; Yak. 5:7, 8.

12. Ni mfundo zina ziti zimene tiphunzilapo pa citsanzo ca Habakuku?

12 Habakuku anatsimikiza mtima kuyembekezela Yehova. Kodi ise tiphunzilapo ciani? Coyamba, olo tikumane na mavuto abwanji, tisaleke kupemphela kwa Yehova. Caciŵili, tizimvela zimene Yehova amatiphunzitsa kupitila m’Mawu ake komanso m’gulu lake. Cacitatu, tiziyembekezela Yehova moleza mtima, tili na cikhulupililo cakuti adzathetsa mavuto athu pa nthawi yake yoyenela. Ngati tipitiliza kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima, kumvetsela kwa iye, na kumuyembekezela moleza mtima monga anacitila Habakuku, tidzakhala na mtendele wa mu mtima. Mtendele umenewo udzatithandiza kupilila mavuto. Cinanso, ciyembekezo cimatithandiza kukhala woleza mtima kwambili. Ndipo kuleza mtima kumatithandiza kukhalabe acimwemwe ngakhale tikumane na mavuto ambili. Ciyembekezo cimatithandizanso kukhala na cikhulupililo cakuti Atate wathu wakumwamba sadzalephela kucitapo kanthu.—Aroma 12:12.

13. Ni mawu ati olimbikitsa amene ali pa Habakuku 2:3?

13 Ŵelengani Habakuku 2:3. Yehova ayenela kuti anakondwela ataona kuti Habakuku wasankha kuyembekezela pa iye. Pokhala Mulungu Wamphamvuzonse, iye anali kudziŵa bwino mavuto amene Habakuku anali kukumana nawo. Conco, Mulungu anatonthoza mneneli wakeyo mwa kum’tsimikizila mwacikondi ndi mokoma mtima kuti mafunso ake adzayankhidwa. Anam’tsimikizilanso kuti posacedwa, nkhawa zake zonse zidzathetsedwa. Zinali monga kuti Mulungu akuuza Habakuku kuti: “Leza mtima, ndipo uzinidalila. Nidzacitapo kanthu ndithu, olo zioneke monga nikucedwa!” Yehova anakumbutsa Habakuku kuti ali na nthawi yoikidwilatu yokwanilitsa malonjezo ake. Anamulangiza kuti afunika kupitiliza kuyembekezela, ndipo pamapeto pake zonse zimene iye analonjeza zidzacitika.

N’cifukwa ciani timacita zonse zimene tingathe potumikila Yehova? (Onani palagilafu 14)

14. Kodi tifunika kutsimikiza mtima kucita ciani tikakumana na mavuto?

14 Kuyembekezela pa Yehova moleza mtima na kumvetsela mwachelu zimene amatiphunzitsa, kudzatilimbikitsa kuti tizim’dalila. Komanso kudzatithandiza kukhala na mtendele wamumtima, olo pamene tikumana na mavuto. Yesu anakamba kuti tiyenela kudalila Yehova, monga Wosunga Nthawi Wamkulu. Ndipo sitifunika kudela nkhawa za “nthawi kapena nyengo” zimene Mulungu sanatiululile. (Mac. 1:7) Conco, tisaleme kuyembekezela pa Yehova modzicepetsa, moleza mtima, komanso mwacikhulupililo. Ndipo tiziseŵenzetsa mwanzelu nthawi yathu mwa kucita zonse zimene tingathe potumikila Yehova.—Maliko 13:35-37; Agal. 6:9.

TIKAMADALILA YEHOVA, TIDZAPEZA MOYO WENI-WENI NA TSOGOLO LABWINO

15, 16. (a) Kodi m’buku la Habakuku muli malonjezo ati olimbikitsa? (b) Nanga tiphunzilapo ciani pa malonjezo amenewo?

15 Yehova analonjeza anthu olungama amene amam’dalila kuti: “Wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa cikhulupililo cake.” Analonjezanso kuti: “Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziŵa ulemelelo wa Yehova.” (Hab. 2:4, 14) Inde, anthu oleza mtima amene amadalila Mulungu, adzalandila mphoto ya moyo wosatha.

16 Lonjezo la pa Habakuku 2:4 ni lolimbikitsa kwambili. Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo anagwila mawu a m’vesi imeneyi katatu m’makalata ake ouzilidwa. (Aroma 1:17; Agal. 3:11; Aheb. 10:38) Ngakhale titakumana na mavuto aakulu bwanji, ngati tikhalabe okhulupilika kwa Yehova komanso kukhala na cikhulupililo mwa iye, tidzaona kukwanilitsika kwa colinga cake. Yehova amatilimbikitsa kuti tiziganizila za madalitso a kutsogolo.

17. Kodi Yehova walonjeza kuti adzaticitila ciani ngati tim’dalila?

17 M’buku la Habakuku, muli mfundo zothandiza kwambili kwa ise masiku ano otsiliza. Yehova walonjeza moyo wosatha kwa anthu onse olungama amene amam’khulupilila na kum’dalila. Conco, kaya tili na nkhawa yotani kapena tikukumana na mavuto otani, tiyeni tipitilize kulimbitsa cikhulupililo na cidalilo cathu mwa Mulungu. Kupitila m’buku la Habakuku, Yehova akutitsimikizila kuti adzaticilikiza na kutipulumutsa. Iye akutipempha mokoma mtima kuti tizim’dalila na kuyembekezela moleza mtima nthawi yake yoikika, pamene Ufumu wa Mulungu udzalamulila dziko lapansi. Pa nthawiyo, dziko lonse lidzadzaza na olambila ake ofatsa ndi acimwemwe.—Mat. 5:5; Aheb. 10:36-39.

MUZIDALILA YEHOVA, NDIPO MUDZAKHALABE ACIMWEMWE

18. Kodi mawu a Yehova anam’limbikitsa bwanji Habakuku?

18 Ŵelengani Habakuku 3:16-19. Mawu a Yehova anam’limbikitsa kwambili Habakuku. Iye anasinkhasinkha pa nchito zazikulu zimene Yehova anacitila anthu ake kumbuyoko. Cidalilo cake mwa Yehova cinalimbanso, cifukwa anadziŵa kuti iye adzacitapo kanthu mwamsanga. Izi zinam’tonthoza mneneliyu, ngakhale kuti anadziŵa kuti mavuto ake angapitilize kwa kanthawi ndithu. Habakuku sanakhalenso na cikayikilo. M’malomwake, anakhala na cikhulupililo colimba cakuti Yehova adzam’pulumutsa. Ndipo anakamba mawu ocititsa cidwi kwambili oonetsa kuti anali kudalila Mulungu. Akatswili ena a Baibo amakamba kuti mawu a pa vesi 18, angamasulidwenso kuti, “Nidzalumpha cifukwa cokondwela mwa Ambuye. Nidzavina mozungulila cifukwa cosangalala mwa Mulungu.” Ndithudi, mawu a pa Habakuku 3:16-19 ni olimbikitsa kwambili kwa ise tonse! Yehova watilonjeza zinthu zokondweletsa ngako, komanso watitsimikizila kuti sadzacedwa kukwanilitsa malonjezo ake.

19. Kodi tiyenela kucita ciani kuti titonthozedwe mmene Habakuku anatonthozedwela?

19 Mfundo yofunika kwambili imene tiphunzilapo m’buku la Habakuku ni yakuti tizidalila Yehova. (Hab. 2:4) Tingapitilize kudalila Yehova ngati tilimbitsa ubwenzi wathu na iye mwa (1) kulimbikila kupemphela, na kumuuza mavuto athu na nkhawa zathu zonse; (2) kumvetsela mwachelu Mawu a Yehova na malangizo amene timalandila m’gulu lake; komanso (3) kukhala wokhulupilika na woleza mtima pamene tiyembekezela pa Yehova. Izi n’zimene Habakuku anacita. Pamene anayamba kufunsa mafunso Yehova, Habakuku anali wopanikizika maganizo kwambili ndi wankhawa. Koma pamapeto pake analimbikitsidwa, ndipo anakhala na cimwemwe. Titengele citsanzo cabwino ca Habakuku. Ndipo tikatelo, tidzatonthozedwa mwacikondi na Atate wathu Yehova. Kukamba zoona, kulibe kulikonse kumene tingapeze citonthozo m’dziko loipali kuposa kwa Yehova!

^ par. 8 Mawu akuti “anthu inu” pa Habakuku 1:5, anaonetsa kuti cilango ca Mulungu cidzakhudza mtundu wonse wa Ayuda.