Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Ndidzayenda M’coonadi Canu”

“Ndidzayenda M’coonadi Canu”

“Inu Yehova, ndilangizeni za njila yanu. Ndidzayenda m’coonadi canu.”—SAL. 86:11.

NYIMBO: 31, 72

1-3. (a) Kodi tifunika kuciona bwanji coonadi ca m’Baibo? Fotokozani fanizo. (Onani mapikica pamwambapa.) (b) Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani ino?

MASIKU ANO, kubweza katundu amene munthu wagula n’kofala kwambili. Ofufuza anapeza kuti m’maiko ena, anthu amabweza pafupi-fupi 9 pesenti ya katundu amene agula m’shopu. Ndipo ciŵelengelo ca katundu wogulidwa pa intaneti amene amabwezedwa, cingapitilile pa 30 pesenti. Anthu amabweza katundu, mwina cifukwa cakuti si wabwino monga mmene anali kuganizila, ni wowonongeka, kapena sanaukonde cabe. Conco, iwo amakabweza katunduyo kwa ogulitsa kuti awapatse wina kapena kuti awabwezele ndalama zawo.

2 Nthawi zina, na ise tingapemphe ogulitsa malonda kuti atibwezele ndalama pa katundu amene tinagula. Koma sitingafune ngakhale pang’ono kubweza kapena kuti ‘kugulitsa’ “coonadi” cimene ‘tinagula.’ (Ŵelengani Miyambo 23:23; 1 Tim. 2:4) Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, tinagula coonadi mwa kupatula nthawi yoculuka kuti ticiphunzile. Tinaphunzilanso kuti ena a ise tinagula coonadi mwa kusiya nchito yapamwamba, komanso kupilila pamene anzathu na acibululu anali kutisala kapena kutitsutsa. Ndipo ena anayesetsa kusintha maganizo na khalidwe lawo, komanso analeka miyambo na zikondwelelo zosagwilizana na Malemba kuti agule coonadi. Komabe, zinthu zimene tinatailapo n’zocepa kwambili poyelekeza na madalitso amene tapeza.

3 Pa nkhani ya mmene timaonela coonadi ca m’Baibo, maganizo athu ni olingana ndi a munthu wa m’fanizo la Yesu. Pofuna kuonetsa kuti coonadi ca Ufumu wa Mulungu n’camtengo wapatali kwa anthu amene acipeza, Yesu anakamba fanizo la wamalonda woyendayenda amene anali kusakila ngale zabwino, ndipo anapezako imodzi. Ngale imene anapezayo inali yamtengo wapatali kwambili kwa iye cakuti ‘mwamsanga’ anapita kukagulitsa zinthu zake zonse kuti akagule ngaleyo. (Mat. 13:45, 46) Mofananamo, coonadi conena za Ufumu wa Mulungu, komanso mfundo zonse za coonadi zimene tinaphunzila m’Baibo, n’zamtengo wapatali kwambili cakuti tinatailapo zambili kuti ticipeze. Tikamaona coonadi kukhala camtengo wapatali, sitidzayesa n’komwe ‘kucigulitsa’. Koma n’zacisoni kuti atumiki ena a Mulungu analeka kuona coonadi kukhala camtengo wapatali, ndipo anafika ngakhale pocigulitsa. Tisalole zaconco kuticitikila! Tingaonetse kuti timakonda kwambili coonadi na kuti sitingayese kucigulitsa, mwa kumvela malangizo a m’Baibo akuti ‘tipitilizebe kuyenda m’coonadi.’ (Ŵelengani 3 Yohane 2-4) Kuyenda m’coonadi kumaphatikizapo kucikonda, kapena kuti kucita zinthu mogwilizana na coonadi, komanso kuciika patsogolo mu umoyo wathu. Tsopano tiyeni tikambilane mafunso aya: Kodi anthu ena amacigulitsa bwanji coonadi? Nanga n’cifukwa ciani amatelo? Tingapewe bwanji kucita zinthu zomvetsa cisoni zimenezi? Nanga n’ciani cingatithandize ‘kupitilizabe kuyenda m’coonadi’?

MMENE ENA ‘AMAGULITSILA’ COONADI, NA CIFUKWA CAKE

4. M’nthawi ya Yesu, n’cifukwa ciani anthu ena ‘anagulitsa’ coonadi?

4 M’nthawi ya Yesu, anthu ena amene poyamba anamvetsela mwacidwi ziphunzitso zake, pambuyo pake analeka kuyenda m’coonadi. Mwacitsanzo, tsiku lina Yesu atadyetsa khamu la anthu mozizwitsa, khamulo linamutsatila ku tsidya lina la Nyanja ya Galileya. Kumeneko, Yesu anakamba zinthu zimene zinawadabwitsa kwambili. Anati: “Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, mulibe moyo mwa inu.” M’malo mopempha Yesu kuti awamasulile tanthauzo la zimenezi, iwo anakhumudwa ndipo anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndani angamvetsele zimenezi?” Cifukwa cokhumudwa, “ophunzila ake ambili anamusiya ndi kubwelela ku zinthu zakumbuyo, ndipo sanayendenso naye.”—Yoh. 6:53-66.

5, 6. (a) N’cifukwa ciani masiku ano Akhristu ena asiya coonadi? (b) Kodi munthu angasiye bwanji coonadi pang’ono-pang’ono?

5 N’zacisoni kuti masiku ano, Akhristu ena alephela kucigwilitsitsa coonadi. Ena anakhumudwa cifukwa ca kusintha kwa kamvedwe ka lemba linalake, kapena cifukwa ca zimene m’bale wina waudindo anakamba kapena kucita. Palinso ena amene anakhumudwa cifukwa ca uphungu wa m’Malemba umene anapatsiwa. Ndipo ena anasiya coonadi cifukwa cokhumudwitsana na Mkhristu mnzawo. Komanso, ena anayamba kugwilizana ndi ampatuko kapena anthu otsutsa amene amapotoza ziphunzitso zathu. Zotulukapo zake, iwo anayamba ‘kucoka’ kwa Yehova, ndipo analeka kugwilizana na mpingo wacikhristu. (Aheb. 3:12-14) Ndithudi, cikanakhala bwino anthu amenewo akanasungabe cikhulupililo cawo na kupitiliza kudalila Yesu, monga mmene mtumwi Petulo anacitila. Pamene Yesu anafunsa atumwi ngati anali kufuna kumusiya, mwamsanga Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.”—Yoh. 6:67-69.

6 Akhristu ena anasiya coonadi mwapang’ono-ng’ono, mwina ngakhale mosazindikila. Anthu amene amasiya coonadi pang’ono-pang’ono ali monga boti imene imafendela yokha pang’ono-pang’ono kucoka pa doko. Baibo imakamba kuti iwo ‘amatengeka pang’ono-pang’ono’ n’kusiya cikhulupililo. (Aheb. 2:1) Mosiyana na munthu amene amacoka m’coonadi mwadala, munthu amene amatengeka pang’ono-pang’ono, amasiya coonadi mosazindikila. Ngakhale n’conco, munthu wotelo amasokoneza ubwenzi wake na Yehova, ndipo m’kupita kwa nthawi ubwenziwo ungatheletu. Kodi tingacite ciani kuti zaconco zisaticitikile?

KODI TINGAPEWE BWANJI KUGULITSA COONADI?

7. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tipewe kugulitsa coonadi?

7 Kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, tifunika kukhulupilila na kumvela mawu onse a Yehova. Tifunika kuika coonadi patsogolo mu umoyo wathu, komanso kutsatila mfundo za m’Baibo. Popemphela kwa Yehova, Mfumu Davide anati: “Ndidzayenda m’coonadi canu.” (Sal. 86:11) Davide anatsimikiza mtima kuyenda m’coonadi. Na ise tiyenela kukhala wotsimikiza mtima kupitiliza kuyenda m’coonadi ca Mulungu. Apo ayi, tingayambe kuganiza kuti tinataya mwayi posiya zinthu zina kuti tigule coonadi, ndipo tingamalakalake kubwelelanso ku zinthu zimenezo. Conco, tiyenela kukhulupilila mfundo zonse za coonadi. Sitiyenela kucita kusankha mfundo zimene tingakhulupilile. Paja Baibo imakamba kuti tifunika kuyenda “m’coonadi conse.” (Yoh. 16:13) M’nkhani yapita, tinakambilana zinthu zisanu zimene tinatailapo kuti tigule coonadi. Tiyeni manje tikambilanenso zinthu zimenezo. Kucita izi kudzatithandiza kuti tisamalakalake kubwelelanso ku zinthu zimenezo.—Mat. 6:19.

8. Kodi kuseŵenzetsa nthawi mosasamala kungapangitse bwanji Mkhristu kutengeka pang’ono-pang’ono mpaka kusiya coonadi? Fotokozani citsanzo.

8 Nthawi. Kuti tisatengeke pang’ono-pang’ono mpaka kusiya coonadi, tifunika kumaseŵenzetsa nthawi yathu mwanzelu. Ngati sitisamala, tingayambe kuthela nthawi yoculuka pa zosangalatsa, kufufuza zinthu pa Intaneti, kapena kutamba TV. Zosangalatsa mwa izo zokha zilibe vuto. Koma zingayambe kutidyela nthawi yocita phunzilo laumwini na zinthu zina zauzimu. Mwacitsanzo, ganizilani za mlongo wina dzina lake Emma. * Kuyambila ali wacicepele, anali kukonda maseŵela okwela mahosi, ndipo anali kuthela nthawi yambili pocita maseŵelawa. Patapita nthawi, Emma anayamba kuda nkhawa na nthawi imene anali kutayila pa maseŵelawa. Conco, anapanga masinthidwe oyenelela, ndipo analeka kutayila nthawi pa zosangalatsa. Iye analimbikitsiwanso na citsanzo ca Cory Wells, amene anali katswili wa maseŵela okwela pa hosi. * Tsopano Emma amatayila nthawi yambili pa zinthu zauzimu, komanso poceza na banja lake na Akhristu anzake. Iye amaona kuti ubwenzi wake na Yehova walimba, ndipo ali na mtendele wa mu mtima, podziŵa kuti amaseŵenzetsa nthawi yake mwanzelu.

9. Kodi kufuna-funa cuma cakuthupi kungapangitse bwanji Akhristu ena kuyamba kunyalanyaza zinthu zauzimu?

9 Cuma cakuthupi. Kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, tifunika kupewa kuika zinthu zakuthupi patsogolo mu umoyo wathu. Pamene tinaphunzila coonadi, tinayamba kuona zinthu zauzimu kukhala zofunika kwambili kuposa zinthu zakuthupi. Ndipo tinalolela kudzimana zinthu zina zakuthupi kuti tiyambe kuyenda m’coonadi. Komabe, m’kupita kwa nthawi, tingayambe kuona anzathu akugula zipangizo zamakono zodula, kapena kusangalala na zinthu zina zakuthupi. Tingayambe kuganiza kuti tikumanidwa zabwino. Posakhutila na zinthu zofunika kwambili zimene tili nazo, tingayambe kunyalanyaza zinthu zauzimu pofuna kudziunjikila cuma. Izi zitikumbutsa nkhani ya Dema. Iye analeka kutumikila pamodzi na mtumwi Paulo cifukwa cokonda “zinthu za m’nthawi ino.” (2 Tim. 4:10) Mwina Dema anakonda kwambili zinthu zakuthupi kuposa kutumikila Mulungu. N’kuthekanso kuti sanafunenso kupitiliza na umoyo wodzimana kuti azitumikila pamodzi na Paulo. Izi zitiphunzitsa kuti ngati kale tinali na mtima wokonda cuma, tiyenela kukhala wosamala kuti tisakhalenso na mtima umenewu, cifukwa ungatilepheletse kukonda coonadi.

10. Kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, sitiyenela kugonja ku ciani?

10 Mabwenzi komanso acibululu. Kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, sitifunika kugonja ngati ena amatitsutsa. Pamene tinayamba kuyenda m’coonadi, mgwilizano wathu na acibululu komanso anthu ena amene si Mboni unasintha. Ena anangololela, koma ena anayamba kutitsutsa kwambili. (1 Pet. 4:4) Timayesetsa kukhala bwino na abululu athu, komanso kucita nawo zinthu mokoma mtima. Komabe, tifunika kukhala osamala kuti tisanyalanyaze mfundo za coonadi pofuna kuwakondweletsa. Tifunika kupitiliza kucita zimene tingathe kuti tizikhala mwamtendele na abululu athu. Koma mogwilizana ndi cenjezo la pa 1 Akorinto 15:33, tiyenela kupewelatu kupanga ubwenzi wathithithi ndi anthu amene sakonda Yehova.

11. Kodi tingapewe bwanji makhalidwe osagwilizana na Malemba?

11 Maganizo osayenela komanso makhalidwe oipa. Anthu onse amene amayenda m’coonadi afunika kukhala oyela. (Yes. 35:8; ŵelengani 1 Petulo 1:14-16.) Pamene tinaphunzila coonadi, ise tonse tinasintha makhalidwe athu na kuyamba kutsatila mfundo zolungama za m’Baibo. Ena anali na makhalidwe oipa kwambili, koma anasintha. Mosasamala kanthu kuti tinali na khalidwe lotani tisanaphunzile coonadi, sitiyenela kusinthanitsa khalidwe loyela limene tili nalo na makhalidwe onyansa a m’dzikoli. Kodi tingapewe bwanji makhalidwe oipa? Tizikumbukila kuti pofuna kutithandiza kukhala oyela, Yehova anapeleka nsembe yamtengo wapatali kwambili, imene ni magazi a Mwana wake, Yesu Khristu. (1 Pet. 1:18, 19) Conco, kuti tikhalebe oyela pa maso pa Yehova, nthawi zonse tizikumbukila nsembe yamtengo wapatali ya dipo la Yesu.

12, 13. (a) N’cifukwa ciani kuona zikondwelelo mmene Yehova amazionela n’kofunika nthawi zonse? (b) Kodi tidzakambilana ciani tsopano?

12 Miyambo na zikondwelelo zosagwilizana na Malemba. Acibululu, anzathu a ku nchito, ndiponso anzathu a ku sukulu, angayese kutikopa kuti ticiteko zikondwelelo zosemphana na Malemba. Tingacite ciani kuti tisagonje ngati anthu akutituntha kuti ticite nawo miyambo na zikondwelelo zosalemekeza Yehova? Tizikumbukila nthawi zonse mmene Yehova amaonela miyambo na zikondwelelo zimenezo. Kuŵelenganso nkhani za m’mabuku athu, zofotokoza mmene zikondwelelo zofala zinayambila n’kothandiza. Ngati tikumbukila zifukwa za m’Malemba zimene siticitila nawo zikondwelelo zimenezo, timakhala okhutila kuti tikuyenda m’njila ‘yovomelezeka kwa Ambuye.” (Aef. 5:10) Kukhulupilila Yehova na Mawu ake a coonadi kudzatiteteza ku msampha ‘woopa anthu.’—Miy. 29:25.

13 Kuyenda m’coonadi kulibe polekezela. Ndise ofunitsitsa kuyendabe pa njila imeneyi mpaka muyaya. Koma n’ciani cingatithandize ‘kupitilizabe kuyenda m’coonadi’? Tiyeni tikambilane zinthu zitatu.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUPITILIZE KUYENDA M’COONADI

14. (a) Kodi kupitiliza kugula coonadi kapena kuti kuciphunzila kungatithandize bwanji kuti tisacigulitse? (b) N’cifukwa ciani malangizo, kumvetsa zinthu, na nzelu n’zofunika kwambili?

14 Coyamba, tiyenela kupitiliza kuphunzila na kusinkhasinkha pa coonadi camtengo wapatali ca m’Mawu a Mulungu. Nthawi zonse tizipatula nthawi yogula coonadi, kapena kuti kuciphunzila. Tikatelo, tidzayamba kucikonda kwambili, ndipo sitidzayesa ngakhale pang’ono kucigulitsa. Kuwonjezela pa kugula coonadi, Miyambo 23:23 imakambanso kuti tiyenela kugula “nzelu, malangizo ndi kumvetsa zinthu.” Komabe, kudziŵa zinthu pakokha si kokwanila. Tifunika kumaseŵenzetsa coonadi cimene taphunzila. Kukhala womvetsa zinthu, kumatithandiza kuti tizitha kuona kugwilizana kwa mfundo za Yehova. Ndipo nzelu zimatisonkhezela kucita zimene tinaphunzila. Komanso, nthawi zina coonadi cimatiwongolela, mwa kutithandiza kudziŵa zimene tifunika kukonza mu umoyo wathu. Conco, tikalandila malangizo, nthawi zonse tiziyesetsa kugwililapo nchito. Malangizo ni amtengo wapatali kuposa siliva.—Miy. 8:10.

15. Kodi lamba wa coonadi amatiteteza bwanji?

15 Caciŵili, tiziyesetsa kucita zinthu mogwilizana na coonadi tsiku lililonse. Tiyenela kumanga coonadi m’ciuno mwathu. (Aef. 6:14) M’nthawi zakale, msilikali anali kumanga lamba m’ciuno pofuna kuteteza ciunoco na ziwalo zina za m’thupi lake. Komabe, kuti lambayo amuteteze, anafunika kum’manga kwambili. Ngati sanam’mange kwambili, kapena kunjata, sanali kum’teteza mokwanila. Kodi lamba wathu wa coonadi amatiteteza bwanji? Ngati timanga kwambili coonadi monga lamba m’ciuno mwathu, cidzatiteteza kuti tisasoceletsedwe na maganizo olakwika, komanso cidzatithandiza kupanga zosankha mwanzelu. Ndipo ngati takumana na ciyeso kapena mavuto, coonadi ca m’Baibo cidzatilimbikitsa kuti tisagonje pa kucita zabwino. Mofanana ndi msilikali amene sangapite ku nkhondo alibe lamba, na ise sitifunika kuvula lamba wathu wa coonadi kapena kum’manga pang’ono. M’malomwake, tifunika kum’manga zolimba mwa kupitiliza kucita zinthu mogwilizana ndi coonadi. Cinanso, lamba wa msilikali anali malo abwino okoloŵekapo lupanga lake. Mfundo imeneyi yatifikitsa pa cinthu cacitatu cimene cingatithandize kupitiliza kuyenda m’coonadi.

16. Kodi kuphunzitsa ena coonadi kumatilimbikitsa bwanji kuyendabe m’coonadi?

16 Cacitatu, muzitengako mbali mokwanila pa nchito yophunzitsa anthu coonadi ca m’Baibo. Kucita izi kudzakuthandizani kugwilitsitsa lupanga laumzimu, limene ni “mawu a Mulungu.” (Aef. 6:17) Monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu, ise tonse tifunika kuyesetsa kunola luso lathu, kuti tizitha ‘kuphunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a coonadi.” (2 Tim. 2:15) Pamene tiseŵenzetsa Baibo pothandiza ena kumvetsetsa coonadi na kukana ziphunzitso zabodza, timakhomeleza mawu a Mulungu mu mtima na m’maganizo mwathu. Kucita izi kumatilimbikitsa kuyendabe m’coonadi.

17. N’cifukwa ciani mumaona coonadi kukhala camtengo wapatali?

17 Coonadi ni mphatso yamtengo wapatali imene Yehova watipatsa. Mphatso imeneyi imatithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba na Atate wathu wakumwamba. Ubwenzi umenewu ni cinthu camtengo wapatali kwambili kuposa ciliconse cimene tili naco. Zimene Yehova watiphunzitsa kufika pano ni dyonkho cabe. Iye watilonjeza moyo wosatha. Ndipo panthawiyo tidzaphunzila mfundo zambili-mbili za coonadi, kuwonjezela pa zimene taphunzila kale. Conco, muziona coonadi monga ngale yamtengo wapatali. Pitilizani ‘kugula coonadi ndipo musacigulitse.” Mukatelo, mofanana ndi Davide, na imwe ‘mudzayenda m’coonadi” ca Yehova.—Sal. 86:11.

^ par. 8 Dzina lasinthidwa.

^ par. 8 Pitani pa JW Broadcasting (ku Chichewa), ndi kuona pa mbali yakuti ZOCHITIKA PA MOYO WA ANTHU ENA> MFUNDO ZA M’BAIBULO ZIMASINTHA ANTHU.