Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingapereke Chiyani kwa Yehova?

Kodi Ndingapereke Chiyani kwa Yehova?

PA NTHAWI ina Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pa nkhani ya ubwenzi wathu ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Yehova watipatsa mphatso zambirimbiri zomwe zimatithandiza kukhala osangalala. Koma tikhoza kusangalala kwambiri tikamapereka mphatso kwa Yehova. Kodi ndi mphatso ziti zimene tingapereke kwa Yehova? Lemba la Miyambo 3:9 limanena kuti: “Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.” Mawu oti ‘zinthu zamtengo wapatali’ angatanthauze zinthu monga nthawi, luso, mphamvu komanso chuma chathu. Tikamagwiritsa ntchito zinthu zimenezi kuti zithandizire pa kulambira Mulungu, timakhala tikupereka mphatso kwa Yehova ndipo timasangalala kwambiri.

Kodi tingatani kuti tisamaiwale kupereka chuma chathu kwa Yehova? Mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Korinto kuti “aziika kenakake pambali” koti adzapereke kwa Yehova. (1 Akor. 16:2) Ndiye kodi mungadziwe bwanji njira zimene mungaperekere? Onani bokosi lotsatirali.

Kupereka kudzera pa intaneti ndi kosatheka m’mayiko ena. Koma malangizo okhudza kupereka m’njira zina amapezeka pa jw.org. M’mayiko ena, amaikaponso mayankho a mafunso amene anthu amadzifunsa okhudza zopereka.