Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

‘Yehova Waticitila Zinthu Zabwino’

‘Yehova Waticitila Zinthu Zabwino’

INE na mkazi wanga, Danièle, titangofika pa hotela inayake, wolandila alendo pa hotelayo ananiuza kuti: “Bambo, tumilani foni apolisi a ku boda cifukwa afuna kukamba namwe!” Apa n’kuti tangena camanje-manje m’dziko la Gabon, limene lili ku m’madzulo kwa Africa. Umu munali m’zaka za m’ma 1970, ndipo nchito yathu inali yoletsedwa m’dzikolo.

Popeza nthawi zonse mkazi wanga anali kukhala chelu, mwamsanga anazindikila zimene zinali kucitika, ndipo anakamba nane moŵeleŵesa amvekele: “Musawatumile apolisi, afika kale kuno.” Nitatembenuka, n’naona motoka ya apolisi ikufika panja pa hotelayo. Patapita maminetsi ocepa, tinamangiwa. Koma popeza Danièle anali atanicenjezelatu, n’napeza mpata wopatsa m’bale wina mafaelo ofunikila amene n’nali nawo.

Pamene anali kupita nase ku polisi, mu mtima n’nali kuyamikila cifukwa cokhala na mkazi wolimba mtima komanso wauzimu. Ici ni cocitika cimodzi cabe mwa zocitika zambili-mbili, pamene ine na mkazi wanga tinacitila zinthu pamodzi monga banja. Lekani tsopano nikusimbileni za umoyo wanga, kuti mudziŵe zimene zinacitika kuti niyambe kuyendela abale ku maiko kumene nchito yathu inali yoletsedwa.

YEHOVA ANANITSEGULA MASO

N’nabadwa mu 1930, m’tauni yaing’ono ya Croix, kumpoto kwa France. Makolo anga anali Akatolika. Wiki iliyonse, tonse pa banja pathu tinali kupita ku chechi kukacita Misa. Ndipo atate anali kukhala na zocita zambili kuchechiko. Koma pamene n’nali na zaka 14, panacitika zinthu zina zimene zinanitsegula maso kuti nione cinyengo ca atsogoleli a chechi yathu.

Pa nthawi ya nkhondo yaciŵili ya dziko lonse, asilikali a Germany analanda dziko la France. Pa nthawiyo, wansembe wathu polalikila anali kutilimbikitsa kuti tizicilikiza boma la Vichy, limene linali logwilizana na ulamulilo wa Germany. Tinali kudabwa kwambili na ulaliki wake. Mofanana ndi anthu ambili mu France, na ise tinali kumvetsela nyuzi mwakabisila pa wailesi ya BBC, pamene anali kuulutsa zokhudza maiko olimbana na Germany. Asilikali a Germany atayamba kugonja mu France, wansembe uja anasintha mbali yocilikiza. Ndipo mu September 1944, iye anapanga makonzedwe ocita mwambo wokondwelela kupambana kwa maiko olimbana na Germany. Izi zinanikhumudwitsa, komanso zinapangitsa kuti nileke kuwadalila atsogoleli a chechi yathu.

Patapita nthawi yocepa kucokela pamene nkhondo inatha, atate anamwalila. Pa nthawiyo, mlongosi wanga wamkulu anali ataloŵa kale m’banja, ndipo anali kukhala ku Belgium. Conco, n’naona kuti nili na udindo wosamalila amayi. N’nakaloŵa nchito ku kampani yoomba nsalu. Abwana anga ndi ana awo, onse anali Akatolika. Zinthu zinali kuniyendela bwino pa nchito, koma posapita nthawi, n’nakumana na mayeselo.

Mu 1953, mlongosi wanga, Simone, anabwela kudzationa. Pa nthawiyo, anali atakhala Mboni ya Yehova. Poseŵenzetsa Baibo yake, iye anatifotokozela momveka bwino kuti ziphunzitso za helo wa moto, Utatu, na mzimu wosafa, zimene chechi ya Katolika imaphunzitsa n’zabodza. Poyamba, n’namutsutsa cifukwa sanali kuseŵenzetsa Baibo ya Katolika. Koma pambuyo pake n’nakhutila kuti zimene anali kuniuza n’zoona. Patapita nthawi, ananibweletsela magazini akale a Nsanja ya Mlonda. N’nawaŵelenga madzulo, ndipo n’nali na cidwi kwambili. Nthawi yomweyo, n’nazindikila kuti zimene n’nali kuŵelenga ni coonadi. Koma n’nali kuyopa kukhala wa Mboni cifukwa coganiza kuti nidzacotsewa nchito.

Conco, kwa miyezi ingapo, n’nali kuŵelenga Baibo na nkhani za mu Nsanja ya Mlonda panekha. Koma m’kupita kwa nthawi, n’nayamba kupita ku Nyumba ya Ufumu kukasonkhana. N’nakondwela kwambili na mzimu wa ubwenzi umene mpingo unanionetsa. Ndiyeno, n’nayamba kuphunzila Baibo na m’bale wina wofikapo ku uzimu. Titaphunzila kwa miyezi 6, n’nabatizika mu September 1954. Zinali zokondweletsa kuti posapita nthawi yaitali, nawonso amayi na mlongosi wanga wamng’ono anakhala Mboni.

KUDALILA YEHOVA MU UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE

Mu 1958, n’nali na mwayi wopezeka pa msonkhano wacigawo wa maiko, ku New York. Amayi anali atamwalila mawiki angapo msonkhanowu usanacitike, ndipo n’nali na cisoni cacikulu. N’tabwelela ku nyumba, n’naleka nchito na kuyamba upainiya cifukwa n’nalibenso udindo wosamalila banja. Pa nthawiyo, n’nafunsila mlongo Danièle Delie, amene anali mpainiya wokangalika. Ndipo tinakwatilana mu May 1959.

Danièle anayambila upainiya m’dela la ku midzi, m’cigawo ca Brittany, kutali kwambili na kwawo. Iye anafunika kulimba mtima kuti azilalikila m’dela limenelo la Akatolika ambili, komanso kuti azipita yekha na njinga ku madela a ku midzi amenewo. Mofanana na ine, Danièle anali wacangu pa nchito yolalikila. Tonse tinali kudziŵa kuti mapeto ali pafupi. (Mat. 25:13) Mtima wake wodzimana unathandiza kwambili kuti tipitilize kupilila pa utumiki wathu.

Patapita masiku oŵelengeka kucokela pamene tinakwatilana, anatitumiza m’nchito ya m’dela. Tinaphunzila kukhala na umoyo wosalila zambili. Mpingo woyamba umene tinacezela unali na ofalitsa 14, ndipo abale anali na umoyo wosaukila cakuti sanakwanitse kutipezela malo ogona. Conco, tinali kugona pa pulatifomu m’Nyumba ya Ufumu. Sipanali pabwino kweni-kweni kugonapo, koma panali nkhasako kusiyana n’kugona panja.

Tinali kuyendela mipingo poseŵenzetsa motoka yathu yaing’ono

Tinali kukhala otangwanika, koma mkazi wanga anajaila msanga umoyo watsopanowo. Nthawi zambili, anali kuniyembekezela m’motoka yathu pamene tikucita miting’i ya akulu yamwadzidzidzi. Koma sanadandaulepo olo tsiku limodzi. Tinatumikila m’dela kwa zaka ziŵili cabe. Pa nthawiyo, tinaphunzila kufunika kwakuti anthu okwatilana azikambitsana moona mtima komanso kucitila zinthu pamodzi monga banja.—Mlal. 4:9.

TINAPATSIWA UTUMIKI WATSOPANO

Mu 1962, tinaitanidwa kuti tikacite nawo maphunzilo a miyezi 10 a kilasi namba 37 ya Sukulu ya Giliyadi ku Brooklyn, mu mzinda wa New York. Pa ophunzila 100, panali mabanja 13 cabe, ndipo tinaona kuti unali mwayi kupezekapo monga banja. Siniiŵala maceza olimbikitsa amene tinali nawo na abale olimba m’cikhulupililo, monga M’bale Frederick Franz, Ulysses Glass, na Alexander H. Macmillan.

Tinakondwela kwambili kungena Sukulu ya Giliyadi monga banja

Pamene tinali kuphunzila, tinalimbikitsidwa kukulitsa luso la kuyang’ana zinthu mwachelu. Nthawi zina pa Ciŵelu tikatsiliza kuphunzila m’kilasi, madzulo tinali kukaona malo osiyana-siyana mu mzinda wa New York, monga mbali ya maphunzilo athu. Tikabwelako, tinali kudziŵa kuti pa Mande tidzalemba mayeso okhudza zimene tinaona. Nthawi zambili tinali kubwelako olema. Koma m’bale wa pa Beteli, amene anali kukationetsa malo, anali kutifunsa mafunso pofuna kutithandiza kukumbukila mfundo zofunika zimene zingakatithandize polemba mayeso. Tsiku lina pa Ciŵelu masana, tinayenda m’madela osiyana-siyana a mu mzindawo mpaka madzulo. Tinapita ku malo oonela zinthu zakuthambo. Kumeneko, tinaphunzila za mametiyo komanso mametiyolaiti. Tinapitanso ku nyumba yosungila zinthu zacilengedwe zocititsa cidwi, ndipo tinaona mitundu yosiyana-siyana ya ng’ona. Titabwelela ku Beteli, m’bale amene anali kutitsogolela pokaona malo anatifunsa kuti, “Malinga n’zimene mwaona, kodi miyala ya metiyo imasiyana bwanji na miyala ya metiyolaiti?” Mkazi wanga anali atalema, ndipo anayankha kuti, “Manu a metiyolaiti ni aatali kuposa a metiyo!

Tinali kuyendela abale na alongo athu okhulupilika ku Africa

Titatsiliza sukulu, tinakondwela kwambili pamene anatiuza kuti tikatumikile pa nthambi ya ku France. N’natumikila limodzi na mkazi wanga pa ofesiyi kwa zaka zoposa 53. Mu 1976, n’naikidwa kukhala mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi. N’napatsiwanso nchito yoyendela abale m’maiko a ku Africa na ku Middle East, kumene nchito yathu inali yoletsedwa. Ndiye cifukwa cake tinakafika ku Gabon, kumene tinakumana na zimene nafotokoza kuciyambi. Kukamba zoona, nthawi zina n’nali kuona kuti siningakwanitse kusamalila maudindo amenewa. Koma mkazi wanga, Danièle, ananithandiza kwambili posamalila maudindowa.

Nikumasulila nkhani ya M’bale Theodore Jaracz pa msonkhano wacigawo wa mu 1988, wa mutu wakuti “Cilungamo Caumulungu”

TINAPILILA MAYESELO AAKULU

Kungoyambila pamene tinafika, tinaukonda ngako umoyo wa pa Beteli. Mkazi wanga anakhala womasulila waluso kwambili wa zofalitsa za citundu cathu, olo kuti anaphunzila Cizungu kwa miyezi isanu cabe tisanapite ku Giliyadi. Tinali kukondwela kwambili na nchito yathu pa Beteli, ndipo kugwilizana na mpingo kunali kuwonjezela cimwemwe cathu. Nikumbukila tsiku lina madzulo pamene tinali m’njila pobwelela ku Beteli, tinali olema maningi. Koma tinali okondwa cifukwa tinali titatsogoza maphunzilo a Baibo opita patsogolo. Patapita kanthawi, Danièle anayamba kudwala, ndipo anali kulephela kutumikila mokangalika monga mmene anali kufunila.

Mu 1993, anamupeza na khansa ya kumaŵele. Anamucita opaleshoni, komanso anamupatsa mankhwala amphamvu kwambili. Patapita zaka 15, anamupezanso na khansa ina, yoopsa kwambili. Olo zinali conco, anali kuikonda kwambili nchito yake yomasulila, cakuti atayamba kumvelako bwino, anapitiliza kuseŵenza.

Olo kuti Danièle anali kudwala matenda aakulu, sitinaganizileko zoleka utumiki wa pa Beteli. Komabe, kudwalila pa Beteli kumakhala na mavuto ake, maka-maka ngati ena sadziŵa kukula kwa matendawo. (Miy. 14:13) Ngakhale pamene anafika zaka za m’ma 70, mkazi wanga anali kuonekabe wokongola olo kuti anali kudwala. Ndipo sanali kukhalila kudandaula za matenda ake. M’malomwake, anali kuyesetsa kulimbikitsa ena. Anali kudziŵa kuti kumvetsela mwachelu ena akamafotokoza mavuto awo kungawalimbikitse. (Miy. 17:17) Mogwilizana na zimene anakumana nazo, mkazi wanga anali kulimbikitsa ena kuti asamaope khansa.

Tinapililanso zovuta zina zobwela na matenda. Cifukwa ca kufooka kwa nthanzi, mkazi wanga Danièle sanali kukwanitsa kuseŵenza tsiku lonse. Conco, anayamba kuseŵenzetsa nthawi imene anali kukhala nayo ponicilikiza m’njila zina zambili. Izi zinanithandiza kupitiliza kutumikila monga mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi kwa zaka 37. Mwacitsanzo, anali kuphikilatu cakudya, n’colinga cakuti pa nthawi ya cakudya ca masana tikhale na mpata wodyela pamodzi na kucezako.—Miy. 18:22.

KULIMBANA NDI NKHAWA ZA TSIKU NA TSIKU

Ngakhale kuti Danièle anali na matenda aakulu, sanataye mtima, ndipo sanali kungokhalila kudandaula. Patapita nthawi, anadwalanso khansa kacitatu. Tinathedwa nzelu. Mankhwala amphamvu amene anali kupatsidwa anali kum’fooketsa, cakuti nthawi zina anali kulephela ngakhale kuyenda. Zinanimvetsa cisoni kwambili kuona mkazi wanga, yemwe anali womasulila waluso, akusoŵa mawu olemba pomasulila.

Zinthu zinali zovuta kwambili, koma sitinaleke kupemphela. Ndipo tinali kukhulupilila kuti Yehova sadzalola kuti tivutike mpaka kufika poti sitingathe kupilila. (1 Akor. 10:13) Nthawi zonse, tinali kuyamikila thandizo limene Yehova anali kutipatsa kupitila m’Mawu ake, madokota a pa nthambi, komanso abale na alongo ena.

Nthawi zambili, tinali kupemphela kwa Yehova kuti atitsogolele posankha cithandizo camankhwala. Panthawi ina, tinalibiletu cithandizo ciliconse cifukwa mkazi wanga anali kukomoka akapatsiwa mankhwala. Ndipo dokota amene anamuthandiza kwa zaka 23, sanali kudziŵa cifukwa cake. Komanso sanapeze njila ina yom’thandizila. Izi zinatidetsa nkhawa kwambili cakuti tinali kuona kuti sitidzapeza cithandizo cina camankhwala. Patapita nthawi, dokota wina anavomela kuthandiza mkazi wanga. Zinali monga kuti Yehova watikonzela njila yotithandizila kupilila mavuto athu.

Tinaphunzilanso kupilila nkhawa za tsiku lililonse palokha, mogwilizana ndi zimene Yesu anakamba. Anati: “Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.” (Mat. 6:34) Kuona zinthu moyenela komanso kukhala wosangalala kunali kutithandiza. Mwacitsanzo, pamene Danièle sanali kulandila cithandizo camankhwala kwa miyezi iŵili, mwacimwemwe ananiuza kuti: “Tsopano nimvelako bwino.” (Miy. 17:22) Ngakhale kuti anali wodwala, anali kupeza cimwemwe mwa kupatula nthawi yoimba nyimbo zatsopano za Ufumu mokweza.

Danièle sanali kukonda kudandaula za matenda ake. Izi zinanilimbikitsa kuti na ine nisamadandaule na zolephela zanga. Pa zaka 57 zimene tinakhala m’cikwati, anali kunisamalila m’njila zambili. Nthawi zonse anali kuniphikila, cakuti sin’naphunzile ngakhale kuphika ndiwo zosavuta monga mazila. Conco, pamene matenda ake anakula kwambili, n’nafunika kuphunzila kutsuka mbale, kuwacha, komanso kuphika. Ndipo mkati mophunzila nchito zimenezi, n’naphwanyako makapu. Komabe, kugwila nchitozi kunali kunikondweletsa kwambili, cifukwa n’nali kudziŵa kuti nikucita zinthu zokondweletsa mkazi wanga. *

NIMAYAMIKILA KUKOMA MTIMA KUMENE YEHOVA WANIONETSA

Mavuto amene tinakumana nawo cifukwa ca matenda komanso ukalamba aniphunzitsa zambili. Coyamba, naphunzila kuti tisamatangwanike kwambili mpaka kuiŵala kusamalila mkazi kapena mwamuna wathu. Pamene tikali na mphamvu, tifunika kucita zonse zimene tingathe posamalila wokondedwa wathu. (Mlal. 9:9) Caciŵili, tisamade nkhawa kwambili na zinthu zazing’ono, cifukwa nkhawa ingatipangitse kuti tisamaone madalitso ambili amene timalandila tsiku lililonse.—Miy. 15:15.

Nikaganizila umoyo wathu mu utumiki wanthawi zonse, nimaona kuti Yehova anatidalitsa kwambili kuposa mmene tinali kuganizila. Ndipo nimamvela monga mmene wamasalimo anamvelela, pamene anati: ‘Yehova wanicitila zinthu zabwino.’—Sal. 116:7.

^ par. 32 Mlongo Danièle Bockaert anamwalila ali na zaka 78, pa nthawi imene nkhani ino inali kukonzewa.