Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mulungu Adzacita Ciani Kutsogolo?

Kodi Mulungu Adzacita Ciani Kutsogolo?

Mukakumana na vuto, mosakaikila mumayembekezela mnzanu wa pamtima kukuthandizani. Podziŵa izi, ena amakamba kuti Mulungu si bwenzi labwino cifukwa amaona kuti iye saŵathandiza akakumana na mavuto. Koma m’ceni-ceni, Mulungu waticitila kale zambili zotithandiza. Kuwonjezela apo, iye adzacitapo kanthu kuti acotsepo mavuto onse amene timakumana nawo. Kodi Mulungu adzacita ciani kutsogolo?

ADZACOTSAPO MAVUTO ONSE

Mulungu adzacotsapo mavuto onse mwa kuwononga gwelo lake. Ndipo Baibo imaonetsa gwelo lake pamene imati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Yesu anakamba kuti “woipayo” ni “wolamulila wa dzikoli,” Satana Mdyelekezi. (Yohane 12:31) Ulamulilo wa Satana pa anthu, ndiye umabweletsa mavuto onse padziko lapansi. Nanga kodi Mulungu adzacitapo ciani?

Posacedwa, Yehova Mulungu adzaseŵenzetsa Mwana wake Yesu Khristu kuti “awononge Mdyelekezi, amene ali ndi njila yobweletsela imfa.” (Aheberi 2:14; 1 Yohane 3:8) Ndipo Baibo imati Mdyelekezi adziŵa “kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa” kuti awonongedwe. (Chivumbulutso 12:12) Mulungu adzawononganso onse ocita zoipa.—Salimo 37:9; Miyambo 2:22.

ADZAKONZA DZIKOLI KUKHALA PARADAISO

Pambuyo pocotsapo mavuto onse padziko, Mlengi wathu adzakwanilitsa colinga cake cakuti anthu akhale padziko lapansi kwamuyaya. Kodi tingayembekezele zinthu zabwanji?

Mtendele wosatha na citetezo. “Anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:11.

Cakudya cokwanila copatsa thanzi. “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.”—Salimo 72:16.

Nyumba zabwino na nchito yokhutilitsa. “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. . . . Anthu anga osankhidwa mwapadela adzapindula mokwanila ndi nchito ya manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.

Kodi ndimwe wofunitsitsa kukhala m’dziko laconco? Posacedwa, umu ni mmene umoyo wathu tonse udzakhalila.

ADZACOTSAPO MATENDA NA IMFA

Tonse timadwala na kufa, koma zimenezi posacedwa zidzacotsedwapo. Mulungu adzakwanilitsa zonse zimene anatilonjeza kupitila mu nsembe la dipo la Yesu kuti “aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kodi dipo idzakwanilitsanso ciani?

Matenda adzacotsedwapo. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’ Anthu okhala mmenemo adzakhala amene macimo awo anakhululukidwa.”—Yesaya 33:24.

Imfa siidzavutitsanso anthu. “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”—Yesaya 25:8.

Anthu adzakhala na moyo kwamuyaya. “Mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 6:23.

Akufa adzaukitsidwa. “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Iwo adzapindula na mphatso yocokela kwa Mulungu ya dipo.

Kodi Mulungu adzakwanilitsa bwanji zonsezi?

ADZAKHAZIKITSA BOMA LABWINO KWAMBILI

Mulungu adzakwanilitsa colinga cake cokhudza anthu na dziko lapansi, mwakuseŵenzetsa boma lake lakumwamba. Ndipo anasankha Yesu Khristu kukhala Wolamulila. (Salimo 110:1, 2) Imeneyi ni boma kapena kuti ufumu umene Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphelela pamene anati, “Atate wathu wakumwamba, . . . Ufumu wanu ubwele.”—Mateyu 6:9, 10.

Ufumu wa Mulungu udzalamulila padziko lapansi na kucotsapo mavuto onse. Ufumu umenewu ni boma labwino kwambili limene anthu angakonde kukhala nalo! N’cifukwa cake Yesu analimbikila kwambili kulengeza “uthenga wabwino wa Ufumu” pamene anali padziko lapansi, ndipo analimbikitsa ophunzila ake kucita cimodzi-modzi.—Mateyu 4:23; 24:14.

Mwacikondi cake cacikulu, Yehova Mulungu analonjeza anthu kuti adzawacitila zabwino zonsezi. Kodi zimenezi sizikupangitsani kufuna kum’dziŵa bwino na kukhala naye pa ubwenzi? Kodi kum’dziŵa bwino Mulungu na kukhala naye pa ubwenzi kungakupindulitseni bwanji? Nkhani yotsatila idzafotokoza zimenezi.

KODI MULUNGU ADZACITA CIANI KUTSOGOLO? Mulungu adzacotsapo matenda na imfa. Ndipo mu ulamulilo wa boma lake la Ufumu, adzagwilizanitsa mtundu wonse wa anthu na kukonza dziko lapansi kukhala paradaiso