Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungakhale pa Ubwenzi na Mulungu

Mungakhale pa Ubwenzi na Mulungu

ANTHU ENA AMAONA KUTI . . .

Mulungu sasamala za ise ndipo ni wapamwamba kwambili, woyela, komanso wosafikilika.

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

“Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8.

‘M’tulileni nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

KODI TINGACITE CIANI KUTI TIKHALE PA UBWENZI NA MULUNGU?

  • Muzikamba naye.—Salimo 145:18, 19.

  • Muzimumvela.—Salimo 32:8.

  • Muzitsatila malangizo ake.—Miyambo 3:5, 6.

  • Limbikilani kuti mukhale bwenzi lake.—Mateyu 7:7, 8.