Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Inde, Moyo Ukali na Phindu kwa Imwe!

Inde, Moyo Ukali na Phindu kwa Imwe!

Faizal anafunika kucitidwa opaleshoni kumtima, patangopita caka cimodzi kucokela pamene mkazi wake anamwalila. Iye anati: “Pamene n’naŵelenga buku la Yobu, n’nadziŵa kuti Yehova anaiika m’Baibo na colinga. Tikapeza cocitika ca m’Baibo cimene cifanana na zimene tikupitamo, zimakhala zotonthoza mtima kwambili.” Faizal anakambanso kuti: “Moyo ulidi waphindu.”

Tarsha anali wamng’ono pamene amayi ake anamwalila. Iye anakamba kuti: “Kudziŵa Mlengi n’kumene kumapangitsa moyo kukhala waphindu, komanso kumatipatsa ciyembekezo na cimwemwe, ngakhale tikumane na mavuto. Yehova angatipatse mphamvu, komanso kutithandiza kulimbana na mavuto a tsiku na tsiku.”

NKHANI ZAPITA zafotokoza zocitika zosiyana-siyana zovutitsa maganizo, zimene zingapangitse umoyo kuoneka wosapililika. Pamene mulimbana na mavuto anu, mungayambe kukaikila ngati moyo ulidi waphindu, kapena ngati pali aliyense amene amakudelani nkhawa. Koma dziŵani kuti Mulungu amakudelani nkhawa pamene muvutika. Ndimwe wofunika kwambili kwa iye.

Wolemba Salimo 86 anaonetsa cidalilo mwa Mulungu pamene anati: “Pa tsiku la nsautso yanga ndidzaitana pa inu, ndipo inu mudzandiyankha.” (Salimo 86:7) Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi Mulungu adzaniyankha bwanji “pa tsiku la nsautso yanga”?’

Ngakhale kuti Mulungu sangathetse mavuto anu panthawi imeneyo, Mawu ake, Baibo, amakutsimikizani kuti iye angakupatseni mtendele wa m’maganizo kuti mupilile. “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” (Afilipi 4:6, 7) Conde, onani mmene mavesi a m’Baibo otsatilawa atitsimikizila kuti Mulungu amatidela nkhawa.

Mulungu Amakudelani Nkhawa

“Palibe ngakhale [mpheta] imodzi mwa izo imene imaiwalika kwa Mulungu. . . Ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zambili.”Luka 12:6, 7.

GANIZILANI IZI: Mbalame zing’ono-zing’ono monga mpheta zimaoneka ngati zosafunika, koma osati kwa Mulungu. Palibe ngakhale kambalame kamodzi ka mpheta, kamene Mulungu sakadziŵa bwino. Kalikonse n’kofunika kwa iye. Koma anthu ni ofunika kwambili kwa Mulungu kuposa mbalame zimenezi. Pa zonse zimene Mulungu analenga padziko lapansi, anthu ni apadela kwambili. Iwo analengedwa “m’cifanizilo” cake, ndipo angakwanitse kutengela na kuonetsa makhalidwe ake apamwamba.—Genesis 1:26, 27.

“Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa. . . . Mumadziwa maganizo anga . . . Ndisanthuleni ndi kudziwa malingalilo anga amene akundisowetsa mtendele.”Salimo 139:1, 2, 23.

GANIZILANI IZI: Mulungu amakudziŵani bwino pamwekha. Iye amadziŵa bwino mmene mumvelela mumtima, komanso nkhawa zanu. Ngakhale kuti ena sangamvetsetse bwino-bwino kukula kwa vuto limene mwakumana nalo, Mulungu amakudelani nkhawa ndipo amafuna kukuthandizani. Conco, moyo wanu ni wofunika.

Moyo Wanu Ni Wofunikabe

“Inu Yehova, imvani pemphelo langa. Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo. . . . Chelani khutu lanu kwa ine. Fulumilani kundiyankha pa tsiku limene ndikuitana. . . Iye adzamvetsela pemphelo la anthu amene alandidwa ciliconse.” Salimo 102:1, 2, 17.

GANIZILANI IZI: Zili monga kuti kucokela paciyambi pa mavuto a anthu, Yehova wakhala akuona kulila kwawo ndipo amasunga misozi yawo. (Salimo 56:8) Izi ziphatikizapo ngakhale kulila kwanu. Mulungu akumbukila masautso anu onse na kulila kwanu, cifukwa ndimwe wamtengo wapatali kwa iye.

“Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza . . . Ine Yehova Mulungu wako . . . amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” Yesaya 41:10, 13.

GANIZILANI IZI: Mulungu ni wokonzeka kukuthandizani mukakumana na mavuto.

Pali Ciyembekezo ca Tsogolo Labwino

“Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”Yohane 3:16.

GANIZILANI IZI: Mulungu amakukondani kwambili cakuti anapeleka Mwana wake Yesu, monga nsembe cifukwa ca imwe. Nsembe imeneyi imakupatsani ciyembekezo cokakhala na moyo wacimwemwe, komanso waphindu kwamuyaya. *

Nthawi zina mungazivutika maganizo, ndipo umoyo wanu ungaoneke kuti wafika posapililika. Ngakhale n’conco, muziŵelenga Mawu a Mulungu mozama, na kulimbitsa cikhulupililo canu m’ciyembekezo cimene Mulungu analonjeza. Kucita zimenezi kudzakupatsani cimwemwe, komanso mudzaona kuti kukhala na moyo n’kwaphindu.

^ Kuti mudziŵe zambili za mmene mungapindulile na dipo la Yesu, tambani vidiyo yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu pa webusaiti ya www.pr418.com. Onani polemba kuti ZOKUDZA IFE MBONI > CIKUMBUTSO.