Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 6

Khalanibe na Mtima Wamphumphu!

Khalanibe na Mtima Wamphumphu!

“Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—YOBU 27:5.

NYIMBO 34 N’dzayenda mu Umphumphu Wanga

ZA M’NKHANI INO *

1. Kodi Mboni zitatu zochulidwa m’ndime iyi zinaonetsa bwanji kukhulupilika kwawo kwa Yehova?

ONANI zimene Akhristu atatu akusankha kucita pamene apezeka m’zocitika izi: (1) Mtsikana ali ku sukulu, ndipo a tica auza ana a sukulu onse m’kilasi yawo kuti acite cikondwelelo cinacake. Podziŵa kuti cikondweleloco n’cosagwilizana na mfundo za Mulungu, mwaulemu mlongoyo akukana kutengamo mbali. (2) M’bale wacicepele wamanyazi akulalikila ku nyumba na nyumba. Iye wazindikila kuti pa nyumba imene akupita kukalalikilapo, pamakhala mnyamata wina wa ku sukulu kwawo, amene amakonda kunyoza Mboni za Yehova. Ngakhale n’conco, iye akupitabe kukalalikila pa nyumbayo. (3) M’bale wina amagwila nchito molimbika kuti asamalile banja lake. Koma tsiku lina, abwana ake anam’pempha kuti acite zinthu zinazake zacinyengo panchito. M’baleyo anafotokozela abwana ake kuti Mulungu safuna kuti atumiki ake azicita cinyengo kapena kuphwanya malamulo. Conco, iye anakana kucita zimenezo, olo kuti zikanapangitsa kuti acotsedwe nchito.—Aroma 13:1-4; Aheb. 13:18.

2. Kodi tidzakambilana mafunso ati? Nanga n’cifukwa ciani?

2 Ni makhalidwe abwino ati amene mwaona mwa Akhristu atatu amenewa? Mwina mwaonako angapo, monga kulimba mtima na kuona mtima. Koma pali khalidwe lina lapamwamba kwambili limene onse ali nalo. Ali na mtima wamphumphu. Onse atatu ni okhulupilika kwa Yehova. Aliyense wa iwo wakana kuphwanya mfundo za Mulungu. Cimene cawalimbikitsa kucita zimenezi ni mtima wawo wamphumphu. Mwacionekele, Yehova ananyadila kuona atumiki ake amenewa akucita zinthu zoonetsa kuti ali na mtima wamphumphu. Na ife, timafuna kukondweletsa Atate wathu wakumwamba. Tsopano, tiyeni tikambilane mafunso aya: Kodi kukhala na mtima wamphumphu kumatanthauzanji? N’cifukwa ciani tifunika kukhala na mtima wamphumphu? Nanga n’ciani cingatithandize kukhalabe na mtima wamphumphu m’masiku ovuta ano?

KODI KUKHALA NA MTIMA WAMPHUMPHU KUMATANTHAUZANJI?

3. (a) Kwa atumiki a Mulungu, kodi kukhala na mtima wamphumphu kumatanthauzanji? (b) N’zitsanzo ziti zimene zingatithandize kumvetsetsa tanthauzo la kukhala na mtima wamphumphu?

3 Kwa atumiki a Mulungu, kukhala na mtima wamphumphu kumatanthauza kukonda Yehova na mtima wonse, komanso kudzipeleka kwathunthu kwa iye, moti pa zosankha zawo zonse, amaika Mulungu patsogolo. Tiyeni tione mmene mawuwa akuwaseŵenzetsela m’Baibo. M’Baibo, mawu akuti, “mtima wamphumphu,” kweni-kweni amatanthauza cinthu cathunthu, cabwino-bwino, kapena conse. Mwacitsanzo, Aisiraeli anali kupeleka nsembe za nyama kwa Yehova. Ndipo Cilamulo cinakamba kuti nyamazo zinafunika kukhala zopanda cilema. * (Lev. 22: 21, 22) Aisiraeli sanaloledwe kupeleka nsembe nyama zodwala, zopanda mwendo umodzi, khutu, kapena diso. Yehova anali kufuna kuti nyama yopelekedwa nsembe izikhala yathunthu, komanso yabwino-bwino. (Mal. 1:6-9) Izi zionetsa kuti Yehova amafuna kuti tikhale na mtima wamphumphu kapena kuti wathunthu. Tiyelekezele motele: Tikapita ku msika, sitingagule cipatso conyemeka, buku long’ambika mapeji, kapena cipangizo cowonongeka mbali zina. Timafuna kugula cinthu cimene n’cathunthu, komanso cabwino-bwino. Yehova naye amafuna kuti tikhale okhulupilika kwathunthu kwa iye. Amafunanso kuti tizim’konda na mtima wonse.

4. (a) N’cifukwa ciani tikamba kuti n’zotheka ife anthu opanda ungwilo kukhala na mtima wamphumphu? (b) Malinga na Salimo 103:12-14, kodi Yehova amayembekezela ciani kwa ife?

4 Kodi izi zitanthauza kuti ife anthu opanda ungwilo sitingakwanitse kukhala na mtima wamphumphu? Iyai. N’zoona kuti timalakwitsa nthawi zambili. Koma izi sizifunika kutigwetsa mphwayi. Cifukwa ciani? Onani zifukwa ziŵili izi. Coyamba, Yehova sayang’ana kwambili pa zolakwa zathu. Mawu ake amati: “Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?” (Sal. 130:3) Iye amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo, komanso ocimwa, ndipo ni wokonzeka kutikhululukila na mtima wonse. (Sal. 86:5) Caciŵili, Yehova amadziŵa zimene tingakwanitse kucita, ndipo satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse. (Ŵelengani Salimo 103:12-14.) Nanga zingatheke bwanji kukhala amphumphu komanso abwino-bwino pa maso pake?

5. N’cifukwa ciani cikondi n’cofunika kuti tikhalebe na mtima wamphumphu?

5 Kwa atumiki a Yehova, cinsinsi cokhalila na mtima wamphumphu ni cikondi. Tifunika kukonda Mulungu na mtima wonse, komanso kukhala wodzipeleka kwathunthu kwa iye. Tikatelo, ndiye kuti olo tiyesedwe bwanji, tidzakhalabe okhulupilika. (1 Mbiri 28:9; Mat. 22:37) Ganizilaninso za Mboni zitatu zija zimene tachula kuciyambi kwa nkhani ino. N’cifukwa ciani iwo anakhalabe okhulupilika? Kodi mlongo wacitsikana uja safuna kusangalala ku sukulu? Kodi m’bale wacinyamata uja amakondwela kunyozedwa mu ulaliki wa nyumba na nyumba? Nanga bwanji m’bale wina uja wapanchito? Kodi sadela nkhawa zocotsedwa nchito? Kutalitali! M’malomwake, Akhristu amenewa anadziŵa kuti mfundo za Yehova n’zolungama, ndipo anafuna kukondweletsa Atate wawo wakumwamba. Cikondi cawo pa Mulungu cinawasonkhezela kuika cifunilo cake patsogolo popanga zosankha. Mwa ici, iwo anaonetsa kuti ali na mtima wamphumphu.

CIFUKWA CAKE TIFUNIKA KUKHALA NA MTIMA WAMPHUMPHU

6. (a) N’cifukwa ciani tifunika kukhala na mtima wamphumphu? (b) Kodi Adamu na Hava analephela bwanji kuonetsa mtima wamphumphu?

6 N’cifukwa ciani kukhala na mtima wamphumphu n’kofunika kwambili kwa aliyense wa ife? Cifukwa Satana anatsutsa ulamulilo wa Yehova, komanso aliyense wa ife. Mngelo wopanduka ameneyu anadzisandutsa yekha kukhala Satana, kapena kuti “Wotsutsa.” Izi zinacitika zaka zambili kumbuyoko, m’munda wa Edeni. Iye anaipitsa dzina la Mulungu mwa kukamba mawu oonetsa kuti Mulungu ni Wolamulila woipa, wodzikonda, komanso wacinyengo. N’zomvetsa cisoni kuti Adamu na Hava anapandukila Yehova, na kukhala ku mbali ya Satana. (Gen. 3:1-6) Umoyo wa mu Edeni unawapatsa mwayi waukulu wolimbitsa cikondi cawo pa Yehova. Koma pamene Satana anawayesa, cikondi cawo pa Mulungu sicinali cathunthu. Cinali copeleŵela. Pambuyo pake, panabukanso funso lina lakuti: Kodi n’zotheka munthu kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova Mulungu cifukwa com’konda? M’mawu ena tingati, kodi anthu angakwanitse kukhala na mtima wamphumphu? Funso limeneli linabuka m’masiku a Yobu.

7. Malinga na Yobu 1:8-11, kodi Yehova anamvela bwanji na kukhulupilika kwa Yobu, nanga Satana anamvela bwanji?

7 Yobu anakhalako pa nthawi imene Aisiraeli anali ku Iguputo. Pa nthawiyo, panalibenso munthu wina wa mtima wamphumphu monga Yobu. Koma mofanana ndi ife, Yobu anali wopanda ungwilo, ndipo nthawi zina anali kulakwa. Ngakhale n’conco, Yehova anam’konda Yobu cifukwa ca mtima wake wamphumphu. Cioneka kuti pa nthawiyi, Satana anali atayamba kale kutonza Yehova pa nkhani yakuti anthu sangakhale okhulupilika kwa iye. Conco, Yehova anauza Satana kuti aone mtumiki wake wokhulupilika Yobu. Zocita za Yobu zinaonetselatu kuti Satana ni wabodza. Koma Satana anapempha Yehova kuti amulole kuti ayese Yobu. Yehova anam’dalila bwenzi lake Yobu, ndipo analola kuti Satana amuyese.—Ŵelengani Yobu 1:8-11.

8. Kodi Satana anamuzunza bwanji Yobu?

8 Satana ni wankhanza, komanso wopha anthu. Anawononga cuma conse ca Yobu, anapha anchito ake, na kumuwonongela mbili yake yabwino. Anamuphelanso ana ake onse 10. Kenako, anamugwetsela matenda oopsa a zilonda, zimene zinakuta thupi lake lonse, kuyambila ku mutu mpaka ku phazi. Cifukwa ca cisoni komanso kuthedwa nzelu, mkazi wake anamuuza kuti angotukwana Mulungu kuti afe. Yobu anafika polaka-laka kufa cabe, koma sanaleke kukhala na mtima wamphumphu. Ndiyeno, Satana anaseŵenzetsa njila ina. Anagwilitsila nchito amuna atatu, amene anali anzake a Yobu. Amuna amenewo anapita kukaona Yobu, ndipo anakhala kumeneko kwa masiku angapo. Koma sanam’tonthoze. M’malomwake, anali kungomunena na kum’dzudzula mwakhanza. Anali kukamba kuti Mulungu ndiye anamubweletsela mavuto, komanso kuti analibe nazo kanthu zakuti iye ali na mtima wamphumphu. Anafika pokamba mawu oonetsa kuti Yobu anali munthu woipa, ndipo anali kulandila malipilo a zoipa zake.—Yobu 1:13-22; 2:7-11; 15:4, 5; 22:3-6; 25:4-6.

9. Pamene Yobu anayesedwa, kodi anakana kucita ciani?

9 Kodi iye anacitanji atayesedwa? Monga munthu wopanda ungwilo, anadzudzula mwaukali anzakewo na kukamba mawu amene pambuyo pake anavomeleza kuti anali opanda pake. Komanso, anagogomeza kwambili za kulungama kwake kuposa za kulungama kwa Yehova. (Yobu 6:3; 13:4, 5; 32:2; 34:5) Olo kuti zinthu zinafika poipa kwambili, Yobu anakana kupandukila Mulungu. Sanakhulupilile mabodza amene anzake aja anamuuza. Anati: “Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.” (Yobu 27:5) Inde, Yobu anatsimikiza mtima kukhalabe na mtima wamphumphu, zivute zitani. Mofanana na Yobu, ifenso tingakhale na mtima wamphumphu.

10. Kodi nkhani imene Satana anayambitsa ponena za Yobu imatikhudza bwanji?

10 Kodi nkhani imene Satana anayambitsa ponena za Yobu imatikhudza bwanji ife? Satana amakamba kuti cikondi canu pa Yehova Mulungu n’caciphamaso, cakuti ngati mwakumana na mavuto, mungaleke kum’tumikila. Amati simungathe kukhala na mtima wamphumphu. (Yobu 2:4, 5; Chiv. 12:10) Ndithudi, zimenezi n’zopweteka mtima ngako. Koma Yehova amatidalila kwambili. Ndipo watipatsa mwayi wamtengo wapatali wothandiza kutsimikizila kuti Mdyelekezi ni wabodza. Wacita izi mwa kulola Satana kutiyesa. Iye amakhulupilila kuti tingathe kukhalabe na mtima wamphumphu. Ndipo walonjeza kuti adzatithandiza kucita zimenezi. (Aheb. 13:6) Ni mwayi wamtengo wapatali cotani nanga kuti Mfumu ya cilengedwe conse imatidalila! Kodi mwaona tsopano kuti kukhala na mtima wamphumphu n’kofunika kwambili? Kumatithandiza kutsutsa mabodza a Satana, kukweza dzina loyela la Atate wathu, na kucilikiza ulamulilo wake. Nanga tingacite ciani kuti tikhalebe na mtima wamphumphu?

ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUKHALABE NA MTIMA WAMPHUMPHU MASIKU ANO

11. Tingaphunzile ciani kwa Yobu?

11 Satana akumenya nkhondo zolimba polimbana na atumiki a Mulungu “masiku otsiliza” ano. (2 Tim. 3:1) Kodi n’ciani cingatithandize kukhalabe na mtima wamphumphu? Tingaphunzile zambili kwa Yobu. Asanakumane na ciyeso, Yobu anali kale na cizoloŵezi cocita zinthu na mtima wamphumphu. Onani mfundo zitatu zimene tingaphunzile kwa iye, zotithandiza kukhalabe na mtima wamphumphu.

N’zinthu zina ziti zimene tiyenela kucita kuti tikhalebe na mtima wamphumphu? (Onani ndime 12) *

12. (a) Mogwilizana na Yobu 26:7, 8, 14, n’ciani cinathandiza Yobu kuti aziopa Yehova na kumumvela? (b) Tingacite ciani kuti tikhale na mtima woopa Mulungu?

12 Yobu anakulitsa cikondi cake pa Yehova mwa kuphunzila kumuopa. Yobu anali kupatula nthawi yosinkha-sinkha pa zinthu zodabwitsa zimene Yehova analenga. (Ŵelengani Yobu 26:7, 8, 14.) Iye anacita cidwi na zinthu monga dziko lapansi, mitambo, na mabingu. Koma anavomeleza kuti zimene anali kudziŵako za cilengedwe ca Mulungu, zinali zocepa cabe. Cinanso, Yobu anali kulemekeza kwambili Mawu a Yehova. Pokamba za Mawu a Mulungu, iye anati: “Ndasunga mosamala mawu a pakamwa pake.” (Yobu 23:12) Yobu anali kudabwa kwambili na ukulu wa Yehova, ndipo anali kumulemekeza kwambili. Anali kum’konda kwambili Atate wake wakumwamba, ndipo anali kufuna kum’kondweletsa. Izi zinam’limbikitsa kukhalabe na mtima wamphumphu. Tiyenela kutengela citsanzo cake. Masiku ano, timadziŵa zinthu zambili zodabwitsa zimene Mulungu analenga. Komanso tili na Baibo yathunthu imene ingatithandize kum’dziŵa bwino Yehova. Zonsezi zingatithandize kuti tizimuopa na kum’lemekeza. Kuyopa Yehova na kum’lemekeza kudzatilimbikitsa kum’konda na kumumvela, ndipo pamapeto pake tidzakhala ofunitsitsa kukhalabe na mtima wamphumphu.—Yobu 28:28.

Zinthu zina zimene zingatithandize kukhalabe na mtima wamphumphu ni kupewa kuonelela zamalisece, (Onani ndime 13) *

13-14. (a) Malinga na Yobu 31:1, kodi Yobu anaonetsa bwanji kuti anali womvela? (b) Ndipo ife tingatengele bwanji citsanzo cake?

13 Cizoloŵezi comvela malamulo a Mulungu cinam’thandiza Yobu kukhalabe na mtima wamphumphu. Yobu anali kudziŵa kuti kumvela n’kofunika kuti munthu akhale na mtima wamphumphu. Ndipo nthawi iliyonse tikacita zinthu zoonetsa kuti ndife omvela, timalimbikitsidwa kukhalabe na mtima wamphumphu. Yobu anali kuyesetsa kumvela Mulungu pa umoyo wake wa tsiku na tsiku. Mwacitsanzo, Yobu anali kusamala na mmene anali kucitila zinthu ndi akazi. (Ŵelengani Yobu 31:1.) Monga mwamuna wokwatila, anali kudziŵa kuti n’kulakwa kuyang’ana mkazi amene si wake momukhumbila. M’dzikoli, muli zinthu zambili zosonkhezela cilakolako coipa ca kugonana. Conco, funso n’lakuti, kodi tidzatengela citsanzo ca Yobu mwa kupewa kuyang’anitsitsa aliyense amene si mwamuna wathu kapena mkazi wathu? Kodi tidzapewanso kuona zithunzi zamalisece kulikonse kumene zimapezeka? (Mat. 5:28) Ngati tsiku lililonse tiyesetsa kukhala odziletsa, tidzalimbikitsidwa kukhalabe na mtima wamphumphu.

Zinthu zina zimene zingatithandize kukhalabe na mtima wamphumphu ni kuona zinthu zakuthupi moyenela (Onani ndime 14) *

14 Yobu anali kumvelanso Yehova pa nkhani ya mmene anali kuonela zinthu zakuthupi. Iye anaona kuti kudalila cuma, kungakhale kulakwa kofunika cilango. (Yobu 31:24, 25, 28) Masiku ano, anthu ambili ni okonda cuma. Ngati tiyesetsa kuona ndalama na katundu moyenela, monga mmene Baibo imatilangizila, tidzakhalabe na mtima wamphumphu.—Miy. 30:8, 9; Mat. 6:19-21.

Zinthu zina zimene zingatithandize kukhalabe na mtima wamphumphu, ni kuganizila za ciyembekezo cathu nthawi zonse (Onani ndime 15) *

15. (a) Ni ciyembekezo ca mphoto iti cimene cinathandiza Yobu kukhalabe na mtima wamphumphu? (b) N’cifukwa ciani tifunika kumakumbukila mphoto imene Yehova adzatipatsa?

15 Yobu anakhalabe na mtima wamphumphu cifukwa anaika maganizo ake pa mphoto imene Mulungu anam’lonjeza. Anali kudziŵa kuti Mulungu anali kuona na kuyamikila kukhulupilika kwake. (Yobu 31:6) Yobu anali kukhulupilila kuti olo akumane na mavuto, Yehova adzamudalitsa pamapeto pake. Cikhulupililo cimeneci cinam’limbikitsa kupitiliza kukhala na mtima wamphumphu. Yehova anakondwela ngako cifukwa ca kukhulupilika kwa Yobu, cakuti anamukhuthulila madalitso ambili. (Yobu 42:12-17; Yak. 5:11) Ndipo kutsogoloku, adzalandila madalitso osaneneka. Kodi imwe mumakhulupilila na mtima wonse kuti Yehova adzakudalitsani cifukwa cokhala na mtima wamphumphu? Kumbukilani kuti Mulungu wathu sanasinthe. (Mal. 3:6) Kukumbukila kuti iye amayamikila tikakhala na mtima wamphumphu, kudzatithandiza kukhala na ciyembekezo camphamvu ca tsogolo labwino.—1 Ates. 5:8, 9.

16. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani?

16 Conco, muzicita ciliconse cotheka kuti mukhalebe na mtima wamphumphu! Nthawi zina, mungaone kuti anzanu ambili sakucita zimenezi. Koma musataye mtima, simuli mwekha. Muli pakati pa gulu la anthu okhulupilika mamiliyoni, amene akuyesetsa kukhalabe na mtima wamphumphu. Komanso mudzakhala pa gulu la amuna na akazi okhulupilika akale, amene anakhalabe na mtima wamphumphu, olo pamene anawopsezedwa kuti adzaphedwa. (Aheb. 11:36-38; 12:1) Tiyeni tonse titengele citsanzo ca Yobu, amene anati: “Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.” Inde, tiyeni tikhalebe na mtima wamphumphu, kuti Yehova alemekezeke kwamuyaya!

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

^ ndime 5 Kodi kukhala na mtima wamphumphu kumatanthauzanji? N’cifukwa ciani Yehova amaona kuti kukhala na mtima wamphumphu n’kofunika kwambili? Nanga kukhala na mtima wotelo kuli na ubwino wanji kwa ife? Nkhani ino idzafotokoza mayankho a m’Baibo pa mafunso amenewa. Idzafotokozanso zimene zingatithandize kuti tsiku lililonse tizicita zinthu zoonetsa kuti tili na mtima wamphumphu. Ndipo tikatelo, tidzadalitsidwa kwambili.

^ ndime 3 Liwu la Ciheberi lomasulidwa kuti “yopanda cilema” pokamba za nyama, n’logwilizana na liwu laciheberi lomasulidwa kuti “mtima wamphumphu” pokamba za anthu.

^ ndime 50 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Yobu, pamene anali tate wacinyamata, akuphunzitsa ena mwa ana ake za cilengedwe codabwitsa ca Yehova.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’bale akukana kuonelela zithunzi zamalisece zimene anzake ku nchito akuonelela;

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’bale akukana kugula ci TV cacikulu cimene n’codula komanso cosafunikila kweni-kweni kwa iye;

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’bale akupemphela na kuganizila za ciyembekezo ca Paradaiso.