Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 8

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kuonetsa Kuyamikila?

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kuonetsa Kuyamikila?

“Sonyezani kuti ndinu oyamikila.”—AKOL. 3:15.

NYIMBO 46 Tikuyamikani Yehova

ZA M’NKHANI INO *

1. Kodi Msamariya wina amene anacilitsidwa na Yesu anaonetsa bwanji kuyamikila?

PANALI amuna 10 odwala khate, amene analibiletu ciyembekezo cakuti adzacila. Koma tsiku lina, anaona Yesu, Mphunzitsi Waluso akudutsa capatali. Iwo anali atamvela kuti Yesu anali kucilitsa matenda a mtundu uliwonse, ndipo anali na cikhulupililo cakuti nawonso angacilitsidwe. Conco, anafuula mokweza mawu kuti: “Yesu, Mlangizi, ticitileni cifundo!” Ndipo onse 10 anacilitsidwadi. Mwacidziŵikile, onse anayamikila kukoma mtima kumene Yesu anawaonetsa. Koma mmodzi wa iwo sanangoyamikila cabe mumtima mwake. Anacitapo kanthu mwa kupita kwa Yesu kukaonetsa kuyamikila * kwake. Mtima wake woyamikila unam’sonkhezela kutamanda Mulungu “mokweza mawu.”—Luka 17:12-19.

2-3. (a) N’ciani cingatipangitse kuiŵala kuonetsa kuyamikila? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

2 Mofanana na Msamariya uja, timafuna kuonetsa kuti timawayamikila anthu amene amacita zinthu zabwino. Koma nthawi zina, tingaiŵale kuonetsa kuyamikila kwathu mwa mawu na zocita zathu.

3 M’nkhani ino, tidzakambilana cifukwa cake kuonetsa kuyamikila m’mawu na m’zocita zathu n’kofunika. Tidzaphunzila zitsanzo za anthu ena a m’Baibo, amene anali oyamikila komanso amene sanali oyamikila. Ndiyeno, tidzakambilana njila zina zimene tingaonetsele kuyamikila.

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUONETSA KUYAMIKILA?

4-5. N’cifukwa ciani tifunika kuonetsa kuyamikila?

4 Yehova amapeleka citsanzo cabwino pa nkhani yoyamikila ena. Njila imodzi imene amacitila zimenezi ni mwa kudalitsa anthu ocita zinthu zom’kondweletsa. (2 Sam. 22:21; Sal. 13:6; Mat. 10:40, 41) Ndipo Malemba amatilimbikitsa ‘kutsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.’ (Aef. 5:1) Conco, cifukwa cacikulu cimene timaonetsela kuyamikila, n’cakuti timafuna kutengela citsanzo ca Yehova.

5 Palinso cifukwa cina cimene timayamikilila ena. Kuyamikila ena kuli monga cakudya cabwino. Tikapatsidwa cakudya cabwino, timakondwela. Komanso tikapatsa ena cakudya cabwino, nawonso amakondwela. Mofananamo, anthu ena akatiyamikila pa zimene timacita, timakondwela. Komanso, tikayamikila ena pa zimene amacita, nawonso amakondwela. Zili conco cifukwa ngati munthu tamuyamikila, amaona kuti zinthu zimene anaticitila kapena kutipatsa sizinapite pacabe. Zotulukapo zake n’zakuti ubwenzi wathu na iye umalimba.

6. Kodi mawu oyamikila amalingana bwanji na maapozi agolide?

6 Kukamba mawu oyamikila n’kofunika ngako. Baibo imati: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenela ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miy. 25:11) Tangoyelekezelani cabe mmene maapozi opangidwa na golide angakongolele ataikidwa m’mbale ya siliva! Kodi mungamvele bwanji mutalandila mphatso ngati imeneyo? Umu ni mmenenso mawu anu oyamikila ena amakhalila. Cinanso n’cakuti, maapozi agolide angakhalepo kwa zaka zambili-mbili osawonongeka. Mofananamo, mawu oyamikila amene tingakambe kwa munthu, angawakumbukile kwa zaka zambili, mwina kwa moyo wake wonse.

ANAONETSA MZIMU WOYAMIKILA

7. Malinga na Salimo 27:4, kodi Davide ndi amuna ena amene analemba masalimo anaonetsa bwanji kuyamikila Yehova?

7 Atumiki a Mulungu ambili akale, anaonetsa khalidwe loyamikila. Mmodzi wa iwo anali Davide. (Ŵelengani Salimo 27:4.) Iye anayamikila kwambili mwayi wa kulambila koona, ndipo anacitapo kanthu poonetsa kuyamikila kwake. Mwacitsanzo, anapeleka zinthu zambili zamtengo wapatali zothandizila pa nchito yomanga kacisi. Mbadwa za Asafu zinaonetsa kuyamikila mwa kulemba masalimo, kapena kuti nyimbo zotamanda Mulungu. M’nyimbo ina, iwo anayamikila Mulungu, komanso analengeza ‘nchito zake zodabwitsa.’ (Sal. 75:1) Davide na mbadwa za Asafu anayamikila Yehova cifukwa ca zinthu zonse zabwino zimene iye anawacitila. Kodi tingatengele bwanji citsanzo cawo?

Kodi tiphunzila ciani pa nkhani yoyamikila ena tikaganizila kalata imene Paulo analembela Akhristu a ku Roma? (Onani ndime 8-9) *

8-9. Kodi mtumwi Paulo anawayamikila bwanji abale na alongo ake? Nanga payenela kuti panakhala zotulukapo zanji?

8 Mtumwi Paulo anali kuona Akhristu anzake kukhala ofunika kwambili. Anaonetsa zimenezi m’zokamba zake. Nthawi zonse popemphela, Paulo anali kuyamika Mulungu kaamba ka iwo. Komanso, m’makalata amene anawalembela, anali kukambamo mawu owayamikila. Mwacitsanzo, pa Aroma 16: 1-15, Paulo anachula maina 27 a Akhristu anzake. Paulo anakamba kuti Purisika ndi Akula “anaika miyoyo yawo paciswe” cifukwa ca iye. Anakambanso kuti Febe “anateteza abale ambilimbili,” kuphatikizapo iyeyo. Paulo anawayamikila abale na alongo ake okondedwa cifukwa cotumikila mwakhama.

9 Paulo anali kudziŵa kuti panali zinthu zina zimene abale na alongo sanali kucita bwino. Ngakhale n’telo, cakumapeto kwa kalata imene analembela Akhristu a ku Roma, iye anakamba kwambili za makhalidwe awo abwino. N’zosakayikitsa kuti pamene kalatayo inali kuŵelengedwa mu mpingo, Akhristuwo analimbikitsidwa kwambili. Mwacionekele, izi zinacititsa kuti ubwenzi wawo na Paulo ulimbileko. Kodi imwe muli na cizolowezi coyamikila abale na alongo mu mpingo pa zabwino zimene amakamba na kucita?

10. Kodi tingaphunzile ciani tikaona mmene Yesu anayamikilila otsatila ake?

10 M’mauthenga a Yesu opita ku mipingo ya ku Asia Minor, iye anayamikila otsatila ake cifukwa ca nchito imene anacita. Mwacitsanzo, mu uthenga wake wopita ku mpingo wa Tiyatira, iye anayamba na mawu akuti: “Ndikudziŵa nchito zako, cikondi cako, cikhulupililo cako, utumiki wako, ndi kupilila kwako. Ndikudziŵanso kuti nchito zako zapanopa n’zambili kuposa zoyamba zija.” (Chiv. 2:19) Yesu anayamikila Akhristuwo cifukwa ca kuculuka kwa nchito zawo zabwino, komanso cifukwa ca makhalidwe abwino amene anawasonkhezela kugwila nchitozo. Ngakhale kuti colinga cake cinali kupeleka uphungu kwa Akhristu ena mu mpingomo, iye anayamba na kutsiliza uthenga wake na mawu olimbikitsa. (Chiv. 2:25-28) Pokhala mutu wa mipingo yonse, Yesu ali na udindo waukulu kwambili, cakuti safunika kucita kutiyamikila pa nchito zimene timam’citila. Ngakhale n’telo, iye amayesetsa kutiyamikila. Ndithudi, iye n’citsanzo cabwino kwambili kwa akulu!

SANAONETSE MZIMU WOYAMIKILA

11. Kodi Aheberi 12:16, ionetsa kuti Esau anali kuziona bwanji zinthu zopatulika?

11 N’zomvetsa cisoni kuti anthu ena ochulidwa m’Baibo, sanaonetse mzimu woyamikila. Mwacitsanzo, olo kuti Esau analeledwa na makolo amene anali kukonda Yehova na kum’lemekeza, iye sanayamikile zinthu zopatulika. (Ŵelengani Aheberi 12:16.) Kodi anaonetsa bwanji kusayamikila? Mosaganiza bwino, Esau anagulitsa udindo wake monga woyamba kubadwa kwa mng’ono wake Yakobo, posinthanitsa na cakudya cabe ca mphodza. (Gen. 25:30-34) Pambuyo pake, Esau anadzimvelela cisoni kwambili cifukwa ca zimene anacita. Koma popeza kuti sanayamikile mwayi umene anali nawo, sanafunikile kudandaula pamene anamanidwa madalitso a mwana woyamba kubadwa.

12-13. Kodi Aisiraeli anaonetsa bwanji mzimu wosayamikila? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

12 Nawonso Aisiraeli anali na zifukwa zambili zoyamikilila Yehova. Mwacitsanzo, iye anawamasula ku ukapolo ku Iguputo pambuyo pogwetsela dzikolo milili 10. Kenako, Mulungu anawapulumutsa mwa kuwononga asilikali onse a Iguputo pa Nyanja Yofiila. Aisiraeli anam’yamikila ngako Yehova, moti anaimba nyimbo yacipambano yom’tamanda. Koma kodi iwo anakhalabe na mtima woyamikila?

13 Pamene Aisiraeli anakumana na mavuto ena, anaiŵala zabwino zonse zimene Yehova anawacitila. Ndipo anayamba kucita zinthu zoonetsa kusayamikila. (Sal. 106:7) Zinthu zotani? Baibo imati: “Khamu lonse la ana a Isiraeli linayamba kung’ung’udzila Mose ndi Aroni.” M’ceni-ceni, iwo anali kung’ung’udza motsutsana na Yehova. (Eks. 16:2, 8) Yehova sanakondwele na mtima wosayamikila umene anthu ake anaonetsa. Conco, anakambilatu kuti m’badwo wonse wa Aisiraeli udzafela m’cipululu, kusiyapo cabe Yoswa na Kalebe. (Num. 14:22-24; 26:65) Lomba tiyeni tikambilane mmene tingapewele kutengela zitsanzo zoipa zimenezi, na mmene tingatsatilile zitsanzo zabwino.

MMENE TINGAONETSELE KUYAMIKILA MASIKU ANO

14-15. (a) Kodi ali pa banja angaonetse bwanji kuti amayamikilana? (b) Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana kukhala oyamikila?

14 M’banja. Banja lonse limapindula ngati aliyense m’banjamo amaonetsa mtima woyamikila. Ngati mwamuna na mkazi wake amakonda kuyamikilana, amakondananso kwambili. Ndipo cimakhalanso cosavuta kukhululukilana wina akalakwitsa. Mwamuna amene amakondadi mkazi wake, amayang’ana pa zabwino zimene mkaziyo amacita, komanso “amaimilila n’kumutamanda.” (Miy. 31:10, 28) Nayenso mkazi wanzelu amayamikila mwamuna wake, mwa kuchula zinthu zabwino zimene mwamunayo amacita.

15 Inu makolo, kodi mungaphunzitse bwanji ana anu kuonetsa mtima woyamikila? Kumbukilani kuti ana anu amatengela zimene mumakamba na kucita. Conco, onetsani citsanzo cabwino mwa kukamba zikomo pamene ana anu akucitilani zinthu zinazake. Komanso, aphunzitseni kukamba zikomo pamene anthu ena awacitila zinthu zinazake. Athandizeni kudziŵa kuti kuyamikila kuyenela kukhala kocokela pansi pa mtima, komanso kuti angathe kulimbikitsa ena kwambili na mawu awo. Mwacitsanzo, mlongo wina wacitsikana, dzina lake Clary, anati: “Pamene amayi anali na zaka 32, atate anamangidwa, ndipo amayi anatsala okha, moti anafunika kulela okha ana atatu, ine na azilongosi anga aŵili. Pamene n’nakwanitsa zaka 32, n’nazindikila kuti zinali zovuta kwambili kwa amayi kuti akwanitse kutilela pamene anali pa msinkhu umenewo. Conco, n’nawauza kuti nimayamikila kwambili pa zonse zimene anacita potilela. Posacedwa, iwo ananiuza kuti sadzawaiŵala mawu amene n’nawauza. Anakambanso kuti nthawi zambili akawaganizila mawuwo, amalimbikitsidwa kwambili.”

Phunzitsani ana anu kuti azionetsa kuyamikila (Onani ndime 15) *

16. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti kuyamikila ena kumawalimbikitsa.

16 Mu mpingo. Abale na alongo athu, amalimbikitsidwa kwambili tikamawayamikila. Mwacitsanzo, Jorge, m’bale wa zaka 28 amene ni mkulu, pa nthawi ina anadwala kwambili. Iye sanakwanitse kupezeka ku misonkhano kwa mwezi wathunthu. Ngakhale pamene anayamba kupezekako, sanali kukwanitsa kukamba nkhani. Iye anati: “N’nayamba kudziona monga munthu wopanda pake, cifukwa colephela kusamalila maudindo anga a mu mpingo. Koma tsiku lina pambuyo pa msonkhano, m’bale wina ananiuza kuti: ‘Nikukuyamikilani cifukwa ca citsanzo cabwino cimene mwaonetsa ku banja lathu. Takhala tikulimbikitsidwa kwambili na nkhani zanu m’zaka zapitazi. Zalimbitsa kwambili cikhulupililo cathu.’ Mawu amenewa ananikhudza kwambili, cakuti n’nagwetsa misozi yacisangalalo. Analidi mawu a pa nthawi yake kwa ine.”

17. Malinga na Akolose 3:15, kodi tingaonetse bwanji kuti timam’yamikila Yehova kaamba ka kuwolowa manja kwake?

17 Kwa Mulungu wathu woolowa manja. Yehova watipatsa cakudya cauzimu ca mwana alilenji. Mwacitsanzo, timalandila malangizo othandiza kupitila m’misonkhano, m’magazini, na m’mawebusaiti athu. Kodi munatambako vidiyo ya JW Broadcasting, kuŵelenga kapena kumvetsela nkhani pa msonkhano, imene inakukhudzani kwambili cakuti m’nakamba kuti, ‘Koma nkhani iyi ni ya pa nthawi yake’? Kodi tingaonetse bwanji kuti timam’yamikila Yehova? (Ŵelengani Akolose 3:15.) Njila imodzi imene tingaonetsele zimenezi, ni mwa kum’yamikila m’pemphelo nthawi zonse kaamba ka mphatso zabwino zimene amatipatsa.—Yak. 1:17.

Kugwila nawo nchito yoyeletsa pa Nyumba ya Ufumu, ni njila yabwino yoonetsela kuyamikila (Onani ndime 18)

18. Kodi tingaonetse m’njila ziti kuti timayamikila Nyumba yathu ya Ufumu?

18 Timaonetsanso kuyamikila Yehova mwa kuonetsetsa kuti pa malo athu olambilila m’poyela komanso paukhondo. Timatengako mbali nthawi zonse pa nchito yoyeletsa na kukonzanso Nyumba yathu ya Ufumu. Komanso, abale amene ali na udindo wosamalila zokuzila mawu pa mpingo, amayesetsa kuziseŵenzetsa mosamala kuti zisawonongeke. Ngati tisamala bwino Nyumba zathu za Ufumu, siziwonongeka mwamsanga, ndipo sipakhala zambili zofunika kukonzedwa. Kucita izi kumathandiza kuti pakhale ndalama zambili zomangila na kukonzanso Nyumba zina za Ufumu padziko lonse.

19. Kodi mwaphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila woyang’anila dela wina na mkazi wake?

19 Kwa amene amatumikila molimbika kaamba ka ife. Mawu athu oyamikila angathandize kucepetsa nkhawa imene anthu ena ali nayo cifukwa ca mavuto amene akukumana nawo. Ganizilani citsanzo ca woyang’anila dela wina na mkazi wake. Tsiku lina m’nyengo yozizila, iwo analalikila kwa tsiku lonse, ndipo anabwelela ku nyumba ali olema kwambili. Tsiku limenelo, kunazizila kwambili cakuti mlongoyo anagona atavala khoti yamphepo. Kutaca m’maŵa, mlongoyo anauza mwamuna wake kuti sadzakwanitsa kupitiliza kutumikila m’dela. M’maŵa umenewo, banjalo linalandila kalata yocokela ku ofesi ya nthambi, ndipo analembela mlongoyo. M’kalatayo, anamuyamikila kwambili cifukwa ca utumiki umene anali kucita, komanso kupilila kwake. Kalatayo inakamba kuti n’zoona kuti umoyo wokuka-kuka wiki iliyonse umakhala wovuta. Mwamuna wake anati: “Mkazi wanga analimbikitsidwa kwambili na kalatayi, cakuti sanakambenso zofuna kuleka utumikiwu. Ndipo nthawi zambili ine n’kakhala na maganizo ofuna kuleka, iye na amene anali kun’limbikitsa kuti tipitilize.” Banja limeneli linatumikila m’dela kwa zaka pafupi-fupi 40.

20. Kodi tsiku lililonse tiziyesetsa kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kucita zimenezi?

20 Conco, tiyeni tiziyesetsa tsiku lililonse kuonetsa kuyamikila mwa zokamba na zocita zathu. Kuyamikila ena mocokela pansi pa mtima, mwa zokamba na zocita zathu, kungawathandize kupilila mavuto amene akukumana nawo m’dziko losayamikali. Kuyamikila ena kungatithandizenso kupanga ubwenzi wolimba ndi anthu ena, umene ungakhalepo kwamuyaya. Ndipo koposa zonse, tikakhala na mtima woyamikila, ndiye kuti tikutengela Atate wathu Yehova, amene ni wooloŵa manja, komanso woyamikila.

NYIMBO 20 Munapeleka Mwana Wanu Wokondeka

^ ndime 5 Kodi tingaphunzile ciani kwa Yehova, Yesu, na Msamariya wina wakhate, pankhani yoonetsa kuyamikila? M’nkhani ino, tidzakambilana zitsanzo zimenezi, na zina zambili. Tidzaphunzila cifukwa cake kuonetsa kuyamikila n’kofunika kwambili. Tidzaphunzilanso njila zina zimene tingaonetsele kuyamikila.

^ ndime 1 MAWU OFOTOKOZEDWA: Kuyamikila munthu kapena cinthu cinacake, kumatanthauza kuzindikila kufunika kwa munthuyo kapena cinthuco. Liwuli limatanthauzanso kuthokoza kocokela pansi pamtima.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Kalata ya Paulo ikuŵelengedwa mu mpingo wa Aroma, ndipo Akula, Purisika, Febe, na Akhristu ena akondwela pomvela maina awo akuchulidwa.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Mlongo akuphunzitsa mwana wake kuyamikila mlongo wacikulile cifukwa ca citsanzo cake cabwino.