Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 9

Cikondi na Cilungamo M’nthawi ya Aisiraeli

Cikondi na Cilungamo M’nthawi ya Aisiraeli

“Iye amakonda cilungamo ndi ciweluzo cosakondela. Dziko lapansi ladzaza ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova.SAL. 33:5.

NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

ZA M’NKHANI INO *

1-2. (a) Kodi tonse timafuna kucitilidwa zinthu motani? (b) Kodi sitiyenela kukayikila za ciani?

TONSE timafuna kuti anthu ena azitikonda. Timafunanso kuti azicita nafe zinthu mwacilungamo. Ngati nthawi zambili timacitilidwa zinthu mopanda cikondi, kapena mopanda cilungamo, tingadzimve kukhala opanda pake, komanso tingataye mtima.

2 Yehova amadziŵa kuti timafuna kucitilidwa zinthu mwacikondi komanso mwacilungamo. (Sal. 33:5) Sitiyenela kukayikila kuti iye amatikonda kwambili, ndipo amafuna kuti tizicitilidwa zinthu mwacilungamo. Izi zimaonekela bwino, tikaganizila kwambili za Cilamulo cimene Yehova anapatsa mtundu wa Aisiraeli, kupitila mwa Mose. Ngati mtima umakuŵaŵani cifukwa cocitilidwa zinthu mopanda cilungamo kapena cikondi, onani mmene Cilamulo ca Mose * cimaonetsela cikondi ca Yehova pa anthu ake.

3. (a) Mogwilizana na Aroma 13:8-10, n’ciani cimene timaona pamene tiphunzila Cilamulo ca Mose? (b) Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani ino?

3 Pamene tiphunzila za Cilamulo ca Mose, timaona kuti Mulungu wathu Yehova ni wacikondi kwambili. (Ŵelengani Aroma 13:8-10.) M’nkhani ino, tidzakambilanako malamulo ocepa a m’cilamulo, amene anapelekedwa kwa Aisiraeli. Ndipo tidzayankha mafunso aya: N’cifukwa ciani tingakambe kuti Cilamulo cinazikidwa pa cikondi? Kodi cilamulo cinalimbikitsa bwanji cilungamo? Kodi akulu na oweluza anali kucitsatila bwanji Cilamulo poweluza? Nanga cinali kuteteza ndani maka-maka? Kukambilana mayankho pa mafunso amenewa, kudzatitonthoza mtima, kutipatsa ciyembekezo, na kutithandiza kuyandikila kwambili Atate wathu wacikondi.—Mac. 17:27; Aroma 15:4.

CILAMULO CA MOSE CINAZIKIDWA PA CIKONDI

4. (a) N’cifukwa ciani tingakambe kuti Cilamulo ca Mose cinazikidwa pa cikondi? (b) Malinga na Mateyu 22:36-40, ni malamulo ati amene Yesu anagogomeza?

4 Tingakambe kuti Cilamulo ca Mose cinazikidwa pa cikondi cifukwa zilizonse zimene Yehova amacita, amazicita cifukwa ca cikondi. (1 Yoh. 4:8) Malamulo onse a m’cilamulo amene Yehova anapeleka, anazikidwa pa malamulo aŵili akulu-akulu—lakuti uzikonda Mulungu, ndi lakuti uzikonda mnzako. (Lev. 19:18; Deut. 6:5; ŵelengani Mateyu 22:36-40.) Conco, lililonse mwa malamulo oposa 600 a m’Cilamulo ca Mose, limatiphunzitsa mbali inayake ya cikondi ca Yehova. Tiyeni tikambilane zitsanzo.

5-6. N’ciani cimene Yehova amafuna kwa anthu amene ali pabanja? Ndipo n’ciani cimene iye amatha kuona? Fotokozani citsanzo.

5 Muzikhala wokhulupilika kwa mnzanu wa m’cikwati, ndiponso muzisamalila bwino ana anu. Yehova amafuna kuti anthu ali pa banja azikondana kwambili, moti cikondi cawo n’kukhalapo kwa moyo wawo wonse. (Gen. 2:24; Mat. 19:3-6) Kucita cigololo ni chimo lalikulu kwambili, komanso n’kupanda cikondi. Ndiye cifukwa cake, lamulo la namba 7 pa Malamulo Khumi, linaletsa kucita cigololo. (Deut. 5:18) Kucita cigololo “n’kucimwila Mulungu,” ndiponso n’kucitila nkhanza mnzako wa m’cikwati. (Gen. 39:7-9) Mwamuna kapena mkazi akacita cigololo, mnzake wosalakwayo angavutike maganizo kwa zaka zambili.

6 Yehova amaona mmene mwamuna na mkazi wake m’cikwati amacitila zinthu kwa wina na mnzake. M’nthawi ya Aisiraeli, Mulungu anali kufunitsitsa kuti akazi azisamalidwa bwino. Mwamuna amene anali kulemekeza Cilamulo, anali kukonda mkazi wake, ndipo anali kupewa kum’sudzula pa zifukwa zosamveka. (Deut. 24:1-4; Mat. 19:3, 8) Ngati mkazi wapezeka na vuto linalake lalikulu, mwamuna anali kukhala na ufulu wom’sudzula. Koma anali kufunika kum’patsa kalata ya cisudzulo. Kalatayo inali kum’teteza ku zinenezo zakuti wacita cigololo. Kuwonjezela apo, mwamuna asanapatse mkazi wake kalata yacisudzulo, zioneka kuti anali kukafunsila malangizo kwa akulu a mumzinda coyamba. Mwa ici, akuluwo anali kukhala na mpata wothandiza banjalo kuti lipulumutse cikwati cawo. Ngati mwamuna waciisiraeli wasudzula mkazi wake pa zifukwa zosamveka, si nthawi zonse pamene Yehova anali kuloŵelelapo. Komabe, iye anali kukhudzika poona cisoni na mavuto amene mkaziyo anali kukumana nawo.—Mal. 2:13-16.

Yehova amafuna kuti makolo aziŵalela mwacikondi ana awo na kuwaphunzitsa, n’colinga cakuti azidzimva kukhala otetezeka. (Onani ndime 7-8) *

7-8. (a) Kodi Yehova analamula makolo kuti azicita ciani? (Onani cithunzi pacikuto.) (b) Ndipo tiphunzilapo ciani?

7 Cilamulo cinaonetsanso kuti Yehova amafuna kuti ana azikhala acimwemwe komanso otetezeka. Yehova analamula makolo Aciisiraeli kuti azisamalila ana awo mwakuthupi ndi mwauzimu. Iwo anafunika kuseŵenzetsa mpata uliwonse pothandiza ana awo kukonda Yehova, kumvetsetsa Cilamulo cake, na kucilemekeza. (Deut. 6:6-9; 7:13) Cimodzi mwa zifukwa zimene Yehova analangila Aisiraeli, n’cakuti anali kucitila nkhanza kwambili ana awo. (Yer. 7:31, 33) Makolo anafunika kukonda ana awo monga colowa, kapena kuti mphatso yocokela kwa Yehova. Ndipo sanafunike kuwanyalanyaza kapena kuwazunza.—Sal. 127:3.

8 Zimene tiphunzilapo: Yehova amaona mmene okwatilana amacitila zinthu kwa wina na mnzake. Iye amafunanso kuti makolo azikonda ana awo. Ndipo makolo amene amazunza ana awo, adzawalanga.

9-11. N’cifukwa ciani Yehova anapeleka lamulo loletsa kukhumbila mwansanje?

9 Musasilile mwansanje. Lamulo lotsiliza pa Malamulo Khumi linali kuletsa kusilila mwansanje, kapena kuti kukhumbila cinthu ca mwini mosayenela. (Deut. 5:21; Aroma 7:7) Yehova anapeleka lamulo limeneli pofuna kuphunzitsa anthu ake mfundo yofunika. Iwo anafunika kuteteza mtima wawo, kutanthauza kupewa maganizo oipa na zilako-lako zosayenela. Yehova adziŵa kuti maganizo na zilako-lako zosayenela, n’zimene zimapangitsa munthu kucita zoipa. (Miy. 4:23) Ngati Mwisiraeli anali kulola zilako-lako zosayenela kukula mumtima mwake, cinali cosavuta kucitila anzake zinthu mopanda cikondi. Zaconco n’zimene zinagwetsela Mfumu Davide m’chimo. Iye anali munthu wabwino. Koma panthawi ina, anakhumbila mkazi wa mwini. Cilako-lako cake cinabala chimo. (Yak. 1:14, 15) Davide anacita cigololo na mkaziyo, kenako anayesa kupusitsa mwamuna wake, ndipo pamapeto pake anamuphetsa mwamunayo.—2 Sam. 11:2-4; 12:7-11.

10 Yehova anali kudziŵa ngati Mwisiraeli wayamba kukhumbila mosayenela zinthu za mwini, cifukwa iye amadziŵa za mu mtima mwa munthu. (1 Mbiri 28:9) Lamulo loletsa kukhumbila mwansanje, linathandiza Aisiraeli kupewa maganizo amene akanawapangitsa kucita zinthu zoipa. Ndithudi, Atate wathu Yehova ni wanzelu komanso wacikondi kwambili!

11 Zimene tiphunzilapo: Yehova saona cabe maonekedwe akunja a munthu. Koma amaonanso zimene zili mu mtima. (1 Sam. 16:7) Iye amaona zonse zimene timacita, kuganiza na kulaka-laka. Amayang’ana zabwino mwa ife, ndipo amatilimbikitsa kupitiliza kucita zabwino. Iye amafuna kuti maganizo oipa akabwela mu mtima mwathu, tiziwacotsa mwamsanga kuti asatigwetsele m’chimo.—2 Mbiri 16:9; Mat. 5:27-30.

CILAMULO CA MOSE CINALI KULIMBIKITSA CILUNGAMO

12. Kodi Cilamulo ca Mose cimaonetsa ciani?

12 Cilamulo ca Mose cimaonetsanso kuti Yehova amakonda cilungamo. (Sal. 37:28; Yes. 61:8) Iye anapeleka citsanzo cabwino kwambili pa nkhani yocitila ena zinthu mwacilungamo. Pamene Aisiraeli anamvela malamulo amene Yehova anawapatsa, iye anali kuwadalitsa. Koma akanyalanyaza malamulo ake olungama, anali kugwela m’mavuto. Tsopano tiyeni tikambilane malamulo ena aŵili pa Malamulo Khumi.

13-14. Kodi malamulo aŵili oyambilila pa Malamulo Khumi anali akuti bwanji? Nanga kumvela malamulo amenewa kunawapindulitsa bwanji Aisiraeli?

13 Muzilambila Yehova yekha. Malamulo aŵili oyambilila pa Malamulo Khumi, anali akuti Aisiraeli anafunika kulambila Yehova yekha, komanso kuti anayenela kupewa kulambila mafano. (Eks. 20:3-6) Sikuti Malamulo amenewa anapindulitsa Yehova ayi. M’malomwake, anapindulitsa anthu ake. Pamene iwo anakhala okhulupilika kwa iye, zinthu zinali kuwayendela bwino. Koma akayamba kulambila mafano, anali kukumana na mavuto.

14 Ganizilani za Akanani. Iwo anali kulambila milungu yopanda moyo, m’malo molambila Mulungu woona komanso wamoyo. Zotulukapo zake zinali zakuti anadzinyazitsa okha. (Sal. 115:4-8) Pa kulambila kwawo, iwo anali kucita zinthu zonyansa zaciwelewele, na kupeleka nsembe ana awo. Nawonso Aisiraeli pamene anasiya Yehova n’kuyamba kulambila mafano, anali kudzinyazitsa okha na kubweletsa mavuto m’mabanja awo. (2 Mbiri 28:1-4) Cinanso, pamene akulu ndi oweluza analeka kutsatila malamulo olungama a Yehova, anali kuseŵenzetsa ulamulilo wawo molakwika, komanso kupondeleza anthu osauka ndi ovutika. (Ezek. 34:1-4) Yehova anacenjeza Aisiraeli kuti adzalanga anthu amene amazunza akazi ndi ana amasiye. (Deut. 10:17, 18; 27:19) Komabe, anali kuwadalitsa anthu ake akakhala okhulupilika kwa iye, ndiponso akamacita zinthu mwacilungamo kwa wina na mnzake.—1 Maf. 10:4-9.

Yehova amatikonda, ndipo amaona pamene anthu ena aticitila zinthu zopanda cilungamo (Onani ndime 15)

15. Kodi taphunzila ciani ponena za Yehova?

15 Zimene tiphunzilapo: Ngati anthu ena otumikila Mulungu akunyalanyaza malamulo ake na kuvutitsa Akhristu anzawo, sitiyenela kuimba mlandu Yehova. Koma tiyenela kukumbukila kuti Yehova amatikonda, ndipo amaona tikamavutitsidwa. Iye amatimvela cisoni kwambili, kuposa ngakhale cisoni ca mayi akaona mwana wake akuvutika. (Yes. 49:15) N’zoona kuti nthawi zina Yehova sangacitepo kanthu nthawi yomweyo. Komabe, panthawi yake, iye adzalanga anthu osalapa amene amavutitsa anzawo.

KODI CILAMULO CINALI KUTSATILIDWA BWANJI?

16-18. Kodi Cilamulo ca Mose cinali kukhudza mbali ziti za umoyo wa Aisiraeli? Nanga tiphunzilapo ciani?

16 Cilamulo ca Mose cinali kukhudza mbali zonse za umoyo wa Aisiraeli. Conco, zinali zofunika kwambili kuti akulu aziyesetsa kuweluza anthu a Yehova mwacilungamo. Iwo anali na udindo woweluza Aisiraeli pa nkhani zokhudza kulambila, komanso pa milandu ing’ono-ing’ono na ikulu-kulu. Onani zitsanzo izi:

17 Ngati Mwisiraeli wapha munthu, sanali kuphedwa nthawi yomweyo. Akulu a mu mzinda anali kufufuza nkhaniyo coyamba kuti adziŵe ngati wolakwayo anafunikadi kuphedwa kapena ayi. (Deut. 19:2-7, 11-13) Akuluwo anali kuweluzanso Aisiraeli pa nkhani zina zosiyana-siyana, monga zokhudza mikangano ya malo kapena katundu, ngakhalenso mikangano ya m’banja. (Eks. 21:35; Deut. 22:13-19) Pamene akulu anaweluza mwacilungamo, komanso Aisiraeli n’kumvela Cilamulo, aliyense anali kupindula. Ndipo mtunduwo unali kucititsa Yehova kulandila ulemelelo.—Lev. 20:7, 8; Yes. 48:17, 18.

18 Zimene tiphunzilapo: Zilizonse zimene timacita mu umoyo wathu, zimam’khudza Yehova. Iye amafuna kuti tizicita zinthu mwacikondi komanso mwacilungamo ndi ena. Ndipo amaona zonse zimene timacita na kukamba, ngakhale zamseli.—Aheb. 4:13.

19-21. (a) Kodi akulu na oweluza anafunika kuweluza bwanji anthu a Mulungu? (b) Kodi Cilamulo ca Mose cinali kuteteza bwanji anthu? Nanga tiphunzilapo ciani?

19 Yehova anali kufuna kuteteza anthu ake kuti asatengele makhalidwe oipa a mitundu yowazungulila. Conco, iye anafuna kuti akulu ndi oweluza aziseŵenzetsa Cilamulo mosakondela poweluza. Anafunanso kuti asamaweluze mwankhanza kapena mopanda cifundo. M’malomwake, oweluzawo anafunika kukonda cilungamo.—Deut. 1:13-17; 16:18-20.

20 Yehova amamvela cifundo anthu ake. Conco, anaika malamulo n’colinga cakuti aliyense aziweluzidwa mwacilungamo. Mwacitsanzo, Cilamulo cinacepetsa vuto la kunenezana milandu ya bodza. Munthu woimbidwa mlandu anali kukhala na ufulu wodziŵa munthu amene anali kumuimba mlandu. (Deut. 19:16-19; 25:1) Ndipo panafunikila mboni zosacepela ziŵili kuti munthuyo aweluzidwe kuti ni wolakwa. (Deut. 17:6; 19:15) Nanga bwanji ngati Mwisiraeli wacita colakwa cimene caonedwa na munthu mmodzi cabe? Sikuti munthuyo anali na mwayi wozemba cilango, cifukwa Yehova anali kuona zonse. M’banja, tate ndiye anali na ulamulilo. Koma ulamulilo wake unali na malile. Mikangano ina ya m’banja inali kusamalidwa na akulu a mu mzinda, ndipo iwo ndiwo anali kupeleka cigamulo cothela.—Deut. 21:18-21.

21 Zimene tiphunzilapo: Yehova amapeleka citsanzo cabwino kwambili pa nkhani yocita zinthu mwacilungamo. (Sal. 89:14) Iye amadalitsa anthu amene amatsatila miyezo yake mokhulupilika. Koma amalanga anthu amene amaseŵenzetsa ulamulilo wawo molakwika. (2 Sam. 22:21-23; Ezek. 9:9, 10) Anthu ena angacite zoipa na kuganiza kuti azemba cilango. Koma panthawi yake yoyenela, Yehova adzawaweluza mogwilizana na zolakwa zawo. (Miy. 28:13) Ndipo ngati salapa, posacedwa adzazindikila kuti “kulandila cilango cocokela kwa Mulungu wamoyo n’cinthu coopsa.”—Aheb. 10:30, 31.

KODI CILAMULO CINALI KUTETEZA NDANI MAKA-MAKA?

Pothetsa mikangano, akulu anafunika kuweluza anthu mwacikondi komanso mwacilungamo potengela Yehova. (Onani ndime 22) *

22-24. (a) Kodi Cilamulo ca Mose cinali kuteteza ndani maka-maka? Nanga tiphunzilapo ciani za Yehova? (b) Kodi pa Ekisodo 22:22-24 pali cenjezo lanji?

22 Cilamulo cinali kuteteza maka-maka anthu amene sakanakwanitsa kudziteteza okha, monga ana amasiye, akazi amasiye, komanso alendo. Oweluza a mu Isiraeli anauzidwa kuti, “Usapotoze ciweluzo ca mlandu wa mlendo kapena mlandu wa mwana wamasiye, ndipo usalande mkazi wamasiye covala cake monga cikole.” (Deut. 24:17) Yehova anali kuonetsa cifundo na cikondi capadela kwa anthu ovutika, osoŵelatu thandizo. Ndipo amene anali kuvutitsa anthu otelo, Yehova anali kuwalanga.—Ŵelengani Ekisodo 22:22-24.

23 Cilamulo cinatetezanso anthu a m’banja ku khalidwe lonyansa la kugonana kwa pa cibululu kwa mtundu uliwonse. (Lev. 18:6-30) Anthu a mitundu yoyandikana na Isiraeli anali kulekelela mcitidwe umenewu. Koma anthu a Yehova anafunika kuona mcitidwe umenewu kukhala wonyansa kwambili, monga mmene Yehova amauonela.

24 Zimene tiphunzilapo: Yehova amafuna kuti anthu amene wawapatsa udindo wa uyang’anilo, azisamalila anthu ake mwacikondi. Iye amazonda khalidwe loipa la ciwelewele. Ndipo amafuna kuti aliyense, maka-maka anthu ooneka ngati osatetezeka, azicitilidwa zinthu mwacilungamo ndi kuti azikhala motetezeka.

CILAMULO CINALI CITHUNZI-THUNZI CABE CA “ZINTHU ZABWINO ZIMENE ZIKUBWELA”

25-26. (a) N’cifukwa ciani tingakambe kuti cikondi na cilungamo zili ngati moyo na mpweya wa moyo? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila yofotokoza cifukwa cake sitiyenela kukayikila kuti Yehova amatikonda?

25 Cikondi na cilungamo zili ngati moyo na mpweya wa moyo. Zinthu ziŵilizi zimadalilana, moti cimodzi sicingakhalepo popanda cinzake. Tikaona kuti Yehova amaticitila zinthu mwacilungamo, timayamba kum’konda kwambili. Ndipo kukonda Mulungu na Malamulo ake olungama, kumatisonkhezela kukonda anthu anzathu na kuwacitila zinthu mwacilungamo.

26 Cilamulo ca Mose cinathandiza Aisiraeli kukhala paubwenzi wolimba kwambili na Yehova. Koma cilamulo cimeneco cinasiya kugwila nchito pamene Yesu anadzipeleka monga nsembe ya dipo. Ndipo cinaloŵedwa m’malo na Cilamulo cina cabwino koposa. (Aroma 10:4) Mtumwi Paulo anakamba kuti Cilamulo ca Mose cinali cithunzi-thunzi cabe ca “zinthu zabwino zimene zikubwela.” (Aheb. 10:1) M’nkhani yotsatila pankhani zinayi zofotokoza cifukwa cake sitiyenela kukayikila kuti Yehova amatidela nkhawa, tidzakambilana zina mwa zinthu zabwino zimene zikubwela. Komanso, tidzaphunzila cifukwa cake cikondi na cilungamo n’zofunika mu mpingo wacikhristu.

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse

^ ndime 5 Ino ni imodzi mwa nkhani zinayi zimene zifotokoze cifukwa cake sitiyenela kukayikila kuti Yehova amatidela nkhawa. Nkhani zitatu zinazo zidzatuluka mu Nsanja ya Mlonda ya May 2019. Mitu ya nkhanizo ni yakuti: “Cikondi na Cilungamo mu Mpingo Wacikhristu,” “Cikondi na Cilungamo M’dziko Loipali” ndi wakuti, “Kulimbikitsa Amene Anacitilidwapo Zolaula.”

^ ndime 2 MAWU OFOTOKOZEDWA: Malamulo oposa 600 amene Yehova anapatsa Aisiraeli kupitila mwa Mose, amachedwa “Cilamulo,” “Cilamulo ca Mose,” kapena kuti “malamulo.” Kuwonjezela apo, mabuku 5 oyambilila a m’Baibo (Genesis mpaka Deuteronomo), kaŵili-kaŵili amachedwa Cilamulo. Nthawi zina, mawu akuti Cilamulo amagwilitsidwa nchito pochula Malemba onse Aciheberi ouzilidwa.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI PACIKUTO: Mayi waciisiraeli akuceza mosangalala ndi ana ake aakazi pamene akukonza cakudya. Ca kumbuyo kwawo, tate akuphunzitsa mwana wake kusamalila nkhosa.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Akulu pa geti ya mzinda, akuthandiza mwacikondi mkazi wamasiye na mwana wake, amene acitilidwa zinthu zacinyengo na munthu winawake wa zamalonda.