Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 12

Muzimvelela Ena Cifundo

Muzimvelela Ena Cifundo

“Nonsenu mukhale . . . omvelana cisoni.”—1 PET. 3:8.

NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake

ZA M’NKHANI INO *

1. Mogwilizana na 1 Petulo 3:8, n’cifukwa ciani timakondwela kukhala ndi anthu amene amatimvelela cifundo na kutidela nkhawa?

TIMAKONDWELA kukhala ndi anthu amene amatimvelela cifundo na kutidela nkhawa. Anthu acifundo amayesetsa kuzindikila zimene tikuganiza na mmene tikumvelela. Amayesetsanso kuganizila zosoŵa zathu, ndipo amatithandiza, mwina tisanapemphe thandizo n’komwe. Anthu amene ‘amatimvelela cisoni,’ * timawakonda na kuwayamikila.—Ŵelengani 1 Petulo 3:8.

2. N’cifukwa ciani nthawi zina zingakhale zovuta kuonetsa cifundo kwa ena?

2 Pokhala Akhristu, timafuna kuonetsa kuti timamvelela ena cifundo. Koma kucita zimenezi nthawi zina kumakhala kovuta. Cifukwa ciani? Cifukwa coyamba n’cakuti ndife anthu opanda ungwilo. (Aroma 3:23) Timakonda kuganizila zofuna zathu cabe. Conco, pamafunika khama kuti tizicita zinthu moganizila ena. Komanso, ena a ife zimativuta kumvelela ena cifundo cifukwa ca mmene tinakulila, kapena cifukwa ca zokumana nazo mu umoyo. Cinanso, tingayambe kutengela khalidwe la anthu amene tikhala nawo. Masiku otsiliza ano, anthu ambili saganizila anzawo. Ndipo ni “odzikonda.” (2 Tim. 3:1, 2) Nanga tingacite ciani kuti zimenezi zisatilepheletse kuonetsa cifundo kwa ena?

3. (a) Tingakulitse bwanji khalidwe la cifundo? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

3 Tingakulitse khalidwe la cifundo mwa kutengela citsanzo ca Yehova Mulungu na Mwana wake, Yesu Khristu. Yehova ni Mulungu wacikondi, ndipo watipatsa citsanzo cabwino koposa pa nkhani yomvelela ena cifundo. (1 Yoh. 4:8) Yesu anatengela kwambili makhalidwe a Atate wake. (Yoh. 14:9) Pamene anali pa dziko lapansi, anapeleka citsanzo ca mmene tingaonetsele cifundo kwa ena. M’nkhani ino, tidzakambilana mmene Yehova na Yesu anaonetsela kuti amamvelela cifundo anthu. Kenako, tidzakambilana mmene tingatsatilile citsanzo cawo.

CITSANZO CA YEHOVA PA NKHANI YOMVELELA ENA CIFUNDO

4. Kodi lemba la Yesaya 63:7-9 lionetsa bwanji kuti Yehova amamvelela cifundo atumiki ake?

4 Malinga n’zimene Baibo imakamba, Yehova amamvelela cifundo atumiki ake. Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yehova anamvelela pamene Aisiraeli anali kukumana na mavuto osiyana-siyana. Mawu a Mulungu amati: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.” (Ŵelengani Yesaya 63:7-9.) Pa nthawi ina, Yehova kupitila mwa mneneli Zekariya anakamba kuti, ngati anthu ake akuzunzidwa, cimamuŵaŵa kwambili monga kuti iye ndiye akuzunzidwa. Yehova anauza atumiki ake kuti: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.” (Zek. 2:8) Ndithudi, awa ni mawu amphamvu kwambili oonetsa cifundo cimene Yehova ali naco pa anthu ake!

Yehova anaonetsa cifundo mwa kumasula Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo (Onani ndime 5)

5. Fotokozani citsanzo ca mmene Yehova anapulumutsila anthu ake amene anali kuvutika.

5 Kuphatikiza pomvelela cifundo atumiki ake amene akuvutika, Yehova amacitapo kanthu kuti awathandize. Mwacitsanzo, pamene Aisiraeli anali kuzunzidwa monga akapolo ku Iguputo, Yehova anali kuona zoŵaŵa zawo, ndipo anacitapo kanthu. Pokamba na Mose, Yehova anati: “Ndaona nsautso ya anthu anga . . . , ndipo ndamva kulila kwawo . . . Zoonadi, ndikudziwa bwino zowawa zawo. Conco nditsikila kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo.” (Eks. 3:7, 8) Yehova anamvelela cifundo anthu ake. Ndiye cifukwa cake anawamasula mu ukapolo. Zaka zambili pambuyo pake, pamene Aisiraeli anali m’Dziko Lolonjezedwa, adani anayamba kuwaukila. Kodi Yehova anamvela bwanji? Iye “anali kuwamvela cisoni akamva kubuula kwawo cifukwa ca owapondeleza ndi owakankhakankha.” Apanso, cifundo cinam’sonkhezela Yehova kulanditsa anthu ake. Iye anawapatsa oweluza kuti awapulumutse kwa adani awo.—Ower. 2:16, 18.

6. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti Yehova amaganizila atumiki ake, ngakhale pamene ali na maganizo olakwika.

6 Yehova amawaganizila anthu ake, ngakhale pamene ali na maganizo olakwika pa nkhani ina. Mwacitsanzo, ganizilani za Yona. Yehova anam’tuma kuti akalengeze uthenga waciweluzo kwa anthu a ku Nineve. Anineve atalapa, Mulungu anaganiza kuti asawawononge. Koma Yona sanakondwele nazo zimenezi. Iye ‘anakwiya koopsa,’ cifukwa uthenga wake waciweluzo sunakwanilitsike. Koma Yehova anacita naye zinthu moleza mtima, ndipo anam’thandiza kusintha maganizo. (Yona 3:10–4:11) M’kupita kwa nthawi, Yona anamvetsetsa mfundo imene Yehova anafuna kum’phunzitsa. Ndipo Yehova anafika mpaka pomugwilitsila nchito kulemba nkhaniyi kuti tonsefe tiphunzilepo kanthu.—Aroma 15:4. *

7. Kodi mmene Yehova anacitila zinthu ndi atumiki ake, zimatitsimikizila ciani?

7 Mmene Yehova anacitila zinthu ndi anthu ake, zimatitsimikizila kuti amamvelela cifundo atumiki ake. Iye amaona mavuto amene aliyense wa ife amakumana nawo, pakuti Yehova ‘amadziŵa bwino mtima wa ana a anthu.’ (2 Mbiri 6:30) Iye amadziŵa bwino maganizo athu, mmene timvelela mkati mwa mtima, komanso zolephela zathu. Ndipo “sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile.” (1 Akor. 10:13) Kukamba zoona, mawu amenewa ni olimbikitsa kwambili.

CITSANZO CA YESU PA NKHANI YOONETSA ENA CIFUNDO

8-10. N’zifukwa ziti ziyenela kuti zinathandiza Yesu kukhala na mtima womvelela cifundo ena?

8 Pamene Yesu anali padziko lapansi, anali wacifundo kwambili kwa anthu. Payenela kuti panali zifukwa zitatu zimene zinapangitsa Yesu kukhala wacifundo kwa ena. Coyamba, monga mmene takambila kuciyambi, Yesu anatengela kwambili makhalidwe a Atate ake akumwamba. Mofanana na Atate wake, Yesu anali kukonda anthu. Ngakhale kuti Yesu anali kukondwela na zonse zimene Yehova analenga kudzela mwa iye, zinthu zimene zinali kumusangalatsa kwambili, ‘zinali zokhudzana ndi ana a anthu.’ (Miy. 8:31) Inde, cikondi n’cimene cinasonkhezela Yesu kumvelela anthu cifundo.

9 Caciŵili n’cakuti, mofanana na Yehova, Yesu anali kukwanitsa kudziŵa za mu mtima mwa anthu. Anali kudziŵa zolinga zawo komanso mmene amvelela. (Mat. 9:4; Yoh. 13:10, 11) Conco, Yesu akazindikila kuti anthu ni acisoni, anali kuwamvelela cifundo. Ndipo izi zinali kumulimbikitsa kuti awatonthoze.—Yes. 61:1, 2; Luka 4:17-21.

10 Cacitatu, Yesu anakumanapo na mavuto ena amene anthu a m’nthawi yake anali kukumana nawo. Mwacitsanzo, cioneka kuti iye anabadwila m’banja losauka. Pamene anali kuseŵenza na Yosefe, atate wake omulela, iye anaphunzila kugwila nchito zolemetsa. (Mat. 13:55; Maliko 6:3) Komanso, zioneka kuti Yosefe anamwalila Yesu asanayambe utumiki wake. Conco, n’zoonekelatu kuti Yesu anaona mmene cimaŵaŵila ngati munthu amene umakonda wamwalila. Iye anali kudziŵanso bwino mavuto amene amakhalapo m’banja, ngati anthu ali na zikhulupililo zosiyana. (Yoh. 7:5) Zokumana nazo zimenezi na zina, ziyenela kuti zinathandiza Yesu kumvetsetsa mavuto amene anthu ena anali kukumana nawo, komanso mmene anali kumvelela.

Yesu atamvela cifundo munthu wogontha anacoka naye pagulu na kupita naye pambali kuti am’cilitse (Onani ndime 11)

11. Ni pa zocitika ziti pamene cifundo ca Yesu cinaonekela kwambili? Fotokozani. (Onani cithunzi pacikuto.)

11 Yesu anaonetsa bwino kwambili cifundo cake mwa kucita zozizwitsa. Iye sanacite zozizwitsa mwamwambo cabe. Koma anali ‘kugwidwa cifundo,’ poona anthu ovutika. (Mat. 20:29-34; Maliko 1:40-42) Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yesu anali kumvelela pamene anatenga munthu wogontha, kucoka naye pa gulu la anthu kuti akamucilitse. Ganizilaninso mmene anamvelela pamene anali kuukitsa mwana yekhayo wa mkazi wa masiye. (Maliko 7:32-35; Luka 7:12-15) Yesu anawamvelela cifundo anthu amenewa, ndipo anafuna kuwathandiza.

12. Mogwilizana ndi Yohane 11:32-35, kodi Yesu anaonetsa bwanji cifundo kwa Marita na Mariya?

12 Yesu anamvelelanso cifundo Marita na Mariya. Iye “anagwetsa misozi” ataona cisoni cimene iwo anali naco kaamba ka imfa ya m’bale wawo Lazaro. (Ŵelengani Yohane 11:32-35.) Sikuti iye anagwetsa misozi pa cifukwa cabe cakuti anataikilidwa bwenzi lake lapamtima. Ndi iko komwe, iye anali kudziŵa kuti adzamuukitsa Lazaro. Yesu anagwetsa misozi cifukwa anakhudzidwa kwambili ataona cisoni cacikulu cimene mabwenzi ake anali naco cifukwa ca imfa ya Lazaro.

13. Kodi kudziŵa kuti Yesu anali wacifundo n’kolimbikitsa bwanji kwa ife?

13 Kudziŵa kuti Yesu anali wacifundo n’kolimbikitsa ngako kwa ife. Timam’konda cifukwa cakuti anali kumvelela cifundo anthu ena. (1 Pet. 1:8) Timalimbikitsidwa kudziŵa kuti iye, tsopano akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndipo posacedwa adzacotsapo mavuto onse. Popeza kuti Yesu anakhalapo munthu padziko lapansi, iye ndiye woyenelela kwambili kupulumutsa anthu ku mavuto onse amene ulamulilo wa Satana wabweletsa. Ndithudi, ndife odala kukhala na Wolamulila amene ‘amatimvela cisoni pa zofooka zathu.’—Aheb. 2:17, 18; 4:15, 16.

TENGELANI YEHOVA NA YESU PA NKHANI YOONETSA CIFUNDO

14. Malinga n’zimene Aefeso 5:1, 2 imakamba, kodi citsanzo ca Yehova na Yesu cimatilimbikitsa kucita ciani?

14 Tikaganizila citsanzo cimene Yehova na Yesu amapeleka pa nkhani ya kuonetsa cifundo, nafenso timalimbikitsidwa kukulitsa khalidwe limeneli. (Ŵelengani Aefeso 5:1, 2.) N’zoona kuti sitingathe kudziŵa za mu mtima mwa munthu. Ngakhale n’telo, tingakwanitse kuzindikila zosoŵa za ena komanso mmene akumvelela. (2 Akor. 11:29) Mosiyana ndi anthu odzikonda amene ali m’dzikoli, ife timapewa kuganizila ‘zofuna zathu zokha, koma timaganizilanso zofuna za ena.’—Afil. 2:4.

(Onani ndime 15-19) *

15. N’ndani maka-maka amene afunika kuonetsa khalidwe la cifundo?

15 Akulu mu mpingo ndiwo afunika kuonetsa kwambili khalidwe la cifundo. Iwo amadziŵa kuti adzayankha mlandu kaamba ka mmene amasamalila nkhosa za Mulungu zimene zaikizidwa m’manja mwawo. (Aheb. 13:17) Kuti akulu akwanitse kuthandiza bwino Akhristu anzawo, afunika kukhala acifundo. Kodi iwo angaonetse bwanji kuti ni acifundo?

16. Kodi mkulu wacifundo amacita ciani? Ndipo n’cifukwa ciani kucita zimenezo n’kofunika?

16 Mkulu wacifundo amapeza nthawi yokambilanako na abale na alongo. Amawafunsa mafunso na kuwamvetsela mwachelu na moleza mtima. Kucita izi n’kofunika kwambili, maka-maka ngati m’bale kapena mlongo afuna kum’fotokozela maganizo ake na kumuuza mmene akumvelela, koma akulephela kufotokoza bwino-bwino. (Miy. 20:5) Ngati mkulu amapatula nthawi yocezako na Akhristu anzake, iwo amayamba kum’dalila kwambili, ndipo ubwenzi na cikondi pakati pa iye na Akhristuwo zimalimba.—Mac. 20:37.

17. Kodi abale na alongo ambili amati ni khalidwe lanji limene amakonda kwambili mwa akulu? Fotokozani citsanzo.

17 Abale na alongo ambili amakamba kuti cifundo ndilo khalidwe limene amakonda kwambili mwa akulu. Cifukwa ciani? Mlongo Adelaide anati: “Akulu acifundo savuta kukamba nawo, cifukwa umacita kudziŵilatu kuti adzakumvetsetsa.” Anakambanso kuti: “Zimene amacita ngati ukamba nawo, zimacita kuonetselatu kuti amakudela nkhawa.” M’bale wina poyamikila mmene mkulu anaonetsela cifundo kwa iye, anati: “Pamene n’nali kufotokoza vuto langa kwa mkuluyo, n’naona misozi ikulenjeka m’maso mwake. Sinidzaiŵala zimenezi.”—Aroma 12:15.

18. Tingakulitse bwanji khalidwe la cifundo?

18 Koma sikuti akulu okha ndiwo afunika kuonetsa cifundo kwa ena. Tonse tifunika kukulitsa khalidwe limeneli. Motani? Yesetsani kuganizila zimene anthu a m’banja mwanu komanso Akhristu anzanu akupitamo. Muzicita cidwi na Akhristu acinyamata mu mpingo, odwala, okalamba, komanso amene ataikilidwa okondedwa awo mu imfa. Afunseni mmene zinthu zikuyendela mu umoyo wawo. Amvetseleni mwachelu pamene afotokoza nkhawa zawo. Onetsani kuti mukumvetsetsa mavuto amene akupitamo. Citani zilizonse zimene mungathe kuti muwathandize. Tikacita zimenezi, ndiye kuti tikuonetsa cikondi ceni-ceni m’zocita zathu.—1 Yoh. 3:18.

19. N’cifukwa ciani tifunika kukhala ololela pamene tikuthandiza ena?

19 Tifunika kukhala ololela pamene tithandiza ena. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anthu amacita zinthu mosiyana-siyana akakumana na mavuto. Ena amakhala omasuka kukamba mmene amvelela, pamene ena samasuka kufotokoza. Conco, pamene tithandiza ena, tifunika kupewa kuwafunsa mafunso pa nkhani zaumwini. (1 Ates. 4:11) Nthawi zina, munthu angamasuke na kutifotokozela mmene akumvelela. Koma mwina tingaone kuti maganizo ake ni osiyana na mmene ife tionela zinthu. Zikakhala telo, sitifunika kum’tsutsa, koma tiyenela kumvetsetsa mmene iye akumvelela. Tiyenela kukhala ofulumila kumva, koma odekha polankhula.—Mat. 7:1; Yak. 1:19.

20. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

20 Monga taonela, tifunika kuonetsa khalidwe la cifundo mu mpingo. Koma khalidwe labwino limeneli tifunika kulionetsanso mu utumiki wathu. Kodi tingaonetse bwanji cifundo popanga ophunzila? Tidzakambilana funso limeneli m’nkhani yotsatila.

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

^ ndime 5 Yehova na Yesu amamvelela cifundo anthu. M’nkhani ino, tidzakambilana zimene tingaphunzilepo pa citsanzo cawo. Tidzakambilananso cifukwa cake tifunika kumvelela cifundo ena, komanso mmene tingacitile zimenezi.

^ ndime 1 MAWU OFOTOKOZEDWA: “Kumvelana cisoni” kumatanthauza kuyesetsa kuganizila mmene ena akumvelela na kuyesetsa kumvela monga mmene iwo akumvelela. (Aroma 12:15) M’nkhani ino, mawu akuti “kumvelana cisoni,” ndi akuti “kumvelela ena cifundo” ali na tanthauzo lofanana.

^ ndime 6 Yehova anaonetsanso cifundo kwa atumiki ake ena okhulupilika amene anali opsinjika maganizo komanso amantha. Mwacitsanzo, ganizilani za Hana (1 Sam. 1:10-20) Eliya (1 Maf. 19:1-18), ndi Ebedi-meleki (Yer. 38:7-13; 39:15-18).

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Pa misonkhano ya mpingo, timakhala na mipata yambili ya mayanjano olimbikitsa. Tikuona (1) mkulu akukambilana mwaubwenzi na wofalitsa wacicepele ndi amayi ake, (2) m’bale na mwana wake wamkazi athandiza mlongo wacikulile pamene ayenda kukakwela motoka, komanso (3) akulu aŵili amvetsela mwachelu pamene mlongo afunsila malangizo kwa iwo.