NKHANI YOPHUNZIRA 12

Tizichita Zinthu Moganizira Ena

Tizichita Zinthu Moganizira Ena

“Nonsenu mukhale . . . omverana chisoni.”​1 PET. 3:8.

NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Malinga ndi 1 Petulo 3:8, n’chifukwa chiyani timasangalala kukhala ndi anthu amene amachita zinthu motiganizira?

ANTHUFE timasangalala tikakhala ndi anthu amene amatiganizira. Anthuwo amaganizira mmene iwowo akanamvera zikanakhala kuti vutolo akumana nalo ndi iwowo, n’kuzindikira zimene tikuganiza komanso mmene tikumvera. Iwo amazindikira zimene tingafunikire ndipo amatithandiza ngakhale tisanawapemphe. Mwachidule tingati timayamikira kwambiri kukhala ndi anthu amene amachita zinthu moganizira ena * kapena kuti mowamvera chisoni.​—Werengani 1 Petulo 3:8.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama kuti tizichita zinthu moganizira ena?

2 Akhristufe timafunika kuchita zinthu moganizira ena. Koma kuti tichite zimenezi pamafunika khama. Tikutero chifukwa chakuti anthufe si angwiro. (Aroma 3:23) Choncho timafunika kulimbana ndi mtima womangoganizira zofuna zathu. Enafe tingavutike kuchita zinthu moganizira ena chifukwa cha mmene tinakulira kapena chifukwa cha mavuto amene tinakumana nawo. Tingalepherenso kuchita zimenezi chifukwa choti tili m’dziko limene anthu ambiri saganizira anzawo. M’masiku otsiriza ano, anthu ambiri ndi “odzikonda” ndipo amangoganiza za iwo okha basi. (2 Tim. 3:1, 2) Kodi tingatani kuti tizichita zinthu moganizira ena?

3. (a) Tingatani kuti tizitha kuchita zinthu moganizira ena? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Kuti tizitha kuchita zinthu moganizira ena tiyenera kutsanzira Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu. Yehova ndi Mulungu wachikondi ndipo amapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yochita zinthu moganizira ena. (1 Yoh. 4:8) Nayenso Yesu anatengera Atate ake ndendende. (Yoh. 14:9) Yesu ali padzikoli anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhani yosonyeza chifundo. Munkhaniyi tiyamba n’kukambirana chitsanzo cha Yehova ndi Yesu pa nkhani yoganizira ena. Kenako tiona zimene tingachite powatsanzira.

YEHOVA AMACHITA ZINTHU MOGANIZIRA ENA

4. Kodi lemba la Yesaya 63:7-9 limasonyeza bwanji kuti Yehova amaganizira kwambiri atumiki ake?

4 Baibulo limasonyeza kuti Yehova amaganizira kwambiri mmene atumiki ake amamvera. Chitsanzo ndi mmene anamvera pa nthawi imene Aisiraeli ankazunzika. Baibulo limati: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.” (Werengani Yesaya 63:7-9.) Pa nthawi ina, Yehova kudzera mwa mneneri Zekariya ananena kuti anthu ake akamazunzidwa zimakhala ngati akuzunzidwa ndi iyeyo. Yehova anauza atumiki ake kuti: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.” (Zek. 2:8) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yehova amakhudzidwa kwambiri ndi zimene zikuchitikira anthu ake.

Yehova anasonyeza chifundo populumutsa Aisiraeli ku Iguputo(Onani ndime 5)

5. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amathandiza atumiki ake akakumana ndi mavuto.

5 Koma sikuti Yehova amangomva chisoni akaona atumiki ake akuvutika. Iye amawathandiza. Mwachitsanzo, Aisiraeli atazunzika ku ukapolo ku Iguputo, Yehova anamvetsa mavuto awo ndipo anawathandiza. Yehova anauza Mose kuti: “Ndaona nsautso ya anthu anga . . . ndipo ndamva kulira kwawo . . . ndikudziwa bwino zowawa zawo. Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo.” (Eks. 3:7, 8) Yehova anamva chisoni ndi mavuto a anthu ake, choncho anawamasula ku ukapolo. Aisiraeli atakhala m’Dziko Lolonjezedwa kwa zaka zambiri, anaukiridwanso ndi mitundu ina ya anthu. Kodi Yehova anatani? Baibulo limati iye “anali kuwamvera chisoni akamva kubuula kwawo chifukwa cha owapondereza ndi owakankhakankha.” Mtima woganizira ena ndi umene unachititsa Yehova kuti athandize anthu ake. Iye anatumiza oweruza kuti apulumutse Aisiraeli kwa adani awo.​—Ower. 2:16, 18.

6. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amachita zinthu moganizira anthu ngakhale pamene maganizo awo si abwino kwenikweni?

6 Yehova amachitanso zinthu moganizira atumiki ake ngakhale pamene maganizo awo si abwino kwenikweni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yona. Yehova anamutuma kuti akapereke uthenga wachiweruzo kwa anthu a ku Nineve. Anthuwo atalapa, Mulungu sanawawononge. Koma zimenezi sizinasangalatse Yona m’pang’ono pomwe. Iye “anakwiya koopsa” poona kuti zimene analosera sizinachitike. Koma Yehova anamulezera mtima kwambiri ndipo anamuthandiza kuti asinthe maganizo ake. (Yona 3:10–4:11) Kenako Yona anamvetsa maganizo a Yehova ndipo anamugwiritsira ntchito kuti alembe nkhani yakeyi n’cholinga choti ifeyo tiphunzirepo kanthu.​—Aroma 15:4. *

7. Kodi zimene Yehova wakhala akuchita ndi atumiki ake zimasonyeza chiyani?

7 Zimene Yehova wakhala akuchita ndi atumiki ake zimasonyeza kuti ali ndi mtima woganizira ena. Iye amadziwa mavuto amene munthu aliyense akukumana nawo. Yehova ‘amadziwa bwino mtima wa anthu.’ (2 Mbiri 6:30) Iye amadziwa maganizo athu, zimene zili mumtima mwathu komanso zimene sitingathe kuchita. Ndipo ‘sangalole kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapirire.’ (1 Akor. 10:13) Kunena zoona, mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri.

YESU AMACHITA ZINTHU MOGANIZIRA ENA

8-10. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinathandiza Yesu kuti azichita zinthu moganizira ena?

8 Yesu ali padziko lapansi ankachita zinthu moganizira ena. Zikuoneka kuti pali zinthu zitatu zimene zinamuthandiza kuti azichita zimenezi. Choyamba, malinga ndi zimene takambirana kale zija, Yesu amatsanzira Atate ake akumwamba ndendende. Mofanana ndi Atate ake, Yesu amakonda anthu. Yesu ankasangalala ndi zinthu zonse zimene anathandiza Atate ake kuzipanga. Koma zinthu zimene zinkamusangalatsa kwambiri “zinali zokhudzana ndi ana a anthu.” (Miy. 8:31) Chikondi n’chimene chinathandiza Yesu kuti azichita zinthu moganizira ena.

9 Chachiwiri, mofanana ndi Yehova, Yesu ankadziwa zimene zili mumtima mwa munthu. Iye ankadziwa zolinga za anthu komanso mmene akumvera mumtima mwawo. (Mat. 9:4; Yoh. 13:10, 11) Choncho akaona kuti munthu akuvutika mumtima ankamumvera chisoni n’kumuthandiza.​—Yes. 61:1, 2; Luka 4:17-21.

10 Chachitatu, Yesu nayenso anakumanapo ndi mavuto. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti Yesu analeredwa m’banja losauka. Iye anaphunzira kugwira ntchito mwakhama limodzi ndi Yosefe, yemwe anali bambo ake omulera. (Mat. 13:55; Maliko 6:3) Zikuonekanso kuti Yosefe anamwalira Yesu asanamalize utumiki wake padzikoli. Choncho amadziwa mmene zimapwetekera munthu amene umamukonda akamwalira. Yesu anakuliranso m’banja limene munali anthu osiyana zikhulupiriro. (Yoh. 7:5) Zinthu zimene tatchulazi komanso mavuto ena, zinathandiza Yesu kumvetsa mavuto amene anthu ankakumana nawo.

Yesu watengera pambali munthu amene ali ndi vuto losamva asanamuchiritse (Onani ndime 11)

11. Kodi umboni woti Yesu anali ndi mtima woganizira anthu unkaonekera akamachita chiyani? Fotokozani. (Onani chithunzi patsamba loyamba.)

11 Umboni wakuti Yesu anali ndi mtima woganizira ena unkaonekera akamachita zozizwitsa. Sikuti ankangochita zozizwitsa pongofuna kuthana ndi mavuto a anthuwo. Iye ankachitira chifundo anthu amene ankavutika. (Mat. 20:29-34; Maliko 1:40-42) Mwachitsanzo, taganizirani zimene Yesu anachita pochiritsa munthu amene anali ndi vuto losamva komanso poukitsa mwana wa mkazi wamasiye. (Maliko 7:32-35; Luka 7:12-15) Yesu anamvera anthuwo chisoni ndipo anali ndi mtima wofuna kuwathandiza.

12. Kodi lemba la Yohane 11:32-35 limasonyeza bwanji kuti Yesu anamvera chisoni Marita ndi Mariya?

12 Baibulo limasonyeza kuti Yesu anamvera chisoni Marita ndi Mariya. Mwachitsanzo, “Yesu anagwetsa misozi” ataona azimayi awiriwa ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya Lazaro. (Werengani Yohane 11:32-35.) Sikuti analira chifukwa choti mnzake wapamtima wamwalira. Tikutero chifukwa chakuti ankadziwa zoti amuukitsa. Koma analira chifukwa chokhudzidwa ndi chisoni cha anzakewo.

13. Kodi kudziwa zoti Yesu ali ndi mtima woganizira ena kumatilimbikitsa bwanji?

13 Mfundo yakuti Yesu ali ndi mtima woganizira ena ndi yolimbikitsa kwambiri. N’zoona kuti ife si angwiro ngati mmene iye analili. Koma timasangalala tikaganizira mmene iye ankachitira zinthu ndi anthu. (1 Pet. 1:8) Timasangalalanso kudziwa kuti panopa Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo posachedwapa athetsa mavuto onse. Popeza nayenso anakhalapo munthu, iye ndi woyenera kwambiri kuthandiza anthu m’njira yabwino kuti aiwale mavuto onse amene akumana nawo mu ulamuliro wa Satana. Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala ndi Wolamulira amene ‘angatimvere chisoni pa zofooka zathu.’​—Aheb. 2:17, 18; 4:15, 16.

TIZITSANZIRA YEHOVA NDI YESU

14. Mogwirizana ndi Aefeso 5:1, 2, kodi tonsefe timafunitsitsa kuchita chiyani?

14 Tikaganizira zimene Yehova ndi Yesu amachita pothandiza anthu, timafunitsitsa kuwatsanzira kwambiri. (Werengani Aefeso 5:1, 2.) N’zoona kuti ifeyo sitingadziwe zimene zili mumtima mwa anthu. Koma tikhoza kuzindikira mmene akumvera komanso zimene akufunikira. (2 Akor. 11:29) Mosiyana ndi anthu odzikonda am’dzikoli, ifeyo timayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afil. 2:4.

(Onani ndime 15-19) *

15. Ndani ayenera kuyesetsa kwambiri kuti azichita zinthu moganizira ena?

15 Akulu mumpingo ndi amene ayenera kuyesetsa kwambiri kuti azichita zinthu moganizira ena. Iwo amadziwa kuti adzayankha mlandu pa zimene amachitira nkhosa zimene akuziyang’anira. (Aheb. 13:17) Kuti akulu athandize bwino Akhristu anzawo, amafunika kukhala omvetsa. Ndiye kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amaganizira ena?

16. Kodi mkulu woganizira ena amatani, nanga zimenezi ndi zofunika bwanji?

16 Mkulu woganizira ena amapeza nthawi yoti acheze ndi abale ndi alongo. Iye amafunsa mafunso n’kumamvetsera mwatcheru zimene munthu akulankhula. Zimenezi zimathandiza kwambiri ngati m’bale kapena mlongo akufuna kufotokoza zimene zili mumtima mwake koma akusowa mawu oti anene. (Miy. 20:5) Mkulu akamapeza nthawi yocheza ndi abale ndi alongo amayamba kuwakonda komanso kugwirizana nawo.​—Mac. 20:37.

17. Kodi abale ndi alongo ambiri amanena kuti amasangalala ngati akulu ali otani? Perekani chitsanzo.

17 Abale ndi alongo ambiri amanena kuti amasangalala kwambiri ngati akulu ali ndi mtima woganizira ena. N’chifukwa chiyani amatero? Mlongo wina dzina lake Adelaide ananena kuti: “Zimakhala zosavuta kulankhula ndi akulu otere chifukwa umadziwiratu kuti akumvetsa. Ukamalankhula nawo umachita kuoneratu kuti amakuganizira ndiponso akukumvetsa.” Pa nkhani imeneyi, m’bale wina anati: “Tsiku lina nditafotokozera mkulu wina mavuto anga, ndinangoona misozi ikulengeza m’maso mwake. Iye anamvetsa zimene ndinkakumana nazo ndipo sindidzaiwala zimene zinachitikazi.”​—Aroma 12:15.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi mtima woganizira ena?

18 Komabe si akulu okha amene amafunika kuchita zinthu moganizira ena. Tonsefe tiyenera kukhala ndi mtima umenewu. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kumvetsa mavuto amene anthu a m’banja lathu komanso mumpingo akukumana nawo. Tiyenera kuchita zinthu moganizira achinyamata, anthu odwala, okalamba komanso amene aferedwa. Ndi bwino kuwafunsa mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Akamafotokoza mavuto awo tiziwamvetsera bwino. Tiziwasonyeza kuti tikumvetsa mavuto amene akukumana nawo. Kenako tiziwathandiza m’njira yoyenera. Tikamatero tidzasonyeza kuti tili ndi chikondi chenicheni.​—1 Yoh. 3:18.

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mozindikira pothandiza ena?

19 Koma tiyenera kuchita zinthu mozindikira pothandiza ena. Tikutero chifukwa chakuti zimene wina angachite akakumana ndi mavuto zimakhala zosiyana ndi zimene wina angachite. Ena amamasuka kufotokoza mavuto awo pomwe ena samasuka. Ndiye pothandiza anthu tiyenera kupewa kufunsa mafunso amene ena angachite nawo manyazi. (1 Ates. 4:11) Munthu amene akufotokoza mavuto ake akhozanso kunena zinthu zimene ifeyo sitingagwirizane nazo. Zimenezi zikachitika tiyenera kungovomereza kuti ndi mmene iwowo akumvera. Tiyenera kukhala ofulumira kumva koma odekha polankhula.​—Mat. 7:1; Yak. 1:19.

20. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

20 Tiyeneranso kuchita zinthu moganizira ena tikakhala mu utumiki. Munkhani yotsatira, tidzakambirana mmene tingachitire zinthu moganizira ena tikamaphunzitsa anthu.

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

^ ndime 5 Yehova ndi Yesu amachita zinthu moganizira mmene anthu ena akumvera mumtima mwawo. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite powatsanzira. Tikambirananso chifukwa chake tiyenera kuchita zinthu moganizira ena komanso mmene tingachitire zimenezo.

^ ndime 1 MATANTHAUZO A MAWU ENA: Kuchita zinthu moganizira ena kumatanthauza kumvetsa mavuto amene anthu ena akukumana nawo komanso kuzindikira mmene akumvera mumtima mwawo.​—Aroma 12:15.

^ ndime 6 Yehova anathandizanso mokoma mtima anthu amene ankapwetekedwa kwambiri mtima kapena kuchita mantha. Mwachitsanzo, anathandiza Hana (1 Sam. 1:10-20), Eliya (1 Maf. 19:1-18) komanso Ebedi-meleki (Yer. 38:7-13; 39:15-18).

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Tikapita kumisonkhano timakhala ndi mwayi wocheza ndi anthu. Pachithunzipa pali (1) mkulu akulankhula ndi kamnyamata komanso mayi ake, (2) bambo ndi mwana wawo akuthandiza mlongo wachikulire kuti akakwere galimoto, (3) akulu awiri akumvetsera bwino pamene mlongo akupempha malangizo pa vuto lake.