Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 13

Onetsani Cifundo Pamene Muli mu Ulaliki

Onetsani Cifundo Pamene Muli mu Ulaliki

“Anawamvela cifundo . . . Conco anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.”—MALIKO 6:34.

NYIMBO 70 Funa-funani Oyenelela

ZA M’NKHANI INO *

1. Ni mbali ina iti ya umunthu wa Yesu imene imaticititsa cidwi kwambili? Fotokozani.

MBALI imodzi yocititsa cidwi kwambili ya umunthu wa Yesu ni yakuti, iye amamvetsa mavuto amene ife anthu opanda ungwilo timakumana nawo. Pamene iye anali padziko lapansi, anali ‘kusangalala ndi anthu amene anali kusangalala,’ komanso ‘kulila ndi anthu amene anali kulila.’ (Aroma 12:15) Mwacitsanzo, tsiku lina Yesu anatumiza ophunzila ake 70 kuti akalalikile, ndipo ulaliki unayenda bwino. Atabwelako ali osangalala, nayenso Yesu “anakondwela kwambili mwa mzimu woyela.” (Luka 10:17-21) Koma panthawi ina, Yesu ataona mmene imfa ya Lazaro inakhudzila acibale na mabwenzi ake, “anadzuma povutika mumtima ndi kumva cisoni.”—Yoh. 11:33.

2. N’ciani cinathandiza Yesu kuonetsa cifundo kwa anthu?

2 N’ciani cinathandiza Yesu, munthu wangwilo, kuti azimvelela cifundo kwambili anthu opanda ungwilo? Cacikulu cimene cinam’thandiza n’cakuti anali kukonda anthu. Monga tinakambila m’nkhani yapita, Malemba amakamba kuti ‘zinthu zimene zinali kumusangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.’ (Miy. 8:31) Cikondi cake pa anthu, cinam’sonkhezela kudziŵa bwino mmene anthuwo amaganizila. Mtumwi Yohane anati: “[Yesu] anali kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu.” (Yoh. 2:25) Yesu anali na cifundo cacikulu kwa anthu. Iwo anali kuona kuti iye anali kuwakonda, ndipo izi zinawasonkhezela kumvetsela uthenga wa Ufumu umene anali kulalikila. Nafenso ngati tikonda kwambili anthu, tidzakwanitsa kuwathandiza mokwanila mu ulaliki.—2 Tim. 4:5.

3-4. (a) Ngati timamvelela ena cifundo, kodi nchito yathu yolalikila tidzayamba kuiona bwanji? (b) Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani?

3 Mtumwi Paulo anadziŵa kuti anali na udindo wolalikila. Na ife tili na udindo umenewu. (1 Akor. 9:16) Koma ngati timamvelela ena cifundo, sitidzaona utumiki wathu monga udindo cabe. Tidzauona monga mwayi wathu woonetsa kuti timakonda anthu, ndipo ndife ofunitsitsa kuwathandiza. Tidziŵa kuti “kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Tikamalalikila na colinga cofuna kuthandiza anthu, tidzayamba kuikonda kwambili nchito yolalikila.

4 M’nkhani ino, tidzakambilana mmene tingaonetsele cifundo kwa ena mu ulaliki. Koma coyamba, tidzakambilana zimene tiphunzilapo pa citsanzo ca Yesu coonetsa cifundo kwa anthu. Ndiyeno, tidzakambilana njila zinayi za mmene tingatsatilile citsanzo cake.—1 Pet. 2:21.

YESU ANALI KUONETSA CIFUNDO MU ULALIKI

Cifundo cinasonkhezela Yesu kulalikila uthenga wacitonthozo (Onani ndime 5-6)

5-6. (a) Kodi Yesu anamvelela cifundo anthu otani? (b) Mogwilizana na ulosi wa pa Yesaya 61:1, 2, n’cifukwa ciani Yesu anamvelela cifundo anthu amene anali kuŵalalikila?

5 Ganizilani citsanzo ca mmene Yesu anaonetsela cifundo. Pa nthawi ina, iye na ophunzila ake analema kwambili pambuyo polalikila uthenga wabwino kwa nthawi yaitali. Iwo anasoŵa ngakhale “nthawi . . . yoti adye cakudya.” Conco, Yesu anapita na ophunzila ake “kwaokhaokha kumalo opanda anthu” kuti ‘akapumule pang’ono.’ Koma khamu la anthu linathamangila kumene Yesu na ophunzila ake anali kupita. Pamene iye anafika kumeneko n’kuona anthuwo, kodi anacita ciani? Baibo imati: “Anawamvela cifundo, * cifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Conco, anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.”—Maliko 6:30-34.

6 N’ciani cinapangitsa Yesu kuwamvelela cifundo anthu amenewo? Baibo imati iye anaona kuti “[anthuwo] anali ngati nkhosa zopanda m’busa.” Mwina, Yesu anaona kuti ena mwa anthuwo anali osauka, ndipo anali kugwila nchito zolemetsa kuti asamalile mabanja awo. N’kuthekanso kuti ena anali na cisoni cifukwa cotaikilidwa okondedwa awo mu imfa. Ngati zinali conco, Yesu ayenela kuti anamvetsa mavuto awo. Monga tinakambilana m’nkhani yapita, iye ayenela kuti anakumanako na mavuto amenewa. Conco, cifundo cimene Yesu anali naco pa anthu, cinam’sonkhezela kuwauzako uthenga wacitonthozo.—Ŵelengani Yesaya 61:1, 2.

7. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu?

7 Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yesu cimeneci? Mofanana na Yesu, timakhala na anthu amene ali “ngati nkhosa zopanda m’busa.” Iwo akulimbana na mavuto ambili. Koma ife tili na uthenga wa Ufumu umene ungawatonthoze. (Chiv. 14:6) Conco, potengela citsanzo ca Mbuye wathu, timalalikila uthenga wabwino cifukwa ‘timamvela cisoni anthu onyozeka ndi osauka.’ (Sal. 72:13) Timamvelela cifundo anthu, ndipo timafuna kucitapo kanthu kuti tiwathandize.

MMENE TINGAONETSELE CIFUNDO

Muziganizila zosoŵa za munthu aliyense payekha (Onani ndime 8-9)

8. Ni njila imodzi iti imene tingaonetsele cifundo kwa anthu mu ulaliki? Fotokozani citsanzo.

8 N’ciani cingatithandize kuti tizionetsa cifundo kwa anthu amene timawalalikila? Tifunika kuganizila mmene iwo akumvelela, na kucita nawo zinthu mmene ife tingafunile kuti ena aticitile. * (Mat. 7:12) Nanga tingacite bwanji zimenezi? Tiyeni tikambilane njila zinayi. Yoyamba, muziganizila zosoŵa za munthu aliyense payekha. Nchito yathu yolalikila ili monga ya udokotala. Dokotala wabwino amaganizila zovuta za wodwala aliyense payekha. Iye amafunsa mafunso na kumvetsela mwachelu pamene wodwalayo afotokoza mmene amvelela. M’malo mongolemba mankhwala msanga-msanga, dokota wabwino amayesetsa kudziŵa zowonjezeleka zokhudza vuto la wodwalayo, ndipo pambuyo pake amapeleka thandizo loyenelela. Mofananamo, sitifunika kuseŵenzetsa ulaliki umodzi-modzi kwa munthu aliyense amene takumana naye mu ulaliki. M’malomwake, tiyenela kumasintha-sintha ulaliki wathu kuti ugwilizane na anthu amene tikuwalalikila.

9. Kodi tifunika kupewa kuganiza ciani? Nanga ni njila yabwino iti imene tingatsatile kuti tidziŵe zambili zokhudza munthu?

9 Tikakumana na munthu mu ulaliki, sitiyenela kuganiza kuti tidziŵa kale za umoyo wake, zimene amakhulupilila, komanso cifukwa cake amazikhulupilila. (Miy. 18:13) M’malomwake, tiyenela kum’funsa mafunso mwaluso kuti tim’dziŵe bwino, komanso kuti tidziŵe zimene amakhulupilila. (Miy. 20:5) Ngati n’zololeka pa cikhalidwe canu, mungam’funseko zokhudza banja lake, nchito yake, zimene wakumana nazo mu umoyo, na mmene amaonela zinthu zina. Ngati tifunsa ena mafunso mwanjila imeneyi, zimatithandiza kudziŵa bwino zosoŵa zawo. Tikadziŵa zimenezo, ndiye kuti mofanana na Yesu, tidzawamvelela cifundo na kuwathandiza mogwilizana na zosoŵa zawo.—Yelekezelani na 1 Akorinto 9:19-23.

Ganizilani mmene zinthu zilili mu umoyo wa munthu amene mufuna kum’lalikila (Onani ndime 10-11)

10-11. Mogwilizana na lemba la 2 Akorinto 4:7, kodi njila yaciŵili imene tingaonetsele cifundo kwa ena ni iti? Fotokozani citsanzo.

10 Njila yaciŵili, muziyesetsa kuganizila mmene zinthu zilili mu umoyo wawo. N’zotheka kumvetsetsa mavuto amene anthu ena amakumana nawo, cifukwa pokhala anthu opanda ungwilo, nafenso timakumana na mavuto. (1 Akor. 10:13) Tidziŵa kuti umoyo m’dongosolo lino la zinthu ni wovuta kwambili. Ndipo ife timakwanitsa kupilila cifukwa ca thandizo la Yehova. (Ŵelengani 2 Akorinto 4:7, 8.) Ganizilani za anthu amene sali paubwenzi wolimba na Yehova. Ziyenela kuti zimakhala zovuta kwambili kwa iwo kupilila mavuto popanda thandizo la Yehova. Mofanana na Yesu, timawamvelela cifundo anthu amenewo, ndipo timafunitsitsa kuwauzako “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”—Yes. 52:7.

11 Ganizilani citsanzo ca m’bale wina, dzina lake Sergey. Asanaphunzile coonadi, iye anali wamanyazi komanso anali wosamasuka ndi anthu. M’kupita kwa nthawi, anayamba kuphunzila Baibo. Sergey anati: “Pamene n’nayamba kuphunzila Baibo, n’nazindikila kuti Akhristu ali na udindo wouzako ena zimene amakhulupilila. Kukamba zoona, n’nali kuona kuti siningakwanitse kulalikila.” Koma m’baleyu anayamba kuganizila za anthu amene sanamvelepo coonadi, ndipo anazindikila kuti umoyo wawo uyenela kuti ni wovuta cifukwa sadziŵa Yehova. Iye anati: “Mfundo zatsopano za m’Baibo zimene n’nali kuphunzila, zinanibweletsela cimwemwe coculuka komanso mtendele wa m’maganizo. N’nazindikila kuti anthu ena nawonso afunika kuphunzila mfundo za coonadi zimenezi.” Pamene Sergey anakulitsa khalidwe la cifundo, m’pamenenso anakhala wolimba mtima kulalikila ena. Iye anati: “N’zocititsa cidwi kuti pamene n’nayamba kuuzako ena za m’Baibo, vuto langa la manyazi linacepa kwambili. Komanso zinalimbitsa cikhulupililo canga.” *

Zingatenge nthawi kwa ena kuti apite patsogolo mwauzimu (Onani ndime 12-13)

12-13. N’cifukwa ciani tifunika kukhala oleza mtima kwa anthu amene timaphunzila nawo mu ulaliki? Fotokozani citsanzo.

12 Njila yacitatu, muzileza mtima na anthu amene mumaphunzila nawo. Kumbukilani kuti iwo akhoza kukhala kuti sanaganizilepo mfundo zina za coonadi ca m’Baibo zimene ife timadziŵa bwino. Ndipo ambili mwa iwo ali na zikhulupililo zozika mizu kwambili. Iwo angaone kuti zikhulupililo za cipembedzo cawo zimawagwilizanitsa na mabanja awo, cikhalidwe cawo, ndi anthu a m’dela lawo. Kodi tingawathandize bwanji?

13 Ganizilani citsanzo ici: Kodi anthu amacita ciani ngati afuna kucotsa buliji yakale komanso yosalimba kuti amange ina? Nthawi zambili, buliji yatsopano imamangidwa pamene buliji yakale ikali kugwila nchito. Akamaliza kumanga buliji yatsopanoyo, m’pamene amacotsa yakale ija. Mofananamo, sitiyenela kungouza anthu kuti aleke zikhulupililo zawo “zakale” zimene amazikonda kwambili. Koma coyamba, tifunika kuwathandiza kumvetsetsa komanso kukonda mfundo za coonadi ca m’Baibo, zimene poyamba kuphunzila sanali kuzidziŵa. Akayamba kukonda mfundo za coonadi, m’pamene angakhale okonzeka kuleka zikhulupililo zawo zakale. Zingatenge nthawi yaitali kuti tithandize munthu kupanga masinthidwe amenewa.—Aroma 12:2.

14-15. Kodi tingawathandize bwanji anthu amene amadziŵa zocepa, kapena amene sadziŵa ciliconse cokhudza ciyembekezo cokakhala na moyo wamuyaya pa dziko lapansi m’paradaiso? Fotokozani citsanzo.

14 Ngati timaleza mtima ndi anthu amene timawalalikila, sitidzayembekezela kuti akangomvetsela coonadi ca m’Baibo, nthawi yomweyo adzamvetsetsa kapena kulabadila. M’malomwake, cifukwa cowamvelela cifundo, tidzayesetsa kuwathandiza kuganizila mosamala zimene Baibo imakamba. Ndipo m’kupita kwa nthawi, angamvetsetse mfundo za coonadi. Mwacitsanzo, ganizilani mmene tingathandizile munthu kumvetsa za ciyembekezo cathu cokakhala na moyo wamuyaya padziko lapansi m’paradaiso. Anthu ambili sadziŵa zambili zokhudza ciphunzitso cimeneci, ndipo ena sacidziŵa n’komwe. Ena amakhulupilila kuti imfa ni mapeto a zonse. Ndipo ena amaganiza kuti anthu onse abwino amayenda kumwamba. Kodi tingawathandize bwanji?

15 M’bale wina anafotokoza mmene amathandizila anthu kumvetsetsa za ciyembekezo cimeneci. Coyamba, amaŵelenga Genesis 1:28. Kenako, amafunsa mwininyumba kuti, ‘Kodi Mulungu anafuna kuti anthu azikhala kuti, nanga anafuna kuti akhale na umoyo wotani?’ Ambili amayankha kuti, “Anafuna kuti tizikhala padziko lapansi, na umoyo wacimwemwe.” Ndiyeno, m’baleyo amaŵelenga Yesaya 55:11, na kufunsa ngati colinga ca Mulungu cinasintha. Nthawi zambili, mwininyumba amayankha kuti sicinasinthe. Potsiliza, m’baleyo amaŵelenga Salimo 37:10, 11, na kufunsa mwininyumba mmene umoyo wa anthu udzakhalila kutsogolo. Mwa kuseŵenzetsa njila imeneyi, m’baleyu wathandiza anthu ambili ndithu kudziŵa kuti Mulungu amafuna kuti anthu abwino akakhale na moyo wosatha pa dziko lapansi m’Paradaiso.

Kucita zinthu zocepa zoonetsa kukoma mtima, monga kutumizila ena kalata yacilimbikitso, kungakhale na zotulukapo zabwino kwambili (Onani ndime 16-17)

16-17. Malinga n’zimene Miyambo 3:27 imakamba, n’zinthu zina ziti zimene tingacite poonetsa cifundo kwa ena? Fotokozani citsanzo.

16 Njila yacinayi, muzisakila mipata yoonetsela kuti mumaganizila ena na kuwakonda. Mwacitsanzo, ngati tafika pa nyumba ya munthu pa nthawi yolakwika, tingapepese na kumuuza kuti tidzabwelanso pa nthawi ina. Bwanji ngati taona kuti mwininyumba afunikila thandizo pa kanchito kenakake kocepa? Kapena bwanji ngati tapeza munthu wina amene sacoka panyumba cifukwa ca kudwala kapena ukalamba, ndipo afuna wina woti amucitile kanchito kenakake? Zikakhala telo, tingadzipeleke kuti tiwathandize.—Ŵelengani Miyambo 3:27.

17 Mwacitsanzo, mlongo wina anacitila banja lina zinthu zooneka ngati zocepa, ndipo panakhala zotulukapo zabwino kwambili. Iye analembela banjalo kalata yacitonthozo kaamba ka imfa ya mwana wawo. M’kalatayo, analembamo mfundo zolimbikitsa za m’Baibo na mavesi owatonthoza. Kodi iwo anakhudzidwa bwanja na kalatayo? Mayi wa mwanayo anati: “Dzulo n’nali na cisoni cosaneneka, koma kalata imene munatilembela inatitonthoza kwambili. Nicita kusoŵa cokamba poyamikila cifukwa ca kalata yotonthoza kwambili imeneyi, moti dzulo n’naiŵelenga mwina maulendo oposa 20. Kukamba zoona, kalatayi inatitonthoza komanso inatilimbikitsa kwambili. Niyamikila kucokela pansi pa mtima.” Nafenso tiyenela kuyesetsa kumvetsetsa mmene anthu amene akumana na mavuto amvelela. Tikatelo, mosapeneka konse, zotulukapo zake zidzakhala zabwino.

ZINDIKILANI MALILE A ZIMENE MUNGATHE KUCITA

18. Mogwilizana na 1 Akorinto 3:6, 7, kodi tifunika kukumbukila ciani ponena za nchito yathu yolalikila? Ndipo n’cifukwa ciani?

18 Pamene tigwila nchito yathu yolalikila, tifunika kukumbukila kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kucita. Timaphunzitsa anthu coonadi ponena za Mulungu, koma Yehova ndiye amacita mbali yaikulu panchitoyi. (Ŵelengani 1 Akorinto 3:6, 7.) Iye ndiye amakoka anthu. (Yoh. 6:44) Cinanso, kuti munthu alabadile uthenga wabwino, kweni-kweni zimadalila mmene mtima wake ulili. (Mat. 13:4-8) Tisaiŵale kuti anthu ambili m’nthawi ya Yesu sanalabadile uthenga wake, ngakhale kuti iye anali Mphunzitsi waluso kuposa munthu aliyense. Conco, sitifunika kugwa mphwayi ngati anthu ambili amene timawalalikila, salabadila uthenga wathu.

19. Kodi pamakhala mapindu otani ngati timvelela cifundo ena mu ulaliki?

19 Ngati timvelela cifundo ena mu ulaliki, padzakhala zotulukapo zabwino. Tidzayamba kukondwela kwambili na nchito imeneyi. Ndipo tidzakhala na cimwemwe coculuka cimene cimabwela cifukwa copatsa. Komanso, cidzakhala cosavuta kuti anthu amene ali “ndi maganizo abwino, amene angawathandize kukapeza moyo wosatha” amvetsele uthenga wabwino. (Mac. 13:48) Conco, “ngati tingathe, tiyeni ticitile onse zabwino.” (Agal. 6:10) Tikatelo, tidzakhala na cimwemwe podziŵa kuti zocita zathu zikupeleka ulemelelo kwa Atate wathu wakumwamba.—Mat. 5:16.

NYIMBO 64 Timasangalala Kuthandiza pa Nchito Yokolola

^ ndime 5 Ngati timaonetsa ena cifundo mu ulaliki, tingawonjezele cimwemwe cathu, komanso anthu angakhale ofunitsitsa kumvetsela uthenga wathu. N’cifukwa ciani zili conco? M’nkhani ino, tidzakambilana zimene tiphunzilapo pa citsanzo ca Yesu. Tidzakambilananso njila zinayi zimene tingaonetsele cifundo kwa anthu amene timapeza mu ulaliki.

^ ndime 5 MAWU OFOTOKOZEDWA: Liwu lakuti cifundo, limatanthauza kumvelela cisoni munthu amene wakumana na mavuto, kapena amene akuzunzidwa. Cifundo cimasonkhezela munthu kucita zilizonse zimene angathe kuti athandize ena.

^ ndime 8 Onani nkhani yakuti, “Muzionetsa Khalidwe Lopambana mu Ulaliki” mu Nsanja ya Mlonda ya May 1, 2014.

^ ndime 11 Onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 2011, peji 21-22.